Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 6/8 tsamba 31-32
  • Moyo—Mphatso Yoyenera Kuyamikiridwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo—Mphatso Yoyenera Kuyamikiridwa
  • Galamukani!—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yochotsa Mimba?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kupatsa Ana Zimene Amafunikira
    Galamukani!—2004
  • Kukhala ndi Pakati kwa Azaka Zapakati pa 13 ndi 19 Kodi Msungwana Angachitenji?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 6/8 tsamba 31-32

Moyo—Mphatso Yoyenera Kuyamikiridwa

PAMENE Yehova Mulungu anapereka mwaŵi wakubala ana kwa banja la anthu loyambirira, inali mphatso yabwino chotani nanga! Mwana wokongola akabadwa ndikulandiridwa ndi manja oyembekezera a okwatirana achimwemwe amene amakondana ndipo ali okonzekera kuyamikira ndi kusamalira chotulukapo cha kugwirizana kwawo kwa m’banja. Pamene mwanayo akukula, banjalo likakhala ndi chimwemwe chokhachokha.

Koma kuchimwa kwa Adamu ndi Hava kunabweretsa zotulukapo zoipa kwa ana obadwira m’mtundu wa anthu. Chifukwa cha kuchimwa, mayi wathu woyamba anatembereredwa ndi nsautso ndi zoŵaŵa zakuthupi pakubala kwake. Ndipo mikhalidwe yauchimo imene anawo anabadwiramo inapangitsa kulera ana kukhala vuto lalikulu. Chifukwa chake, nkosadabwitsa kuti m’dziko locholoŵana lamakono kutenga mimba sikumakondwereredwa nthaŵi zonse. Komabe, kodi Mlengi amalingalira motani za mwana wosabadwa? Kodi iye wasintha lingaliro lake chifukwa cha kusintha kwa makhalidwe? Ndithudi ayi. Lingaliro lake ndi kudera nkhaŵa kwake kaamba ka ana osabadwa a m’dzikoli sikunasinthe.

Malemba amamveketsa bwino kuti mkati mwa nakubalayo muli munthu wapadera amene akuumbika. Moyo umayamba pakutenga mimba. Kubadwa kumangosonyeza anthu mwana amene Mulungu anamuwona kale. Ezekieli amalankhula za “oyamba kubadwa.” (Ezekieli 20:26) Yobu analongosola za “makomo [a] mimba ya mayi anga,” ndipo amatcha kupita padera kukhala “makanda osawona kuunika.”—Yobu 3:10, 16.

Tawonani chisamaliro chachikondi cha Yehova Mulungu cha moyo wanthete womaumbika m’mimba. Iye anauza Yeremiya kuti: “Ndisanakulenge iwe m’mimba ndinakudziŵa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe.” (Yeremiya 1:5) Davide anati: “Thupi langa silinabisikira inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m’munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya.” (Salmo 139:15, 16) Yobu amatcha Mulungu “Iye amene anandilenga ine m’mimba,” amene “anatiumba m’mimba.”—Yobu 31:15.

Koma bwanji za kudera nkhaŵa kwa Mulungu ndi mayi woyembekezera wotaya mtima amene sakumfuna mwanayo? Pakati pa anthu onse, Mlengi amadziŵa mathayo owopsa akukhala kholo. Ngati mayi woyembekezerayo asankha kusunga mwana wake chifukwa cholemekeza zofunika zaumulungu, ngakhale kuti ali m’mikhalidwe yovuta, kodi iye sakadalitsa chosankha chake? Kholo lingakhoze ndipo liyenera kupempherera chithandizo chake polera mwana wachimwemwe. M’masamba a Mawu ake, Mulungu anapereka kale uphungu wabwino kwambiri wolerera ana. Kugwiritsira ntchito malamulo amkhalidwe a Baibulo m’moyo wa banja kudzatulutsa zotulukapo zabwino. Kholo lonyadira lililonse lingavomereze kuti chimwemwe ndi mphotho zakulera ana opembedza zimaposa kudzimana kumene kumapangidwa powalera.

Kodi Yehova amawona zinthu mosiyana ngati mwanayo ali chotulukapo cha kugwiriridwa chigololo kapena kugonana kwapachibale? Ngakhale kuti kachitidweko kanali kaupandu kwa nakubalayo, mwanayo alibe mlandu. Kupha moyo wake kukangokhala kuthetsa upandu ndi upandu unzake. Ndithudi Yehova amadziŵa kupweteka kwamaganizo kumene mikhole yotero imakumana nako ndipo angathandize nakubala ndi mwanayo kulaka ziyambukiro zake mwachikatikati.

Bwanji ngati dokotala auza mkazi wapakati kuti kukhala ndi mimbayo kufikitsa nthaŵi yokwanira kukaika moyo wake pangozi? Dr. Alan Guttmacher ananena kuti: “Lerolino nkotheka pafupifupi kwa wodwala aliyense kukhala wapakati mpaka nthaŵi yokwanira ali ndimoyo, kusiyapo kokha ngati akudwala matenda owopsa monga kansa kapena leukemia, ndipo ngati ndichoncho, kutaya mimba sikungapulumutse konse moyo wake.” The Encyclopedia Americana ikufotokoza kuti: “Popeza kuti akazi ambiri amakhoza kukhala ndi pakati mpaka nthaŵi yokwanira ngakhale kuti ali ndi matenda owopsa, kutaya mimba kochepa kwambiri kukafunikira kutetezera umoyo wa nakubalayo. Kutaya mimba kochuluka kumachitidwa chifukwa chofuna kupeŵa kukhala ndi mwana.” Zochitika zoterozo nzakamodzikamodzi. Komabe, ngati zichitika panthaŵi yakubala, pamenepo makolo ayenera kupanga chosankha pakati pa moyo wa nakubalayo ndi wa mwanayo. Nchosankha chawo.

Kodi nkodabwitsa kuti Mlengi wa moyo anaika malangizo omveka bwino onena za kugwiritsira ntchito ziŵalo zobalira? Kwa iye, kupanga moyo umene munthuyo sakufuna kuusamalira nditchimo, monga momwe kupha moyo kuliri tchimo.

Kunena zowona, mkanganowo udzapitirizabe kufikira mapeto a dongosolo lino. Koma kwa Mlengi wa moyo, Yehova Mulungu, limodzinso ndi awo amene amakonda malamulo ake, palibe mkangano konse. Moyo ngwamtengo wapatali—mphatso yofunikira kusamaliridwa ndi kukondedwa kuyambira pachiyambi.

Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)

[Bokosi patsamba 32]

Kuwona Kutaya Mimba m’Lingaliro la Mulungu

BWANJI za msungwana wachichepere amene amatenga mimba asanakwatiwe ndipo sali wokonzekera konse kukhala nakubala? Kodi ayenera kuloledwa kubala mwanayo? Malingaliro a Mulungu kulinga kwa mwanayo sanasinthe kokha chifukwa chakuti mayi wakeyo anachita mwanjira yopanda nzeru ndi yachiŵereŵere. Kubadwa kwa mwanayo kungathandizedi mayi wakeyo kuzindikira zotulukapo zachibadwa za chisembwere chake ndipo motero kukhomereza mwa iye nzeru ya malamulo a Mulungu. Kuchotsa umboni wa kugonana kwake kwachisembwere kungampangitse kukhala wopwetekedwa ndi liŵongo, kapena kungakhwimitse machitidwe ake achiŵereŵere amtsogolo.

Ngati palibe tate wothandizana naye thayolo, kulera mwanako sikudzakhala kokhweka. Koma unansi wamphamvu ndi Atate wathu wakumwamba ungapatse nakubalayo chikumbumtima cholimba ndi kulimbitsa mtima wake, chichilikizo, ndi chitsogozo chakuchita tero. Iye waperekanso mpingo Wachikristu kuthandiza kupeputsa mtolo wa makolo okhala okha.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena