Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 3/8 tsamba 4-7
  • Kuthandiza Anthu Kuŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthandiza Anthu Kuŵerenga
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusoŵa Mpata
  • Kufotokoza Mkhalidwe wa Wophunzira Wachikulire
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Yang’anirani ‘Luso Lanu la Kuphunzitsa’
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 3/8 tsamba 4-7

Kuthandiza Anthu Kuŵerenga

KODI mamiliyoni ameneŵa amene sangathe kuŵerenga kapena kulemba ndani? Ambiri ali nzika zamathayo zogwira ntchito molimba. M’maiko osatukuka, zimapezera chakudya, zovala, ndi nyumba unyinji wa anthu. M’maiko otukuka, zimagwira ntchito imene palibe aliyense amafuna kuichita—ntchito zimene zili zotopetsa, zobwerezabwereza, ndi zotsika, komabe zofunika m’chitaganya.

Kaŵirikaŵiri, kusoŵa mpata ndiko chifukwa chimene anthu samapezera maluso a kuŵerenga ndi kulemba. Monga gulu, osaphunzira sianthu opusa, opulukira, kapena osakhoza. “Ndilibe vuto la kuganiza,” wongoyamba kuphunzira wina anatero. “Vuto langa ndilakuŵerenga basi.”

Kusoŵa Mpata

Kwa ambiri, kusaphunzira nkogwirizana ndi umphaŵi. M’banja, umphaŵi umatanthauza kuti nkhaŵa yaikulu imene anthu amakhala nayo ndikupeza chakudya kuposa kupeza maphunziro. Pamene ana afunikira kugwira ntchito panyumba, samapita kusukulu. Ambiri amene amapitako samapitiriza.

Umphaŵi umavulazanso dziko. Maiko osatukuka amene ali ndi ngongole zochuluka zakunja kwa dziko amakakamizika kuchepetsa ndalama za maphunziro. Mwachitsanzo, mu Afrika, ndalama zonse za maphunziro zinachepetsedwa ndi pafupifupi 30 peresenti mkati mwa theka loyamba la ma 1980. Pamene kuli kwakuti maiko olemera amawononga ndalama zoposa $6,000 pachaka pamwana wawo mmodzi aliyense wasukulu, maiko ena osauka mu Afrika ndi South Asia amangowononga $2. Chotulukapo chimakhala masukulu ndi aphunzitsi oŵerengeka ndi ana ochulukitsitsa.

Nkhondo ndi zipolowe nazonso zimachititsa kusaphunzira. United Nations Children’s Fund ikuyerekezera kuti ana mamiliyoni asanu ndi aŵiri akukhala m’misasa ya othaŵa, kumene kaŵirikaŵiri masukulu ali osakwanira. M’dziko limodzi lokha la mu Afrika, ana mamiliyoni 1.2 osakwanitsa zaka 15 zakubadwa sanapite kusukulu chifukwa cha nkhondo yachiweniweni yosautsa.

Awo amene amasoŵa mpata paubwana nthaŵi zina amakhala ndi mpata wa kuphunzira kuŵerenga ndi kulemba pambuyo pake m’moyo, koma sionse amene amakuona kukhala kofunikira kuyesayesa. Ponena za osaphunzira akumidzi, buku lakuti Adult Education for Developing Countries limati: “Wachikulire amene wapambana kuchita zinthu m’moyo popanda kuŵerenga ndi kulemba sangakhoze, kusiyapo m’mikhalidwe yapadera, kukhala ndi chikumbo chachikulu cha kuŵerenga ndi kulemba. . . . Pamene kuli kwakuti kunena kuti iye ali wokhutira kotheratu ndi mkhalidwe wake kungakhale bodza lenileni, iye sangakhale wokhutira kwambiri kwakuti angafune kuchita zochuluka kuti ausinthe.”

Komabe, ambiri ali ndi chikhumbo champhamvu cha kudziwongolera. Ndithudi, zolinga zimasiyana. Ena amangofuna kuwongolera maphunziro awo ndi ulemu waumwini. Ena amasonkhezeredwa ndi mkhalidwe wa zandalama. Awo amene samagwira ntchito amaganiza kuti kuphunzira kudzawathandiza kupeza ntchito; awo amene amagwira ntchito angafune ina yabwinopo.

Pozindikira kugwirizana kwakukulu pakati pa kuphunzira ndi chitukuko cha munthu payekha ndi cha dziko, maboma ndi magulu ayamba maprogramu a kuphunzitsa achikulire kuŵerenga ndi kulemba. Imeneyi ndintchito yovuta imene imafuna aphunzitsi kukhala achifundo limodzi ndi kumvetsetsa mikhalidwe yapadera ya wophunzira wachikulire.

Kufotokoza Mkhalidwe wa Wophunzira Wachikulire

Awo amene amaphunzitsa achikulire ayenera kuzindikira kusiyana pakati pa ophunzira achikulire ndi ophunzira achichepere. Umunthu, zizoloŵezi, mikhalidwe, ndi zokonda zili zozika mizu kwambiri mwa achikulire kuposa mwa ana, zikumachititsa achikulire kukhala oumirapo ndi osafuna kwenikweni kusintha. Komabe, achikulire ali ndi chidziŵitso chochuluka monga maziko ndipo akhoza kuzindikira bwino lomwe maumboni ndi ziphunzitso zimene zingasokoneze achichepere. Kaŵirikaŵiri samakhala ndi nthaŵi yochuluka ya kupanda zochita yonga imene ana ali nayo. Kusiyana kwina kofunika kwambiri nkwakuti ophunzira achikulire, mosiyana ndi ana, ali ndi ufulu wa kuleka maphunziro awo nthaŵi iliyonse.

Achikulire ambiri osaphunzira ali ndi maluso apadera ndipo apambana m’mbali zina za moyo; iwo sanakulitse maluso akuŵerenga ndi kulemba basi. Mphunzitsi wawo afunikira kuwalimbikitsa kugwiritsira ntchito mkhalidwe wakusinthika, luso la kupanga zinthu, ndi chipiriro zimene asonyeza m’mbali zina za moyo.

Pamafunikira kulimba mtima kwa wosaphunzira kuvomereza zosoŵa zake ndi kupempha chithandizo. Ngakhale kuti mikhalidwe ndi anthu omwe amasiyana, achikulire ambiri amachita maphunziro a kuŵerenga ndi kulemba mwamantha ndi mosoŵa chidaliro. Ena angakhale ndi mbiri yaitali ya kulephera m’maphunziro. Ena angaganize kuti akalamba kwambiri moti sakhoza kuphunzira zinthu zatsopano. “Nkovuta kuphunzira kugwiritsira ntchito dzanja lamanzere paukalamba,” umatero mwambi wa ku Nigeria.

Aphunzitsi angakulitse chidaliro ndi kuchirikiza chikondwerero mwa kufulumira kuona ndi kuyamikira kupita kwawo patsogolo. Maphunziro ayenera kulinganizidwa m’njira yakuti achepetse kulephera pamaphunziro ndi kutsimikiziritsa chipambano chobwerezabwereza chomapitiriza cha zonulirapo za maphunziro. Chofalitsidwa chakuti Educating the Adult chimati: “Chofunika koposa, chipambano mwinamwake ndicho chinthu chimodzi chachikulu chochititsa chisonkhezerocho kupitiriza.”

Kaŵirikaŵiri achikulire amadziŵa zimene afuna m’maphunziro ndipo amafuna kuona kuti akupita patsogolo mwamsanga kulinga ku zonulirapo zawo. Profesa wina wa maphunziro a achikulire mu Afrika anati: “Amafuna kuloŵa m’kalasi, kuphunzira zimene afuna kudziŵa mwamsanga monga momwe kungathekere, ndiyeno kutuluka.”

Nthaŵi zina zonulirapo zimene wophunzira amadziikira zimakhala zopambanitsa. Kuyambira pachiyambi mphunzitsi ayenera kuthandiza wophunzira kukhazikitsa zonulirapo zotsatizana zakanthaŵi, ndiyeno kuthandiza wophunzira kuzifikira. Mwachitsanzo, tinene kuti Mkristu wina walembetsa m’kalasi lakuphunzira kuŵerenga ndi kulemba chifukwa chakuti akufuna kudziŵa kuŵerenga Baibulo ndi zofalitsidwa zofotokoza Baibulo. Zonulirapo zimenezi zimatenga nthaŵi yaitali. Pozikalimira, mphunzitsi angalimbikitse wophunzirayo kukhazikitsa zonulirapo zotsatizana zakanthaŵi, zonga kudziŵa zilembo za alifabeti, kupeza ndi kuŵerenga malemba osankhidwa, ndi kuŵerenga mabuku osavuta ofotokoza Baibulo. Kufikira zonulirapozo nthaŵi ndi nthaŵi kumachirikiza chikhumbo ndi kusonkhezera wophunzira kupitirizabe kuphunzira.

Aphunzitsi ogwira mtima angachite zochuluka kusonkhezera chikhumbocho mwa kulimbikitsa ndi kuyamikira ophunzira awo ndi mwa kuwathandiza kukalimira zonulirapo zopindulitsa ndi zofikirika. Komabe, kuti apite patsogolo, achikulire sayenera kuyembekezera kumangothandizidwa. Afunikira kukhala ofunitsitsa kusenza thayo la maphunziro awo ndi kulimbikira pakuphunzira. Mwa kuchita zimenezo, adzadziŵa kuŵerenga ndi kulemba, ndipo maluso ameneŵa adzasintha miyoyo yawo.

[Bokosi patsamba 6]

Zitsogozo Zophunzitsira Achikulire Kuŵerenga ndi Kulemba

1. Nkofunika kusonkhezera chikhumbo mwa wophunzira. Kuyambira pachigawo choyamba, gogomezerani mapindu a kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba, ndi kulimbikitsa wophunzira kuika zonulirapo zoyenera zotenga nthaŵi yaitali ndi zakanthaŵi.

2. Kuti apite patsogolo wophunzirayo ayenera kuphunzitsidwa nthaŵi zingapo pamlungu umodzi. Kamodzi pamlungu sikokwanira. Wophunzira ayenera kumachita homuweki asanayambe phunziro lotsatira.

3. Musafune zopambanitsa kapena kupatsa wophunzirayo zinthu zochuluka kopambana pachigawo chimodzi. Zimenezi zingamchititse kukhala wolefulidwa ndi kuleka kupezeka m’kalasi.

4. Khalani wolimbikitsa ndi womangirira nthaŵi zonse. Maluso a kuŵerenga ndi kulemba amakulitsidwa mwapang’onopang’ono. Wophunzira ayenera kukhutira ndi kupita patsogolo kwake.

5. Limbikitsani wophunzirayo kugwiritsira ntchito mwamsanga monga momwe kungathekere zimene akuphunzira m’moyo wake wa tsiku ndi tsiku.

6. Musatayire nthaŵi pankhani zina. Achikulire ndianthu otanganitsidwa. Gwiritsirani ntchito bwino magawo akuphunzira kuphunzitsira zinthu zofunika.

7. Nthaŵi zonse khalani waulemu kwa wophunzira, mukumampatsa ulemu umene amayenerera. Musamnyazitse kapena kumchepsa.

8. Zindikirani mavuto aumwini. Wophunzira angakhale wosakhoza kuŵerenga zilembo zazing’ono chifukwa chakuti afunikira magalasi. Wina angakhale ndi vuto la kusamva bwino ndipo motero ambiri amavutika kumva matchulidwe olondola a mawu.

9. Wophunzira ayenera kuphunzira kulemba (mosindikiza) zilembo za alifabeti asanayambe kulemba chikhukhuza (kalembedwe kolumikiza zilembo). Kulemba mosindikiza nkosavuta kuphunzira ndipo nkosavuta kukuchita, ndiponso zilembo zake zimafanana kwambiri ndi zija zosindikizidwa pamasamba.

10. Njira yabwino yophunzitsira kulemba zilembo ndiyo ya kulola wophunzira kujambula mwa kuyang’ana pachitsanzo. Angajambule chilembocho kangapo asanayese kuchilemba popanda kutsanzira zina.

11. Kaŵirikaŵiri kupita patsogolo m’kuŵerenga kumachitika mofulumira kuposa kupita patsogolo m’kulemba. Musazengereze kuyambitsa maphunziro atsopano oŵerenga ngati wophunzirayo sakhoza kuchita homuweki mwa kulemba. Komabe, kumbukirani kuti zilembo zatsopano zimaphunziridwa ndi kukumbukiridwa mosavuta ngati wophunzira akuyesa kuzilemba.

12. Ngakhale kuti wophunzira wachikulire angakhoze kuchita ntchito yocholowana ndi manja ake, kulemba ndi peni kapena pensulo kungakhale chokumana nacho chovuta ndi chogwiritsa mwala kwa iye. Musaumirire zilembo zolembedwa bwino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena