Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 12/8 tsamba 8-9
  • Mtsogolo Mosangalatsa mwa Ana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtsogolo Mosangalatsa mwa Ana
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Masokawo Ngonenedweratu
  • Mtsogolo Mosangalatsa
  • Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Dziko Latsopano Layandikira!
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Chiwonongeko cha Dziko Chonenedweratucho Chidzadza Liti?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Chifuno cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Posachedwapa
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 12/8 tsamba 8-9

Mtsogolo Mosangalatsa mwa Ana

PAMSONKHANO Wadziko wa Ana, atsogoleri adziko ambiri analankhula mwachidaliro ponena za mtsogolo. Iwo adaneneratu “nyengo yatsopano” ya ana, “kudzipereka kwatsopano kuzosoŵa za mwana.” Iwo analankhula za “‘chigwirizano chatsopano’ chopatsa ‘moyo kumgwirizano waumodzi ndi wotsimikizirika wadziko’” wa kuthandiza ana.

Amenewotu ndimawu abwino. Koma tidzawona kuti mitundu idzafika mpaka pati m’kufikira zonulirapo zake. Nkoyenera kuzindikiridwa kuti mkati mwa miyezi isanu pambuyo pa msonkhanowo, mitundu inamenya nkhondo ya Persian Gulf imene inatsimikizira kukhala yodya ndalama kopambana—mamiliyoni zikwi US$61—ndi yowononga malo okhala koposa ina iriyonse. Itatha zikwi mazana ambiri za anthu m’Iraq ndi Kuwait zinali zopanda pokhala. Zikwi zambiri zinafa—panthaŵi ina anthu mazana ambiri tsiku lirilonse—kufa ndi njala, kusatetezereka, kusadya mokwanira, ndi matenda. Pafupifupi okwanira 8 mwa 10 alionse anali akazi ndi ana.

Masokawo Ngonenedweratu

Ophunzira Mawu a Mulungu amadziŵa kuti mavuto amene akusautsa ana a padziko pano ananenedweratu pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo. Baibulo lidaloseratu za “masiku otsiriza” ano kuti:

◻ “Kudzakhala . . . miliri.”—Luka 21:11.

◻ “Kudzakhala njala.”—Mateyu 24:7.

◻ “[Anthu adzakhala] akuwononga dziko.”—Chivumbulutso 11:18.

◻ “Mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzake.”—Marko 13:8.

◻ “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, . . . opanda chikondi chachibadwidwe.”—2 Timoteo 3:1-3.

Baibulo lidaneneratunso kuti nthaŵi iri pafupi kudza pamene mitundu idzalingalira kuti ikugonjetsa mokwanira mavuto a mtundu wa anthu kotero kuti idzalengeza kuti: “Mtendere ndi chisungiko!”—1 Atesalonika 5:3, NW.

Mtsogolo Mosangalatsa

Komabe, chilengezocho, kwenikweni chidzasonyeza nthaŵi yoti Mulungu aloŵerere m’zochitika za anthu. Mwanjira ya Ufumu wake wakumwamba, Mulungu adzachotsa dongosolo lamakonoli lazinthu ndi kuyambitsa dziko lake latsopano la mtendere weniweni ndi chisungiko chokhalitsa, kwa ana ndi kwa achikulire omwe.—Miyambo 2:21, 22; Daniel 2:44; Mateyu 6:10.

M’kakonzedwe kabwino kopambana ka Ufumu wa Mulungu, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Kudya mosakwanira kudzakhala kutatha: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” (Salmo 72:16) Ngakhale nkhondo siidzakhalakonso, pakuti Baibulo limalonjeza kuti: “[Yehova] aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi.”—Salmo 46:9.

Koma bwanji za ana onse—ndi ena—amene afa kale ndi kudya mosakwanira, matenda, kapena zochititsa zina? Mawu ouziridwa a Mulungu akulengeza kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Machitidwe 24:15.

Pamene anali padziko lapansi, Yesu Kristu anasonyeza kuti kuukitsidwira ku moyo padziko lapansi m’dziko latsopano la Mulungu kukaphatikizapo achichepere. Mwachitsanzo, pamene buthu lazaka 12 linafa, “anthu onse anali kumlira ndi kudziguguda pachifuwa.” Komano, atagwira dzanja la wachichepereyo, Yesu anati kwa iye: “Buthu, tauka.” Cholembedwa cham’mbiricho chikufotokoza kuti: “Ndipo anauka pomwepo; ndipo iye anawauza kuti ampatse kanthu kakudya.” Kodi makolo ake anachita motani? ‘Anakondwera kwambiri ndi chimwemwe chachikulu.’—Luka 8:40-42, 49-56; Marko 5:42.

Pachochitika china, Yesu anakumana ndi mpingo wa maliro wophatikizapo mkazi wamasiye amene mwana wake wamwamuna mmodzi yekha anafa. Yesu “anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka. Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo [Yesu] anampereka kwa amake.” Awo amene anali pafupi “analemekeza Mulungu.”—Luka 7:11-16.

Chotero, muulamuliro wolungama wa boma Laufumu la Mulungu, ana, kuphatikizapo oukitsidwawo, adzakhala ndi mtsogolo mothekera mosangalatsa kopambana. Iwo adzakhoza kukulira m’dziko lachilungamo ndi mtendere lokongola kwambiri, losungika kwambiri, laulemerero kwambiri, kotero kuti Yesu moyenerera akulitcha “Paradaiso.”—Luka 23:43.

[Chithunzi patsamba 9]

M’dziko latsopano la Mulungu, ana adzakula ali osungika, athanzi labwino, ndi achimwemwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena