Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 9/8 tsamba 28-30
  • Kufunafuna Kwanga Dziko Labwinopo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufunafuna Kwanga Dziko Labwinopo
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chonulirapo Changa—Mfuti Yokaphera
  • Moyo Wachipembedzo—Ziyembekezo Poyerekezera ndi Zenizeni
  • Ntchito Yanga Yandale Zadziko
  • Moyo Wanga Wamtseri—Chogwiritsa Mwala Chachikulu Koposa
  • Posinthira
  • Umunthu Watsopano Wachikristu Ulowa Mmalo mwa Chiwawa
  • Mmene Ndinaphera Ludzu la Mawu a Mulungu
    Galamukani!—2003
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Chowonadi cha Baibulo Chimasula Mvirigo m’Bolivia
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Baibulo Limasintha Anthu
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 9/8 tsamba 28-30

Kufunafuna Kwanga Dziko Labwinopo

Monga momwe yasimbidwira ndi yemwe kale anali mvirigo Wachikatolika

DZIKO labwinopo—kodi limenelo linali lotheka? Ndithudi dziko lodzala ndi udani, chiwawa, umbombo, chivundi, chisalungamo, ndi mavuto sindilo dziko limene Mulungu analinganiza pamene analilenga. Payenera kukhala dziko labwinopo. Ngati limenelo linali lotheka, pamenepo ndinali wotsimikiza kuthandizira kulidzetsa.

Ndinabadwira ndi kukulira m’chigawo cha Corrientes, Argentina, malo otchuka ndi kulambira kwake Namwali wa ku Itatí. Anthuwo ali Akatolika, ali opembedzetsa, ndipo amapanga maulendo ambiri chaka chirichonse okalambira namwali ameneyo. Ndinali pakati pawo. Kuyambira paubwana ndinali ndi chikhumbo cha kudziŵa Mulungu ameneyu amene zambiri zinali kunenedwa ponena za iye, koma atate wanga anandikaniza kukafika pamakalasi akatekisima. Pambuyo pake, pamene ndinali msungwana, atate wanga anafikira kukhala chidakwa, chifukwa cha mayanjano awo oipa. Tonsefe tinavutika koma makamaka amayi wanga, amene anatukwanidwa ndi kumenyedwa. Monga chotulukapo, ndinafikira podana ndi amuna, ndikumalingalira amuna onse kukhala oipa ndi osalingalira.

Chonulirapo Changa—Mfuti Yokaphera

Komabe, sukulu inandipangitsa kukulitsa makhalidwe abwino. Ndinaphunzira mwachangu ndi mwakhama, ndikumalandira madiploma a kusoka ndi maphunziro azamalonda ndipo pambuyo pake ndikumamaliza sukulu ndi magiredi apamwamba monga mphunzitsi. Zikhumbo zanga zofunika koposa zinali kuyamba kukwaniritsidwa: kupezedwa kwa maina aulemu ndi madiploma amene akandiwonjola pagoli la atate. Panthaŵi imodzimodziyo, ndinapanga makonzedwe a kugwira ntchito zolimba kotero kuti ndiwongolere mkhalidwe wa amayi ndiyeno—kugula mfuti yodzaphera atate!

Zimenezo, ndithudi, sizinandisangalatse konse, sizinadzetse mtendere ndi chimwemwe. Mmalo mwake, ndinadziwona kukhala ngati nyama yoikidwa m’chikwere. Ndinali wausinkhu wa zaka 20 ndipo ndinadzipeza ndiri muukonde wopanda potulukira.

Moyo Wachipembedzo—Ziyembekezo Poyerekezera ndi Zenizeni

Pafupifupi panthaŵi imeneyi ndinayamba kugwirizana ndi avirigo ndiponso ndi Akomonisti. Mbali zonse ziŵiri zinayesa kundikakamiza kulandira malingaliro awo. Koma lingaliro la kuthandiza aumphaŵi m’maiko akutali onga Afirika ndi Asiya linandipangitsa kusankha malo a avirigo.

Kwazaka 14 ndinakhala m’malo a avirigo. Moyo wanga m’malo a avirigo unali wabwino, wabata, ndi wamtendere. Kufikira pamene ndinayamba kugwira ntchito ndi ansembe okhala ndi chiphunzitso chozikidwa pa kuyesa kutukula makhalidwe azachuma ndi a anthu sindinazindikire kusiyana pakati pa mtundu wa moyo umene avirigofe tinakhala nawo ndi moyo wa anthu wamba—moyo wopweteka ndi wachisalungamo umene anthu anavutika nawo m’goli lopsinja la apamwamba ndi amphamvu.

M’dongosolo langa lachipembedzo, la Theresian Carmelite Missionaries, zambiri zinanenedwa ponena za chiweruzo cholungama, koma akulu anga anawonekera kukhala akuchinyalanyaziratu m’zochita zawo ndi ena. Ziŵalo za gulu la aphunzitsi zinalandira malipiro ochepa kwambiri koposa mlingo wolamulidwa ndi boma, popandiratu mapindu kaamba ka iwo eni ndi mabanja awo, ndipo zinkachotsedwa ntchito popanda chidziŵitso chapasadakhale ndi popanda chiwongola dzanja. Chithandizo cha m’banja chinali choipirapo; pambuyo pa kugwira ntchito maola 10 kufikira 12 m’sukulu, iwo anafunikira kupeza ntchito yapadera kuti apeze ndalama zowonjezereka ndi kudyetsa mabanja awo. Ndinafuna kuwongolera mkhalidwe wachisalungamo umenewo.

Pamene ndinauza mkulu wa avirigo, iye anandiuza kuti ndinangofunikira kunyamula mfuti ya chiwaya paphewa panga kuti ndikhale woyenerera kusintha ulamuliro! Panthaŵi imeneyo ndinalingalira kuti ndikakonda kukhala womenyera kusintha ulamuliro koposa kukhala wankhalwe monga momwe iwo analiri. Chotero, ndinapempha kuchotseredwa malumbiro osalekeza olonjeza chiyero, umphaŵi, ndi kumvera amene ndinali nditapanga. Ndinafuna kuthandiza tchalitchi m’njira zambiri. Kuchotseredwako kunavomerezedwa mosavuta.

Ntchito Yanga Yandale Zadziko

Pamenepo ndinayambadi kuwona mmene kuliri kukhala wopanda zinthu zakuthupi. Nthaŵi zambiri ndikanakhala wopanda ngakhale nyenyeswa ya mkate pakanapanda anthu amtima wabwino amene anali pafupi nane. Kwanthaŵi yoyamba, ndinawona mmene anthu wamba anakhaliradi. Ndinagwira ntchito zolimba ndi tchalitchi chamomwemo m’mbali zonse—yachipembedzo, yamakhalidwe, ndi yandale zadziko. Monga wophunzitsa achikulire, ndinali ndi mipata yambiri ya kulankhula nawo za mikhalidwe yoluluzika imene chitaganya chinawakakamiza kulowamo, zochititsa zake ndi zothetsera zothekera. Kodi zothetsera zimenezi zinali chiyani? Choyamba, kugwira ntchito mwanjira yabata ndi kusonyeza kusakondwa; ndiyeno, ngati kuli koyenerera, kugwiritsira ntchito chiwawa kuti mufikire chonulirapo cholakalakikacho, chilungamo.

Gulu la chipembedzo chosanganikirana ndi ndale zadziko limene ndinagwirizana nalo, lolinganizidwa ndi ansembe Achikatolika ndi lochirikizidwa ndi ziŵalo za anthu opembedza wamba, limalunjikitsa ntchito zake m’madera osatukuka a Afirika, Asiya, ndi Latin America. Limachirikiza masinthidwe amwamsanga, aakulu a makhalidwe a anthu ndi azachuma mwa mchitidwe wa chipanduko, limodzi ndi kukanidwa kwamtu wagalu kwa mitundu yonse ya kulamulidwa m’zachuma, m’zandale zadziko, ndi m’zamakhalidwe. Cholinga chake ndicho kuyambitsa sosholizimu ya Latin America imene imapititsa patsogolo kupangidwa kwa hombre nuevo (munthu watsopano), womasuka kuukapolo wochititsidwa ndi madongosolo andale zadziko autsamunda.

Tinadzipereka kulowa mowonjezereka mumpambo wa amphaŵi, tikumadziphatika mumkhalidwe wawo wa moyo. Polingalira za mavuto amenewa, ndinayesayesa mwamphamvu kuthandiza aliyense—wachichepere ndi wokalamba, womakula ndi wachikulire.

Moyo Wanga Wamtseri—Chogwiritsa Mwala Chachikulu Koposa

M’kumenyera kwanga kuwongolera mikhalidwe ya amphaŵi, ndinaiŵala kuti mtima ungakhale wonyenga. Ndinakondana ndi bwana wanga, wansembe, amene ndinakhala naye kwazaka ziŵiri. M’kupita kwanthaŵi ndinali ndi pakati. Pamene wansembeyo anadziŵa, anafuna kuti nditaye mimbayo, zimene ndinakana, popeza kuti kutero kukanakhala kupha mwambanda. Kuti ndikakhale ndi mwana, ndinafunikira kuleka kugwira ntchito ndi wansembeyo ndi kutuluka mumzindawo kuwopera kuti kungadzadziŵidwe kuti ndinali dona wake.

Ndinachoka mumzindawo ndiri wovutika mtima kwambiri ndipo ndinalingalira za kudzipha mwa kudzigwetsera panjanje, koma kanthu kena kanandiletsa. Ndinapirira. Mabwenzi, ziŵalo zabanja, ndi anthu okoma mtima a m’tauni yakwathu anandisonyeza chikondi chawo, chifundo, ndi kumvetsetsa—kanthu kena kamene mwamuna yekha amene ndinakonda sanandichitire. Pamene mwana wanga wamwamuna anabadwa, amenewa ndiwo amene anatisamalira. Ndinafuna kuti mwana wanga akule kukhala mwamuna wolimba, wamphamvu, wokwaniritsa zikhutiro zake ndi wofunitsitsa kufera zolinga zake. Kusonyeza chikhumbo chimenechi, ndinampatsa dzina lapakati lakuti Ernesto mokumbukira Ernesto Che Guevara (womenya nkhondo yachizembera wa ku Argentina wotchuka), amene anandichititsa kaso kwambiri.

