Mashantikompaundi Nthaŵi Zovuta m’Chipwirikiti cha m’Tawuni
Ndi mtola nkhani wa Galamukani! mu Afirika
MWANA wa m’shantikompaundi alikuyenda wopanda nsapato m’khwalala la mzinda wa kumadzulo kwa Afirika. Pamutu pake wanyamula malalanje makumi aŵiri ndi anayi, m’lichero. Msungwana wowonda ameneyu wavala delesi lachikasu lopatsidwa. Akutulutsa thukuta.
M’kupikisana ndi achichepere ena a m’mabanja osauka, iye akugulitsa m’khwalala. “Malalanje pano!” ndiko kuitanira kwamasiku onse. Koma mwanayu wangokhala chete; mwinamwake ali ndi njala, kapena akudwala, kapena wangotopa.
Kuchokera kunjira ina kukubwera asungwana akusukulu aŵiri ovala mayunifomu akusukulu amawonekedwe a blu wodera. Aliyense wavala masokosi oyera ndi masandasi oyera. Aliyense wanyamula chola chamabuku chodzala ndi mabuku. Asungwanaŵa akuyenda mofulumira, akukambitsirana nkhani mwachimwemwe. Iwo sakumuikako nzeru msungwana winayo, koma iye akuwakhumbira. Akuwapenyetsetsa mwachidwi kwambiri.
Asungwana akusukuluwo pomalizira afika kunyumba zawo, zabwino ndi zachisungiko. Koma pamene mwana winayo apita kunyumba, kutada madzulo, lidzakhala dziko losiyana kwambiri. Kunyumba kwake ndimalo a tizinyumba tothithikizana tomangidwa ndi zidutswa za matabwa ndi malata.
Shantikompaundi
Khwalala lalikulu kunoko ndinjira yaing’ono yafumbi yosindirika. M’nyengo yamvula, imakhala matope okhaokha. Iri yopapatiza moti galimoto silingathe kuyendamo. M’khwalalamu mulibe malo apolisi, mulibe dipatimenti yozimitsa moto, mulibe kiliniki, ndipo mulibiretu ngakhale mtengo umodzi wokha. M’mwamba mulibe mawaya amagetsi kapena afoni. Pansi palibe mapaipi a madzi azimbudzi kapena amadzi ogwiritsira ntchito.
Anthu ngothithikizana. Mawu akumvekera wowo, wowo, kulikonse! Kukambitsirana nkosakanizana ndi kuseka, kutsutsana, kulira, ndi nyimbo. Amuna ovala mikanjo yoyera akhala pamabenchi, akukambitsirana. Akazi akuphika mpunga umene ukutulutsa nthunzi m’miphika pamoto wankhuni. Ana ali paliponse—akuseŵera, kugona, kugwira ntchito, kulankhula, kugulitsa. Ambiri, mofanana ndi mwana wonyamula malalanje uja, sadzawonapo malo osungirako zinyama, kapena kutchova njinga, kapena kuwona mkati mwa sukulu.
M’dziko limene chiyembekezo cha avareji ya moyo pakubadwa ndicho zaka 42 zokha, anthu m’maloŵa amafa akali ana. Pausinkhu wa zaka zisanu ndi zinayi, mwana amakhala atapulumuka ena a masoka oipitsitsita m’dziko amene amalepheretsa kupulumuka zaka zinayi zoyambirira za moyo. Mkati mwanthaŵi imeneyo anali ndikuthekera kwa kufa koŵirikiza nthaŵi 40 kufikira 50 kuposa ndimmene zikanakhalira akadakhala m’dziko lotukuka. Anzake ambiri kunoko sanafike msinkhu wazaka zisanu. Ngati ati akhalebe ndi moyo, adzakhala wothekera kwambiri kufa ndi mimba kapena pobala kuposa mkazi wa ku Ulaya kapena ku North America—kuthekera koŵirikizika nthaŵi 150.
Mamiliyoni mazana ambiri akukhala m’makomboni atimisasa ndi mashantikompaundi omakulakula monga ino pano. Malinga ndi ziŵerengero za United Nations, 1.3 ya mamiliyoni chikwi chimodzi ngodzaza mizinda ya maiko osatukuka, ndipo amawonjezereka ndi 50 miliyoni chaka chirichonse.
Umoyo m’Maiko Osatukuka
Kodi nyumba yanu iri ndi zinthu zina zanuzanu, mpopi wamadzi, chimbudzi? Kodi pali amene amadzakuchotserani zinyalala? Mamiliyoni mazana ambiri a anthu m’maiko osatukuka alibe zinthu zimenezi.
M’mizinda yambiri malo okhala anthu osauka ali ndi anthu ochulukitsitsa kwakuti nkosadabwitsa kuwona banja la anthu khumi likumakhala m’chipinda chimodzi. Kaŵirikaŵiri, anthu ali ndi chipinda chochezera pamitala imodzi mbali zonse zinayi. M’mbali zina za mzinda wina wa Kummaŵa Kwadziko, ngakhale zipinda zazing’ono zimagaŵidwanso kuti mukhale anthu owonjezereka, ndi mabedi osanjika otchingidwa ndi waya kulola malo amtseri ndi kutsekereza mbala. M’dziko lina, mchitidwe wakubwereketsa bedi palendi umatheketsa anthu kuchititsa lendi mabedi pamaola kotero kuti anthu aŵiri kapena atatu akhoza kugonapo mosinthanasinthana patsiku lomodzi.
Malinga ndi lipoti lapachaka la 1991 la UNICEF (United Nations Children’s Fund), anthu 1.2 ya mamiliyoni chikwi chimodzi padziko lonse ali ndi madzi osayenera. Mamiliyoni amagula madzi kwa ogulitsa m’khwalala kapena kukatunga kumfuleni kapena pazitsime. Kumene kumapezeka madzi akumpopi, nthaŵi zina anthu oposa chikwi chimodzi amalimbanira mpopi umodzi.
UNICEF imayerekezeranso kuti anthu 1.7 ya mamiliyoni chikwi chimodzi alibe zimbudzi za madzi oyenda. Sikwachilendo kwa 85 peresenti ya nzika za m’shantikompaundi kukhala zopanda zimbudzi zamadzi oyenda. M’mizinda yambiri mu Afirika ndi Asia, kuphatikizapo ina yambiri yokhala ndi anthu oposa miliyoni imodzi, mulibiretu zimbudzi zamadzi oyenda. Chimbudzi cha anthu chimapita m’mifuleni, mitsinje, m’mayenje okumbidwa, m’ngalande, ndi m’ming’alu yanthaka.
Zinyalala ndizo vuto lina. M’mizinda ya Maiko Osatukuka, kuyambira pa 30 kufika ku 50 peresenti ya zinyalala zambiri sizimachotsedwa. Malo okhala anthu osauka amanyalanyazidwa koposa. Chifukwa choyamba nchakuti osauka samataya zinyalala zochuluka zimene zingapindulitse ochotsa zinyalala kapena amalonda ogwiritsira ntchito zinyalalazo kupanganso zinthu zatsopano. Chifukwa chachiŵiri nchakuti popeza kuti malo ambiri okhala anthu osauka samazindikiridwa kukhala alamulo, maboma amawamana mautumiki operekedwa kwa anthu. Vuto lachitatu nlakuti malo ambiri okhala anthu osauka, chifukwa cha kumene ali ndi kuchulukitsitsa kwa anthu, ngovuta ndi odula kutumikira.
Kodi nchiyani chimachitika ku zinyalalazo? Zimataidwa ndi kumawolera m’makwalala, pamphambano, ndi m’mitsinje ndi m’nyanja.
Maupandu Pathanzi
Mkhalidwe wa osauka a m’matauni umasiyanasiyana m’malo osiyanasiyana. Komabe, zinthu zitatu ziri pafupifupi zofanana. Choyamba nchakuti nyumba zawo siziri chabe zosakhala bwino, izo nzaupandu. Bukhu lakuti The Poor Die Young limanena kuti: “Anthu osachepera pa 600 miliyoni okhala m’mizinda ya maiko osatukuka amakhala m’nyumba ndi malo amene angatchedwe aupandu pamoyo ndi thanzi.”
Kodi ndimotani mmene kupereŵera kwa nyumba kungaikire thanzi paupandu? Mikhalidwe yakuchulukitsitsa kwa anthu m’madera okhala anthu osauka m’matauni imawonjezera kufalikira kwa matenda, monga ngati kholozi, fuluwenza, ndi meninjaitisi. Kuchulukitsitsa kwa anthu kumawonjezeranso upandu wa ngozi zapanyumba.
Kusoŵeka kwa madzi abwino okwanira kumawonjezera matenda oyambukira kudzera m’madzi, monga ngati nthenda yam’mimba ya typhoid, kutupa chiŵindi, ndi kamwazi. Kumachititsanso matenda akutseguka m’mimba, amene paavareji, amapha mwana mmodzi patimphindi 20 tiritonse m’maiko osatukuka. Kusoŵeka kwa madzi okwanira ochapira ndi osamba kumachititsa anthu kuyambukiridwa mosavuta ndi matenda a maso ndi a khungu. Ndipo pamene anthu osauka alipira ndalama zochuluka pamadzi, amatsala ndi ndalama zosakwanira za chakudya.
Kuipitsidwa kwa madzi ndi chakudya kumachititsa matenda am’kamwa ndi am’mimba ndi njoka zam’mimba, zonga mahookworm, maroundworm, ndi matapeworm. Zinyalala zosachotsedwa zimaitana makoswe, ntchentche, ndi mphemvu. Madzi osayenda amakhala malo oswera a udzudzu umene umapatsira malungo a maleliya ndi a filariasis.
Kutitimira m’Thope la Umphaŵi
Mkhalidwe wina wa umoyo wa m’shantikompaundi ngwakuti kumakhala kovuta kwenikweni kwa okhalamo kuti achokemo. Ambiri amene amabwera kumizinda ndiaja amene amathaŵa umphaŵi kumudzi. Polephera kupeza nyumba zabwino, amangokakhala m’timisasa ndi m’shantikompaundi, ndipo kaŵirikaŵiri amakhala kumeneko moyo wawo wonse.
Ochuluka a anthu ameneŵa amakhala amanja antchito ndipo ofunitsitsa kugwira ntchito zolimba, koma amakhala opanda chosankha kusiyapo kuloŵa ntchito za maola ambiri ndi malipiro ochepa. Makolo opanikizidwa ndi mavuto kaŵirikaŵiri amatuma ana awo kukagwira ntchito mmalo mwakupita kusukulu, ndipo ana osaphunzira kwambiri kapena osaphunzira konse kwenikweni samakhala ndi chiyembekezo cha kupeza moyo wabwinopo kuposa wa makolo awo. Chinkana kuti achichepere amapeza ndalama zochepa kwambiri, zimene amapezazo kaŵirikaŵiri zimakhala zofunika kwambiri ku mabanja awo. Chifukwa chake, ochuluka a osauka a m’matauni, samakhala ndi chiyembekezo chenicheni cha kuwongolera mkhalidwe wa moyo wawo; chonulirapo chawo chimangokhala kukhala ndi moyo kwa tsiku ndi tsiku.
Osakondedwa, Osafunidwa
Mbali yachitatu ya umoyowo njakuti utali wakukhala pamalo ngwosatsimikizirika. Kwa maboma ambiri, mashantikompaundi ndi makomboni atimisasa amakhala zochititsa manyazi. Mmalo mwakuyesayesa kukonza bwino mashantikopaundi, zosatheka nthaŵi zina, kaŵirikaŵiri maboma amatumiza akatapila kukagwetsa komboniyo.
Maboma angapereke chodzikhululukira chogumulira shantikompaundi mwakunena kuti nkofunikira kotero kuti mzinda uwoneke bwino, kapena kuchotsa apandu, kapena kuti amangenso bwino pamalopo. Chirichonse chimene chingakhale chifukwacho, osauka ndiwo amavutika. Kaŵirikaŵiri amakhala opanda kopita ndipo amalipiridwa ndalama zochepa kapena kusapatsidwa kalikonse. Koma pamene akatapila afika, anthuwo amakhala opanda chochita koma kuchoka basi.
Ntchito ya Boma
Kodi nchifukwa ninji maboma samapereka nyumba zokwanira zokhala ndi madzi, zimbudzi zamadzi oyenda, ndi mautumiki ochotsa zinyalala kwa onse? Bukhu lakuti Squatter Citizen limayankha kuti: “Maiko osatukuka ambiri ali ndi chuma chochepa kwambiri ndi mwaŵi wochepa kwambiri wa kukulitsa mbali yokhazikika pamsika wadziko lonse kwakuti kumakhala kothekera kukaikira kwambiri kuthekera kwawo kwa kukhalabe monga maboma amaiko. Munthu sayenera konse kusuliza boma chifukwa cha kulephera kukwaniritsa zosoŵa za nzika zake pamene kuli kwakuti dziko lonselo liri ndi kupereŵera kwakukulu kwa chuma, kwakuti malinga ndi mikhalidwe imene iripo, palibe chuma chadziko chokwanira kupezera zosoŵa zazikulu.”
M’maiko ambiri mkhalidwe wachuma ukunyonyotsoka. Chaka chatha, mlembi wamkulu wosiya ntchito wa Mitundu Yogwirizana anasimba kuti: “Mkhalidwe wa maiko ambiri osatukuka malinga ndi chuma chapadziko lonse wakhala ukunyonyotsoka kwa nthaŵi yakutiyakuti. . . . Anthu oposa mamiliyoni chikwi chimodzi tsopano ali amphaŵi kotheratu.”
Bwanji za Chithandizo cha Maiko Akunja?
Kodi nchifukwa ninji maiko okhupuka samachita zowonjezereka kuti athandize? Pofotokoza chiyambukiro cha kuthandiza kumeneko pa umphaŵi, Lipoti la World Bank Development likuvomereza kuti: “Maiko opereka chithandizo chowapindulanso [amene amapereka 64 peresenti ya chithandizo chonse cha maiko akunja] . . . amapereka chithandizo pazifukwa zambiri—zandale, maubwino azankhondo, malonda, ndi kuthandiza anthu. Kuchepetsa umphaŵi kwangokhala chimodzi cha zolinga, ndipo kaŵirikaŵiri chimakhala chosafunika koposa.”
Kumbali ina, ngakhale pamene maboma ali nacho chuma chowongolerera mkhalidwe wa osauka, iwo samatero nthaŵi zonse. Vuto m’maiko ambiri nlakuti, pamene kuli kwakuti boma lachigawo liyenera kupereka nyumba ndi mautumiki, mbali zapamwamba za boma ladzikolo sizimapereka mphamvu kapena chuma chochitira ntchitozo.
Mizinda Yamtsogolo
Malinga ndi zochitika zofala m’zaka makumi zaposachedwapa, akatswiri akuwona mtsogolo mwamdima kwa osauka a m’mizinda m’maiko osatukuka. Kuchuluka kofulumira kwambiri kwa anthu m’mizinda, iwo akutero, kudzapitiriza, ndipo maboma adzakhala osakhoza kupatsa ambiri okhala m’mizinda madzi akumpopi, zimbudzi za madzi oyenda, ngalande za madzi, misewu yokonzedwa bwino, chithandizo cha mankhwala, ndi mautumiki amwadzidzidzi.
Mowonjezerekawonjezereka, nyumba zidzamangidwa pamalo angozi, monga ngati m’mbali mwamapiri, m’zidikha zamaliyambwe, kapena malo oipitsidwa. Mowonjezerekawonjezereka, anthu adzadwala matenda chifukwa cha kuchulukitsitsa kwa anthu, mikhalidwe yauve. Mowonjezerekawonjezereka, osauka a m’mizinda nthaŵi zonse adzakhala pansi pachiwopsezo cha kuchotsedwa pamalopo.
Kodi zimenezi zimatanthauza kuti palibe chiyembekezo kwa okhala m’mashantikompaundi monga msungwana wonyamula malalanje wofotokozedwa kuchiyambi kwa nkhani ino? Kutalitali!
Kusintha Kwakukulu Kulinkudza
Mawu a Mulungu, Baibulo, amasonyeza kuti kusintha kwakukulu kwa mkhalidwe wabwino kudzakhalapo—ndipotu posachedwapa. Kusintha kumeneku kudzadza, osati mwa zoyesayesa za maboma aumunthu, koma mwa Ufumu wa Mulungu, boma lakumwamba limene posachedwapa lidzalamulira dziko lonse lapansi.—Mateyu 6:10.
Pansi pa Ufumu wa Mulungu, m’malo mwakuthithikizana m’makomboni atimisasa ndi mashantikompaundi, mabanja opembedza Mulungu adzakhala m’paradaiso. (Luka 23:43) Mmalo mwakukhala ndi mantha nthaŵi zonse akuwopa kuchotsedwa pamalo, Baibulo limanena kuti “adzakhala munthu yense patsinde pampesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.”—Mika 4:4.
Pansi pa Ufumu wa Mulungu, mmalo mwakumwalira akali ana m’malo ochulukitsitsa, anthu “adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda ya mpesa, ndi kudya zipatso zake. . . . Pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga.”—Yesaya 65:21, 22.
Malonjezoŵa angakhale ovuta kwa inu kuwakhulupirira, koma mungakhale wotsimikizira kuti adzakwaniritsidwa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Mulungu sanama, ndipo “palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.”—Luka 1:37; Numeri 23:19.
[Chithunzi patsamba 13]
Pansi pa Ufumu wa Mulungu, umphaŵi ndi mashantikompaundi zidzaloŵedwa m’malo ndi mikhalidwe yaparadaiso