Lipoti la Olengeza Ufumu
Yemwe Anali M’virigo kwa Zaka 25 Potsirizira Pake Aphunzira Chowonadi
BAIBULO linalosera kuti ‘khamu lalikulu’ lochokera m’mitundu yonse likabwera ndi kulambira pakachisi wauzimu wa Yehova. (Chibvumbulutso 7:9) Zimenezi zikuchitika lerolino, ndipo tikusangalala kuwona kuti ambiri, mwa thandizo la chowonadi cha Mulungu, akudula nsinga za chipembedzo chonyenga. Zokumana nazo zotsatirazi zikuchitira fanizo zimenezi.
◻ Mkazi wina wa ku Roma, Italiya, akusimba kuti: “Kuyambira pamene ndinali wamng’ono chiyembekezo changa chachikulu chinali kukhala m’virigo, popeza kuti ndinakhumba kutumikira Mulungu ndi mtima wanga wonse. Ndinakhoza kukwaniritsa chonulirapo changa pamsinkhu wa zaka 32, pa December 8, 1960, pamene ndinapanga lumbiro langa loyamba la chimvero, umphaŵi, ndi chiyero. Ntchito yanga inali yakusamalira usana ndi usiku pafupifupi ana 30 osauka ndi onyanyalidwa omwe anali amasiye kapena ana a akaidi. Ndinapeza chikhutiro m’ntchito yanga.
“Chikhulupiriro changa chinagwedezeka pambuyo pa zaka khumi zautumiki pamene panabuka mkangano pamalopo. Ndinadabwa kuti, ngati Mulungu ankatitsogolera, nchifukwa ninji akalola kukangana ndi kupanda dongosolo koteroko kuchitika m’nyumba mwake.”
M’virigoyo adali ndi mchemwali yemwe ankakhala ku Falansa ndipo anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye anachitira umboni kwa m’virigoyo mwakulemba makalata ndipo anamtumizira New World Translation of the Holy Scriptures. M’virigoyo akusimba kuti: “Pambuyo pa zaka 23, imeneyo inali nthaŵi yanga yoyamba kukhala ndi Mawu a Mulungu.” Pamenepo mpamene anavomereza phunziro la Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye akuti: “Pamene ndinapita patsogolo ndi phunzirolo, ndinadziŵa Yehova Mulungu ndi ziyeneretso zake limodzinso ndi mikhalidwe yake yodabwitsa. Ndinaipidwa kwambiri pamene ndinaphunzira kuti samavomereza kugwiritsira ntchito mafano, popeza kuti malowo anali odzaza ndi mafano amisinkhu ndi mitundu yosiyanasiyana. Ndinamvetsetsa kuti ngati ndinafuna kukondweretsa Yehova, sindikapitiriza kukhala mmalo amenewo. Pambuyo pa zaka 25 za utumiki wodzipereka monga m’virigo, pomalizira pake ndinachipeza chowonadi. Chotero pa October 1, 1985, ndinapereka chidziŵitso changa cha kuchoka, ndikumakhumudwitsa akuluakulu anga.
“Abale ndi alongo anga achikondi anandithandiza ponse paŵiri mwakuthupi ndi mwauzimu. Mwachiyamikiro kwa Yehova ndi gulu lake, ndinabatizidwa pa August 30, 1986, ndipo ndinayamba kuyenda pa msewu wa ku moyo wosatha.”
Yehova Adalitsa Chikhumbo cha Wachichepere cha Kutumikira Mulungu
◻ Mphunzitsi wapasukulu m’Brazil yemwe anali mmodzi wa Mboni za Yehova pamene ankachonga mapepala asukulu anawona kuti wophunzira wina wazaka 14 zakubadwa analemba za chikhumbo chake chakuphunzira zambiri ponena za Mulungu. Iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi wophunzirayo, koma pamene msungwanayo anapita patsogolo, banja lake Lachikatolika linaletsa phunzirolo ndikuwononga mabuku ake. Wophunzira wachichepereyo anayamba kuphunzira Baibulo panthaŵi yopumula kusukulu, koma anapezedwa. Chotero phunzirolo linachitidwa mwakulemba makalata. Komabe, posakhalitsa banja lake linapeza makalata ake ndikuwawotcha. Atate ake anayamba kumkakamiza kunka ku Misa. Iye anapita nawo koma anatenga kope la Nsanja ya Olonda lokaŵerenga nthaŵi ya mapempheroyo, akumalibisa pakati pa masamba a kabukhu kakutchalitchi. Izi zinachitika kwa miyezi isanu ndi umodzi, kufikira tsiku lina anazemba kunyumba kuti apite ku Nyumba Yaufumu. Mkati mwa msonkhanowo bambo ake anafika pakhomo nawuza abalewo kuuza mwana wake kuti akamkwapula akafika kunyumba. Zoyesayesa za abalewo za kulingalira ndi bamboyo sizinaphule kanthu.
Tsiku lotsatira, iye anapita kukawona abalewo ali wachimwemwe ndi womwetulira. Iye anawawonetsa mabala ambiri pathupi pake mmene bambo ake anammenya. Nangano, kodi nchifukwa ninji anali wachimwemwe? Pamene anachoka pa Nyumba Yaufumu, bambo ake anafunsa anthu angapo m’tauni, kuphatikizapo meya, ponena za maubwino ndi kuipa kwakuti mwana wake akhale mmodzi wa Mboni za Yehova. Meyayo ananena kuti Mboni ndi anthu abwino, otheka kuwadalira. Iye anawonjezera kuti ali ndi miyezo yamakhalidwe yabwino koposa ndikuti kungakhale bwino koposa kukhala ndi mwana wa miyezo imeneyi, imene iri yapamwamba kwambiri kuposa ya achichepere ambiri.
Mosasamala kanthu za zimenezi, msungwanayo anakwapulidwa. Koma bambowo anamuuza kuti ankamkwapula chifukwa chakuti anachoka panyumba osatsazika. Ndipo ananena kuti adzamkwapulanso ngati aleka kuphunzira Baibulo kapena kupezekapo pamisonkhano ya Mboni za Yehova! Msungwanayo tsopano ndi wofalitsa wachangu, ndipo ena a m’banja lake akusonyeza chikondwerero m’chowonadi.
Zowonadi, Yehova amadalitsa achichepere amene ali ndi chikhumbo chowona mtima cha kumtumikira, monga momwe chokumana nachochi chikusonyezera.—Salmo 148:12, 13.