Pamene boma la Argentina linagwetsedwa ndi asilikali, timagulu totsutsa boma tinazunzidwa. Atsamwali anga ambiri anamangidwa. Nthaŵi zambiri nyumba yanga inaloŵeredwa ndi encapuchados (ovala zinyawu), amene anafunkha kanthu kalikonse ndi kuba pafupifupi zinthu zanga zonse. Nthaŵi zambiri ndinaitanidwa kukawonekera pamaso pa olamulira kuti ndikaulule kumene kunali anzanga, koma ndinakhalabe wokhulupirika kwa mabwenzi anga, ndikumasankha kufa koposa kusanduka mpereki.

Posinthira

Pokhala pansi pa chitsenderezo choterocho, ndinafunikira winawake wolankhula naye, winawake amene ndikanakhulupirira ndi kudalira monga bwenzi lowona. Panali panthaŵiyi pamene aŵiri a Mboni za Yehova anadza pakhomo panga. Ndinawalandira mwachimwemwe, ndikumawona mwa iwo mkhalidwe wabata ndi waubwenzi zimene ndinakopeka nazo. Ndinafuna kuti adzabwerenso kudzaphunzira nane Baibulo. Pamene anatero, ndinawafotokozera mkhalidwe wovuta umene ndinalimo ndipo ndinawauza mosabisa mawu kuti sindinafune kuti iwo aphatikizidwe monga ololerana nazo. Iwo ananditsimikizira kuti sanali kuwopa, popeza kuti olamulirawo anadziŵa amene iwo anali.

Phunziro lathu Labaibulo linali lovutavuta kuyambira pachiyambi. Popeza kuti ndinali nditataikiridwa ndi chikhulupiriro ndi chidaliro mwa Mulungu, kunali kovuta kwambiri kwa ine kuvomereza mfundo zachiphunzitso m’bukhu lothandizira kuphunzira Baibulo lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Ndinatsala pang’ono kusiya phunzirolo, ndikumalingalira kuti Baibulo linali nthanthi ndi kuti Marx ananenetsa pamene anati chipembedzo chinali “mankhwala ogonetsa anthu tulo.” Pamene ndinafotokozera Mbonizo malingaliro anga ndi kuziuza kuti zisawonongenso nthaŵi ina pa ine, zinandiyankha kuti sizinakulingalire kukhala kuwononga nthaŵi kuthandiza anthu amene anafunikiradi chithandizo.

Ndinapeza lingaliro losiyana pamene ndinaitanidwira ku Nyumba Yaufumu. Ndinatopa ndi misonkhano kumene kusinthana malingaliro, kulemekezana, ndi ubwenzi zinali zosoŵeka kwambiri. Komabe, misonkhano ya Mboni za Yehova inali yosiyana. Njozikidwa pa Baibulo ndipo njolimbikitsa chikhulupiriro, ndipo imatisonkhezera kukukondana wina ndi mnzake ndi kukonda ngakhale adani athu.

Umunthu Watsopano Wachikristu Ulowa Mmalo mwa Chiwawa

Potsiriza ndinapeza njira yopangira dziko kukhala labwinopo. Pa June 8, 1982 ndinachitira chizindikiro kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi, ndiyeno pamenepo koposa ndi kale lonse chinafikira kukhala chikhumbo changa kuvula umunthu wakale, hombre nuevo wandale zadziko wa chiwawa, ndi kuvala umunthu watsopano, limodzi ndi zipatso zake zabwino, zofotokozedwa pa Agalatiya 5:22, 23. Tsopano ndikuphatikizidwa m’nkhondo yamtundu wina, nkhondo Yachikristu, yolalikira mbiri yabwino ya Ufumuwo ndi kudzipereka inemwini kukuphunzitsa ena za chowonadi Chaufumu cha dziko labwinopo lirinkudzalo.

Ndidalitso lotani nanga kukhoza kuphunzitsa mwana wanga wamwamuna wamng’onoyo kuti mmalo mwa kukula kuti adzatsatire Ernesto Che Guevara, iye angathe kuyenda m’mapazi a Kristu Yesu, Mtsogoleri ndi Chitsanzo chathu! Ndikupempherera kuti mwana wanga wamwamuna ndi ine, limodzi ndi okonda chilungamo onse, kuphatikizapo amene kale anali mabwenzi anga ndi achibale, aloŵe m’dziko labwino kosatha limenelo, dziko laparadaiso lodzazidwa ndi chisangalalo, mtendere, chimwemwe, ndi chilungamo. Chiwawa sichimapindulitsa aliyense; chimangokulitsa kokha udani, magawano, zogwiritsa mwala, ndi mavuto amene samatha konse. Ndikulankhula zimene ndidziŵa, pakuti ndadziwonera ndekha.—Ndi Eugenia María Monzón.

[Chithunzi patsamba 30]

Kulalikira kunyumba ndi nyumba m’Argentina

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena