Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 11/8 tsamba 11
  • Uyo Amene Adzatetezera Nyama Zathu za Kuthengo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uyo Amene Adzatetezera Nyama Zathu za Kuthengo
  • Galamukani!—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Nyama Zakutchire Zachepa ndi 73 Peresenti Poyerekezera ndi Zaka 50 Zapitazi—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nkhani Zina
  • Kodi Ndani Amene Amatetezera Nyama za Kuthengo za mu Afrika?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Dziko Lapansili Likhalapobe Mpaka Kalekale?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Dziko Lapansi Lidzawonongedwa?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 11/8 tsamba 11

Uyo Amene Adzatetezera Nyama Zathu za Kuthengo

KUYAMBIRA pachiyambi cha mbiri ya mtundu wa anthu, munthu wakondweretsedwa ndi kuphunzira makhalidwe a nyama za kuthengo. Komabe, mwachisoni, Mulungu ataloleza munthu kuwonjezera nyama pachakudya chake, kuyamikira nyama za kuthengo kunayamba kuchepachepa kufikira pakupha nyama kosafunikira ndi uzimba wankhanza kaamba ka mitu yake yokometsera m’nyumba.—Genesis 2:19, 20; 9:2; 10:9; 25:27.

Koma anthu ena anapitirizabe kuzizwa ndi nyama za kuthengo za padziko lapansi. Pafupifupi zaka 3,000 zapitazo, mawu a Salmo 104 analembedwa ndi munthu wokonda nyama za kuthengo. Iye akutchula zolengedwa za kuthengo zosiyanasiyana mwa dzina lake, monga ngati mbidzi, mikango, zinkhoma, mbira, ndi chumba. Kuchokera m’phunziro lake la mbalame, nyimbo za mbalame, ndi nyama za kuthengo, wamasalmoyo anasonkhezeredwa kunena motamanda kuti: “ [Yehova anachita] zonse mwanzeru.”—Salmo 104:10-12, 17-21, 24.

Ndithudi, Yehova Mulungu moyenerera angakondweretsedwe ndi ntchito zake za chilengedwe zabwino kwambirizo. (Genesis 1:31) Motero, tingatsimikizire kuti sadzalola nyama za kuthengo za padziko lapansi zotsalapozo kuthetsedwa. Mogwirizana ndi zimenezo, Mulungu anauzira wamasalmo kulemba mawu amene ayenera kukhala mbiri yabwino kwa onse okonda nyama za kuthengo. Timauzidwa kuti “dziko lapansi . . . silidzagwedezeka kunthaŵi yonse.” (Salmo 104:5) Nkhawa yotero kaamba ka ubwino wamuyaya wa pulaneti imeneyi imaphatikizapodi zolengedwa zimene zimakhalapo ndi moyo. (Yesaya 45:18) Yesu Kristu anachitira umboni za nkhawa ya Mulungu pa zolengedwa za kuthengo pamene anati: “Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiŵiri? ndipo palibe imodzi ya izo iiŵalika pamaso pa Mulungu.” (Luka 12:6) Nkhawa ya Mulungu pazolengedwa zake yafotokozedwanso pa Salmo 104, vesi 14, pamene pamati: “Ameretsa msipu ziudye ng’ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m’nthaka.”

Mogwirizana ndi maumboni ameneŵa, Yehova Mulungu sadzalekerera kosatha anthu amene amamkana ndi amene amawopseza mtsogolo mwa dziko lapansi ndi nyama zake za kuthengo. Pogogomezera zimenezi, Salmo 104 limamaliza ndi mawu otsimikizira akuti: “Ochimwa athedwe kudziko lapansi, ndi oipa asakhalenso.”—Salmo 104:35.

Nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti Mulungu watsimikiza “kuwononga iwo akuwononga dziko.” (Chivumbulutso 11:18) Panthaŵiyo maulosi ena amene akukwaniritsidwa tsopano lino mophiphiritsa adzakwaniritsidwa kwenikweni. Mwachitsanzo, kupyolera mwa mneneri wake Hoseya, Yehova Mulungu amalengeza kuti: “Tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwaŵa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m’dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.”—Hoseya 2:18; Yesaya 11:6-9.

Dziyerekezereni muli m’Paradaiso wa padziko lapansi amene akudzayo. Ha, imeneyo idzakhala nthaŵi yokondweretsa chotani nanga! ‘Koma,’ inu mungafunse motero, ‘kodi nchiyani chimene chikufunika kuti munthu adzalandire madalitso otero?’ Choyamba, nkofunika kuphunzira Mawu a Mulungu. Ndiyeno, kwa awo amene amagonjera chitsogozo cha Baibulo, Yehova Mulungu amanena lonjezo labwino lakuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena