Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 5/8 tsamba 23-27
  • Kodi Ndiyenera Kusamukira ku Dziko Lokhupuka Kwambiri?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiyenera Kusamukira ku Dziko Lokhupuka Kwambiri?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Musafulumire Kusankha
  • Musakhulupirire Zonse Zimene Mumamva
  • Pendani Mapindu ndi Kuipa Kwake
  • Kuphunzirira pa Zolakwa za Esau
  • Chititsani Chosankha Chanu Kukhala Chaphindu
  • Kumbukirani Zosoŵa Zanu Zenizeni
  • Muzisankha Zinthu Mwanzeru Kuti Musataye Madalitso Anu
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Moyo Wabwino Kwambiri Potumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kusamuka?
    Galamukani!—1994
  • Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Kodi Ndingapeze Bwanji Anzanga Enieni?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 5/8 tsamba 23-27

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndiyenera Kusamukira ku Dziko Lokhupuka Kwambiri?

TARA anasamuka ku Trinidad kumene anabadwira, Sheila anasamuka ku Jamaica, ndipo Erick anasamuka ku Suriname. Achichepere atatu onsewa anasamukira kudziko lokhupuka kwambiri. Chifukwa ninji?

“Achicheperefe m’Trinidad muno,” akulongosola motero Tara, “timasonkhezeredwa kwambiri ndi zimene timawona m’magazini ndi pa TV. Mwachisoni, zimenezi zimatichititsa kukhala ndi chithunzi chokopa cha United States ndi maiko ena okhupuka.”

Sheila alinso ndi nkhani yofanana: “Ndikumbukira kuuzidwa za mwaŵi waukulu wa kuloŵa ntchito ndi maphunziro aulere.” Komabe, iye anawonjezera kuti: “Sindidziŵa chifukwa chimene iwo amene anapitako kumaiko ameneŵa sanatchulire mbali zina zosakondweretsa. Mwina anachita manyazi kuvomera kuti zinthu komweko sizili bwino kwenikweni.”

Chikhalirechobe, anthu akusamukabe. Lipoti la mu Los Angeles Times linasonyeza kuti kuyambira 1980 mpaka 1990, chiŵerengero cha anthu osamukira kumaiko ena chinaŵirikiza kaŵiri ndipo chikuyembekezeredwa kuŵirikizanso kaŵiri pofika chaka cha 2000. Chaka chilichonse anthu oposa 700,000 amasamukira ku United States. Lililonse la maikowa Australia, Canada, Côte d’Ivoire, ndi Saudi Arabia limalandira odzakhala m’dziko oposa kwambiri pa 50,000 chaka chilichonse, ambiri a iwo amafunafuna moyo wokhupuka kwambiri.

Ngati mukhala m’dziko losauka kapena losatukuka, nanunso mungalingalire kuti mwina mtsogolo mwanu mungakhale mwabwinopo m’dziko lolemera kwambiri. Chimenechi nchosankha chachikulu. Kodi ndimotani mmene mungasankhire mwanzeru?

Musafulumire Kusankha

Erick, wochokera ku Suriname, akhulupirira kuti simuyenera kudya mfulumira koma muyenera choyamba kupeza chidziŵitso chilichonse chothekera. “Ngakhale ku Suriname,” iye akutero, “mabanja ambiri ali ndi achibale awo m’maiko okhupuka, ndipo muyenera kupeza chidziŵitso chatsopano ndi kudziŵa chowonadi ponena za mkhalidwe wachuma wa dziko lonse.”

Musanasankhe chochita, kumbukirani: “Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.” (Miyambo 15:22) Chotero kambitsiranani zosankha zanu mowona mtima ndi makolo anu, akulu Achikristu, ndi ena amene ali ndi chidziŵitso ndi amene amakukondani.

Musakhulupirire Zonse Zimene Mumamva

Pamene mumva malipoti abwino onena za maiko akutali okhupuka, kukhala ndi kachikaikiro kochepa koyenera kuli bwino. “Wachibwana akhulupirira mawu onse,” umatero mwambi wanzeru, “koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”—Miyambo 14:15.

Sheila, amene anali kukhala ku Jamaica, anati: “Mphunzitsi wanga wa Chingelezi anaumirira kuti kusamukira ku United States kukakhala chinthu chabwino koposa choyenera ine kuchita. Achikulire ena anandiuza kuti ngati ndikasamukira ku Canada, United States, kapena ku Mangalande, ndikapeza mapindu mosasamala kanthu za ntchito imene ndikasankha. Mwachidule, ndikakhala wopanda nzeru kukana mwaŵi umenewu.”

Kodi kusamukira kwake ku United States kunamthandizadi? “Moyo wanga unawongokeradi m’mbali zochuluka, komanso mabwenzi anga amene anatsala ku Jamaica anawongolera miyoyo yawo. Kaŵirikaŵiri umasinthanitsa vuto lina ndi linzake. Kumene ukhala sikumawongolera zinthu mwaikokokha.”

Tara, amene anasamukira ku United States kuchokera ku Trinidad, akuvomereza: “Anthu anapereka chithunzi chakuti kumaiko okhupuka kuli mwaŵi waukulu wakuwongolera zinthu m’moyo—kuphunzira, kugwira ntchito, kupeza ndalama zambiri, ndi kukhala m’mikhalidwe yabwino. Koma tsopano amene anasamuka akuzindikira kuti mikhalidwe ikuipiraipira kulikonse. Ena abwerera kwawo.”

Pendani Mapindu ndi Kuipa Kwake

Kuti musankhe bwino, pendani zochuluka osati chabe malipoti abwino a kuchuluka kwa chuma m’maiko ena. Pendani mapindu ndi kuipa kumene kusamukako kungakhale nako—m’zachuma, kakhalidwe ka anthu, makhalidwe abwino, ndi mkhalidwe wauzimu.

Mwachitsanzo, mkhalidwe wa chuma ungakhale woipa kumene mukhala. Koma kodi kulibe mwaŵi wa ntchito kwanuko? “Kwathu,” akutero Tara, “kusoŵa ntchito kunali kwakukulu, makamaka kwa aja amene sanaphunzire kwambiri.” Chotero msungwanayu anasamuka; alongo ake anatsala. “Alongo anga aang’ono aŵiri anachita kosi yopanga mipando. Tsopano iwo amagwira ntchito m’mafakitale ndi kwa anthu amene amakonda zimene iwo apanga. Mwinamwake iwo akuchita bwino kwambiri kumene ali kuposa mmene ndikuchitira kuno ku ‘dziko la mwaŵi.’”

Mutasamuka, mwachiwonekere mudzayang’anizana ndi vuto la kukhala mlendo, mwinamwake ngakhale kutairatu malamulo amakhalidwe abwino omwe mumalemekeza kwambiri. Kodi kuli bwino kusamuka ndi kukhala pangozi yotero? Ndiyenonso, kukondetsa zinthu zakuthupi nkofala m’maiko okhupuka. Kodi kumeneko kungayambukire motani mkhalidwe wanu wauzimu?

Kuphunzirira pa Zolakwa za Esau

Ponena za kupenda mapindu a zosankha ndi kuipa kwake, Esau wa m’nthaŵi za m’Baibulo anali ndi vuto lalikulu kwambiri. Mobwerezabwereza iye analephera kuyang’ana pa zinthu zofunika kwambiri—mkhalidwe wake wauzimu ndi banja lake. Chotero, zosankha zake zina zazikulu zinakhala zatsoka.

Baibulo limatsutsa “ [aliyense wosayamikira zinthu zopatulika, NW] , monga Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nawo mtanda umodzi wa chakudya.” (Ahebri 12:16) Ukulu wobadwa nawo umenewu unali wopatulika. Mulungu anapereka mwaŵi ku banja la Esau wakukhala mumzera wa makolo a Mesiya, mfungulo ya chipulumutso cha mtundu wonse wa anthu. (Genesis 22:18) Koma “Esau ananyoza ukulu wake.” Iye anaugulitsa mosavuta ndi mphodza zophika! (Genesis 25:30-34) Chuma chanu chopatulika koposa ndicho unansi wanu ndi Mlengi wanu. Musaugulitse, kuunyalanyaza, kapena kuuika pangozi chifukwa cha phindu lakuthupi.—Marko 12:30.

Pambuyo pake, pamene Esau anasamuka kumudzi umene anakulira kukakhala kudziko lina, anakwatira akazi aŵiri Ahiti. Maukwati ameneŵa pazifukwa zina angakhale anawoneka kukhala othandiza, koma mwauzimu anadzetsa mavuto okhaokha chifukwa akaziwo sanalambire Mulungu wa makolo a Esau, Isake ndi Rebeka. Akazi amenewo “anapweteka mtima” wa makolo ake.—Genesis 26:34, 35.

Kuli kofala kwa achichepere kukwatira kuti apeze chabe chilolezo choloŵera m’dziko lokhupuka kwambiri. Zamveka kuti anthu oloŵa m’maukwati okwanira 4,000 pachaka amasamuka ku India kupita ku United States, ndi ongoyerekezera 10,000 akuyembekezera kutero. Komabe, ukwati ndimphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Suyenera kupeputsidwa, kugwiritsidwa ntchito monga tikiti wamba loloŵera m’dziko lina. Talingaliraninso mmene mungapwetekere mtima wa Yehova ndi ziŵalo zokhulupirika za banja lanu ngati mukhala ‘womangidwa m’goli ndi wosakhulupirira.’—2 Akorinto 6:14.

Chititsani Chosankha Chanu Kukhala Chaphindu

Kuchitapo kanthu kwabwino pa chosankha chanu kungakhale kofunika kuposa chosankha chenichenicho. Kaya musankhe kukhala kumene muli kapena kusamuka, chinthu chachikulu ndicho kuchititsa chosankha chanu kukhala chaphindu.

Ngati mwasankha kukhala: Musasulize awo osamuka. Chosankha chawo chili thayo lawolawo. (Aroma 14:4; Agalatiya 6:4, 5) Phunzirani kuyamikira zinthu zokongola ndi mapindu amene ali m’dziko lanu lokha. Kulitsani chikondi pa anthu ndi chifundo pa zoyesayesa ndi mavuto awo.

Ngati mwasankha kusamuka: Taikani zinthu zanu zoyamba mwanzeru pamene muphunzira makhalidwe atsopano ndipo mwinamwake chinenero chatsopano. Musadzitanganitse ndi kugwira ntchito kwa maola opambanitsa kokha kuti mupeze zinthu zakuthupi zimene simunafunikire ndi kalelonse. Apo phuluzi mungakhale wotangwanitsidwa kwambiri posapita nthaŵi moti nkusoŵa nthaŵi ya zinthu zauzimu.

“Nkofunika kwambiri kukhala ndi ntchito m’dziko lamakono,” Sheila akuvomereza motero. “Komabe, banja, mabwenzi, ndi zinthu zauzimu nzofunika koposa. Zinthu zina zonse zitalephera, iwo ndiwo amatichilikiza.” Baibulo mwanzeru limatichenjeza za ‘kusachititsa [nalo dziko lapansi]; pakuti mawonekedwe a dziko ili apita.’ (1 Akorinto 7:31) Awo amene amapezadi chipambano amaika nkhaŵa zawo za ntchito ndi ndalama m’malo oyenera—zosoŵa za banja ndi zinthu zauzimu zimakhala zoyamba.

Sankhani mabwenzi anu atsopano mwanzeru. Erick akuti: “Pitirizani kuyanjana ndi mabwenzi amene amachilikiza njira ya moyo yomangirira.”

Kumbukirani Zosoŵa Zanu Zenizeni

Zinthu zimene timafunikiradi kuti tipeze chimwemwe sizimasintha. “Mosasamala kanthu za kumene tikhala,” akutero Sheila, “Zimene Yehova afuna kwa ife nzimodzimodzi.” Kodi nziti? Yesu anati momvekera: “Odala ali osauka mumzimu.” “Musadere nkhaŵa” za kukhala ndi chakudya ndi zovala zokwanira. Ikani pamalo oyamba “ufumu wake ndi chilungamo cha [Mulungu], ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 5:3; 6:31, 33.

Kutsatira malamulo amkhalidwe ameneŵa kungakuthandizeni kupeza moyo wabwinopo m’dziko lililonse.

[Zithunzi patsamba 23]

Maiko okhupuka angawoneke kukhala okopa kwambiri kuposa ndi mmene alili

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena