Kusungulumwa—Kodi Ndinu Wofunitsitsa Kulimbana Nako ndi Kupambana?
KODI ndinu wosungulumwa? Pali nthaŵi zina m’moyo pamene kusungulumwa kumakhala kwachibadwa, kaya ndinu wokwatira kapena mbeta, kaya ndinu mwamuna kapena mkazi, kaya ndinu wokalamba kapena wachichepere. Zindikiraninso kuti kukhala nokha sindiko kwenikweni kumachititsa kusungulumwa. Wophunzira amene ali yekha komano namwerekera m’kufufuza samakhala wosungulumwa. Katswiri wojambula amene ali yekha akumajambula chithunzithunzi samamva kusungulumwa mpang’ono ponse. Iwo amakonda nthaŵi yakukhala okha, ndipo kukhala okha kumakhala bwenzi lawo labwino koposa.
Kumva kukhala wosungulumwa kumachokera mwa ife eni osati kwa ena. Kusungulumwa kungayambitsidwe ndi chochitika chomvetsa chisoni—imfa, chisudzulo, kuchotsedwa ntchito, kapena tsoka linalake. Pamene tiunikira dziko la mkati mwathu moŵala, kusungulumwako kungachepe, mwinamwake ngakhale kuzimiririka m’kupita kwanthaŵi, ndipo kutayikiridwa kumene kunatisautsa mtima kungapiririke, kuzoloŵereka.
Zopweteka za kusungulumwa zimachokera m’malingaliro anu. Mutazoloŵerana ndi kutayikiridwako ndipo zopweteka zimene kumachititsa zitachepetsedwa, ndiyo nthaŵi yakukulitsa malingaliro amene amakulolani kupitiriza ndi moyo wokangalika.
Dzisonkhezereni. Dzilamulireni. Zilipo zinthu zolimbikitsa zimene mungachite. Chotero khalani woyanjana ndi ena. Imbirani lamya munthu wina. Lembani kalata. Ŵerengani buku. Itanirani anthu ena kunyumba kwanu. Patsananani malingaliro. Kuti mukhale ndi mabwenzi, muyenera kusonyeza kukhala waubwenzi inu mwininu. Dzipendeni nokha kotero kuti mudzipereke kwa ena. Chitani zinthu zazing’ono zosonyeza kukoma mtima. Kambitsiranani mfundo zotonthoza zauzimu ndi ena. Mudzapeza mawu a Yesu kukhala owona akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” Mudzazindikira mwambi wina wa chowonadi wakuti: “Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”—Machitidwe 20:35; Miyambo 11:25.
Ndithayo Lanu
Kodi mukuti nzovuta? Kodi nzosavuta kunena kuposa kuzichita? Chinthu chilichonse chopindulitsa nchosavuta kunena kuposa kuchichita. Nzimene zimapangitsa kuchichita kukhala kokhutiritsa kwa inu. Muyenera kuyesayesa mwamphamvu. Mbali ya zoyesayesa zanu imaloŵa m’kupatsa, ndipo chikhutiro ndi chisangalalo zimakula mkati mwanu. Ndithayo lanu la kuchitapo kanthu kuti mugonjetse kusungulumwa kumene kumafuna kukulamulirani. Mlembi wina wa nkhani za m’magazini a Modern Maturity anati: “Palibe wina aliyense amene ali ndi thayo la kusungulumwa kwanu, koma inuyo mukhoza kuchitapo kanthu. Mukhoza kufutukula moyo wanu mwakukhala ndi bwenzi limodzi. Mukhoza kukhululukira wina amene mulingalira kuti anakulakwirani. Mukhoza kulemba kalata. Mukhoza kuimba lamya. Ndinu nokha amene mungasinthe mkhalidwewo. Palibe munthu aliyense amene angakuchitireni zimenezo.” Iye anagwira mawu kalata imene anailandira imene “inatchula mfundo yeniyeni kuti: ‘Ndimauza anthu kuti lili thayo lawo kuchitapo kanthu kuti miyoyo yawo isakhale yosungulumwa kapena yosakhutiritsidwa. Khalani ogalamuka, chitanipo kanthu!’”
Mabwenzi anu sayenera kukhala anthu okha. Dokotala wa mankhwala a zinyama anati: “Mavuto aakulu amene okalamba amakhala nawo sindiwo matenda akuthupi, koma kusungulumwa ndi kunyanyalidwa kumene amayang’anizana nako. Mwakuwapatsa . . . ubwenzi, zifuyo (kuphatikizapo agalu) zimapereka chifuno ndi tanthauzo m’moyo kwa okalamba panthaŵi imene amakhala okha.” Magazini akuti Better Homes and Gardens anati: “Zifuyo zimathandiza kuthetsa vuto la zopweteka za mtima; zimalimbikitsa odwala, opuŵala, ndi opunduka; ndipo zimatsitsimula osungulumwa ndi okalamba.” Nkhani ya m’magazini ena inanena motere ponena za anthu oyamba kumene kukhala ndi chikondwerero m’zifuyo: “Nkhaŵa za odwala zinachepa ndipo anakhoza kusonyeza chikondi kwa zifuyo zawo popanda mantha akuti adzakanidwa. Pambuyo pake iwo anayamba kulankhula kwa anthu, choyamba akumakamba ponena za zifuyo zawozo. Anayamba kumva kukhala athayo. Anadzimva kukhala ofunikira, odalirika.”
Kaŵirikaŵiri munthu wosungulumwayo samakhala wokhoza kupeza mphamvu yakudzithandiza yekha, kuti adzichotse mumkhalidwe wakusweka mtima. Amakhala ndi mphwayi, kusafunitsitsa kudzikakamiza kumlingo umenewo, koma ngati ati azindikire vuto lenileni la kusungulumwa kwakeko, iye ayenera ndithu kuchita zimenezo. Dr. James Lynch analemba ponena za anthu amene amakana uphungu umene amauona kukhala wovuta kuuvomereza kuti: “Chibadwa cha munthu nchakuti nthaŵi zambiri timakana kumva, kapena timatsutsa kulandira mumkhalidwe wathu, chidziŵitso chimene sitimakonda.” Munthu angafune kuthetsa kusungulumwa kwake, koma angakhale wosafunitsitsa kuyesayesa zolimba kuchita zofunikira kuti akuthetse.
Chitani Zinthu Mmene Mumazikhumbira
Kuti agonjetse kupsinjika mtima kwakukulu, munthu ayenera kulimbikira kukhalabe wosangalala ndi wokoma mtima. (Yerekezerani ndi Machitidwe 20:35.) Zimenezi zimafunikira kuswa mkhalidwe wakusungulumwa mwakuchita zinthu zotsutsana ndi mphwayi yake yovutitsayo. Chitani zinthu mwachimwemwe, vinavinani, imbani nyimbo yosangalatsa. Chitani kanthu kalikonse kosonyeza chisangalalo. Kakulitseni, kachiteni mopambanitsa, tangwanitsani maganizo amphwayiwo ndi malingaliro achisangalalo. Malingaliro otani?
Onga aja opezeka pa Afilipi 4:8 akuti: “Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zowona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”
Chofunikira ndicho kupangitsa moyo wanu kukhala ndi tanthauzo. Ngati mumva kuti moyo wanu uli ndi tanthauzo, mudzakhala ndi nyonga yakuchitapo kanthu ndi kufuna kukwaniritsa tanthauzolo. Mwachionekere simudzachita mphwayi ya kusungulumwa. Mokondweretsa, zimenezi zikusonyezedwa m’buku la Viktor Frankl lakuti Man’s Search for Meaning. Iye akugwirizanitsa mkhalidwewo ndi akaidi m’misasa yachibalo ya Hitler. Awo amene anaona miyoyo yawo kukhala yopanda tanthauzo anakhala osungulumwa ndipo analibe chifuno chokhalira ndi moyo. Koma “kuzindikira kufunika kwa munthuwe kwa mkati ndiko mnangula wa zinthu zapamwamba zauzimu, ndipo sikungagwedezedwe ndi moyo wa mumsasa wachibalo.” Iye anapitiriza kuti: “Kuvutika kumaleka kukhala kuvutika mwanjira ina panthaŵi imene iko kupeza tanthauzo, monga ngati tanthauzo la kupereka nsembe. . . . Nkhaŵa yaikulu ya munthu sindiyo kupeza ubwino kapena kupeŵa zopweteka, koma m’malomwake, kuona tanthauzo la moyo wake. Ndithudi, nchifukwa chake munthu amakhala wofunitsitsa kuvutika, pamaziko akuti kuvutika kwakeko kulidi ndi tanthauzo.”
Unansi Wopambana Umene Mumafunikira
Njira imene mungapezere lingaliro lenileni lauzimu ndiyo kudzipereka kotheratu kwa Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo. Chikhulupiriro mwa Mulungu ndi pemphero la mtima wonse kwa iye zikhoza kupangitsa moyo wathu kukhala watanthauzo. Ndiyeno, ngakhale ngati maunansi aumunthu alephera, sitimatsala tokha, sitimakhala osungulumwa. Monga momwe Frankl ananenera, kuvutika kumene kuli ndi tanthauzo kumapiririka, kumakhaladi magwero achisangalalo. Wochitira ndemanga wina pachibadwa cha munthu anati: “Wofera chikhulupiriro wopachikidwa pamtengo angakhale wachimwemwe kwakuti angakhumbiridwe ndi mfumu yokhala pampando wake wachifumu.”
Atumwi a Kristu anali ndi chisangalalo chochokera kwa Yehova pamene anazunzidwa ndi anthu; kuvutika koteroko kunali ndi tanthauzo lalikulu kwa iwo. “Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: chifukwa uli wawo ufumu wa kumwamba. Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu m’mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.” (Mateyu 5:10-12) Yankho lofananalo linalembedwa pa Machitidwe 5:40, 41 kuti: “Ndipo mmene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula. Pamenepo ndipo anapita kuchokera ku bwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.”
Pamene Ulima Duŵa, Sipamera Munga
Fesani m’nthaka ya maganizo anu mbewu za chifuno chabwino ndi choyenera; musasiyire malo mbewu za kutaya mtima ndi kusungulumwa kodetsa mtima. (Yerekezerani ndi Akolose 3:2; 4:2.) Kodi nzovuta kuchita? M’mikhalidwe ina, zimaoneka kukhala zosatheka. Wolemba ndakatulo wina anati: “Pamene ulima duŵa, . . . sipamera munga,” zimene zimafunikiranso kuyesayesa koyenera ndi kufunitsitsa kotsimikiza mtima. Koma zikhoza kuchitidwa, zikuchitidwa kumene.
Lingalirani chitsanzo cha Laurel Nisbet. Iye anadwala poliyo ndipo pausinkhu wa zaka 36 anaikidwa m’makina othandiza kupuma, mmene anali chigonere chagada kwa zaka 37. Ali wopuŵala kotheratu kuyambira m’khosi lake mpaka kumapazi, anali wokhoza kugwedeza mutu wake wokha. Poyamba anali wachisoni kwambiri ndi wothedwa nzeru kwakuti anadziwona kukhala wopanda pake. Ndiyeno, pambuyo pakudzimverera chisoni kwa tsiku limodzi, anaganiza kuti, ‘Zakwanira!’ Anali ndi ana aŵiri ofunikira kuwalera ndi mwamuna wofunikira kusamaliridwa. Anayamba kulimbikitsanso moyo wake; anaphunzira kusamalira nyumba ali mkati mwa makina othandiza kupumawo.
Laurel anagona tulo tochepa kwambiri. Kodi anachita motani m’nthaŵi yaitaliyo ya maola ausiku? Kugonjera ku kusungulumwa? Ayi. Iye anapemphera kwa Atate wake wakumwamba, Yehova. Anapempherera nyonga yake, anapempherera abale ndi alongo ake Achikristu, ndipo anapempherera kupeza mipata ya kuchitira umboni kwa ena ponena za Ufumu wa Mulungu. Iye analinganiza njira zolalikirira ndipo anasangalatsa anthu ambiri mwakuchitira umboni kwake ponena za dzina la Yehova. Sanalole minga ya kusungulumwa kumera; anali wotanganitsidwa kwambiri ndi kusamalira maluŵa.
Zinalinso motero kwa mmishonale wina wa Watch Tower, Harold King. Atamangidwa kwa zaka zisanu m’chipinda cha yekha m’ndende ya ku China, mwachionekere anayang’anizana ndi kusungulumwa kwa nthaŵi yaitali kwambiri. Koma, iye anakana lingaliro loipa limenelo, ndipo mwa mphamvu ya kufunitsitsa anagwiritsira ntchito maganizo ake panjira yosiyana ndi zimenezo. Iye pambuyo pake anafotokoza njirayo motere:
“Ndinalinganiza programu ya ntchito ‘yolalikira.’ Koma kodi munthu angalalikire kwa yani atabindikiritsidwa m’ndende ya yekha? Ndinaganiza kulinganiza maulaliki a Baibulo kuchokera m’zinthu zimene ndinakumbukira ndiyeno kumalalikira kwa anthu ongoyerekezera. Ndiyeno ndinayamba ntchitoyo, nditero kunena kwake, ndikumagogoda pakhomo loyerekezera ndi kuchitira umboni kwa mwininyumba woyerekezera, ndi kumafikira makomo angapo m’maola a mmaŵa. M’kupita kwanthaŵi ndinakumana ndi Mayi Carter oyerekezera, amene anasonyeza chikondwerero, ndipo pambuyo pa maulendo obwereza angapo tinalinganiza kukhala ndi phunziro la Baibulo lokhazikika. M’kuphunzira kwathu kumeneku tinakambitsirana mitu ya nkhani zazikulu za m’buku lakuti ‘Mulungu Akhale Woona,’ zimene ndinakumbukira. Zonsezi ndinachita mofuula, kotero kuti kumveka kwa zinthu zimenezi kukhomerezeke kwambiri m’maganizo mwanga.”
Zikwi zambiri za Mboni za Yehova zomangidwa m’misasa ya chibalo ya Hitler zikanamasulidwa ngati zikanangokana chikhulupiriro chawo. Zoŵerengeka kwambiri zinachita zimenezo. Zikwi zambiri zinafa zili zokhulupirika—zina mwakunyongedwa, zina mwakudwala ndi kudya mosakwanira. Mboni ina yokhala m’ndende—yotchedwa Josef—inali ndi achimwene ake aŵiri m’misasa ina. Mmodzi wa iwo anakakamizidwa kugona chagada akupenyerera chimpeni chikutsika nichidula mutu wake. Josef akufotokoza kuti: “Pamene ena mumsasamo anamva zimenezi anandithokoza. Mkhalidwe wawo wamaganizo abwino unandigwira mtima kwambiri. Kukhalabe wokhulupirika kunali kofunika kwambiri kwa ife kuposa kupulumuka.”
Mbale wake winayo, ali patsogolo pa gulu lowombera mfuti, anafunsidwa ngati anali ndi mawu okamba. Iye anapempha chilolezo chakuti apemphere, ndipo analoledwa. Pemphero lakelo linali lodzazidwa ndi chisoni limodzinso ndi kusonyeza chisangalalo chachikulu kotero kuti pamene chilengezo cha kuwombera chinaperekedwa, palibe ngakhale mmodzi wa owomberawo analabadira. Chilengezocho chinabwerezedwa, ndipo mmodzi yekha ndiye anawombera, namlasa m’thupi. Atakwiya ndi zimenezo, ofisala wamkuluyo anasolola volovolo yake ndi kumtsiriza.
Chimene Chingapangitse Miyoyo Kukhaladi Yatanthauzo
Zochitika zonsezi zinaloŵetsamo chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu. Pamene zoyesayesa zonse zapangidwa ndi kulephera, nthaŵi zonse chikhoza kutikhozetsa kulaka kusungulumwa ndi kupangitsa miyoyo yathu imene inali yopanda kanthu kukhala ndi tanthauzo lalikulu. Miyoyo yambiri imene imaonedwa kukhala yatanthauzo malinga ndi njira ya dziko ili kwenikweni yopanda tanthauzo. Nchifukwa ninji zili motero? Chifukwa chakuti iyo imathera mu imfa, imabwerera ku fumbi, ndi kuiŵalika, osasiya chisonkhezero chenicheni pa chitaganya cha anthu. Zili monga momwe lemba la Mlaliki 9:5 limanenera kuti: “Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiŵalika.” Lingaliro lililonse lakuti moyo wopanda chifuniro cha Yehova uli watanthauzo lili lopanda pake.
Penyani nyenyezi zakumwamba, talingalirani za kutakata kwa thambo lokhala kumwambalo, ndipo lingaliro la kukhala kwanu wofunika limazimiririka. Mukhoza kumvetsetsa malingaliro a wamasalmo Davide pamene analemba kuti: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?” Mwana wa Davide, Solomo, anasuliza ntchito za munthu, akumati, “Zonse ndi chabe,” namaliza kuti: “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, nusunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—Salmo 8:3, 4; Mlaliki 12:8, 13.
Ndiyeno popeza tapenda zonsezo, kodi ndimotani mmene munthu wosungulumwa, kapena munthu aliyense, angapangitsire moyo wake kukhala wa tanthauzo? Mwakukhala ndi moyo wakuwopa Mulungu, akumamvera malamulo a Mulungu. Ndipokhapo pamene angayenerere zifuno za Mulungu, Mlengi wa chilengedwe chonse chotakata chimenechi, ndi kukhala mbali ya makonzedwe ake aumulungu amuyaya.
Ngati Mulungu Ali Nanu, Simuli Nokha Konse
Mboni ya Yehova ina yokhulupirika ya mu Afirika, itazunzidwa koipitsitsa ndi kumva kukhala yonyanyalidwa, inati ngakhale kuti maunansi ake aumunthu analephera, iye sanali yekha. Anagwira mawu Salmo 27:10 kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” Yesu analingalira mofananamo. “Onani ikudza nthaŵi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi ine.”—Yohane 16:32.
Yesu sanawope kukhala payekha. Iye kaŵirikaŵiri anafuna dala kukhala payekha. Pamene anali yekha, sanali wosungulumwa. Analola mzimu wa Mulungu kufika pa iye ndipo anamva kukhala woyandikana ndi Iye pamene anazingidwa ndi zolengedwa Zake. Nthaŵi zina iye anapeŵa kukhala ndi anthu ena kotero kuti akhale ndi Mulungu yekha. Iye ‘anayandikira kwa Mulungu; Mulungu anayandikira kwa iye.’ (Yakobo 4:8) Iye mosakayikira anali bwenzi lapamtima la Mulungu.
Bwenzi longa limene Malemba amalifotokoza nlofunika kwambiri. (Miyambo 17:17; 18:24) Chifukwa cha chikhulupiriro chake chokwanira mwa Yehova Mulungu ndi kumvera kwake kosaŵiringula kwa iye, Abrahamu “anatchedwa bwenzi la Mulungu.” (Yakobo 2:23) Yesu anati kwa otsatira ake: “Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu. Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziŵa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziŵitsani.”—Yohane 15:14, 15.
Pokhala ndi mabwenzi onga Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu, kodi ndimotani mmene awo okhala ndi chikhulupiriro angalepherere kulimbana ndi kusungulumwa?
Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)
[Zithunzi pamasamba 28, 29]
Pemphero ndi zochita zina zingakuthandizeni kupeŵa kusungulumwa
[Chithunzi patsamba 31]
Zokumana nazo za Harold King ndi zikwi za Mboni za Yehova zina m’misasa ya chibalo zimasonyeza kuti chikhulupiriro mwa Mulungu chingagonjetse kusungulumwa ngakhale m’mikhalidwe yoipitsitsa
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi cha National Archives ya United States