Lingaliro la Baibulo
Kodi Muyenera Kubatizidwanso?
LUCILA anavutika maganizo. Ngakhale kuti analeredwera m’Chikatolika, iye anali atangoyamba kumene phunziro losamalitsa la Baibulo mothandizidwa ndi bwenzi losakhala Lachikatolika. Iye anatha kuona kuti Baibulo limafotokoza ubatizo kukhala kanthu kena kosiyana ndi dzoma limene analandira paukhanda. “Kodi zimenezi zitanthauza kuti ndidzafunikira kubatizidwanso?” iye anafunsa motero mowona mtima. “Ndikuopa kuti mwina kuchita motero kungakwiyitse Mulungu.”
Mamiliyoni mazana ambiri a anthu, Akatolika ndi Aprotestanti omwe, anawazidwa kapena kuthiridwa madzi pamene anali makanda padzoma laubatizo. Mamiliyoni a anthu ena anabatizidwa mumpangidwe wina wa kumizidwa kotheratu m’madzi pamene anali achikulirepo. Zimenezi zimadzutsa funso lakuti, Kodi kwenikweni ubatizo Wachikristu nchiyani? Kodi pali mikhalidwe ina iliyonse imene ingaloleze ubatizo wachiŵiri?
Pocket Catholic Dictionary imafotokoza ubatizo kukhala “sakalamenti imene, mwa madzi ndi mawu a Mulungu, munthu amayeretsedwa nayo machimo onse ndi kubadwanso ndi kuyeretsedwa mwa Kristu kumoyo wosatha.” Ponena za kubatizidwanso, dikishonale imodzimodziyi imati “ubatizo umakhomereza chizindikiro chosatha pamoyo, kutanthauza kuti sungathe, chifukwa sufunikira, kubwerezedwa.” Kodi zimenezi nzimene Baibulo limanena?
Pangani Ophunzira, Mukumawabatiza
Pa Mateyu 28:19, 20, timaŵerenga lamulo lonena za ubatizo umene Kristu woukitsidwa anapereka kwa ophunzira ake asanakwere kumwamba. “Chifukwa chake, pitani, pangani ophunzira a mitundu yonse; abatizeni m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, ndipo aphunzitseni kusunga malamulo onse amene ndinakupatsani.” (The Jerusalem Bible) Mwachiwonekere, ubatizo ngwofunika kwa ophunzira Achikristu—awo amene aphunzitsidwa kusunga malamulo a Kristu—osati makanda.a Zimenezi zimagwirizana ndi chenicheni chakuti maubatizo onse ofotokozedwa m’Malemba anali a ophunzira amene mwachionekere anamizidwa kotheratu m’madzi. Mwachionekere zimenezi zinali choncho pamene Kristu Yesu mwiniyo anabatizidwa ndi Yohane Mbatizi. Cholembedwa cha Baibulo chimasimba kuti atabatizidwa, Yesu “anatuluka m’madzi” a mtsinje wa Yordano. (Mateyu 3:16, JB) Ndithudi, Malemba amasonyeza kuti Yohane anasankha mosamalitsa malo ake obatizira kotero kuti akhale ndi madzi ambiri.—Yohane 3:23.
Pambuyo pake, pofotokoza ubatizo wa mdindo wa ku Aitiopiya, Baibulo limatiuza kuti “Filipo anatsikira m’madzi ndi mdindo ameneyo nambatiza,” pambuyo pake “iwo anatuluka m’madzi.” (Machitidwe 8:38, 39, The New American Bible) Maubatizo a kumiza ameneŵa ngogwirizana ndi tanthauzo lodziŵika la mawu Achigiriki ba·ptiʹzo, “kubatiza,” kuchokera ku baʹpto, kutanthauza “kumiza mkati kapena pansi,” kumene kukuchokera liwu la Chicheŵa lakuti “ubatizo.”
Cholembedwa cha Malemba cha Kubatizanso
Koma bwanji za mamiliyoni ambiri a anthu amene anabatizidwa adakali makanda kapena amene sanamizidwe kotheratu? Kodi kungakhale koyenera kuwabatizanso? Nkhani yofotokozedwa pa Machitidwe 19:1-7 imatithandiza kuyankha mafunso ameneŵa. Mwinamwake munali mkati mwa nyengo yozizira ya 52/53 C.E. pamene mtumwi Paulo anakayenda mumzinda wachuma wa Efeso mu Asia Minor. Kumeneko iye anapezako ophunzira amene anafunikira kubatizidwanso. Atadziŵa kuti anthu ameneŵa anali atabatizidwa ndi ubatizo wa Yohane, Paulo anawabatizanso “m’dzina la Ambuye Yesu.” Iye sanalingalire kuti kuchita motero kukakwiyitsa Mulungu. Mwachionekere, Mulungu anavomerezana ndi kalingaliridwe ka Paulo, ndipo mmalo mwa kukwiya ndi kubatizanso kumeneku, Mulungu anakuvomereza ndi mphatso ya mzimu woyera.
Ngati amuna 12 amenewo akanakana chiphunzitso cha Paulo ponena za m’mkhalidwe wa ubatizo ndi kufunika kwa Mesiya, Kristu Yesu, mosakayikira Paulo sakanachita ubatizowo. Choyamba, amunawo anafunikira kuyenerera ubatizo. Mpokhapo pamene akanabatizidwanso movomerezedwa ndi Mulungu.
Mmene Munthu Amayenerera Ubatizo
Kodi ndimotani mmene timayenerera ubatizo? Lingalirani za khamu la anthu amene anabatizidwa patsiku la Pentekoste wa 33 C.E. Kodi iwo anauyenerera motani? Choyamba, monga Ayuda ndi otembenuzidwira ku Chiyuda, anayamba ali ndi chidziŵitso chabwino cha Yehova Mulungu, zochita zake ndi anthu ake, ndi maulosi Abaibulo onena za Mesiya wolonjezedwa. Chachiŵiri, analoŵetsa chidziŵitso cholongosoka chinanso mkati mwa umboni wouziridwa woperekedwa ndi mtumwi Petro patsikulo. Ndi chotulukapo chotani?
“Pakumva izi, analaswa mtima nati kwa Petro ndi atumwi, ‘Kodi tiyenera kuchitanji, abale?’ ‘Muyenera kulapa,’ anayankha motero Petro, ‘ndipo aliyense wa inu ayenera kubatizidwa m’dzina la Yesu Kristu kaamba ka kukhululukidwa kwa machimo anu, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.’” (Machitidwe 2:37:38, JB) Onani kuti umboni wa Petro sunali wachiphamaso. “Analankhula nawo kwanthaŵi yaitali akumagwiritsira ntchito zigomeko zambiri.” Iwo anakhutiritsidwa ndi kalingaliridwe kake, ndipo anavomereza zimene ananena ndipo anabatizidwa. “Tsiku limenelo anthu pafupifupi zikwi zitatu anawonjezeredwa pachiŵerengero chawo.”—Machitidwe 2:40, 41, JB.
Zinthu zofananazo zimafunika kaamba ka ubatizo wovomerezeka mwa Malemba lerolino: (1) chidziŵitso cholongosoka, (2) kulapa kowona mtima, ndipo (3) kutembenuka, kapena kutembenukira kwa Mulungu ndi kusiyana ndi “mbadwo woluluzika.” Ndiponso, maubatizo ovomerezedwa mwa Malemba ayenera kukhala “m’dzina la Yesu Kristu,” ndiko kuti, ozikidwa pa kuvomereza nsembe yake ya dipo ya chikhululukiro cha machimo ndi kumgonjera monga mfumu yoikidwa pampando wachifumu ya Mulungu.—Machitidwe 2:40, JB; Aroma 5:12-19; 7:14-25.
Anthu owona mtima amene ali oyenerera mwa Malemba kaamba ka ubatizo safunikira kuopa kuti mwa kubatizidwanso adzakwiyitsa Mulungu. Mosiyana ndi zimenezo, ubatizo woyenera mwa Malemba wa anthu oyenerera umasangalatsa Mulungu.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka, onani nkhani yakuti “Ubatizo—Kodi Ngwamakanda?” m’kope la Awake! la October 8, 1986.