Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 9/8 tsamba 16-17
  • ‘Nthyole ya Chilango’ Kodi Njachikale?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Nthyole ya Chilango’ Kodi Njachikale?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Lingaliro Lachikatikati
  • Bwanji za “Nthyole”?
  • Kodi Chilango chiyenera Kuperekedwa Motani?
  • Baibulo Sirimachirikiza Nkhalwe
  • Kumvetsa Cholinga cha Kulanga
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Chilango Chimabala Chipatso cha Mtendere
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Mungatani Kuti Muzilangiza Bwino Ana Anu?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 9/8 tsamba 16-17

Lingaliro la Baibulo

‘Nthyole ya Chilango’ Kodi Njachikale?

‘Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole ya chilango idzauyingitsira kutali.’—Miyambo 22:15.

“Chilango chirichonse chakuthupi chimavulaza malingaliro ndipo sichiyenera kugwiritsiridwa ntchito.”—Parents Anonymous.

KUTCHULA kwa Baibulo kwa ‘nthyole ya chilango’ kumayambitsa mkangano wa mtima bii. Zimenezi ziri zomveka, chifukwa chakuti chaka chirichonse ana zikwi zambiri amafa chifukwa cha kumenyedwa ndi kholo. Mwinamwake ndicho chifukwa chake wothirira ndemanga pa Baibulo wina ananena molakwa za chilolezo cha Baibulo chakupereka chilango chakuthupi kuti changokhala kokha “lingaliro lozikidwa pa zikhulupiriro zamwambo za anthu a m’nthaŵi ya Baibulo.”

Komatu malingaliro achikale sanauzire Baibulo—Mulungu anatero. (2 Timoteo 3:16) Kodi mawu ake onena za ‘nthyole ya chilango’ ngosayenerera? Kuli kofunika kuti tipende “nthyole” m’mawu ake apatsogolo ndi apambuyo. Mwachitsanzo: Mbali imodzi iriyonse ya made simapereka tanthauzo lirilonse. Kuli kokha pambuyo pa kulumikizanitsa mbalizo pamodzi kuti munthu angathe kuwona chithunzithunzi chonse. Mofananamo, “nthyole” iri kokha mbali imodzi ya made. Kuti tiwone chithunzithunzi chonse, tiyenera kulumikizanitsa “nthyole” ndi malamulo ena amakhalidwe abwino a Baibulo ophatikizapo chilango.

Lingaliro Lachikatikati

Kodi Baibulo limatchula chilango chakuthupi chokha? Talingalirani uphungu wotsatirawu:

• “Musakwiyitse anawo.”

• “Musawongolere mopambanitsa ana anu, kuwopera kuti mungawatayitse mtima.”

‘Zimenezo ziri bwino kwambiri kuposa uphungu wa Baibulo,’ ena angatero. Komatu umenewu uli uphungu wa Baibulo. Walembedwa pa Aefeso 6:4 (The New Jerusalem Bible) ndi Akolose 3:21 (Phillips).

Inde, lingaliro la Baibulo liri loyenerera. Limavomereza kuti kaŵirikaŵiri chilango chakuthupi sindicho njira yophunzitsira yogwira mtima koposa. Miyambo 8:33 imati: ‘Mverani mwambo’ osati ‘lawani mwambo.’ Ndipo Miyambo 17:10 imanena kuti “chidzudzulo chiloŵa mkati mwa wozindikira, kopambana ndi kukwakupula wopusa kwambiri.” Ndipo, Deuteronomo 11:19 akuvomereza chilango chotchinjiriza, kupindula ndi nyengo za mwamwaŵi kukhomereza makhalidwe abwino mwa ana amunthuwe. Chotero, lingaliro la Baibulo la chilango nlachikatikati.

Bwanji za “Nthyole”?

Komabe, Baibulo limatchula “nthyole” ya chilango. (Miyambo 13:24; 22:15; 23:13, 14; 29:15) Kodi izi zikutanthauzanji?

Liwu lakuti “nthyole” latembenuzidwa kuchokera ku liwu Lachihebri sheʹvet. Kwa Ahebri, sheʹvet anatanthauza ndodo kapena chikoti, monga chogwiritsiridwa ntchito ndi mbusa. M’lingaliro limeneli ndodo ya ulamuliro imapereka lingaliro lachitsogozo chachikondi, osati nkhalwe yokakala.—Salmo 23:4.

Sheʹvet imagwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri mophiphiritsira m’Baibulo, kuimira ulamuliro. (2 Samueli 7:14; Yesaya 14:5) Posonya ku ulamuliro wa makolo, “nthyole” simasonya ku chilango chakuthupi chokha. Imaphatikizapo mipangidwe yonse yachilango, chimene kaŵirikaŵiri sichifunikira kukhala chakuthupi. Ndipo pamene chilango chakuthupi chigwiritsiridwa ntchito, kaŵirikaŵiri chiri chifukwa chakuti njira zina zalephera. Miyambo 22:15 imanena kuti uchitsiru uli “womangiriridwa” (“womamatira,” NJB; “wozika mizu,” The New English Bible) mumtima wa munthu wolandira chilango chakuthupiyo. Zoposa uchitsiru wa ubwana zikuphatikizidwa.

Kodi Chilango chiyenera Kuperekedwa Motani?

Mu Baibulo, chilango nthaŵi zonse chiri chogwirizanitsidwa ndi chikondi ndi kudekha, osati ndi mkwiyo ndi nkhalwe. Wopereka uphungu waluso ayenera kukhala ‘woleza mtima kwa onse, . . . wodziletsa pa choipa, wolangiza mwachifatso otsutsawo.’—2 Timoteo 2:24, 25.

Chifukwa chake, chilango sindicho potulutsira mkwiyo pa kholo. Mmalomwake, chiri njira yakulangiza. Motero, chiyenera kuphunzitsa mwana wolakwayo. Pamene chiperekedwa mumkwiyo, chilango chakuthupi chimapereka phunziro lolakwa. Chimangokhutiritsa chikhumbo cha kholo, osati kuthandiza mwanayo.

Ndiponso, chilango chogwira mtima chiri ndi malire. ‘Ndidzakulanga iwe kumlingo woyenerera,’ Yehova akutero kwa anthu ake pa Yeremiya 46:28. Mfundoyi njofunika mwapadera kuikumbukira popereka chilango chakuthupi. Kumenya kapena kugwedeza mwana kungachititse kuwononga kwa ubongo kapena ngakhale imfa.a Kupitirira chifuno choperekera chilango—kuwongolera ndi kuphunzitsa—kungapangitse kuvulaza mwana.b

Baibulo Sirimachirikiza Nkhalwe

Asanawongolere anthu ake, Yehova anati: “Usawope, . . . ine ndiri ndi iwe.” (Yeremiya 46:28) Chilango sichiyenera kupangitsa mwanayo kukhala ndi malingaliro akunyanyalidwa. Mmalomwake, mwanayo ayenera kuwona kuti khololo ‘liri naye’ monga chilimbikitso chachikondi ndi chochilikiza. Ngati chilango chakuthupi chiwonekera kukhala chofunika, mwanayo ayenera kumvetsetsa chifukwa chake. Miyambo 29:15 imanena kuti: “Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru.”

Chiri chowonadi chomvetsa chisoni chakuti lerolino ambiri amagwiritsira ntchito “nthyole” yaulamuliro waukholo molakwa. Chikhalirechobe, kulakwako sikungapezedwe m’malamulo amakhalidwe abwino achikatikati a Baibulo. (yerekezerani ndi Deuteronomo 32:5.) Pamene tipenda mawu akuti “nthyole” m’mawu ake apatsogolo ndi apambuyo, timawona kuti imatumikira kuphunzitsa ana, osati kuwachitira nkhalwe. Mofanana ndi m’nkhani zina, Baibulo limatsimikizira kukhala ‘lopindulitsa pachiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.’—2 Timoteo 3:16.

[Mawu a M’munsi]

a Bukhu lakuti Outgrowing the Pain: A Book for and About Adults Abused as Children limachenjeza kuti: “Kupamantha kungakhale kuchitira nkhalwe mwana pamene kuchitidwa m’njira yosalamulirika, mwamphamvu yokulira mokwanira kuvulaza. Kugwiritsira ntchito zida pomenya, kupamantha ndi nkhonya, kumenya ana achichepere kwambiri, ndi kumenya mbali zowopsa (kumaso, m’mutu, pamimba, kumsana, kumpheto) kungawonjezere kuthekera kwa chilango chakumenya kukhala kuchitira nkhalwe mwana.”

b Bukhu lakuti Father Power, lolembedwa ndi Dr. Henry Biller ndi Dennis Meredith, limati: “Kuti chilango chakuthupi chikhale choyenerera chifunikira kukhala chosapambanitsa. Ngati chiperekedwa ndi munthu amene amamkonda ndi amene adziŵa kuti amkonda chisonkhezero pa malingaliro chidzakhala chokwanira kupangitsa mwanayo kuganiza za chimene iye wachita.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

The Bettmann Archive

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena