Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 1/8 tsamba 4-9
  • Kodi Kupatsa kwa pa Krisimasi Nkwanzeru?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kupatsa kwa pa Krisimasi Nkwanzeru?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Kumachita kwa Ana
  • Mphatso za pa Krisimasi ndi Kunena Zowona
  • Kodi Nchizoloŵezi Chachikristu?
  • Mmene Yesu Amawonera Kupatsa
  • Miyambo ya Krisimasi—Kodi Ziyambi Zake Nzotani?
    Galamukani!—1989
  • Khirisimasi—N’chifukwa Chiyani Imachitikanso M’mayiko a Kummaŵa?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Chiyambi cha Krisimasi Yamakono
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Krisimasi Imatanthauzanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 1/8 tsamba 4-9

Kodi Kupatsa kwa pa Krisimasi Nkwanzeru?

NDALAMA zambiri zimawonongedwa pa Krisimasi chifukwa chakuti aliyense amayembekezeredwa kupereka mphatso panthaŵiyo ya chaka. Ngati wina sapereka, iye waswa mwambo wamaziko. Koma katswiri wazachuma James S. Henry, polemba m’magazini a The New Republic, anasuliza “kupatsa kokakamiza” kotero kukhala kothetsa chimwemwe ndi kowawanya ndalama.

“Kupereka mphatso kosayenera kuli umboni wina wa kuwawanyaku,” iye akufotokoza motero. “Malinga ndi masitolo aakulu a ku New York, chaka chirichonse pafupifupi 15 peresenti ya zinthu zogulidwa paselo pa Krisimasi zimabwezedwa kumasitolo. Popeza kuti mphatso zambiri zosayenera zimasungidwa ndi ozilandira . . . , zokwanira chigawo chimodzi mwa zitatu za zinthu zogulidwa zingakhale zosayenera kwa olandirawo.”

Kwenikweni, kodi nkwanzeru kusunga ndalama chaka chonse zokagulira mphatso zimene ena sangafunikire kapena zimene sangafune? Ndipo kodi nkwanzeru kuyesa kukondweretsa ena ndi mphatso zokwera mtengo?

“Mbali yoipa kwambiri ya kugula zinthu kwa pa Krisimasi ndiyo ‘kupatsa kodziwonetsera,’” akutero Henry. “Mphatso zosangalatsa,” iye akutero, “moyenerera zimalinganizidwira awo amene safunikira kwenikweni mphatso iriyonse (‘munthu amene ali ndi chirichonse’). Mphatso zamtengo wapatali zochuluka zotero zimaperekedwa pa Krisimasi; miyezi itatu yomalizira ya chaka, malinga ndi umboni wa masitolo aakulu a ku New York, imakhala ndi malonda oposa theka la malonda a chaka chonse a diamondi, watchi, ndi majekete aubweya.”

Komabe, ngakhale mphatso zokwera mtengo kaŵirikaŵiri sizimakondweretsa olandirawo, makamaka ngati ziperekedwera kuyesa kuwongolera unansi wosweka. Malinga ndi kunena kwa dokotala wa ku Canada Richard Allon, “ngati simungakomerane mtima chaka chonse, simudzawongolera zinthu ndi mphatso yamtengo wapatali. Simudzathetsa liŵongo lanu, ndipo mwinamwake mudzaligaŵira kwa munthu winayo.”

Mwachisoni, mamiliyoni a anthu m’maiko osatukuka alibe zofunika zazikulu za moyo, komabe awo okhala m’maiko otukuka kaŵirikaŵiri amawoneka kuti ali ndi zonse kusiyapo chiyamikiro cha chuma chawo. Mphatso za pa Krisimasi zimalandiridwa ndi mphwayi—“kodi ndidzatani nacho chinthuchi?”—kapena movutika maganizo—“ndithudi, ine sindinafune chimenechi”—kapena mwinamwake ndi mkwiyo ndithu—“mphatso imene ndinampatsa inali yokwera mtengo kuŵirikiza kaŵiri kuposa imeneyi!” Nchifukwa chake gulu lotetezera ana linanena kuti pa Krisimasi zambiri zimaperekedwa ndipo kaŵirikaŵiri mosalingalira kwambiri.

Ndiponso, Krisimasi imavumbula chisalungamo cha anthu, ikumachititsa zitsenderezo zazikulu ndi kupanda chimwemwe. Ena alibe ndalama zokwanira kugulira mphatso, ndipo mu United States, zimenezi mwachiwonekere zimachititsa kuba kochuluka panyengo ya Krisimasi kuposa panthaŵi ina iriyonse ya chaka. Katswiri wazachuma Henry anasimba kuti: “Apolisi amakhulupirira kuti kuba konseku kumachitika chifukwa chakuti mbala nazonso zimafuna kugaŵira mabanja awo mphatso.”

Ambiri amavomerezana ndi wolemba nkhani m’danga lake la nyuzipepala Tom Harpur, amene analemba mu Sunday Star ya ku Toronto, Canada, kuti: “Kumbuyo kwa chikondwerero chokakamiza chonsecho, ndikudziŵa kuti Krisimasi iri kwakukulukulu nthaŵi ya kutekeseka kwakukulu, kusakhutira, liŵongo ndi kutopa kwambiri kwa mamiliyoni m’chitaganya chathu.”

‘Koma zimenezi ziri bwino poti nkuvutikira ana,’ ena angatsutse motero. Komabe, kodi kupatsa kwa pa Krisimasi kumapindulitsadi ana?

Zimene Kumachita kwa Ana

“Ngakhale kuti imeneyi iyenera kukhala nthaŵi ya ‘chimwemwe’ yachaka,” anatero phungu wa sukulu Betty Poloway, “pamakhala ana ochuluka opanda chimwemwe.” Chifukwa? Kodi kupatsa kwa pa Krisimasi kungavulaze ana motani?

Susan James, mayi wa ana aang’ono atatu, anati: “Ndinapenyerera ana anga akutsegula mapaketi a mphatso zawo, imodzi ndi imodzi. Atamaliza, anaimirira mapepala ali mbwe napempha zowonjezereka! Saali ana aumbombo komabe mphatso zonse, kutsatsa malonda ndi malonjezo onse, zinawakopa kwambiri moti anakhala aumbombo.”

Karen Andersson, mkulu wa gulu lopenda zamaganizo a ana pachipatala cha Connecticut, U.S.A., anafotokoza vutolo motere: “Zimakwiitsa kwambiri kutsikira kuchipinda chochezera pa Krisimasi m’maŵa ndi kuwona mphatso zonsezo. Iwo mofulumira amatsegula iriyonse ya mphatso za zoseŵeretsa ndipo samakhala ndi nthaŵi ya kuzipenyetsetsa. Kwa mwana amene angakhale wosakhazikika kapena wansontho, kapena wansangala kopambanitsa ngakhale m’mikhalidwe yabata kopambana, Krisimasi ingakhale yovutitsa.”

“Mphatso sizimadzetsa chimwemwe chimene zinkadzetsa,” inatero nyuzipepala ina ya ku Jeremani pankhani ya Krisimasi. Mkazi wina anadandaula kuti: “Kale ana anali kukhutiritsidwa atalandira bukhu labwino, magulovu, kapena kanthu kena kakang’ono. Koma tsopano mdzukulu wanga amandiuza kuti: ‘Agogo, chaka chino ndifuna kompyuta!’”

Inde, kupatsa kwa pa Krisimasi kumakulitsa umbombo ndi dyera. “Munthu angofunikira kupita [kusitolo la zoseŵeretsa] lirilonse pathaŵi imeneyi ya chaka,” anatero katswiri wazachuma Henry, “kuti awone mmene zitsenderezo zazikulu za nyengo imeneyi zimayambukirira maunansi a makolo ndi ana: amayi okwiya akukoka tiana tomwerekera ndi zoseŵeretsa kuchoka kuzinthu zatsopano zokwera mtengo kwambiri, zosakhalitsa, tikumapalapata ndi kuliritsa.”

Koma palinso mavuto aakulu kwambiri odzutsidwa ndi kupatsa kwa pa Krisimasi.

Mphatso za pa Krisimasi ndi Kunena Zowona

Funsani mwana wachichepere kumene kunachokera mphatso zake, ndipo kodi mwachiwonekere adzayankha motani? Malinga ndi kufufuza kwa New York Times, 87 peresenti ya ana a ku Amereka amsinkhu wapakati pa zaka zitatu ndi khumi amakhulupirira Santa Claus. Makolo ambiri amachirikiza chikhulupiriro chimenechi, akumafunsa kuti: “Kodi nchiyani chimene ufuna kuti Santa akakubweretsere chaka chino?” Komabe, kodi zotsatirapo zakhala zotani?

Yankho likupezeka m’chokumana nacho cha Cynthia Keeler, chosimbidwa mu Daily News ya ku New York. “Amayi, kodi Santa Claus alikodi?” mwana wake wotchedwa Britton, wa zaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa, anafunsa motero.

Cynthia anayesa kuzemba, monga momwe makolo ambiri amachitira atafunsidwa funsolo. “Kodi uganiza bwanji?” iye anafunsa motero.

Britton anati mabwenzi ake anamuuza kuti kulibe, koma kuti anali wosatsimikizira. Ndiyeno anayamba kulira. “Ndiyenera kudziŵa, Amayi,” anatero akugwetsa misozi.

“Ngati sanalire, mwinamwake sindikanamuuza,” Cynthia anatero. “Koma inali nkhani ya moyo ndi imfa kwa iye. Anali kufuna yankho basi. Ndinamuuza kuti Santa weniweni kulibe.”

Daily News inasimba kuti: “Akupitiriza kulira, Britton Keeler anaimba amayi ake mlandu umene makolo onse amawopa pamene bodza ladziŵika ndipo Santa Claus wavumbulidwa: ‘Nchifukwa ninji munandiuza mabodza?’”

Zotsatirapo za kunama kwa makolo kaŵirikaŵiri ziri zosakaza, monga momwe Bruce Roscoe, profesa wa maphunziro a banja pa Central Michigan University, U.S.A., ananenera: “Mwana amadzawona kuti amayi ake ananena bodza ndipo ana ena onse ananena zowona.” Chotero, Profesa Roscoe anatero, mwanayo kaŵirikaŵiri amakaikira zinthu zina zimene makolo ake anamuuza.

Fred Koenig, profesa wa maphunziro openda mmene maganizo amayambukirira kakhalidwe ka anthu pa Tulane University ku New Orleans, Louisiana, U.S.A., anagogomezera kuti: “Atatulukira mabodzawo, kudalirika kwa makolo kumathadi.” Anawonjezera kuti: “Zimakaikiritsa zinthu zambiri.” Mwanayo angaganize kuti “mwinamwake nkhani yonse ya chipembedzo yangokhala chinyengo basi.”

Ndithudi, sikumakhala kwanzeru kuchirikiza bodza mwa kuuza ana kuti munthu wina wongopeka amawapatsa mphatso. Komabe, kodi alendo sanabweretse mphatso kwa Yesu khandalo patsiku lake lobadwa? Chotero kodi iye sangavomereze kupereka mphatso pa Krisimasi lerolino?

Kodi Nchizoloŵezi Chachikristu?

Baibulo limanenadi kuti anzeru, kapena openda nyenyezi, anabweretsa mphatso kwa Yesu. Komabe, kupatsa kwa pa Krisimasi sikumatengera chitsanzo chawo chifukwa chakuti iwo sanapatsane mphatso. Chofunika koposa, sanapereke mphatso pakubadwa kwa Yesu koma panthaŵi ina pambuyo pake. Zochita zawo zinali zogwirizana ndi mwambo wamakedzana wa kulemekeza mafumu. Tawonani kuti Baibulo limati pamene anafika Yesu sanalinso modyera ng’ombe koma anali kukhala m’nyumba. Nchifukwa chake Herode, pamaziko a zimene iwo anamuuza, analamula kuti anyamata onse azaka ziŵiri ndi zocheperapo aphedwe.—Mateyu 2:1-18.

Ndiponso lingalirani izi: Kodi sizodabwitsa kuti patsiku lolingaliridwa kukhala pamene Yesu anabadwa, iye mwiniyo samalandira kalikonse? Mwinamwake samalingaliridwa mpang’ono pomwe! Kwenikweni, kodi nkuti kumene mwambo wa kupatsa kwa pa Krisimasi unayambira?

Polemba m’magazini a Independent a ku Los Angeles, Diane Bailey anafotokoza kuti: “Kupatsana mphatso kunayambira ku Roma wamakedzana, pamene anthu anali kupatsana mphatso zazing’ono zachizindikiro m’madzoma a kulambira dzuŵa ndi chaka chatsopano.”

Pamutu wakuti “Kuvumbula Miyambo ya Yule,” Anita Sama analemba m’nkhani ya Gannett News Service kuti: “Kale kwambiri mapwando Achikristu asanakhale, kupatsana mphatso kunali mbali ya zikondwerero za m’nyengo yachisanu. Aroma ankapatsana nthambi za mitengo yopatulika, ndiyeno anasinthira ku zinthu zazikulu zosonyeza mafuno abwino a chaka chirinkudza—siliva, golidi ndi zakudya zopakidwa uchi.”

Chowonadi nchakuti, Krisimasi iri phwando lachikunja limene linalandiridwa ndi Chikristu Chadziko. December 25 liri tsiku, osati lobadwa Yesu Kristu, koma nditsiku logwirizana ndi phwando lachikunja lamakedzana loluluzika limene Akristu oyambirira anapeŵa.—Wonani bokosilo, “Kodi Magwero Enieni a Krisimasi Nchiyani?” pamasamba otsatira.

Ngati Yesu akanakhala padziko lapansi lerolino, kodi akanakuwona motani kupatsa kwa pa Krisimasi?

Mmene Yesu Amawonera Kupatsa

Ndithudi Yesu samatsutsa kupatsa. Mosiyana, pokhala wofunitsitsa nthaŵi zonse kudzipereka yekha mopanda dyera pakutumikira ena, anaphunzitsa ophunzira ake kuti: “Patsani.” Ndipo iye akumasonyeza kuti kupatsa kungachititse opatsawo kudalitsidwa, anawonjezera kuti: “Ndipo kudzapatsidwa kwa inu.”—Luka 6:38.

Komabe, Yesu sanali kusonya kukupatsana mphatso. Mmalo mwake, anali kugogomezera chowonadi chodziŵika ndi onse chakuti kupatsa kopanda dyera kaŵirikaŵiri kumabwezeredwa. Zimenezi zimakhala choncho makamaka ngati wopatsayo ali ndi cholinga chabwino ndipo amakonda winayo ‘kwenikweni kuchokera mumtima.’—1 Petro 1:22.

Chikondi sichimafuna malipiro a mautumiki ake, choncho Yesu ananena kuti: ‘Popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe chimene lichita dzanja lako lamanja; kotero kuti mphatso zako zachifundo zikhale zamtseri.’ Moyenerera wopatsayo samadziwonetsera iyemwini kapena mphatso yake, komabe sadzakhala wosafupidwa. Yesu anasonyeza zimenezi pamene anawonjezera kuti: ‘Atate wako wakuwona mtseri adzakubwezera iwe.’ (Mateyu 6:3, 4) Ndiponso, wopatsayo ayenera, monga momwe Baibulo limanenera, ‘kuchita monga anatsimikiza mtima, simwachisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.’—2 Akorinto 9:7.

Chotero kupatsa kumene kumakondweretsa Kristu kumasonkhezeredwa ndi chikondi, kumachitidwa popanda kuyembekezera kupatsidwanso kalikonse, ndipo sikumachitidwa mwachisoni kapena mokakamiza. Kupatsa koteroko nkosiyana chotani nanga ndi kupatsa kochuluka kochitidwa pa Krisimasi!

Chotero, kupatsa kumene kuli magwero a chimwemwe sikumadalira pa kalenda kapena pa miyambo. Ndiponso sikumavumbula kuchuluka kwa ndalama zimene wopatsayo wawononga, kumangovumbula ukulu wa kuwoloŵa manja kwake. Ndithudi, Krisimasi yasokeretsa mamiliyoni ambiri kupatsa zinthu zolakwika, kaŵirikaŵiri pazifukwa zolakwika. Pamenepatu, bwanji osayesa kanthu kena koposa kupatsa kwa pa Krisimasi? Yesani mtundu wa kupatsa umene umadzetsa madalitso ochuluka ndi chimwemwe chenicheni, umene uli mutu wa nkhani yotsatira.

[Bokosi/Chithunzi pamasamba 8, 9]

Kodi Magwero Enieni A Krisimasi Nchiyani?

ANTHU ophunzira amadziŵa kuti December 25 sindilo tsiku limene Yesu Kristu anabadwa. New Catholic Encyclopedia imavomereza kuti: “Deti la kubadwa kwa Kristu nlosadziŵika. Mabuku Amauthenga Abwino samasonyeza tsiku kapena mwezi.”

Ndiponso, pali maumboni ambiri akuti Krisimasi ndi miyambo yake inatengedwa kumagwero osakhala Achikristu. Kunena zowona, U.S. Catholic inati: “Nkosatheka kulekanitsa Krisimasi ndi magwero ake achikunja.”

The Encyclopedia Americana inalongosola kuti: “Miyambo yochuluka imene tsopano iri yogwirizanitsidwa ndi Krisimasi poyambirira sinali miyambo ya Krisimasi koma inali miyambo yomwe inaliko Chikristu chisanakhale ndipo sinali Yachikristu koma inangolandiridwa ndi tchalitchi Chachikristu. Saturnalia, phwando Lachiroma lomwe linali kuchitidwa pakati pa December, linapereka chitsanzo cha miyambo yambiri yakusangalala kwa pa Krisimasi. Mwachitsanzo, kuphwando limeneli kunatengedwa madyerero onkitsa, kupereka mphatso, ndi kuyatsa makandulo.”

Ponena za mwambo wa kupereka mphatso, magazini a History Today anati: “Kupereka mphatso paphwando lapakati pa nyengo ya chisanu motsimikizirikadi kunangoyamba monga mwambo wamatsenga osati monga mwambo wamayanjano. Mphatso za pa Saturnalia zinaphatikizapo zidole zaphula, zopatsidwa kwa ana. Mosakaikira, unalingaliridwa kukhala mwambo wabwino panthaŵi imene unayamba, koma unali ndi mbiri yoipa: ngakhale anthu apanthaŵiyo analingalira kuti umenewu mwinamwake unali chotsala cha kupereka nsembe za anthu, za ana, zodzetsa madalitso pakufesa mbewu.”

The New York Times ya December 24, 1991, inasimba nkhani yonena za magwero a miyambo ya Krisimasi, kuphatikizapo kupereka mphatso. Simon Schama, profesa wa mbiri yakale pa Harvard University, analemba kuti: “Krisimasi yeniyeniyo inaphatikizidwa ndi mapwando amakedzana okondwerera kuyamba kwa chisanu . . . M’zaka za zana lachitatu, pamene timagulu tolambira dzuŵa tonga chipembedzo cha Mithra cha ku Peresiya tinapita ku Roma, masiku a mu December anapatulitsidwa kukondwerera kubadwanso kwa Sol Invictus: dzuŵa losagonjetseka. . . .

“Tchalitchi choyambirira m’Roma chinalimbana kwambiri ndi mapwando ena achikunja aakulu aŵiri, Saturnalia lamlungu wonse, limene linayamba pa Dec. 17, ndi Kalends, limene linachingamira Chaka Chatsopano. Phwando loyambalo linali nthaŵi yakudzisungira koluluzika, kaŵirikaŵiri loyang’aniridwa ndi mbuye wa chikondwerero, osati ndi Santa koma ndi Saturn wonenepa iyemwiniyo, wochita mchezo wa kudya, kumwa ndi mitundu ina ya zonyansa. Komabe, panali panthaŵi ya Kalends, pamene chaka chinasintha, pamene panali dzoma la kupatsana mphatso, kaŵirikaŵiri zomangidwa kunthambi za mitengo zimene zinakometsera nyumba mkati mwa mapwando.

“Kaimidwe ka tchalitchi choyambirira pa zikondwerero zoipa zimenezi mwachiwonekere kanali kosalimba. Atsogoleri ake, makamaka St. John Chrysostom wochirikiza mwamphamvu chiletso, sanaumirize kulolera molakwa zonyansa zachikunja. . . . Popeza kuti onse sanali kumvana padeti lenileni la kubadwa kwa Yesu . . . , kuyenera kukhala kutawonekera kothandiza kuliloŵetsa mmalo mwa Saturnalia . . . Motero kubadwanso kwa dzuŵa kunadzakhala kubadwa kwa Mwana wa Mulungu mmalo mwake . . .

“Mofananamo, Kalends inaloŵedwa mmalo ndi Phwando la Epiphany, ndipo mphatso ndi zokometsera zimene Aroma achikunja anali kupatsana zinakhala ulemu wopatsidwa ndi mafumu atatu kwa Mfumu yatsopano ya Dziko. Podzafika chapakati pa zaka za zana lachinayi, mbali zazikulu za kalenda ya Krisimasi zinakhazikitsidwa mwachikhalire.”

Pamene kuli kwakuti anthu ophunzira amavomereza mosavuta magwero achikunja a Krisimasi ndi miyambo yake, ambiri amatsutsa kuti magwero oterowo alibe kanthu kwenikweni. Poyankha nkhani ya Profesa Schama, rabi wosiya ntchito analemba m’kalata yake kwa mkonzi wa Times kuchiyambi kwa chaka chatha kuti: “Magwero a mwambo woikidwa samakhudza kufunika kwake lerolino.” Ponena za Krisimasi ndi mapwando ena oterowo, iye anati: “Okondwerera ake amawapatsa tanthauzo latsopano limene limachititsa moyo wa okondwererawo kukhala ndi chifuno ndi kukondweretsa mtima wawo.”

Komabe, kodi mapwando a Krisimasi amakondweretsa mtima ndi kubala zipatso zabwino za Chikristu? Kunena zowona, monga momwe kwavomerezedwera kale, zipatso kaŵirikaŵiri zimakhala zoipa, osati zabwino. Ndiponso, kodi Akristu ayenera kubwereka mapwando achipembedzo achikunja? Baibulo limachenjeza kuti: ‘Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? . . . Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati [Yehova, NW], ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka.’—2 Akorinto 6:14-17.

Kumbukiraninso zimene Yesu ananena pa kulambira Mulungu Wamphamvuyonse kuti: ‘Omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.’ (Yohane 4:24) Chotero, kuti kulambira kwathu kulandiridwe ndi Mulungu, kuyenera kuzikidwa pa chowonadi. Komabe, Krisimasi imachirikizidwa kukhala tsiku lobadwa Yesu Kristu ngakhale kuti siiri tero. Ndipo bwanji za olingaliridwa kubweretsa mphatso za Krisimasi ongopeka, onga ngati Santa Claus? Pamene ana amachititsidwa kukhulupirira kuti mphatso zimachokera kwa otero, kodi kumeneko kwenikweni sikunyenga anawo?

Ngati ndinu wosamala ponena za Mulungu, mudzamvera lamulo lake loletsa kukhala ndi phande m’zimene ziri zonyansa m’lingaliro lachipembedzo. Kodi ndinu wosamala kwambiri ponena za chowonadi kotero kuti mumapeŵa maholide odzala mabodza?

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi nkwanzeru kunyengeza ana mwa kuwauza kuti Santa Claus amawabweretsera mphatso?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena