Olakika Poyang’anizana ndi Imfa
“Komabe chodabwitsa a Anazi, [Mboni] nazonso sizinafafanizidwe. Pamene zinatsenderezedwa kwambiri, mpamenenso zinalimbirako, kukhala zolimba monga daimondi m’kutsutsa kwawo. Hitler analimbana nazo kowopsa, ndipo zinasunga chikhulupiriro chawo. . . . Chokumana nacho chawo chili nkhani yopindulitsa kwa onse omwe amaphunzira za kupulumuka pansi pa chipsinjo chachikulu. Popeza kuti izo zinapulumukadi.”—Yonenedwa kuti inalembedwa ndi Dr. Christine King, wolemba mbiri yakale, m’magazini a Together.
MBONI ZA YEHOVA ziyenera kuwonedwa monga gulu lachipembedzo lodedwa molakwa ndi lozunzidwa kwambiri padziko lonse lapansi m’mbiri ya zaka za zana la 20. Izo zatengedwa molakwa ndipo kaŵirikaŵiri zazunzidwa kokha chifukwa cha kaimidwe kawo ka uchete Wachikristu ndi kukana kwawo kuphunzira kapena kumenya nkhondo. Kusagwirizana kwawo ndi ndale zadziko zonse kwawabweretsera mkwiyo wa olamulira opondereza ufulu m’maiko ambiri. Komabe, chinthu chimodzi chimene apereka ku mbiri yamakono ndicho cholembedwa chawo cha uchete wolimba ndi umphumphu wosagwedera.a
Wolemba mbiri yakale wa ku Briteni Arnold Toynbee analemba mu 1966 kuti: “M’nthaŵi yathu ku Jeremani kwakhala Akristu ophedwera chikhulupiriro amene anaperekadi miyoyo yawo m’malo molambira Utundu wofala woimiridwa ndi mulungu waumunthu Adolf Hitler.” Maumboni amasonyeza kuti Mboni za Yehova zinali zochuluka pakati pa ophedwera chikhulupiriro amenewo. Zokumana nazo zoŵerengeka zidzasonyeza mmene zinayang’anizirana ndi chizunzo ndipo ngakhale imfa chifukwa cha umphumphu wawo—ndipotu osangoti m’nyengo ya Chinazi yokha. M’mbali zambiri za dziko, cholembedwa chawo cha chilakiko poyang’anizana ndi imfa nchogwirizana ndi chosayerekezereka.
Nkhani ya Ananii Grogul wa ku Ukraine
“Makolo anga anakhala Mboni za Yehova mkati mwa Nkhondo Yadziko II, mu 1942, pamene ndinali ndizaka zakubadwa 13. Mwamsanga pambuyo pake, atate anagwidwa, kuikidwa m’kaidi, ndipo pambuyo pake kusamutsidwira ku misasa ya Soviet Union ku mapiri a Ural. Pamene ndinali ndizaka 15, mu 1944, akuluakulu ankhondo anandiitana kukachita utumiki wokonzekera nkhondo m’magulu ankhondo. Popeza kuti ndinali kale ndi chikhulupiriro cholimba mwa Yehova, ndinakana kuphunzira nkhondo. Pachifukwa chimenechi, pamsinkhu waung’ono umenewo, ndinaweruzidwa kukhala m’ndende zaka zisanu.
“Ndiyeno chinafika chaka chovuta kwambiri cha 1950. Ndinagwidwanso ndipo ndinaweruzidwa kubindikiritsidwa kwa zaka 25 chifukwa cha ntchito yanga monga Mboni. Ndinali ndi zaka 21 zakubadwa. Ndinakhala zaka zisanu ndi ziŵiri ndi miyezi inayi m’misasa yachibalo. Ndinawona anthu ambiri akufa, kuwonda ndi njala ndi kufooka ndi ntchito ya kalavula gaga.
“Pambuyo pa imfa ya Stalin mu 1953, mikhalidwe inayamba kusintha, ndipo mu 1957 olamulirawo ananditulutsa m’ndende. Kachiŵirinso ndinapeza ‘ufulu.’ Koma panthaŵiyi anandithamangitsira ku Siberia kwa zaka khumi.”
Kuzunzidwa Kwankhalwe kwa Mlongo Wanga
“Ku Siberia, ndinagwirizana ndi mlongo wanga wakuthupi, yemwe anakhala wolemala. Iye anagwidwa patangopita milungu iŵiri yeniyeni kuchokera pamene ndinagwidwa mu 1950. Kufufuzidwa kwa nkhani yake kunachitidwa mwanjira yopanda lamulo konse. Iwo anamtsekera m’chipinda chobindikiritsira ali yekha ndiyeno analoŵetsa makoswe m’lumande lake. Makoswewo anachecheta mapazi ake ndi kukwerakwera thupi lake. Pomalizira pake, omuzunzawo anampangitsa kuima m’madzi ozizira ofika m’chifuwa iwo ali khale kupenyerera kuzunzika kwake. Iye anaweruzidwa kukhala m’ndende zaka 25 chifukwa cha ntchito yake yolalikira. Miyendo yake yonse iŵiri inazizira, koma anakhozabe kugwiritsira ntchito manja ndi mikono yake. Anamsunga m’chipatala cha mu msasa wachibalo kwa zaka zisanu ndipo pomalizira pake anamuwona monga wakufa wosayenera kusamaliridwa. Ndiyeno anamsamutsira kwa makolo athu, amene anatumizidwa kuukapolo wa moyo wonse ku Siberia mu 1951.”
Kubwerera ku Ukraine ndi Chizunzo Chowonjezereka
“Ku Siberia ndinakumana ndi Nadia, amene anakhala mkazi wanga ndipo tinakhala ndi ana. Ngakhale pamene tinali ku Siberia tinapitiriza ntchito yathu yolalikira. Ndinaikiziridwa kusindikiza ndi kukopa zofalitsa zofotokoza Baibulo. Usiku uliwonse ine ndi mng’ono wanga Jacob tinali otanganitsidwa m’phanga lokumbidwa m’chipinda chapansi pa nyumba, kukopa Nsanja ya Olonda. Tinali ndi matypewriter aŵiri ndi makina okopera opangidwira panyumba. Nyumba yathu inafufuzidwa mosalekeza ndi apolisi. Apolisiwo anachoka chimanjamanja nthaŵi zonse.
“Undende wanga unatha. Ndinasamukira ku Ukraine pamodzi ndi banja langa lonse, koma chizunzo chinatitsatira. Ndinagaŵiridwa kutumikira monga woyang’anira woyendayenda. Ndinafunikira kupeza ntchito kuti ndidzichilikiza banja langa. Nthaŵi zambiri mwezi uliwonse, ziŵalo za State Security zinafika kumalo anga antchito ndi kuyesayesa kundikakamiza kulolera molakwa chikhulupiriro changa. Panthaŵi ina ndinachiwona chithandizo cha Yehova mwanjira yapadera. Anandigwira ndi kupita nane ku maofesi a State Security ku Kiev, kumene anandisunga kwa masiku asanu ndi limodzi. Nthaŵi yonseyi anayesayesa kundisokoneza ndi manenanena osakhulupirira kukhalako kwa Mulungu. Mwanjira yawo yoipa, ananena za Nsanja ya Olonda ndi zofalitsa zina za Watch Tower Society. Chitsenderezocho chinakula kufikira kukhala pafupifupi chosapiririka. Pamene ndinali m’chipinda chosambira, ndinkagwada pansi ndi kuyamba kulira, kulirira Yehova. Sindinapemphe kumasulidwa koma nyonga kuti ndipirire ndi kuti ndisapereke abale anga.
“Ndiyeno mkulu wa apolisi anabwera kudzandiwona, ndipo atakhala pampando patsogolo panga, anandifunsa ngati ndinali wokhutiritsidwadi ndi zimene ndinali kuchilikiza. Ndinachitira umboni wachidule kwa iye ndi kulengeza kukonzekera kwanga kufera chowonadi. Iye anayankha kuti: ‘Ndiwe munthu wachimwemwe. Ndikanakhala wokhutira kuti chimenechi nchowonadi, ndikanakonzekera kukhala m’kaidi osati kokha kwa zaka 3 kapena 5 koma kuima ndi mwendo umodzi m’ndende kwa zaka 60.’ Iye anakhala chete akulingalira kwakanthaŵi ndiyeno anapitiriza kuti: ‘Ndinkhani ya moyo wosatha. Kodi ungayerekezere zimene moyo wosatha umatanthauzadi?’ Atapuma pang’ono, anati: ‘Pita kunyumba!’ Mawu amenewo anandipatsa nyonga yosayembekezereka. Sindinamvenso njala. Ndinangofuna kuchoka. Ndinatsimikizira kuti anali Yehova amene anandilimbikitsa.
“M’zaka zaposachedwapa zinthu zasintha ku dziko lomwe lidali Soviet Union. Tsopano kuli unyinji wochuluka wa mabuku ofotokoza Baibulo. Timapezeka pamisonkhano yadera ndi yachigawo, ndipo timatenga mbali m’mitundu yonse ya ntchito yolalikira, kuphatikizapo uminisitala wakunyumba ndi nyumba. Zowonadi, Yehova watipatsa chilakiko poyang’anizana ndi ziyeso zambiri!”
Umphumphu Uyesedwa mu Afirika
Chakumapeto kwa ma 1960, Nigeria analoŵetsedwa m’nkhondo yachiweniweni yosakaza kwambiri. Potaikiridwa ndi ochuluka, asilikali a chigawo chopanduka, chomwe panthaŵiyo chinatchedwanso Biafra, analemba mokakamiza amuna achichepere m’gulu lawo lankhondo. Popeza kuti Mboni za Yehova nzauchete pandale zadziko ndipo zimakana kuloŵetsedwa m’nkhondo, Mboni zambiri ku Biafra zinasakidwa, kumenyedwa mwankhanza, ndi kuphedwa. Mmodzi wa Mboni za Yehova ananena kuti: “Tinali ngati makoswe. Tinali kubisala nthaŵi iliyonse imene tinamva asilikali akubwera.” Kaŵirikaŵiri panalibe nthaŵi yobisala.
Tsiku lina pa Lachisanu m’maŵa mu 1968, Philip, minisitala wanthaŵi zonse wazaka 32 zakubadwa, anali m’mudzi wa Umuimo kulalikira kwa mwamuna wokalamba pamene asilikali a Biafra analoŵa m’mudzimo pandawala yawo yolemba asilikali mokakamiza.
“Kodi ukuchita chiyani?” anafunsa motero mtsogoleri wa gululo. Philip anayankha kuti akulankhula za Ufumu wa Yehova ukudzawo.
“Ino sinthaŵi yolalikira!” anakalipa tero msilikali wina. “Ino ndinthaŵi yankhondo, ndipo sitifuna kuwona amuna anyonga akungoyendayenda popanda chochita.” Ndiyeno asilikaliwo anamvula Philip, namanga manja ake pamodzi, namtenga kupita naye. Israel, mkulu Wachikristu wazaka 43 zakubadwa, analibenso nthaŵi yobisala. Iye anagwidwa akukonza chakudya cha ana ake. Pofika 2:00 p.m. asilikaliwo anagwira amuna oposa zana limodzi. Iwo anakakamiza akaidi awo kuthamanga mtunda wa makilomita 25 kupita ku msasa wankhondo ku Umuacha Mgbedeala. Aliyense amene anathamanga pang’onopang’ono anakwapulidwa.
Israel anauzidwa kuti akanyamula mfuti yachiwaya yolemera; Philip akaphunzitsidwa kugwiritsira ntchito mfuti yachiwaya yopepuka. Pamene anafotokoza kuti sangaloŵe usilikali chifukwa Yehova amaletsa zimenezo, mkulu wa gululo analamula kuti atsekeredwe m’kaidi. Pa 4:00 p.m., olembedwa usilikali mokakamiza onse, kuphatikizapo amene anali m’kaidi, analamulidwa kupanga mzera. Asilikaliwo anauza mwamuna aliyense kusaina chipepala kusonyeza kuti wavomereza kuloŵa m’gulu lankhondo. Pamene inafika nthaŵi yake kuti asaine, Philip anatchula mawu a pa 2 Timoteo 2:3, 4 ndi kuuza mkulu wagululo kuti: “Ndine kale ‘msilikali wabwino wa Kristu.’ Sindingamenyere nkhondo Kristu ndi kumenyeranso nkhondo munthu wina. Ngati nditero, Kristu adzandiwona monga mdyera kuŵiri.” Mkulu waguluyo anamkhoma pamutu, nati: “Kukhala kwako msilikali wa Kristu kwatha! Tsopano ndiwe msilikali wa Biafra.”
Philip anayankha kuti: “Yesu sanandidziŵitsebe kuti kuikidwa kwanga monga msilikali wake kwatha, ndipo kuikidwa kwanga kukalipo kufikira pamene ndidzalandira chidziŵitso choterocho.” Pamene anatero, asilikaliwo ananyamula Philip ndi Israel m’malere ndi kuwaponyera pansi. Atachita chizungulire ndipo akukha mwazi m’maso, mphuno, ndi mkamwa, aŵiriwo anachotsedwa.
Pamaso pa Owombera Mfuti
Pambuyo pake tsiku limenelo, Israel ndi Philip anangowona kuti ali pamaso pa owombera mfuti. Koma asilikaliwo sanawawombere. M’malomwake, anawamenya ndi zibakera ndi thendere za mfuti. Ndiyeno mkulu wa msasawo analingalira zowakwapula kufikira imfa. Iye anauza asilikali 24 kuchita zimenezi. Asanu ndi mmodzi anakwapula Philip, ndipo asanu ndi mmodzi ena anakwapula Israel. Asilikali 12 enawo anali kubweretsa ndodo ndi kudikira monga othandiza asilikali enawo akatopa.
Philip ndi Israel anamangidwa manja ndi miyendo. Israel akusimba kuti: “Sindidziŵa kuti tinalandira zikoti zingati usiku umenewo. Pamene msilikali mmodzi anatopa, wina anamlandiza. Anatikwapula ngakhale pamene tinakomoka.” Philip akuti: “Lemba la Mateyu 24:13, limene limalankhula za kupirira kufikira chimaliziro, linadza m’maganizo mwanga pamene ndinali kuzunzidwa, ndipo zimenezo zinandilimbikitsa. Ndinamva kupweteka kwa timphindi tochepa tokha. Kunawoneka ngati kuti Yehova anatumiza mmodzi wa angelo ake kudzatithandiza, monga momwe anachitira m’nthaŵi ya Danieli. Kupanda apo sitikanapulumuka usiku wowopsa umenewo.”
Pamene asilikaliwo anamaliza, Israel ndi Philip anasiyidwa kuti afe. Kunali kugwa mvula. M’maŵa wotsatira mpamene Akristu aŵiriwo anatsitsimuka. Pamene asilikaliwo anawona kuti akali moyo, anawakokeranso m’kaidi.
“Mwayamba Kale Kununkha Ngati Mitembo”
Kukwapulako kunasiya khungu lawo lili lofiira ndi mwazi, ndi mabala pathupi pawo ponse. Israel akukumbukira kuti: “Sitinaloledwe kutsuka mabala athu. Pambuyo pa masiku angapo ntchentche zinatiwundira. Chifukwa cha kuzunzidwako, sitinathe nkudya komwe. Panali patapita mlungu umodzi pamene tinakhoza kumwa madzi okha.”
M’maŵa uliwonse asilikaliwo ankawakwapula—zikoti 24 aliyense. Asilikaliwo monyoza anatcha zimenezo “kadzutsa” kapena “tii wotentha wam’maŵa.” Masana alionse, asilikaliwo anawatulutsira kubwalo kuwaika padzuŵa lotentha mpaka 1:00 p.m. Patapita masiku angapo akuchitiridwa motero, mkuluyo anawaitana nawafunsa ngati anasintha kaimidwe kawo. Iwo anati ayi.
“Mudzafera m’lumande lanu,” anatero mkuluyo. “Kwenikweni, mwayamba kale kununkha ngati mitembo.”
Philip anayankha kuti: “Ngakhale titafa, tikudziŵa kuti Kristu, amene tikumenyera nkhondo, adzatiukitsa.”
Kodi anapirira motani nthaŵi yovuta imeneyi? Israel akuti: “Ine ndi Philip tinalimbikitsana mkati mwa chiyeso chathu. Kuchiyambi kwenikweni, ndinamuuza kuti, ‘Usachite mantha. Mulimonse mmene zikhalire, Yehova adzatithandiza. Inetu, palibe chimene chidzandipangitsa kuloŵa m’gulu lankhondo. Ngakhale nditafa, sindidzagwira mfuti ndi manja angawa.’” Philip ananena kuti naye anapanga chigamulo chofananacho. Onse pamodzi anakumbukira ndi kukambitsirana malemba osiyanasiyana.
Mkulu wankhondo watsopano analingalira zosamutsira olembedwa usilikali mokakamiza zana limodzi ku Ibema, msasa wophunzitsira zankhondo umene unali m’dera la Mbano limene tsopano limadziŵika monga Imo State. Israel akusimba zimene zinachitika: “Galimoto lalikulu linakonzeka, ndipo olembedwa usilikali mokakamiza onse anali mkati. Mkazi wanga, June, anathamangira kwa asilikali ndipo molimba mtima anachonderera kuti asapite nafe kwina. Pamene anamkanira, iye anagwada pafupi ndi galimotolo, anapemphera, ndipo anamaliza ndi mawu omveka kuti amen. Ndiyeno galimotolo linanyamuka.”
Kukumana ndi Msilikali Waganyu Wachifundo
Galimoto lankhondolo linafika kumsasa wa Ibema masana tsiku lotsatira. Mwamuna amene anawoneka kukhala woyang’anira kumeneko anali msilikali waganyu wa ku Israyeli. Pamene anawona mmene Philip ndi Israel anamenyedwera ndi mmene analiri ofooka, iye anafika pafupi nafunsa chifukwa chake anali m’mkhalidwe wotero. Iwo analongosola kuti ali Mboni za Yehova ndipo anakana kuphunzira zankhondo. Mokwiya, iye anatembenukira kwa akuluakulu ankhondo ena kumeneko. “Biafra adzalepheradi nkhondoyi,” iye anatero. “Dziko lililonse limene lili pankhondo limene limavutitsa Mboni za Yehova limagonja. Simuyenera kulemba Mboni za Yehova. Ngati Mboni ivomereza kupita kunkhondo, izo zilibe kanthu. Koma ngati ikana, ilekeni.”
Dokotala wapamsasapo anafunsa ngati Mboni ziŵirizo zinalandira akatemera ndi zikalata zovomereza kuti zili zoyenera kumenya nkhondo. Popeza kuti sizinalandire, msilikali waganyuyo anakana olembedwa usilikali mokakamiza onse nalamula kuti abwezedwe ku Umuacha.
“Dzinkani Kwanu, Katumikireni Mulungu Wanu”
Pambuyo pake, mkazi wa Israel ndi amake a Philip analingalira zopita kumsasa wa Umuacha kuti akamve mbiri iliyonse. Pamene anayandikira, anamva phokoso m’msasamo. Atafika pachipata, mlonda anati: “Mboni ya Yehova iwe! Pemphero lako layankhidwa. Gulu lomwe linatengedwa masiku atatu apitawo labwezedwa.”
Philip ndi Israel anatulutsidwa mumsasawo tsiku lomwelo. Mkulu wankhondoyo anati kwa June: “Kodi udziŵa kuti ndipemphero limene unapereka lija limene lalepheretsa zochita zathu?” Ndiyeno anati kwa Israel ndi Philip: “Dzinkani kwanu, katumikireni Mulungu wanu, ndipo mupitirize kusunga umphumphu wanu kwa Yehova wanu.”
Israel ndi Philip anachira ndipo anapitiriza ntchito Yachikristu. Pambuyo pa nkhondoyo, Israel anayamba kulalikira nthaŵi yonse kwa zaka ziŵiri ndipo wapitiriza kutumikira monga mkulu Wachikristu. Philip anatumikira monga woyang’anira woyendayenda kwa zaka khumi ndipo adakali mlaliki wanthaŵi yonse. Nayenso ndimkulu mumpingo.
Kukana Kupereka Ndalama Zogulira Zida
Zebulan Nxumalo ndi Polite Mogane ndiaminisitala aŵiri anthaŵi zonse achichepere a ku South Africa. Zebulan akufotokoza kuti: “Tsiku lina pa Sande m’maŵa, gulu la amuna angapo linafika kunyumba kwathu natikakamiza kuti tiwapatse R20 (pafupifupi $7, U.S.) yogulira zida. Mwaulemu tinawapempha kuti abwerenso madzulo, popeza kuti ndandanda yathu ya pa Sande sinatilole kupeza mpata wokambitsirana nawo nkhaniyo nthaŵi yomweyo. Modabwitsa, iwo anavomereza. Madzulo amenewo, amuna 15 anafika. Nkhope zawo zinasonyeza kuti sanadzere maseŵera. Pambuyo powauza maina athu mwaulemu, tinawafunsa zimene anafuna. Iwo anafotokoza kuti anafuna ndalama zogulira zida zazikulu ndi zabwinopo zokhaulitsira magulu andale otsutsana nawo.
“Ndinawafunsa kuti: ‘Kodi nkotheka kuzima moto ndi petulo?’
“‘Ayi, zimenezo nzosatheka,’ iwo anayankha choncho.
“Tinalongosola kuti mwanjira yofananayo, chiwawa chingangolimbikitsa chiwawa ndi kulipsira.
“Ndemanga imeneyi inaputa mkwiyo wa amuna angapo amene analipo. Pempho lawo tsopano linakhala chiwopsezo. ‘Kukambitsirana kumeneku kuli kungotaya nthaŵi,’ iwo anafuula motero. ‘Chopereka chokakamizacho nchosakambitsirana. Mungolipira kapena muwone chinameta nkhanga mpala!’
“Panthaŵi imeneyo,” akukumbukira motero Zebulan, “pamene zinthu zinayamba kuvuta, mtsogoleri wawo analoŵa. Iye anafuna kudziŵa kuti chinavuta nchiyani. Tinalongosola kaimidwe kathu, ndipo anamvetsera mosamalitsa. Tinagwiritsira ntchito kudzipereka kwawo ku zikhulupiriro zawo zandale monga fanizo. Tinawafunsa kuti akayembekeza msilikali wophunzitsidwa wa m’gulu lawo kuchita chiyani ngati wagwidwa ndipo akakamizidwa kulolera molakwa kaimidwe kake. Iwo anati munthu ameneyo ayenera kukonzekera kufera zikhulupiriro zake. Anamwetulira pamene tinawayamikira chifukwa cha yankho lawo; sanazindikire kuti anatipatsa mwaŵi wabwino wakufanizira nkhani yathu. Tinalongosola kuti ndife osiyana ndi matchalitchi a Chikristu Chadziko. Monga ochilikiza Ufumu wa Mulungu, ‘lamulo’ lathu nlozikidwa pa Baibulo, limene limatsutsa mtundu uliwonse wa mbanda. Pa chifukwa chimenechi, sitinali okonzeka kupereka ndalama zogulira zida.
“Panthaŵiyi, pamene kukambitsiranako kunafika pakaindeinde, anthu ambiri analoŵa m’nyumba mwathu, kotero kuti pomalizira pake tinali kulankhula kwa khamu lalikulu ndithu. Iwo sanazindikire kuti tinali kupemphera mosalekeza kuti kukambitsirana kwathu kukhale ndi zotulukapo zabwino.
“Titamaliza kufotokoza kaimidwe kathu momvekera bwino, panali bata. Pomalizira pake, mtsogoleri wawo analankhula ndi gululo kuti: ‘Amuna inu, ndikumvetsetsa kaimidwe ka anthuwa. Tikanakhala kuti timafuna ndalama zomangira nyumba yosungira anthu okalamba, kapena ngati mmodzi wa anansi athu anafunikira ndalama zopitira kuchipatala, amunawa akanakhala ofunitsitsa kupereka choperekacho. Koma sali okonzekera kutipatsa ndalama kuti tikaphe. Paine ndekha, sindikutsutsana ndi zikhulupiriro zawo.’
“Atatero, onse anaima. Tinagwirana chanza ndipo tinawathokoza chifukwa cha kuleza mtima kwawo. Mkhalidwe womwe unayamba ngati wowopsa womwe ukanatitengera miyoyo yathu unatha ndi chilaliko chachikulu.”
Magulu Oukira Otsogozedwa ndi Ansembe
Monga momwe yasimbidwira ndi Mboni ya ku Poland, Jerzy Kulesza:
“Pankhani ya changu ndi kuika zabwino za Ufumu patsogolo, atate wanga, a Aleksander Kulesza, anali chitsanzo choyenera kutsatira. Kwa iwo, utumiki wakumunda, misonkhano Yachikristu, ndi phunziro laumwini ndi labanja zinalidi zinthu zopatulika. Mkuntho wa chipale chofeŵa kapena chisanu kapena mphepo kapena kutentha sizinali zopinga kwa iwo. M’nyengo yachisanu ankatenga nsapato zoyendera pachipale chofeŵa, chola choberekera kumbuyo chodzaza ndi mabuku ofotokoza Baibulo, ndipo ankapita kumadera akutali a Poland nakhala kumeneko kwa masiku angapo. Iwo ankakumana ndi ngozi zosiyanasiyana, kuphatikizapo magulu achiwawa omenya nkhondo yachifwamba.
“Nthaŵi zina ansembe anautsa chitsutso molimbana ndi Mboni, namasonkhezera magulu oukira. Iwo ankaziseka, kuziponya miyala, kapena kuzimenya. Koma zinabwerera kunyumba zili zachimwemwe kuti zinapirira chitonzocho chifukwa cha Kristu.
“Mkati mwa zaka zoyambirira za Nkhondo Yadziko II, olamulira analephera kukhazikitsa bata ndi mtendere m’dzikomo. Munali chipwirikiti ndi kuwononga. Apolisi ndi ativitivi ankayendayenda masana, pamene kuli kwakuti magulu omenya nkhondo yachifwamba ndi magulu ena osiyanasiyana ankachita zawo usiku. Umbava ndi kulanda kunachuluka, ndipo kuphana kunali kosaneneka. Mboni za Yehova zopanda chitetezo zinali mikhole yosavuta, makamaka popeza kuti magulu ena otsogozedwa ndi ansembe anali kufuna kwambiri Mbonizo. Iwo analungamitsa kusakaza nyumba zathu mwakunena kuti anali kuchilikiza chipembedzo cha Chikatolika cha makolo awo. Pa zochitika zoterozo iwo ankaphwanya magalasi a m’mazenera, kuba zoŵeta, ndi kuwononga zovala, chakudya, ndi mabuku. Mabaibulo anawaponya m’chitsime.”
Kuphedwera Chikhulupiriro Kosayembekezereka
“Tsiku lina mu June 1946, tisanakumane kuti tipite panjinga kudera lakutali, mbale wina wachichepere, Kazimierz Kądziela, anatichezera nalankhula ndi atate motsitsa mawu. Atate anatitumiza tokha kuderalo, koma iwo sanapite nafe, zimene zinatidabwitsa kwambiri. Tinadzamva chifukwa chake pambuyo pake. Pamene tinabwerera kunyumba, tinamva kuti usiku wapita banja la a Kądziela linamenyedwa mwankhalwe, chotero atate anapita kukasamalira abale ndi alongo ovulazidwa moipa.
“Pamene ndinaloŵa m’chipinda mmene iwo anagona, zimene ndinawona zinandiliritsa. Zipupa ndi chindwi zinali ndi mwazi. Anthu omangidwa mabandeji anagona pamakama, atamenyedwa kotheratu, otupa, ena othyoka nthiti ndi miyendo ndi mikono. Iwo anasinthiratu. Mlongo Kądziela, mayi wa banjalo, anamenyedwa kowopsa. Atate anali kuwathandiza, ndipo asanachoke ananena mawu apadera akuti: ‘O, Mulungu wanga, ndine munthu wathanzi labwino ndi wanyonga [panthaŵiyo anali ndi zaka 45 zakubadwa ndipo anali asanadwalepo], ndipo sindinakhalepo ndi mwaŵi wovutikira inu. Kodi zachitikiranji kwa mlongo wachikulireyu?’ Iwo sanadziŵe zomwe zinali mtsogolo.
“Pamene dzuŵa linaloŵa, tinabwerera kunyumba kwathu mtunda wa [makilomita atatu]. Gulu la amuna 50 onyamula zida anazinga nyumba yathu. Nalonso banja la Wincenciuk linabweretsedwa, chotero tinalipo asanu ndi anayi. Aliyense wa ife anafunsidwa funso lakuti: ‘Kodi ndiwe Mboni ya Yehova?’ Pamene tinayankha kuti inde, tinamenyedwa. Ndiyeno, akumasinthana, aŵiri a amuna ankhanza ameneŵa anamenya atate akumawafunsa ngati adzasiya kuŵerenga Baibulo ndi kulalikira. Iwo anafuna kudziŵa ngati adzapita kutchalitchi kukaulula machimo awo. Anawatonza kuti: ‘Lero, tidzakuika kukhala bishopu.’ Atate sananene kalikonse, ndipo sanabuule mpang’ono pomwe. Anapirira chizunzocho mwabata, monga nkhosa. Pofika mbandakucha, iwo anamwalira patangopita pafupifupi mphindi 15 kuchokera pamene ozunza achipembedzowo anachoka, iwo anamenyedwa mpaka kufa. Koma asanachoke, anandisankha monga mkhole wawo wotsatira. Panthaŵiyo ndinali ndizaka 17 zakubadwa. Akundimenya choncho, ndinakomoka nthaŵi zingapo. Thupi langa linada bii kuyambira m’chuuno mpaka kumutu chifukwa cha kumenyedwako. Tinasautsidwa kwa maola asanu ndi limodzi. Zonsezo chifukwa tinali Mboni za Yehova!”
Chichilikizo cha Mkazi Wokhulupirika
“Ndinali pakati pa gulu la Mboni 22 zimene zinabindikiritsidwa kwa miyezi iŵiri m’lumande lamdima la [mamita khumi] kukula kwake mbali zonse zinayi. Pamapeto pa nyengo imeneyo, chakudya chathu chinachepetsedwa. Tsiku lililonse, tinapatsidwa chidutswa chaching’ono cha mkate ndi kapu yaing’ono ya khofi woŵaŵa. Tinakhoza kugona pansi pasimenti pozizira kokha pamene mmodzi anaitanidwa kupita kukafunsidwa mafunso nthaŵi yausiku.
“Ndinaponyedwa m’ndende chifukwa cha ntchito yanga Yachikristu nthaŵi zisanu, zonse pamodzi, zaka zisanu ndi zitatu. Ndinachitiridwa monga kaidi wapadera. M’cholembedwa changa munali kakalata konena kuti: ‘Mumsautse Kulesza kotero kuti ataye chikhumbo chake chofuna kuyambanso ntchitoyo.’ Komabe, nthaŵi iliyonse imene ndinamasulidwa, ndinadzipereka kuchita utumiki Wachikristu. Boma linasautsanso mkazi wanga, Urszula, ndi ana athu aakazi aŵiri. Mwachitsanzo, kwa zaka khumi mkulu wosungitsa lamulo analanda ena a malipiro opezedwa movutikira a mkazi wanga. Iwo anati umenewo ndimsonkho wanga wosindikizira mabuku ofotokoza Baibulo mwachinsinsi. Zinthu zonse zinalandidwa kusiyapo kokha zimene anazilingalira kukhala zofunika za moyo. Ndikuyamikira Yehova kaamba ka mkazi wanga wolimba mtima, amene anapirira pamodzi nane moleza mtima zizunzo zonsezo, ndi amene anandichilikizadi nthaŵi yonseyo.
“Tapeza chilakiko chauzimu ku Poland kuno; tsopano tili ndi ofesi yanthambi yalamulo ya Watch Tower Society ku Nadarzyn, pafupi ndi Warsaw. Pambuyo pa zaka makumi ambiri zachizunzo, tsopano kuli Mboni zoposa 108,000, za m’mipingo 1,348.”
Kodi Nchifukwa Ninji Pali Ophedwera Chikhulupiriro Ochuluka Motero?
Cholembedwa cha kusunga umphumphu kwa Mboni za Yehova m’zaka za zana lino la 20 chingadzaze mabuku aakulu ambirimbiri—zikwi zambiri zafa monga ophedwera chikhulupiriro kapena kuponyedwa m’ndende ndi kuzunzidwa kosaneneka, kugwiriridwa chigololo, ndi kulandidwa katundu m’malo onga ngati Malaŵi ndi Mozambique, ku Spain muulamuliro wa Chifashizimu, ku Ulaya muulamuliro wa Chinazi, Kum’maŵa kwa Ulaya muulamuliro wa Chikomyunizimu, ndi ku United States mkati mwa Nkhondo Yadziko II. Funso limabuka lakuti, Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti atsogoleri osasintha andale ndi achipembedzo sanafune kulemekeza chikumbumtima chophunzitsidwa ndi Baibulo cha Akristu owona mtima amene amakana kuphunzira kupha ndipo amene sakhala ndi mbali iliyonse m’zochita zandale. Zili monga momwe Kristu ananenera kuti zikatero, monga kwalembedwa pa Yohane 15:17-19 kuti: “Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mnzake. Ngati dziko lapansi lida inu, mudziŵa kuti lidada ine lisanayambe kuda inu. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.”
Mosasamala kanthu za chizunzo chapadziko lonse chimenechi, Mboni za Yehova zawonjezereka—kuchokera pa 126,000 m’maiko 54 mu 1943 kufika pafupifupi 4,500,000 m’maiko 229 mu 1993. Izo zalakika ngakhale poyang’anizana ndi imfa. Izo nzotsimikiza mtima kupitiriza ntchito yawo yapadera yakuphunzitsa yolengeza mbiri yabwino ya Ufumu kufikira pamene Yehova adzanena kuti kwatha.—Yesaya 6:11, 12; Mateyu 24:14; Marko 13:10.
[Mawu a M’munsi]
a Umphumphu ndiwo “kumamatira kotheratu ku lamulo lamakhalidwe abwino kapena mwambo.”—The American Heritage Dictionary, Kope Lachitatu.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]
Kuphedwera Chikhulupiriro m’Jeremani
AUGUST DICKMANN anali ndizaka 23 zakubadwa pamene mtsogoleri wa SS Heinrich Himmler analamula kuti awomberedwe mfuti pamaso pa Mboni zina zonse mu msasa wachibalo wa Sachsenhausen. Gustav Auschner, mboni yowona ndi maso, anasimba kuti: “Anawombera mfuti Mbale Dickmann ndi kutiuza ife kuti tonsefe tidzawomberedwa mfuti ngati sitisaina chilengezo chokana chikhulupiriro chathu. Tikatengedwa ku maenje a mchenga anthu 30 kapena 40 panthaŵi imodzi, ndipo akatiwombera mfuti tonsefe. Tsiku lotsatira, a SS anabweretsa kwa aliyense wa ife chikalata choti tisainepo kupanda apo tikawomberedwa mfuti. Bwenzi mutawona nkhope zawo zokwiya pamene anapita popanda munthu mmodzi wosaina. Iwo anayembekezera kutiwopseza ndi kupha kwapoyera. Koma tinali ndi mantha oposerapo a kusakondweretsa Yehova kuposa zipolopolo zawo. Iwo sanawomberenso mfuti aliyense wa ife poyera.”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]
Imfa
NTHAŴI zina, kulakika poyang’anizana ndi imfa kungaphatikizepo imfa yeniyeni. Kalata yolandiridwa kuchokera ku Mpingo wa Nseleni, kumpoto kwa Natal Province, ku South Africa, ikusimba nkhani yomvetsa chisoni: “Tikulemberani kalatayi kukudziŵitsani za imfa ya mbale wathu wokondedwa Moses Nyamussua. Ntchito yake inali kuwotcherera ndi kukonza galimoto. Tsiku lina anafunsidwa ndi gulu lina la ndale kuti awawotcherere mfuti zawo, zimene iye anakana kuchita. Ndiyeno, pa February 16, 1992, iwo anachita msonkhano wawo wandale, kumene anamenyana ndi gulu lina lotsutsana nalo. Tsiku lomwelo madzulo pochokera kunkhondo kwawoko, iwo anapeza mbaleyo akupita kumasitolo. Anamupha kumeneko ndi mikondo yawo. Kodi anali ndi chifukwa chotani? ‘Unakana kuwotcherera mfuti zathu, ndipo tsopano anzathu afa m’kumenyanako.’
“Zimenezi zawopseza abale kwambiri,” akutero Mbale Dumakude, mlembi wa mpingo. “Koma,” iye akuwonjezera, “tidzapitirizabe uminisitala wathu.”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]
Kuphedwera Chikhulupiriro m’Poland
MU 1944, pamene magulu ankhondo Achijeremani anali kuchoka ndipo nkhondo inali kuyandikira tauni ya kum’maŵa kwa Poland, akuluakulu a magulu ankhondo achiwembuwo anakakamiza anthu wamba kukumba michera yoletsa kuloŵa kwa akasinja ankhondo. Mboni za Yehova zinakana kutengamo mbali. Stefan Kieryło, Mboni yachichepere—yomwe inangobatizidwa miyezi iŵiri papitapo—anakakamizidwa kugwira ntchito m’gulu lankhondo koma molimba mtima anatenga kaimidwe kauchete kamodzimodziko. Njira zosiyanasiyana zinagwiritsiridwa ntchito kuyesayesa kuswa umphumphu wake.
Anammangirira kumtengo m’dambo ali maliseche kotero kuti alumidwe ndi mizaza ndi tizilombo tina. Iye anapirira zimenezo ndi zizunzo zina, chotero analeka kumzunza. Komabe, pamene mkulu wa asilikali anayendera gulu lankhondolo, anauzidwa kuti pali munthu wina amene mwanjira iliyonse sadzamvera lamulo lake. Stefan analamulidwa nthaŵi zitatu kuti akumbe mcherawo. Iye anakana ngakhale kutenga chokumbira m’dzanja lake. Iye anawomberedwa mfuti nafa. Mazana ambiri amene anawonerera chochitikacho ankamudziŵa bwino. Kuphedwera chikhulupiriro kwake kunakhala umboni wa nyonga yaikulu imene Yehova amapereka.
[Chithunzi patsamba 7]
Ananii Grogul
[Chithunzi patsamba 11]
Jerzy Kulesza