Lipoti la Olengeza Ufumu
Mboni za Yehova Zimalalikira Mwamwaŵi Ndikukhala ndi Zotulukapo Zabwino
ANTHU ambiri anadziŵitsidwa chowonadi cha Baibulo kwanthaŵi yoyamba pamene mmodzi wa Mboni za Yehova analalikira kwa iwo mwamwaŵi. Mwakutero Mbonizo zimatsanzira chitsanzo cha Yesu Kristu, amene analalikira mwamwaŵi kwa mkazi Wachisamariya pachitsime pamene mkaziyo anabwera kudzatunga madzi. (Yohane, mutu 4) Kum’maŵa kwa Afirika, mmodzi wa Mboni za Yehova analalikira mwamwaŵi kwa m’virigo Wachikatolika. Ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ikusimba zimene zinatulukapo:
◻ M’mamaŵa tsiku lina pamene inali kupita kutauni, Mboniyo inakumana ndi m’virigo Wachikatolika. Anatenga mwaŵiwo kufunsa m’virigoyo kuti: “Kodi mukupita kuti panthaŵi ino?” Yankho linali lakuti: “Ndikupita kukapemphera kwa Mulungu wanga.” Ndiyeno anamfunsa m’virigoyo kuti: “Kodi mumalidziŵa dzina la Mulungu wanu?” M’virigoyo anayankha nati: “Kodi dzina lake sindilo Mulungu?” Mboniyo inapempha kunka kunyumba kwake masana a tsikulo kukakambitsirana dzina la Mulungu. Pambuyo pa kukambitsiranako m’virigoyo anapita kutchalitchi kwake nafunsa mmodzi wa ansembe ngati anadziŵa tanthauzo la dzina lakuti “Yehova.” Yankho linali lakuti, “Ndi dzina la Mulungu.” M’virigoyo anadabwa kwambiri kumva kuti wansembeyo anadziŵa zimenezi koma sanamphunzitse konse.
Mboniyo inachezera mkaziyu kwa masiku asanu ndi anayi otsatizana namphunzitsa chowonadi ponena za Utatu, moyo, moto wa helo, ndi chiyembekezo cha akufa. Mkaziyo anavomereza zonse ndiyeno anapempha Mboniyo kumpatsa nthaŵi yakusinkhasinkha pa ziphunzitso zatsopano zonsezo. Pambuyo pa milungu iŵiri anatumira lamya Mboniyo napempha kuti akambitsirane zowonjezereka. Panthaŵiyi nkuti m’virigoyo atatsimikiza kale mtima kuchoka kutchalitchi ndipo nkuti atawononga kale mafano ake, makorona, ndi mtanda. Wansembeyo anayesa kumkokosa kuti abwerere, koma mkaziyo anatsimikiza mtima kulondola chowonadi. Pambuyo pake anabatizidwa ndipo watumikira monga mpainiya wothandiza kwa miyezi yambiri mosasamala kanthu za umoyo wamatenda ndi ukalamba.
Popeza kuti nyumba yake njaikulu, anapatsa mpingo kuti udziigwiritsira ntchito monga Nyumba Yaufumu. Abale anachotsa denga lakale, anagwetsa zipupa zamkati, napanga mbali yaikulu ya nyumbayo kukhala malo okongola osonkhanira. Yemwe kale anali m’virigo Wachikatolikayu amakhala m’chipinda cha kumbuyo kwa holoyo. Iye ali wachimwemwe kwambiri kukhala wokhoza kupanga chopereka choterechi ku kulambiridwa kwa Yehova.
◻ Chokumana nacho china chimene chimasonyeza nzeru ya kuchitira umboni mwamwaŵi chikuchokera ku Kampala, Uganda. Pamene mishonale wa Mboni anali kupita ku ofesi yaboma, analankhula mwamwaŵi ndi anthu omwe anali naye m’chikepe. Mwamuna wina, Bambo L————, anafotokoza chikhumbo chakulandira bukhu logaŵiridwalo koma analephera kutero panthaŵiyo. Chotero anapatsa mishonaleyo dzina lake ndi keyala ya ofesi yake. Pambuyo pake mishonaleyo anapitako napempha kuwonana ndi Bambo L————. Anaitanidwa koma zinadabwitsa mishonaleyo kuwona munthu wosiyana akubwera. Paofesipo panali amuna aŵiri okhala ndi maina ofanana. Umboni wachidule unaperekedwa kwa Bambo L———— wachiŵiri, ndipo anasonyeza chikondwerero chachikulu. Pamene kuli kwakuti Bambo L———— woyamba anataya chikondwerero, phunziro Labaibulo linayambitsidwa ndi Bambo L———— wachiŵiri. Iye tsopano ndi Mboni yobatizidwa, ndipo mkazi wake ndi mwana wawo akupanga kupita patsogolo kwabwino kulinga ku ubatizo.
Yesu Kristu ndiye Mbusa Wabwino ndipo amadziŵa onga nkhosa amene mitima yawo iri yokhoterera ku chilungamo. Zokumana nazo zimenezi zimafotokoza mwafanizo kuti iye amatsogolera otsatira ake kwa anthu oterowo. Kulalikira mwamwaŵi kungakhale kophula kanthu!—Yohane 10:14.