Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 6/8 tsamba 8-11
  • Nyimbo Zamakono Kupeŵa Misamphayo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyimbo Zamakono Kupeŵa Misamphayo
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunika kwa Kukhala Wachikatikati
  • Chizoloŵezi Chakupanga Zodzikhululukira
  • Chitanipo Kanthu Mwanzeru
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhalira Kumvetsera Nyimbo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingasungire Nyimbo m’Malo Ake?
    Galamukani!—1993
  • Kusangalala ndi Nyimbo—Nchiyani Chimene Chiri Mfungulo?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Mumasankha Nyimbo Mwanzeru?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 6/8 tsamba 8-11

Nyimbo Zamakono Kupeŵa Misamphayo

ENA amanena za maubwino ndi kuipa kwa kupenda nyimbo za rock zisanaloledwe. Ena amakaikira ziyambukiro zake zoipa pa achichepere. Koma ngati ndinu Mkristu, nkhani zimenezi nzachiŵiri ku nkhani yaikulu yakuti: Kodi nyimbo zingayambukire motani unansi wanu ndi Mulungu?

Moyo wa Mkristu umatsogozedwa ndi Mawu a Mulungu, Baibulo. Ilo lili ndi malamulo onena za mbali zonse za moyo, kuphatikizapo zosangulutsa. Malangizo a Baibulo amachinjiriza anthu omvera ku zinthu zoipa ndi zovulaza. Ndiponso, chivomerezo cha Mulungu chimadalira pa kumvera Mawu ake. Chifukwa chake, malamulo amkhalidwe a Mawu a Mulungu amatsogoza Akristu posankha nyimbo. (Salmo 43:3; 119:105; 2 Timoteo 3:16, 17) Pamenepo, kodi ndimalangizo Amalemba otani amene amatithandiza posankha nyimbo?

Kufunika kwa Kukhala Wachikatikati

Lemba la Mlaliki 7:16 limachenjeza kuti: “Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziwononga wekha?” Musanasulize nyimbo iliyonse kukhala yoipa, dzifunseni ngati kungakhale nkhani ya zimene mamakonda. Kumbukirani kuti mungaipidwe ndi nyimbo yakutiyakuti, koma zimenezo sizimaipanga kukhala nyimbo yoipa.

Mbali ina ya kukhala wachikatikati pankhaniyi yaperekedwa pa Mlaliki 7:17, 18: “Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa, uferenji nthaŵi yako isanafike? Kuli kwabwino kugwira ichi; indetu, usachotsepo dzanja lako pakuti yemwe awopa Mulungu adzatuluka monsemo.”

Pamenepo, bwanji ngati Mkristu amvetsera nyimbo zimene zimalimbikitsa chiwawa, tsankho la fuko, chisembwere, kulambira Mdyerekezi, ndi kudzipha? Lemba la Aefeso 5:3, 4 limanena mwachindunji kuti: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.” Inde, amene amafuna kukhala paubwenzi ndi Yehova sangasanguluke ndi zinthu zoipa. Iwo sadzalungamitsa zinthu kuti malinga ngati sachita zinthu zoipazo, ndiye kuti nkwabwino kusangalala nazo.

Simawu a nyimbo okha amene amaipanga kukhala yabwino kapena yoipa malinga ndi lingaliro Lamalemba. Kodi imalimbikitsa mzimu wotani? Chonde ŵerengani lemba la Agalatiya 5:19 mpaka 23 m’Baibulo lanu. Kodi ndindandanda iti imene ikufotokoza bwino mzimu wa nyimbo zimene mumamvetsera? Ngati nyimbozo zimafanana ndi “ntchito za thupi,” pamenepo lingaliro la Yehova nlomvekera bwino.

Ngati Mkristu ayesa kuphatikiza moyo wake wa utumiki wopatulika kwa Mulungu ndi zosangulutsa za nyimbo zoluluzika, iye adzazindikira kuti sizigwirizana konse. Nkofanana ndi kumwa Fanta yosakanizana ndi paizoni. Fantayo sidzaletsa paizoniyo kukuphani. Mawu opezeka pa 2 Akorinto 6:14-17 amamveketsa mfundoyo: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira? . . . Chifukwa chake, Tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati Ambuye, ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka.”

Pamenepo, zimenezi ndinkhani Zamalemba zimene zimakhudza amene amafuna kukhala ndi unansi wathithithi ndi Mulungu. Ngati mumawona malamulo a Baibulo kukhala aphindu, pendani mosamalitsa nyimbo zimene mumamvetsera. Santhulani mosamalitsa malekodi ndi mavidiyo anu. Tayani amene amawombana ndi malamulo amkhalidwe a Baibulo. Ngati mukukayikira, ingowatayani. Chitani zofananazo ndi makonsati ndi zinthu zoŵerenga—chotsani zonse zimene sizigwirizana bwino ndi chilungamo.

Chizoloŵezi Chakupanga Zodzikhululukira

Ngati mumakopeka ndi nyimbo zokaikitsa kapena zimene zimasemphana ndi malangizo a Malemba, mungakupeze kukhala kovuta kuyang’anizana bwino ndi nkhaniyo. Ena amapanga zodzikhululukira kuyesayesa kudzichinjiriza ndi kulungamitsa kaimidwe kawo kololera molakwa. Ngati zimenezi zimachitika kwa inu, taimani ndi kuganiza. Kodi kulingalira kwanu nkwanzeru, kapena kodi kumangosonyeza kukondetsa kwanu nyimbozo? Talingalirani zigomeko zotsatirazi zoperekedwa ndi ena ndipo onani kuti, zitasanthulidwa mosamalitsa, zigomeko zimenezo zimangokhala zodzikhululukira.

Nkwabwino kwa ine kumvetsera gulu la oimba ameneŵa chifukwa mamembala ake amatsutsa kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa. Koma kodi gululo limatsutsa mwamphamvu machitachita ena oipa, monga ngati dama, chiwawa, ndi kusalemekeza maulamuliro? Lemba la Agalatiya 5:9 limati: “Chotupitsa pang’ono chitupitsa mtanda wonse.”—Yerekezerani ndi Yakobo 2:10.

Moyo m’dzikoli ngwopanda chilungamo. Kodi tingapatsedi mlandu magulu oimba ameneŵa chifukwa chosonyeza kukwiya kwawo ndi mikhalidwe yadziko? Baibulo limalimbikitsa mkwiyo wachilungamo wotsutsana ndi zinthu zoipa za m’dongosolo lino koma limasonya ku Ufumu wa Umesiya monga yankho.—Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.

Chiyembekezo chowala cha Mkristu nchosiyana ndi kulingalira koipa kwa oimba ambiri amene amachilikiza chipanduko monga njira yothetsera kupsinjika maganizo kwa anthu. Ndithudi, mkwiyo wa dziko ngowononga ndi wauchinyama, umasonyeza nzeru ya dongosolo lino la zinthu.—Aroma 12:9; Yakobo 3:15-18.

Oimbawo ngaluso, ndipo ngophunzitsidwa mwaukatswiri. Koma luso limene oimba amachita nalo nlosagwirizana ndi muyezo wopendera malamulo amkhalidwe a Baibulo pankhani ya nyimbo, kodi sichoncho? Mfumu Solomo anali waluso m’zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo nyimbo. Koma pamene anapatuka pa kulambira kowona, Baibulo limasimba kuti, “Yehova anakwiya ndi Solomo, pokhala mtima wake unapambuka kwa Yehova.” Mofananamo, Nimrode anali mmisiri womanga ndi mpalu waluso, koma iye ndi atsamwali ake anayang’anizana ndi mkwiyo wa Mulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Nimrode anali “mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.”—1 Mafumu 11:9; Genesis 10:8, 9.

Nyimbo zoŵerengeka za gulu loimbalo nzabwino, kuphatikizapo nyimbo zina zosakhala zaphokoso. Ngozi panopo njakuti nyimbo yabwino ingachititse munthu kugula ndi kumvetsera tepi kapena lekodi yathunthu yokhala ndi nyimbo zambiri, zambiri za izo zomwe sizingakhale zabwino konse. Monga momwedi madzi a m’chikho chimodzi sangakhale okwanira kutsukira chinthu chokhala ndi matope ambiri, kumvetsera kamodzikamodzi nyimbo yabwino sikumasintha mzimu wonse wa lekodi kapena tepi kapena gulu la oimba loluluzika.

Akatswiriwo samalambiradi Satana kapena kuchita chisembwere. Iwo akungoyerekezera zinthuzo papulatifomu. Mfundo njakuti nyimbo zimene amagwiritsira ntchito kusangulutsa omvetsera zimasakanizidwa ndi zoipa. Lemba la Akolose 3:8 limalangiza Akristu, kusasangalatsidwa ndi zinthu zonga ngati mkwiyo ndi mawu otukwana, koma ‘kutaya zonse.’ Paulo anauza Aefeso kuti ‘asayanjane [nawo ana akusamvera] m’ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso azitsutse.’ Kodi munthu amene amasangalatsidwa ndi ntchito za mdima angadzudzule amene amazichita?—Aefeso 5:6, 11.

Sindimvetsera mawuwo. Ndimangomva maimbidwewo. Koma mawu akhoza kusungika mkati mwa maganizo ndipo angayambitse mavuto pambuyo pake. Ngakhale kuti timaganiza kuti mawuwo achoka m’maganizo mwathu, iwo sangaiwalidwe konse. Pamenepo, nkwaupandu chotani nanga kumvetsera dala mawu amene amatsutsana mwachindunji ndi uphungu wa pa Afilipi 4:8, wakuti tisumike maganizo athu pa zinthu zokoma, zokongola, ndi zolemekezeka.

Kumbukiraninso kuti “amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti dziko la mtundu wa anthu latalikirana ndi Mulungu ndipo mzimu wa dziko uli chotulukapo cha Mdani wamkulu wa Yehova, Satana Mdyerekezi. Tsopano talingalirani zimenezo. Kodi munthu angasangalale ngati mkazi wake aika powonekera chithunzithunzi cha bwenzi lake lakale ngakhale ngati anena kuti alibe malingaliro apadera alionse kwa iye koma kuti chithunzicho nchongokongoletsera m’nyumba? Ayi, mwamunayo adzafuna kuti chichotsedwe m’nyumbamo ndi m’maganizo mwa mkaziyo. Bwanji ngati tiloŵetsa m’nyumba zathu ndi m’mitima yathu nyimbo zimene zimachilikiza chifuno cha Mdani wa Yehova? Kodi zingakhale zomveka kwa Yehova ngati tinena kuti, “Ndimangosangalala ndi maimbidwewo; ndimanyalanyaza mawu ake”?—Yakobo 4:4; 1 Akorinto 10:21, 22.

Chitanipo Kanthu Mwanzeru

Ngati mumamvetsera nyimbo zimene zimagogomezera kuchita zoipa, kodi chifukwa chake chenicheni nchiyani? Mwinamwake simungavomereze malingaliro oipawo, koma nyimbo yeniyeniyo ingakhale yosangalatsa kwambiri kwa inu—kugunda kwake, kungakhale komwerekeretsa, kokopa mtima—kwakuti mumaipeza kukhala yosapeŵeka ndipo simufuna kuileka.

Koma kuchita zinthu zolondola sikumakhala kokhweka nthaŵi zonse. Timayesedwa kwambiri makamaka pamene miyezo ya Mulungu itilangiza kuleka chinthu chimene timakonda kwambiri. Kodi tidzalungamitsa kuti nkhani yathu njapadera ndi kupitiriza ‘kukayikakayika,’ kapena kodi tidzachita mwanzeru kutsutsa zimene Yehova amada?—1 Mafumu 18:21.

Mosasamala kanthu za kudzimana kumene kumaloŵetsedwamo, tidzakhala achimwemwe kwambiri ngati tipanga chosankha chimene chimakondweretsa Yehova. Zimenezi zimatanthauza kuti tiyenera kuleka kukhudza chinthu chodetsedwa chilichonse. Ngati tichita zimenezo, pamenepo Yehova akulonjeza kuti adzatitenga. Inde, adzatiŵerengera pakati pa anthu ake oyanjidwa.—2 Akorinto 6:17.

Yehova amatifunira zabwino koposa. Iye wapanga malamulo ake kuwongolera mtundu wa miyoyo yathu. Vomerezani kudandaulira kwake kowona mtima kopezeka pa Yesaya 48:17, 18. “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”

[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]

Thayo la Makolo

Ngati ndinu kholo, muli ndi thayo Lamalemba kuphunzitsa ana anu kusiyanitsa pakati pa nyimbo zabwino ndi zoipa. Zimenezi zimatanthauza kuti muyenera kudziŵa zimene iwo amamvetsera. Zimatanthauza kuti muyenera kukhala otsimikiza mtima pa nyimbo zimene mudzazilola ndi zimene simudzalola kuloŵa m’nyumba.

Kambitsiranani ndi ana anu. Peŵani mikangano imene imafooketsa kudalirika kwanu. Ndemanga zonga ngati, “Sindidziŵa kuti nchifukwa ninji umamvetsera zinthu zachabechabezo,” zikasonkhezera achichepere kumamatira zolimba ku zosankha zawo za iwo eni. Kuwauza za njira ya moyo yoluluzika ya woimba kungakhale kosakhutiritsa, makamaka ngati sisonyezedwa m’nyimbozo. Mwamuna wina wachichepere anatsutsa kuti: “Ngati munthu anena kuti nyimbo zonse za rap nzoipa, ndimamuwona kukhala mbuli yeniyeni!”

Chotero dziŵani zimene mudzanena. Phunzirani lingaliro la Mulungu pa nkhani zimenezi. Mboni za Yehova zidzakondwera kukuthandizani mwakukupatsani mabuku ofotokoza Baibulo amene amafotokoza mwatsatanetsatane. Dziŵani mfundo zenizeni. Mveketsani mfundo yakuti nkhaniyo njakutsatira miyezo ya Baibulo ndipo osati kuumiriza zokonda zanu pa ana anu.—Aefeso 6:4.

[Chithunzi patsamba 9]

Ngati Mkristu amvetsera nyimbo zoluluza, kodi iye angathandizedi ena kusatero?

[Chithunzi patsamba 11]

Mudzakhala achimwemwe kwambiri ngati mutaya zimene Yehova amanyansidwa nazo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena