Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kukhala ndi Pakati kwa Azaka Zapakati pa 13 ndi 19 Kodi Msungwana Angachitenji?
Kukhala ndi pakati kwa azaka zapakati pa 13 ndi 19 ndi kutaya mimba kuli mavuto a dziko lonse. Ndipo pamene kuli kwakuti ambiri a aŵerengi athu ali Akristu achichepere amene mwanzeru amathaŵa kugonana kwa ukwati usanakhale, Galamukani! imaŵerengedwanso ndi mamiliyoni a anthu ena amakulidwe osiyanasiyana. Kukambitsirana kotsatiraku kwakonzedwa kuthandiza wachichepere aliyense woyang’anizana ndi vuto la ukholo wopanda ukwati, panthaŵi imodzimodziyo kugogomezera zotulukapo zoipa zimene zimakhalapo chifukwa cha kugonana kwa ukwati usanakhale.
“NDINALI ndi zaka 15 ndipo wapakati,” anatero Ann. “Sindinadziŵe zochita—kutaya mimbayo, kupereka mwanayo kuti aleredwe ndi ena, kapena chiyani.” Ann anali kokha mmodzi mwa asungwana oposa miliyoni azaka zapakati pa 13 ndi 19 mu United States amene anakhala ndi pakati chaka chimenecho.
Pamene kuli kwakuti m’zochitika zangozi zoŵerengeka msungwana amakhala ndi pakati chifukwa cha kugwiriridwa chigololo, kukhala ndi pakati kwa azaka zapakati pa 13 ndi 19 kaŵirikaŵiri kuli chotulukapo cha kudziloŵetsa kodzifunira m’kugonana kwa ukwati usanakhale.a M’chochitika chirichonse, kukhala ndi pakati kumapereka kwa msungwana wosakwatiwa zosankha zopweteka zingapo: Kodi akwatiwe? Kodi apereke mwanayo kuti aleredwe ndi ena? Kodi kutaya mimba ndiko kuli yankho? Kunena zowona, chimatengera anthu aŵiri kupanga mwana, ndipo mwanjira iriyonse tate wa mwanayo ayenera kutenga thayo lake. (Onani bokosi.) Koma kaŵirikaŵiri, amakhala msungwana (mwinamwake ndi thandizo la makolo ake) amene amasiyidwa kupanga zosankha zovuta zimenezo. Ndipo zimene amasankha zimakhala ndi chiyambukiro chosatha pa ubwino wake ndi wa mwanayo wakuthupi, maganizo, ndi wauzimu.
‘Kodi Tikwatirane?’
Ambiri angaganize kuti kukwatiwa ndi tate wa mwanayo kungakhale yankho labwino. Ndiiko komwe, zingachepetsere msungwanayo ndi banja lake kuchititsidwa manyazi poyera, ndipo zingalole mwanayo kuleredwa ndi makolo aŵiri. Koma ukwati sumathetsa zonse. Choyamba, kulapa kwaumulungu kokha kungawongolere cholakwacho m’maso mwa Mulungu.b (Yesaya 1:16, 18) Kuwonjezerapo, kuthamangira ukwati kungakulitse mavuto a msungwanayo. Popeza kuti mnyamatayo ndi msungwana adakali mu “unamwali,” iwo sangakhale ndi uchikulire wamaganizo wofunikira kuti ukwati ukhale. (1 Akorinto 7:36) Mwachidziŵikire mnyamatayo sali Mkristu wowona ndipo chotero sali woyeneretsedwa kukhala wamuukwati woyenera.—1 Akorinto 7:39.
Dr. Arthur Elster akulongosola mowonjezereka kuti: “Ukholo wosafikapo kaŵirikaŵiri umapangitsa atate ameneŵa kuleka sukulu, ndipo chotero kumawaika pa malo oipa opeza ntchito.” Mavuto obuka a zachuma angawononge ukwati. Ndithudi, maphunziro ena asonyeza kuti pali liŵiro la kusudzulana loyambira pa 50 peresenti kufika ku 75 peresenti pakati pa maukwati amene anayambitsidwa chifukwa cha kukhala ndi pakati ukwati usanakhale!
Ukwati uli sitepe lalikulu ndipo suyenera kuthamangiridwa. (Ahebri 13:4) Pambuyo polingalira nkhaniyo, onse oloŵetsedwamo angavomereze kuti sichiri chanzeru kukwatira, kuti msungwanayo angakwanitse kulera mwanayo panyumba ndi thandizo la banja lake kuposa ukwati wodzaza ndi mavuto.
Kutaya Mimba—Lingaliro Labaibulo
Msungwana wina wachichepere ananena kuti: ‘Ndikufuna kuchita zambiri ndi moyo wanga, ndipo mwana sangakhalemo ndi malo.’ Chotero kutaya mimba ndiko kuli chosankha cha chifupifupi asungwana okwanira theka la miliyoni chaka chirichonse mu United States mokha. Koma kodi ndikwabwino kapena kolungamitsika kutaya mimba kokha chifukwa chakuti moyo wamwana ‘ulibe malo’ m’mapulani aumwini a munthu?
Onani zimene Baibulo likunena pa Eksodo 21:22, 23 ponena za moyo wa mwana wosabadwa: “Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu . . . Koma ngati kuphweteka kukalipo [kwa mayiyo kapena mwana wosabadwayo], uzipereka moyo kulipa moyo.” Inde, kupha mwana wosabadwa kunalingaliridwa kukhala mbanda!
Zowonadi, adokotala ena amanena kuti mwana wosabadwa ali kokha mluza, kapena minyewa ya mluza—osati munthu. Koma Mulungu amanena zosiyanako. Iye amawona mluza kukhala munthu wapayekha, munthu wamoyo! (Salmo 139:16) Kodi munthu angataye moyo wosabadwa ndi kukhalabe m’chiyanjo cha Mulungu, amene “apatsa zonse moyo”?—Machitidwe 17:25.
Bukhu lakuti Growing Into Love likupereka mtsutsano wina pa kutaya mimba: “Ngakhale kuti zotulukapo za kutenga mimba zimapepukitsidwa mwa kutaya mimba, chochitika chothetsa pakati kaŵirikaŵiri chimakhala chokhumudwitsa ndipo chovutitsa. . . . Wazaka zapakati pa 13 ndi 19 . . . angakhulupirire kuti mluzawo uli kokha zimenezo—mluza . . . Koma palibe unyinji wa kulongosola kwalamulo kumene kumamlola kuiwala, mkati mwa iye yekha, kuti mluza umene anakhala nawo pakati udali ndi kuthekera kwa kukhala ndi moyo.”
Wachichepere wina wotchedwa Linda anapeza zimenezi kukhala zowona. Akumawopa kuti kukhala ndi mwana kukabweretsa manyazi pa banja lake, iye anataya mimba. Komabe, pambuyo pa opareshoniyo, iye akukumbukira kuti: “Ndinayamba kunjenjemera kwambiri kotero kuti ndinalephera kukulamulira. Ndipo ndinayamba kulira, ndipo mwadzidzidzi zinandiyambukira, zimenedi ndinazichita. Ndinachotsa moyo wa mwana wanga wosabadwa, munthu wina!” Kodi tsopano Linda akuganiza motani ponena za kutaya mimba? “Chinali cholakwa choipitsitsa m’moyo wanga wonse.”
‘Sindingampatse Zabwino Koposa’
Amayi ena osakwatiwa amasankha kupereka ana awo kuti aleredwe ndi ena. Iwo kaŵirikaŵiri amadzimva monga mmene anachitira Heather, msungwana wogwidwa mawu m’magazine a Seventeen, amene ananena kuti: “Ndiri ndi mavuto ambiri ochita ndi ine mwini, ndipo sindingathe kusamalira mwana wamng’ono. Ndimasangalatsidwadi ndi ana, ndipo ndimakondadi ana, koma ndinadziŵa kuti sindingapatse mwana ameneyu zabwino koposa.”
Nzowona kuti kupereka mwana kuti aleredwe ndi ena nkwabwino kuposa kuthetsa moyo wake mwakutaya mimba. Ndipo kunena zowona, chiyembekezo cholera mwana ali yekha chingakhale chowopsya kwa msungwana wachichepere ndiponso wopanda luso. Monga mmene mayi wina wosakwatiwa anauzira Galamukani! kuti: “Umatenga thayo lalikulu, lalikulu kwambiri lawekha ndipo lopereka chiyeso ndi limene limafunikira kudzimana kwakukulu.” Ngakhale ndi tero, kumbukirani kuti Mulungu amapereka thayo kwa kholo ‘kusamalira apabanja ake.’ (1 Timoteo 5:8) M’mikhalidwe yambiri, chingakhale chabwino koposa kuti msungwana alere mwanayo yekha.
Ann, wotchulidwa kuchiyambi kwa nkhaniyi, anapanga chosankha chanzeru—ngakhale kuti sichiri chophweka. “Ndinasankha kusunga mwanayo,” iye akutero. “Makolo anga anandithandiza ndipo adakatero.” Kunenadi zowona, kukhala mayi wosakwatiwa nkovuta. Koma sikuli kosatheka, ndipo amayi achichepere ambiri akhala makolo aluso. Zimenezi ziri tero makamaka pamene mayi wosakwatiwayo mwapemphero asankhapo kulera mwana wake “m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].”c (Aefeso 6:4) Makolo olera angakhale okhoza kupereka bwino mwakuthupi. Koma kodi iwo adzapereka chitsogozo chauzimu chimene mwana amachifunikira kuti akule akukonda Mulungu wowona, Yehova?—Deuteronomo 6:4-8.
Kumbukiraninso kuti pamene kuli kwakuti kholo losakwatira silingakhale lokhoza kupatsa mwana wake zabwino koposa mwakuthupi, lingapereke chinachake kwa iye chimene chiri chofunika koposa: chikondi. “Kudya masamba, pali chikondano, Kuposa ng’ombe yonenepa [“nyama yabwino kwabasi,” Today’s English Version] pali udani.”—Miyambo 15:17.
Ndithudi, kuvutika kosayenerera kungapeŵedwe ngati wina apeŵa chimo la dama poyambapo.d Koma ngati msungwana wachimwa m’zimenezi, sayenera kulingalira kuti moyo wake watha. Mwakuchita mwanzeru, angapeŵe kukulitsa cholakwa chake ndi kupanga mkhalidwe wake kukhala wabwino monga mmene angathere. Ndithudi, iye angapeze thandizo ndi chilikizo la Mulungu iyemwini, amene ‘amakhululuka kwakukulu’ awo amene akuleka njira yolakwa.—Yesaya 55:7.
[Mawu a M’munsi]
a Mkhalidwe wachisembwere sumalekereredwa pakati pa Mboni za Yehova, monga mmene sunali kuloledwa pakati pa Akristu a m’zaka za zana loyamba. (1 Akorinto 5:11-13) Mosasamala kanthu za izo, olakwawo angapeze thandizo lachikondi kwa akulu a mpingo. (Yakobo 5:14, 15) Mwakulapa mkhalidwe wawo woipa, oterowo angasangalale ndi chikhululukiro cha Mulungu ndi mpingo Wachikristu.
b Pansi pa Chilamulo cha Mose, Mulungu anafuna kuti mwamuna amene wanyenga namwali amukwatire. (Eksodo 22:16, 17; Deuteronomo 22:28, 29) Koma lamulo limenelo linatumikira zosoŵa za anthu a Mulungu pansi pa mikhalidwe ya nthaŵi ndi mbadwo umenewo. Ndipo ngakhale nthaŵiyo, ukwati sunali chinthu chotsimikizirika, popeza kuti tateyo akadauletsa.—Onani magazine athu ena Nsanja ya Olonda, November 15, 1989, “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga.”
c Mboni za Yehova zathandiza mabanja ambiri kukhazikitsa programu ya chilangizo cha Baibulo yokhazikika. Iwo angafikiridwe mwakulembera afalitsi a magazinewa.
d Onani mutu 24 wa bukhu la Questions Young People Ask—Answers That Work, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Bokosi patsamba 21]
Kukhala ndi Pakati kwa Azaka Zapakati pa 13 ndi 19—Zotulukapo kwa Anyamata
Posonkhezeredwa ndi mantha—kapena kupanda chikondwerero kwadyera—anyamata ena amene akhala ndi mwana kunja kwa ukwati amayesera kuthawa mathayo awo kotheratu. Mnyamata wina amene bwenzi lake linakhala ndi pakati anati: “Ndinangomuuza kuti, ‘Ndidzikuwona.’”
Mwamwaŵi, anyamata ambiri amawoneka kuti amafuna kukhala oloŵetsedwamo mwa mbadwa zawo. Pamene ukwati uwoneka kukhala wosayenera (monga mmene zimakhalira nthaŵi zambiri), ambiri amadzipereka kuthandiza mwazachuma. Ena amafikira pa kudzipereka kuthandiza m’kusamalira kwa tsiku ndi tsiku kwa mwanayo. Koma zoyesayesa zoterozo zimakhala za kanthaŵi kochepa, zolepheretsedwa ndi kuchepa kwa luso la kupeza ndalama la mnyamatayo ndi kusoŵa kwake kuleza mtima ndi maluso ofunikira kusamalira mwana wamng’ono.
Ndiponso, makolo a msungwana nthaŵi zina amakana kulola mnyamatayo kukhala ndi zochita zina ndi mwana wawo wamkazi, kuwopera kuti zimenezi zingatsogoze ku mkhalidwe wina wachisembwere—kapena ukwati wofulumira. Iwo angamkanize kukhala ndi phande lirilonse m’zosankha zimene zikupangidwa ponena za mwanayo, mwinamwake kumkakamiza kukhala wopanda thandizo pamene mwanayo akutaidwa kapena kuperekedwa kuti aleredwe ndi ena, kuthetsa mwaŵi uliwonse wokhala wokhoza kukhala ndi phande m’moyo wa mwana amene iye ali tate wake. Kumbali ina, mnyamata angaloledwedi kukhala ndi unansi ndi mwana wake—kokha kuthetsa chomangira choterocho pamene msungwanayo akwatiwa ndipo mwamuna wina atenga thayo la tate.
Pamenepa, mosakaikira, atate osakwatira nawonso amalipira kaamba ka mkhalidwe wawo wosadzisunga. Tate wina wasokwatira wa zaka 16 zakubadwa ananena kuti: “Pali malingaliro ambiri amene sungathe kuchita nawo. Kuli monga kupempherera kuti ubwerere kumene udali kalelo, koma palibe njira yochitira zimenezo.”—Magazine a “’Teen,” November 1984.