Kupsinjika Mtima Kodi Kungalakidwe Motani?
NJIRA yoyamba yolamulirira kupsinjika mtima ndi iyi: Zindikirani malingaliro akuipidwa.
Yachiŵiri: Limbikirani kuwongolera malingaliro akuipidwawo. Mwachitsanzo, ngati munali ndi lingaliro lakuti, ‘Sindimachita kanthu kalikonse molondola,’ pamenepo loŵetsani m’malo ake lingaliro lakuti, ‘Ndine wofanana ndi wina aliyense; ndimachita zinthu zambiri molondola, koma ndimalakwa nanenso.’
Musayembekezere kupeza bwinopo mwamsanga pambuyo pakuwongolera zimenezi (ngakhale kuti mungatero), ndipo osapitiriza kuphanaphana ndi mtima pankhaniyo. Khalani wotsimikiza ndipo pitirizani ndi njira yotsatira.
Njira yachitatu ndiyo kulimbikira kuchotsa lingaliro lovutalo m’maganizo mwanu. Yesetsani kulichotsa mwamphamvu ndi mwachidaliro monga momwe mungachitire ndi lingaliro lakufuna kuchita tchimo lalikulu. Ngakhale kuti mungathe kuchita zimenezi ndi kuyesayesa kwamphamvu kwamaganizo, chothandiza kwambiri pakutero ndicho njira yachinayi: Dzitanganitseni ndi kanthu kena, kanthu komangirira.
Kutero nkofunika chifukwa malingaliro anu akuipidwa adzayesa mobwerebwereza kuloŵanso m’maganizo mwanu. Koma mwaŵi umene muli nawo ngwakuti: Mumasumika maganizo anu kotheratu pachinthu chimodzi chokha panthaŵi imodzi. Mungatsimikizire zimenezi mwakuyesa kusumika maganizo kotheratu pankhani ziŵiri panthaŵi imodzi. Ngati maganizo anu ali kale otanganidwa kwambiri ndi kanthu kena, kudzakhala kovuta kuti malingaliro anu akuipidwa abwerenso.
Njira imene malingaliro abwino angatengere malo a malingaliro akuipidwa yafotokozedwa mwafanizo ndi Dr. Maxwell Maltz, amene anati: “Pamene rekodi puleya yanu ikuimba nyimbo imene simumaikonda, inu simumayesa kuikakamiza kuimba bwino. . . . Mumangosintha rekodi imene ikuimbayo basi ndipo nyimbo imakhala yosiyana. Gwiritsirani ntchito njira yofananayo pa ‘nyimbo’ imene imaimbidwa ndi makina anu amkati.”
Inde, malingaliro akuipidwa kaŵirikaŵiri ngamphamvu ndithu moti amavuta kuwachotsa. Ayenera kusinthidwa ndi ena. Ikanipo “rekodi” yosiyana, yokondweretsa. Tsegulani “programu” ina, yomangirira, “steshoni” ina, ndipo sumikani maganizo anu pa imeneyo.
Kudzakhala Kovuta
Njira zinayi zotchulidwa pamwambapa zafotokozedwa mosavuta, koma zingakhale zovuta chotani nanga kuzitsatira! Chifukwa chake, musadabwe ngati kulaka malingaliro akuipidwa ndi kupsinjika mtima kukuvutani poyamba. Kuyembekezereni kukhala kovuta, koma dziŵani kuti mkupita kwanthaŵi kudzakhala kofeŵerapo.
Talingalirani chitsanzo cha Cindy, mphunzitsi amene analeredwa ndi amayi ŵake achidakwa. Kwa zaka zambiri Cindy anavutika chifukwa chakudzimva kukhala waliwongo ndi wopanda chisungiko. Ndiyeno anasankha kulimbana ndi vutolo. Kodi nchiyani chimene anachita?
Cindy anafotokoza kuti: “Choyamba ndinalimbikira pakuzindikira malingaliro enieni amene anandichititsa kupsinjika mtima. Paliponse pamene malingaliro ameneŵa anabuka, ndinali kuwapenda, bwinobwino ndipo mosamalitsa. Ndiyeno ndinalimbikira kukulitsa malingaliro abwino. Ndinadzikakamiza kusumika maganizo anga pa amene ndimaphunzira nawo ndi mmene ndikawathandizira. Mwapang’onopang’ono, kunakhala kofeŵerapo, ndipo ndinayamba kulamulira kwambiri mtima wanga.”
Komabe, mungafunse kuti . . .
Nchifukwa Ninji Kuli Kovuta Kwambiri?
Kodi zizoloŵezi zoipa, zonga kudya kapena kusuta kopambanitsa, zimasiidwa mosavuta? Kutalitali! Zimangolakidwa mwakuyesayesa kosamalitsa ndi kotsimikiza panyengo ya nthaŵi yaitali. Kwa ambiri, malingaliro akuipidwa ali chizoloŵezi, ndipo mofanana ndi zizoloŵezi zina zoipa, nkovuta kwambiri kusiya.
Ngati malingaliro akuipidwa ali chizoloŵezi chanu, mothekera, kuwalaka kudzafuna kulimba mtima kofanana ndi kwa munthu amene wayamba kusala kudya kapena amene wasankha kusiya kusuta.
Mfundo njakuti: Musasiye kuyesayesako ndiyeno kusankha kukhalabe wochita tondovi chifukwa chakuti kutero kuli kosavutirapo. Chirimikani m’nkhondo yanu yolimbana ndi malingaliro akuipidwa, ngakhale ngati kungatenge miyezi yambiri kuyesa kuchita izi ndi izi ndipo mwinamwake kubwevuka. Pitirizanibe ndi kuyesayesa kwanu monga ngati kuti mukudzizoloŵeretsa kaamba ka makani othamanga. Yembekezerani zotulukapo zokhalitsa mmalo mwa chikhutiro chamwamsanga.
Kodi Kungathetsedwe Kotheratu?
Kodi kupsinjika mtima kungathetsedwe kotheratu? Eya, ngati mukuyembekezera kupeza chimwemwe changwiro tsopano, mudzakhwethemulidwa ndi kugwiritsidwa mwala. Chimwemwe panthaŵi ino nchaching’ono. Koma zimenezo ziripo bwino kuposa kupanikizika ndi moyo wakupsinjika mtima kozunza ndi kosalekeza.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kupsinjika mtima sikudzalakidwa konse? Kutalitali. Baibulo motsimikiza limafotokoza kuti mkhalidwe wakupanda ungwiro umenewu udzakhala nafe kwakanthaŵi, koma kuti nthaŵi yoikidwiratu idzafika yakuti mkhalidwewo uthetsedwe kosatha. Zimenezo zidzachitika posachedwapa pamene Ufumu wa Mulungu, boma lake lakumwamba limene liri m’manja mwa Yesu Kristu, lidzatenga mphamvu kotheratu yakuyang’anira zochitika zonse za dziko lino lapansi ndi kuyamba ntchito yakufitsa mtundu wa anthu kuungwiro waumunthu. Yesu anatcha ntchitoyo “kulenganso [kapena “kubadwanso,” NW, mawu amtsinde].”—Mateyu 19:28; wonaninso Salmo 37:29; Mateyu 6:9, 10; Chivumbulutso 21:3-5.
Komabe, pakali pano, kuvomereza zolephera zoikidwa pa ife ndi kupanda ungwiro kwaumunthu kudzakuchititsani kupeza bwinopo. Mmalo mwakuchita mopambanitsa pofunafuna mkhalidwe wamaganizo wangwiro, mudzakhala womasuka kulondola zinthu zina m’moyo. Ndipo mudzapeza mtendere wa maganizo ndi chimwemwe chochuluka podziŵa kuti mankhwala enieni a kupsinjika mtima ali m’manja okhoza zonse a Mulungu Wamphamvuyonse.
Kodi malingaliro operekedwa m’nkhaniyi ali zongokhulupirira wamba? Kodi amagwiradi ntchito? Inde amatero, monga momwe nkhani yotsatira yosimba zochitika zenizeni m’moyo ikusonyezera.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Malingaliro akuipidwa angaloŵedwe m’malo ndi malingaliro abwino
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Musasiye kuyesayesako ndiyeno nkusankha kukhalabe wochita tondovi chifukwa chakuti kutero kuli kosavuta
[Chithunzi patsamba 7]
Mofanana ndi kudziwondetsa, kuphunzira kulamulira kukhudzidwa kwa mtima wathu kumafuna nthaŵi ndi kulimbikira