Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 5/8 tsamba 30-32
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chakuti Nkhondo Idzatha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chakuti Nkhondo Idzatha?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyembekezo Chonyenga
  • Awo Amene Akukwaniritsa Lonjezo la Mulungu
  • Mmene Mapeto a Nkhondo Adzafikira
  • Nkhondo Yothetsa Ndhondo
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhondo
    Galamukani!—2017
  • Mtendere—Zenizenizo
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Posachedwapa—Dziko Lopanda Nkhondo!
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 5/8 tsamba 30-32

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chakuti Nkhondo Idzatha?

NKHONDO YADZIKO I, yomenyedwa kuchokera 1914 mpaka 1918, inatchedwa nkhondo yothetsa nkhondo zonse. Koma chiyambire pamenepo pakhala nkhondo zoposa 200, kuphatikizapo yaikulu koposa zonse zochitikapo—Nkhondo Yadziko II.

Mwachiwonekere, zoyesayesa za anthu zakuthetsa nkhondo zalephera kotheratu. Pamenepo, kodi nzodabwitsa kuti ambiri amati, “Nkhondo zidzakhalapo, nthaŵi zonse”? Kodi nzimene mumakhulupirira?

Kukhazikitsidwa kwa Mitundu Yogwirizana mu 1945 pambuyo pa Nkhondo Yadziko II kunali ndi cholinga cha kupatsa anthu otopa ndi nkhondo chiyembekezo cha dziko lopanda nkhondo. Chiyembekezo chinafotokozedwa m’mawu ozokota pachipupa cha nyumba ya Mitundu Yogwirizana m’New York City, amene amati: ADZASULA MALUPANGA AWO AKHALE ZOLIMIRA. NDI THUNGO ZAWO ZIKHALE ANANGWAPE: MTUNDU SUDZANYAMULA LUPANGA KUMENYANA NDI MTUNDU WINA. NDIPO SADZAPHUNZIRANSO NKHONDO.

Momvetsa chisoni, mitundu yanyazitsidwa ndi mawu ameneŵa onenedwa mokongola chifukwa cha mtopola wawo wa nkhondo. Komabe, mawuŵa adzakwaniritsidwa! Zili choncho chifukwa chakuti anachokera ku Magwero oposa anthu opanda ungwiro zaka 2,500 zapitazo. Iwo amaimira lonjezo limene Mulungu Wamphamvuyonse anapereka.—Yesaya 2:4.

Chiyembekezo Chonyenga

Ambiri ayang’ana kumatchalitchi kuti athandize kupanga dziko lopanda nkhondo. Koma kwenikweni, matchalitchi atsimikiziridwa kukhala mtundu umodzi wa magulu ochititsa nkhondo, ndi ogaŵanitsa. Mwachitsanzo, Frank P. Crozier, kazembe wankhondo wa ku Briteni m’Nkhondo Yadziko I, anati: “Matchalitchi Achikristu ndiwo odziŵa koposa kuchilikiza kukhetsa mwazi amene tili nawo ndipo tinawagwiritsira ntchito mwaulere.”

Motero, nkofunika kwambiri kuti tisiyanitse pakati pa Chikristu chowona ndi chonyenga. Kutithandiza kuchita zimenezi, Yesu anapereka njira yosavuta iyi: “Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.” (Mateyu 7:16) Mawu, kapena zikhulupiriro, sizokwanira. Kuchitira chitsanzo zimenezi, Steve Whysall, wolemba wapantchito wa Sun ya ku Vancouver, anati: “Sikuti anthu onse ovala maovolosi akuda ndi mafuta ali amakanika, ngakhale kuti awoneka ngati amakanika, . . . ngakhale ngati anganene kuti ‘Ndife amakanika.’”

Mwakugwiritsira ntchito chitsanzo chimenechi pa Akristu, Whysall anati: “Kaŵirikaŵiri mudzamva anthu akukamba za mmene chakutichakuti chinachitidwira m’dzina la Chikristu ndi mmene chinaliri chinthu choipa kuchichita. Eya, inde, chinali choipa. . . . Koma kodi ndani amene ananenapo konse kuti ali Akristu amene anachita zinthu zoipa zoterozo?

“Eya, inu mungatero kuti, matchalitchi okhazikika amatero. Chabwino, koma kodi ndani ananenapo konse kuti matchalitchi okhazikitsidwa ali Achikristu?

“Papa anadalitsa Mussolini, ndipo pali maumboni osonyeza kuti apapa ena anachita zinthu zoipa kwambiri kalelo. Chotero ndani ananena kuti iwo anali Akristu?

“Kodi muganiza kuti chifukwa munthuyo ndipapa basi ndiye kuti alidi Mkristu? Kungonena kuti ‘ndine Mkristu’ sikumatanthauza kuti munthuyo alidi Mkristu—monga momwedi munthu wodzinenera kukhala makanika angakhale sali makanika.

“Baibulo limachenjezadi Akristu ponena za anthu amene amadziwonetsera kukhala Akristu . . . Palibe Mkristu amene angachite nkhondo ndi Mkristu mnzake—kukakhala ngati munthu wodzimenya yekha.

“Akristu owona ali abale ndi alongo mwa Yesu Kristu. . . . Iwo sakayesa konse, ngakhale mpang’ono pomwe kuvulazana mwadala.”

Chotero tifunikira kugwiritsira ntchito njira ya Yesu ndi kuyang’ana pazipatso zimene matchalitchi amatulutsa. Koma kodi nzipatso zotani? Baibulo limasonyeza chimodzi makamaka, likumati: “M’menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake.”—1 Yohane 3:10-12.

Mmalo molimbikitsa chikondi kwa wina ndi mnzake, matchalitchi achilikiza ndipo ngakhale kuchititsa kuphana wina ndi mbale wake m’nkhondo. Chifukwa chake, iwo akhala ziŵiya zogwiritsira ntchito za Satana Mdyerekezi monga momwedi zinaliri zipembedzo za Aigupto akale, Asuri, Ababulo, ndi Aroma. Yesu Kristu anatcha Satana “mkulu wa dziko ili lapansi” nanena za otsatira Ake owona kuti: “Siali a dziko lapansi monga ine sindiri wa dziko lapansi.” (Yohane 12:31; 17:16; 2 Akorinto 4:4) Komabe, matchalitchi adzipanga okha kukhala mbali yofunika kwambiri ya dziko lino.

Chotero, mwachiwonekere, Mulungu sakugwiritsira ntchito matchalitchiwo kukwaniritsa chifuniro chake cha kulenga dziko lopanda nkhondo. Mosasamala kanthu ndi zimene atsogoleri achipembedzo ndi oimira tchalitchi ena amanena, Mulungu samachilikiza mbali iliyonse m’nkhondo za mitundu.

Kodi lonjezo la Mulungu la kuchotsa nkhondo lidzakwaniritsidwa motani? Kodi pali anthu alionse amene asuladi malupanga awo kukhala zolimira? Ndithudi ena atero.

Awo Amene Akukwaniritsa Lonjezo la Mulungu

Wolemba mbiri ya tchalitchi wotchuka C. J. Cadoux anati: “Akristu oyambirira anakhulupirira Yesu mwa mawu ake okha . . . Iwo anadziŵikitsa chipembedzo chawo ndi mtendere; anatsutsa mwamphamvu nkhondo chifukwa cha kukhetsa mwazi koloŵetsedwamo; anagwiritsira ntchito pa iwo eni ulosi wa Chipangano Chakale umene unalosera za kusanduliza zida za nkhondo kukhala ziŵiya zolimira.”—Yesaya 2:4.

Koma bwanji ponena za lerolino? Kodi pali anthu amene amakhulupirira Yesu mwa mawu ake okha ndi amene amakondanadi wina ndi mnzake? Kodi ameneŵa, kwenikweni, asula malupanga awo kukhala zolimira? Eya, Encyclopedia Canadiana imanena kuti: “Ntchito ya Mboni za Yehova ndiyo kuutsanso ndi kukhazikitsanso Chikristu chakale chotsatiridwa ndi Yesu ndi ophunzira ake mkati mwa zaka za zana loyamba ndi lachiŵiri za nyengo yathu. . . . Onse ali paubale wawo.”

Motero, potsatira lamulo la Kristu la kukondana wina ndi mnzake, Mboni za Yehova zimakana kuda kapena kupha abale awo, ngakhale kuti iwo angakhale a fuko kapena mtundu wina. (Yohane 13:34, 35) Martin Niemöller, mtsogoleri Wachiprotestanti m’Jeremani, ananena kuti “mkati mwa nyengo zonse, [matchalitchi] nthaŵi zonse avomereza kudalitsa nkhondo, asilikali ndi zida zankhondo ndi kuti anapemphera mwanjira yosemphana kwambiri ndi Chikristu kuti adani awo awonongedwe.” Komabe, mosiyana, iye anati, Mbonizo “m’maunyinji a mazana ndi zikwi zapita kumisasa yachibalo ndi kufa chifukwa chakuti zinakana kutumikira m’nkhondo ndi kukana kuwombera anthu.”

Inde, mosiyana ndi anthu a zipembedzo zina, Mboni za Yehova zasuladi malupanga awo kukhala zolimira. Mwakusakhala “a dziko,” monga momwe analangizila Kristu, iwo alidi osiyana ndi zipembedzo zina. (Yohane 15:19) St. Anthony’s Messenger ya Roma Katolika inati: “Mboni za Yehova sizili mbali ya ‘chitaganya’ ndipo zimakana kulandira thayo lililonse la kudalitsa chilichonse chimene boma lisankha kuchita.”

Kodi lonjezo la Mulungu lonena za kuchotsedwa kwa zida zankhondo lidzakwaniritsidwa kokha mwanjira yakuti mamiliyoni angapo a anthu ochokera m’mitundu yonse asula malupanga awo kukhala zolimira? Kutalitali! Lonjezo la Mulungu lidzakwaniritsidwa pamlingo waukulu kwambiri ndipo mwanjira yodabwitsa.

Mmene Mapeto a Nkhondo Adzafikira

Mlengiyo, Yehova Mulungu, adzathetsa nkhondo mwakuchotsa zida zankhondo zonse ndi awo oichititsa. Wamasalmo wa Baibulo anapempha oŵerenga kulingalira chiyembekezo chosangalatsa ichi. “Idzani, penyani ntchito za Yehova,” iye analemba tero, “amene achita zopululutsa pa dziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.” (Salmo 46:8, 9) Ha, nchilengezo chochititsa nthumanzi chotani nanga!

Kodi chiyembekezo cha dziko lopanda nkhondo nchosakhulupirika? Okaikira amaganiza tero. Ngakhale wolemba mbiri ya zausilikali, Gillett Griswold, analingalira motero. Koma iye anadzipatsa nthaŵi yakusanthula umboni mosamalitsa. Monga chotulukapo, anatsimikizira kuti Baibulo lilidi lodalirika. Anapeza kuti maulosi a Baibulo onena za zochitika zoyambirira m’mbiri anakwaniritsidwa mosalephera, ndipo panthaŵi yake. Zimenezi zinampatsa chifukwa chokhulupirira kuti zochitikazo zimene zinaloseredwa kuti zidzachitika zidzaterodi panthaŵi yake.

Mwachitsanzo, lingalirani mmene zochitika zogwedeza dziko zimene zikuchitika tsopano zikugwirizanira bwino lomwe ndi zochitika zimene Baibulo linaneneratu kuti zikasonyeza masiku otsiriza a dongosolo ili la zinthu. (Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5) Izi zimatanthauza kuti tsopano tikukhala panthaŵi yakubwera kwa Ufumu wa Mulungu, kukwaniritsa pemphero limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake, lakuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

Kodi tiyenera kuyembekezera Ufumu wa Mulungu kubwera mwanjira yotani? Ulosi wa Baibulo umati pazimenezi: “Masiku a mafumu aja [kutanthauza, maboma olamulira tsopano] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu [kapena, maboma] awo onse. Nudzakhala [boma la Ufumu wa Mulungu] chikhalire.”—Danieli 2:44.

Inde, Ufumu wa Mulungu udzafika mwanjira yodabwitsa kudzachotsa maboma onse alipowa, monga momwedi Chigumula chadziko lonse chonenedweratucho chinafikira m’tsiku la Nowa. (Mateyu 24:36-39; 1 Yohane 2:17) Popeza kuti chiwonongeko cha maboma onse alipowa chayandikira, limodzinso ndi zipembedzo zowachilikiza, nkofunika kuti aliyense wa ife payekha apende mkhalidwe wake. Kodi tidzayesayesa kuphunzira ponena za Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, ndiyeno kuchita zimene amafuna kwa ife? (Yohane 17:3) Kodi tidzakondana wina ndi mnzake, tikumakana kuvulaza munthu mnzathu, ndipo motero kusonyeza kuti tasula malupanga athu kukhala zolimira?

Ngati mukuvomereza kuti nkhondo ili yopanda pake ndi kuti mukufuna kukhala padziko lapansi pamene mtendere udzakhala kulikonse, kambitsiranani ndi Mboni za Yehova. Izo zidzakondwera kukuthandizani kuphunzira zochuluka ponena za mmene nkhondo idzathera posachedwapa, pansi pa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.

Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)

[Bokosi patsamba 31]

Makonzedwe a Himmler a Mboni za Yehova

HEINRICH HIMMLER anali mkulu wa SS ya Nazi, kapena Elite Guard, ndipo mkati mwa Nkhondo Yadziko II anali wachiŵiri m’kukhala wamphamvu koposa m’Jeremani, wotsatira Adolf Hitler. Ngakhale kuti Himmler anada Mboni za Yehova chifukwa cha kukana kwawo kukhala ndi phande m’makonzedwe a Nazi akugonjetsa dziko lonse, iye anafikira pakuzilemekeza. M’kalata yake ina yolembera mkulu wa Gestapo wotchedwa Ernst Kaltenbrunner, Himmler analemba kuti:

“Zina zimene ndamva ndi zimene ndawona posachedwapa zandichititsa kulinganiza makonzedwe amene ndingakonde kukudziŵitsani. Ndikunena za Mboni za Yehova. . . . Kodi ndimotani mmene tidzalamulirira ndi kutonthoza Russia pamene . . . tidzakhala titagonjetsa mbali zazikulu za magawo ake? . . . Mitundu yonse ya chipembedzo ndi timagulu totsutsa nkhondo ziyenera kuchilikizidwa . . . , ofunika koposa pakati pawo ndizo Mboni za Yehova. Nkodziŵika bwino kuti Mboni za Yehova zili ndi mikhalidwe yabwino modabwitsa yotikomera: Kusiyapo chenicheni chakuti zimakana mautumiki ankhondo ndi chilichonse chochita ndi nkhondo . . . , izo nzodalirika koposa, sizidakwa, sizisuta; zimagwira ntchito zolimba ndipo nzowona mtima mwapadera. Izo zimanena zowona. Imeneyitu ndimikhalidwe yofunika kwambiri . . . , ndi yokhumbika.”

Ayi, Himmler sakanatha konse kunyengerera Mbonizo kugwirira ntchito Anazi. Iye sanafune mikhalidwe yakukonda mtendere ya Mbonizo kaamba ka iye mwini kapena anthu ake, koma anafuna mikhalidwe yabwino imeneyi kuyambukira nzika za Russia. Zimenezi zikawachititsa kukhala anthu amtendere, kuwachititsa kusula malupanga awo kukhala zolimira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena