Lipoti la Olengeza Ufumu
Chowonadi cha Baibulo Chimasula Mvirigo m’Bolivia
ANTHU ambiri owona mtima akuchithaŵa chipembedzo chonyenga, amaphunzira chowonadi cha Baibulo, ndi kudzalambira Yehova, Mulungu wowona. Oposa 7,600 achita zimenezo m’Bolivia, kuphatikizapo mvirigo wina.
Pamene anali ndi zaka zisanu ndi zinayi zokha, M—— anakambitsirana ndi Mboni za Yehova kwanthaŵi yoyamba. Ndiye anakatsegula chitseko pamene Mboni zinagogoda pakhomo, ndipo kwanthaŵi yoyamba, anamva kutchulidwa kwa dzina la Mulungu, Yehova. Linakhala m’maganizo mwake kwa zaka zambiri.
Popeza kuti anali msungwana yekha m’banjamo, kunalingaliridwa kuti akakhale mvirigo. “Ndinali wachimwemwe chotani nanga kuti ndikakhala muutumiki wa Mulungu—nzimene ndinalingalira basi zimenezo,” anatero M——. Koma chisangalalo chake chinakhala chogwiritsa mwala pamene anawona chisalungamo ndi tsankho zochitika m’sukulu ya avirigo. Iye anati: “Mwina sindidzaiŵala konse kupsinjika kumene ndinakhala nako ndi kumenyedwa kwakuthupi ndi kwauzimu kumene kunali kosautsa kwambiri, kumene kunandipangitsa kuwona Mulungu, osati monga Munthu wachikondi, koma Munthu wopereka chilango wopanda chifundo.”
Anapitiriza kuti: “Kufikira pamene ndinakhala mvirigo, sindinathe kupeza dzina la Yehova m’Baibulo. Ndinangopeza ‘Yahweh,’ ndipo zimenezo zinandikwiitsa. Tsiku lina ndinapitadi kukafunafuna anthu aja omwe analankhula za Yehova, koma sindinawapeze.
“Nthaŵi inapitapo, ndipo tsiku lina pamene ndinkapita kunyumba kwa makolo anga, ndinawona chikwangwani, ‘Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova.’ Ndinafuna kuwauza kuti anali aneneri onyenga, koma munalibe aliyense m’holomo. Ndinapitakonso pa Sande. Ndinapeza msonkhano uli pakati, ndipo ambiri anawoneka odabwa kuwona mvirigo pakati pawo ali m’malaya ake. Msonkhano utatha, ndinayesa kutuluka mofulumira. Komabe, mmodzi wa Mbonizo anandipatsa moni, chotero ndinamfunsa kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji anthu inu mumamtonza Woyera mwakutchedwa ndi dzina limenelo?’ Funso langa linatiloŵetsa m’kukambitsirana Baibulo, ndipo ndinapanga makonzedwe akuti akandichezere kunyumba ya makolo anga. Makolo anga anamthamangitsa. Komabe, tinakumananso miyezi iŵiri pambuyo pake, ndipo anandiitanira kwawo kukaphunzira Baibulo. Ndinakondwa kwambiri ndi maumboni amene anandisonyeza, otsimikizira kuti Akristu ayenera kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu. Umboniwo unandipatsa mphamvu zondikhozetsa kutaya zopanda pake zonse zimene ndinaphunzitsidwa monga mvirigo.
“Ndikukumbukirabe zinthu zambiri za moyo wanga m’sukulu ya avirigo. Mwachitsanzo, panthaŵi ina ndinafuna chakudya chowonjezereka. Chotero ndinalembera kalata makolo anga kuwapempha kuti anditumizire, osadziŵa kuti makalata analikutsegulidwa pasukulupo. Pachakudya chotsatira, anandipatsa muulu wa mkate ndi jamu, nandikakamiza kuti ndimalize zonsezo. Zimenezi zinandichulukira kwambiri. Ndinauza anzanga, ndipo wina anati ndinyenye mkate wotsalawo ndi kuumwazira pansi. Pamene ndinachita zimenezo, mwamsanga mvirigo anandigwira mwamphamvu ndikundikankhira pansi, nandilamula mwaukali kuti ndiyeretse pansipo mwakunyambitapo ndi lirime langa. Chipindacho chinali chachikulu kwabasi. Pamene ndinkachita zimenezo, ndinamva ambiri akunong’ona ndi kuseka—osasonyeza chifundo mpang’ono ponse.
“Tsopano ndikuwona mmene kuliri kwabwino kumasuka ku zonsezo. Monga mmene ziyenera kukhalira, chimasuko chimenechi chinaphatikizapo kudzimana. Choyamba, abambo ŵanga anandithamangitsa panyumba. Komabe, ndisanachoke pasukulu ya avirigo, ndinakhala ndi mwaŵi wakuthandiza avirigo ena achichepere kuphunzira chowonadi. Ndine wokondwa kunena kuti ena a ife tapatulira miyoyo yathu kwa Yehova Mulungu!
“Pamene ndinachoka pasukulu ya avirigo, abambo ŵanga analephera kumvetsetsa chifukwa chake ndinakana ntchito zamalipiro ambiri koma zodya nthaŵi. Komabe, ndinafuna nthaŵi yaikulu kaamba ka utumiki wa Mulungu. Tsopano ndikutumikira monga mpainiya wokhazikika, ndi moyo wosavuta koma wofupa kwambiri. Ndipo ndiri ndi chisangalalo chachikulu kunena kuti, amayi ŵanga ndi achimwene akulu pa ine agwirizana nane muutumiki wa Yehova.”
Zowonadi, chowonadi cha Baibulo chimamasula munthu ku dongosolo la chipembedzo chonyenga la dziko lino, ndipo chimadzetsa chisangalalo ndi chimwemwe chokhalitsa.—Yohane 8:32.