“Sitimamanidwa Kanthu!”
Ndemanga zaperekedwa ndi aphunzitsi akusukulu ndi ena kuti ana a Mboni za Yehova amamanidwa kanthu kena mwa kusaloledwa kutenga mbali m’zikondwerero za pasukulu za Krisimasi, Isitala, ndi Halloween. Zotsatirazi ndindemanga zoŵerengeka za ana amene ali Mboni za Yehova, akumafotokoza m’makalata chifukwa chimene iwo eniwo amakanira kukhala ndi mbali iliyonse m’kukondwerera maholide ameneŵa.
“NGAKHALE kuti ndinafotokozera anzanga a kusukulu chifukwa chimene sindimakondwerera zinthu zimenezi, iwo anaganizabe kuti ndinali kumanidwa kanthu kena. Koma sindinali womanidwa kanthu! Mwaona nanga, iwo nthaŵi zonse anafunikira kuyembekezera kufikira pa Krisimasi yawo kapena holide ina kuti alandire mphatso, pamene ine ndinali kupatsidwa zinthu ndi kupita kumapwando chaka chonse. Ndikudziŵa kuti ndimakondedwa osati ndi banja langa lokha komanso ndi mpingo limodzinso ndi Yehova, ndipo zimenezo zimatanthauza zambiri kwa ine kuposa holide iliyonse.”—Becky, wazaka 13.
“Ndimadziŵa kuti maholide onse ali ndi chiyambi choipa. Yesu sanabadwe pa Krisimasi. Banja lathu silifunikira kuchita chilichonse mmalo mwa maholide otero. Ziŵalo za banja langa zikhoza kundithandiza nthaŵi iliyonse imene ndifunikira chithandizo. Zimenezo nzofunika kwambiri kwa ine kuposa mphatso iliyonse imene iwo angandipatse.”—Josh, wazaka 15.
“Krisimasi. Siimandimanitsa kanthu chifukwa siili Yachikristu konse. Ndingakonde kudziŵa kuti makolo anga andipatsa mphatso osati Santa munthu wongopeka. Isitala. Ponena za Isitala njovuta ngakhale kumvetsetsa chifukwa anthu amati nja ‘Yesu ndi chiukiriro’ kapena kuti yangokhala ‘kupita kukafuna mazira.’ Koma ndi iko komwe kodi ndimotani mmene mazira agwirizanira ndi Yesu? Ngakhale dzinalo Isitala linachokera kwa mulungu wachikazi wamakedzana. Halloween. Tanthauzo lenileni la Halloween silimandisangalatsa konse. Mizukwa ndi mfiti, UUU!”—Katie, wazaka 10.
“Monga wachichepere sindinadzimverepo chisoni chifukwa cha kuphonya zikondwerero za maholide a kudziko. Sindinauzidwepo ndi makolo anga kuti ‘sungachite zakutizakuti chifukwa ndiwe mmodzi wa Mboni za Yehova,’ koma ndazoloŵerana ndi Baibulo ndi lingaliro la Yehova la maholide ameneŵa. Ponena za mphatso, kupatsana mphatso nkwachaka chonse m’nyumba mwathu.”—Ryan, wazaka 17.
“Holide iliyonse ili kukondwerera kanthu kena konama ndipo njozikidwa pa zinthu zonama. Achichepere ambiri amene ndimadziŵa amakondwerera maholide chifukwa cha maswiti kapena mphatso. Chinthu chimene ndili nacho chabwino koposa maholide ndicho gulu labwino koposa la Mboni za Yehova. Mmalo mokhala tsiku limodzi, mofanana ndi holide, Mawu a Yehova Mulungu ali ndi uthenga wosangalatsa umene uli wosatha.”—Brooke, wazaka 14.
“Zifukwa zimene sindimalakalakira maholide ndiizi: 1. Baibulo limati ali oipa. 2. Ndilibe nawo ntchito. 3. Amayi ndi atate anga amandipatsa mphatso.”—Brandi, wazaka 6.
“Sindimadzimva kukhala womanidwa kanthu. Ndilibe nazo kanthu. Ndimalandira mphatso, ndipo timachita maseŵera ndi kukhala ndi mapwando. Ndimalandira zinthu zochuluka popanda kukondwerera maholide. Ndifuna kukhalabe Mboni m’zilizonse zimene ndichita ndipo palibe chilichonse chimene chingandibwevutse.”—Brianne, wazaka 9.
“Ndidzayamba giredi lachisanu ndipo sindichita chisoni kuvomereza kuti ndine mmodzi wa Mboni za Yehova. Panthaŵi ina mnyamata wina anati ndiyenera kuchita chisoni chifukwa sindinalandire mphatso iliyonse pa Krisimasi, koma ndinati ndimalandira mphatso chaka chonse. Ndiyeno anati ndili ndi mwaŵi. Ndiyesa sipayenera kukhala Mboni ya Yehova iliyonse imene imachita chisoni chifukwa chokhala Mboni ya Yehova.”—Jeff, wazaka 10.
“Ine ndi mchemwali wanga tinapanga kukondwerera tsiku limene makolo athu anakwatirana kukhala holide ya banja lathu. Ndinapeza chimwemwe chachikulu mwa kukonza mphatso ndi makadi ndi zinthu ndi kuthandiza makolo anga kukonza zinthu zoti adzapatsane mosayembekezera kuposa chimene ndinapeza mwa kulandira mphatso kwa munthu wina. Kupatsa nkwabwino koposa kulandira.”—Rachel, wazaka 16.
“Pamene ndinali wachichepere, kunali kovuta kusuliza maholide ena. Koma pambuyo pake ndinazindikira kuti maholide angachititse umbombo, mikangano, ndi chisoni. Pamene pali nthaŵi zoikidwiratu za kupatsa, sumadabwa konse ndi mphatsoyo. Ndingakonde kulandira mphatso yapadera panthaŵi iliyonse yachaka. Kukondwerera kapena kusakondwerera kwangokhala mbali yaing’ono ya chosankha chokulirapo: kaya kudzipatulira kwa Yehova kapena kusatero. Pamene ndiganiza motero, chosankha cholondola nchodziŵikiratu.”—Ben, wazaka 13.
“Panali nthaŵi zina pamene ndinali mwana pamene ndinkalingalira kuti ndinali kutaikiridwa kanthu kena, koma pambuyo pake ndinaseka pamene ndinaganiza za mmene mazira, Yesu, ndi kalulu wa Isitala zinagwirizanira. Pamene ndinali wachikulirepo ndipo pamene makolo anga anandifotokozera kumene zizindikirozo zinachokera, ndinaiona kukhala yonyansa. Kumandipweteka mtima kuganiza za mmene Yehova ndi Yesu amamvera pogwirizanitsidwa ndi malingaliro achikunja otero.”—Alexa, wazaka 18.
“Panthaŵi ya Krisimasi, kukhala kusukulu kungakhale kolefula kwambiri ndipo kungakuchititse kudzimva kukhala wonyanyalidwa. Ndiyeno ndinazindikira kuti kukondwerera Krisimasi sikungathetse mavuto a munthuwe, sikungagwirizanitse banja lanu, ndipo sikungakudzetsere chimwemwe. Kutsatira miyezo ya Baibulo ndiko kokha kumene kungatero.”—Joe, wazaka 15.
“Mmalo mokhala ndi Krisimasi kapena holide ina iliyonse, timakhala ndi Tsiku Lalikulu la Zoseŵeretsa. Timalandira mphatso ya ndalama zogulira chilichonse chimene tifuna. Chaka china ndinakamba nkhani yonena za chipembedzo changa kwa a m’kalasi langa. Mmalo motsatira njira ya dziko, ndinakhazikitsa njira yanga ya kupita kumisonkhano, kupita muutumiki wakumunda, ndi kupanga pemphero kukhala mbali ya moyo wanga. Ndidzabatizidwa pamsonkhano wadera wotsatira.”—George, wazaka 11.
“Ndimakonda kulandira mphatso, ndipo ndimazilandira chaka chonse. Sindimaphonya kanthu ponena za mapwando. Ndimakondweretsa Yehova pamene ndichirikiza chowonadi. Nkoseketsa kuona ena a anzanga a m’kalasi amene sali Akristu, amene ali Ahindu, Ayuda, ndi ena otero, akukondwerera Krisimasi ndi kulandira mphatso komabe sadziŵa zimene holideyo imatanthauza.”—Julia, wazaka 12.
“Pamene ndinaphonya maholide kusukulu sindinachite chisoni. Achichepere amachita zinthu zachilendo zambiri, zonga kuvalira Halloween. Sindimalakalaka zimenezo ayi. Ndimawauza mmene makolo anga amandigulira zinthu chaka chonse. Iwo amandiuza za matchalitchi awo ndi mmene aliri otopetsa, ndipo ndimawauza za misonkhano imene timakhala nayo m’paki, ndipo amachita nsanje nthaŵi zina. Koma sindimawachitira nsanje. Kunena mwachidule, ndingoti khalani ndi mabwenzi amene amalemekeza zikhulupiriro zanu ndipo musalole wophunzira kapena mphunzitsi kukukakamizani kuchita chilichonse chotsutsana ndi chifuniro cha Yehova.”—Justin, wazaka 12.
“Kodi ndimadzimva kukhala womanidwa kanthu kena? Ayi, chifukwa timakhala ndi mapwando ena, ndipo pamene anthu akondwerera Krisimasi, ana kwakukulukulu amaganiza za Santa Claus, kapena pa Isitala amaganiza za kalulu wa Isitala, koma ndidziŵa kuti zinatengedwa ku zipembedzo zachikunja. Ndimakonda utumiki wakumunda chifukwa umandithandiza kusumika maganizo anga pachowonadi.”—Sharon, wazaka 8.
“Kunena mowona mtima sindinaganizepo kuti ndikusoŵa kanthu pokhala mmodzi wa Mboni za Yehova. M’banja lathu timasanguluka kwambiri. Pamene kusukulu kuli mapwando amayi amapita nane kokacheza kukadya chakudya chamasana. Makolo anga amandibweretsera zabwino kusukulu popanda chifukwa chapadera ndipo achichepere onse amadziŵa kuti timasanguluka. Ndimakondana kwambiri ndi makolo anga ndipo pamene achichepere afunsa chifukwa chake sindikondwerera maholide ndimawauza kuti ndimakhala ndi phwando masiku onse. Kodi ndimotani mmene Mboni ingadzionere kukhala yonyanyalidwa?”—Megan, wazaka 13.
“Halloween. Ana ovala ngati tiziŵanda, anthu a m’mabuku anthano—nzanji? Ana amayendayenda m’makwalala kupita kunyumba ndi nyumba akumalandira maswiti ochuluka. Kapena kuponyera mazira pazinyumba, kukoloŵeka matishu kumitengo, ndipo choipa koposa nchakuti makolo ambiri amavomereza zimenezo.”—Zachary, wazaka 10.
“Sindifunikira kuyembekezera tsiku lapadera kuti ndilandire mphatso. Amayi ndi atate anga amandigulira zoseŵeretsa zambiri nthaŵi zonse. Halloween ili kulambira mizimu ya akufa. Siyabwino. Mulungu yekha amene tiyenera kulambira ndi Yehova.”—Nicholas, wazaka 6.