Kupsinjika Mtima Kodi Mungakulake?
“KUTALITALI! Kupsinjika mtima nkovuta kwambiri. Palibe zimene ndingachite kusiyapo kupirira kufikira kutatha.”
Ndimmene ambiri amatengera lingaliro la kulaka mikhalidwe yopsinja mtima yonga nkhaŵa, mantha, mkwiyo, kugwiritsidwa mwala, liwongo, kudzimvera chisoni, ndi kuchita tondovi. Koma mikhalidwe yopsinja mtimayo ingathe kulakidwa. Mmalo mogonja kwa iyo paliponse pamene ibuka, mungaphunzire kuchepetsa mphamvu yake, mwinamwake ngakhale kuithetsa.
Ndithudi, pali kusiyana kwakukulu pakati pa kupsinjika mtima wamba kumene aliyense amakhala nako ndi kuchita tondovi kowopsa. Komaliziraku kungafunikire kuchiritsa kwa akatswiri. Koyambako sikumatero, ndipo kumeneku ndiko kupsinjika mtima kumene tingaphunzire kuchita nako.
Kwenikweni, sikupsinjika mtima konse kumene kuli kovulaza. Mwachitsanzo, mutalakwa kwambiri, mungaipidwe malinga ndi cholakwacho. Ngati zimenezi zikusonkhezerani kuchiwongolera ndi kupeŵa kuchichitanso mtsogolo, pamenepo kuipidwa kwanuko kwakhala ndi chiyambukiro chabwino chokhalitsa. Kapena nkhaŵa yoyenerera ya vuto lakutilakuti imene mungakhale nayo ingakusonkhezereni kulimbana nalo mwamphamvu ndi kufunafuna chothetsera choyenera. Chimenecho chirinso chiyambukiro chabwino.
Komabe, bwanji ngati mutachita zonse zothekera kuyesa kuwongolera cholakwacho, mudzimvabe waliwongo kapena wopanda pake, mwinamwake mukumatero patapita nthaŵi yaitali? Kapena bwanji ngati mutathetsa vutolo kumlingo wothekera, nkhaŵa zanu zipitirizabe ndipo ngakhale kukula? Pamenepo kupsinjika mtima kwanu kungakuvutitseni. Ndiyeno, ndimotani mmene mungalakire kupsinjika mtimako? Mfungulo ingapezeke m’yankho la funso limeneli.
Tingathe Kulamulira Malingaliro Athu
Ambiri amene amagwira ntchito yowona pamkhalidwe wamaganizo amanena kuti kupsinjika mtima kwathu kumachititsidwa ndi malingaliro athu. Mwachitsanzo, Dr. Wayne W. Dyer ananena kuti: “Simungapsinjike mtima popanda kulingalira choyamba.” Dr. David D. Burns anawonjezera kuti: “Kupsinjika mtima kulikonse kumene mukhala nako kuli chotulukapo cha kulingalira kwanu kwakuipidwa.”
Mokondweretsa, Baibulo mofananamo limasonyeza kuti ambiri a malingaliro amene timalola ndiwo nakatande wa mmene timadzimvera, chotero limagogomezera kufunika kwa kulamulira malingaliro athu. Tawonani mavesi otsatiraŵa:
“Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.”—Miyambo 15:15.
“Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso [maganizo anu, NW], kuti mukazindikire chimene chiri chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”—Aroma 12:2.
‘Tikugonjetsa ganizo lonse kukumvera Kristu.’—2 Akorinto 10:5.
“Inu muyenera kuvula umunthu wakale umene umagwirizana ndi njira yakale ya khalidwe . . . ; muyenera kupangidwa kukhala atsopano mwa mphamvu yosonkhezera maganizo anu, ndipo muyenera kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.”—Aefeso 4:22-24, NW.
“Zinthu zirizonse zowona, zirizonse zolemekezeka, zirizonse zolungama, zirizonse zoyera, zirizonse zokongola, zirizonse zomveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”—Afilipi 4:8.
“Lingalirani zakumwamba osati za padziko ayi.”—Akolose 3:2.
Popeza kuti kukhudzidwa kwa mtima wanu kwakukulukulu kumachititsidwa ndi kulingalira kwanu, mfungulo yolakira kupsinjika mtima kwanu ndiyo kulamulira malingaliro amene amakuchirikiza. Mwakuyesayesa zolimba ndi mkupita kwa nthaŵi yochuluka, mungaphunzire kulamulira kwambiri malingaliro anu. Mwakutero mukhoza kulamulira kukhudzidwa kwa mtima wanu.
Zowona, nkwapafupi kunena kuti tingalake kupsinjika mtima kwathu. Koma kutero kulidi kovutirapo. Pamenepo, ndimotani mmene tingachitire ndi kupsinjika mtima kumeneku kumene kungatidzetsere mavuto ochuluka?
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Sikupsinjika mtima konse kumene kuli kovulaza