Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 3/8 tsamba 3-4
  • Kusaphunzira Vuto la Dziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusaphunzira Vuto la Dziko Lonse
  • Galamukani!—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu
    Galamukani!—1994
  • Amai ndi Atate Ali Osaphunzira Kodi Ndingawalemekeze Bwanji?
    Galamukani!—1990
  • Kuthandiza Anthu Kuŵerenga
    Galamukani!—1994
  • Mmene Mawu Anakhalira Malemba Opatulika Kulemba M’nthawi ya Atumwi
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 3/8 tsamba 3-4

Kusaphunzira Vuto la Dziko Lonse

Ndi mtolankhani wa Galamukani! ku Nigeria

ALMAZ amakhala ku Ethiopia. Pamene mwana wake wamkazi anadwala, dokotala anamlembera botolo la mankhwala. Koma Almaz sanakhoze kuŵerenga mlingo wake wolondola—kodi ndimankhwala ochuluka motani amene anayenera kupatsa mwana wake, ndipo panthaŵi iti? Mwamwaŵi, mnansi wake anakhoza kuŵerenga zimene zinalembedwapo. Mankhwalawo anaperekedwa moyenerera, ndipo mwanayo anachira.

Ramu ndimlimi ku India. Pamene nthaŵi inafika yakuti mwana wake wamkazi akwatiwe, iye anasankha kubwereketsa munda wake kuti apeze ndalama kwa munthu wokongoletsa ndalama wakomweko. Popeza kuti anali wosakhoza kuŵerenga kapena kulemba, anagwiritsira ntchito chala chake chamanthu kusainira chikalata chimene sanamvetsetse. Pambuyo pa miyezi ingapo Ramu anapeza kuti chikalatacho chinali pangano la kugulitsa—munda wake tsopano unakhala wa munthu wina.

Michael amagwira ntchito pafamu yaikulu ku United States. Kapitawo wake anamuuza kupatsa ng’ombe zakudya zowonjezereka. Michael anapeza matumba aŵiri m’nkhokwe, koma sanakhoze kuŵerenga zimene zinalembedwapo. Anasankha lolakwika. Patapita masiku angapo, ng’ombezo zinafa. Michael anazidyetsa poizoni. Pomwepo anachotsedwa ntchito.

Kusaphunzira—kusakhoza kuŵerenga ndi kulemba—kunatayitsa Michael ntchito yake. Kunatayitsa womlemba ntchito gulu la ng’ombe za nyama yabwino. Kunatayitsa Ramu munda wake. Kukanatayitsa Almaz mwana wake.

Malinga ndi kunena kwa bungwe la UNESCO (United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization), anthu oposa chigawo chimodzi mwa zinayi cha anthu achikulire padziko—amuna ndi akazi oposa mamiliyoni 960—sangathe kuŵerenga kapena kulemba.a M’maiko osatukuka, wachikulire 1 pa 3 alionse ngwosaphunzira. Mofanana ndi Almaz, Ramu, ndi Michael, mamiliyoni ameneŵa sakhoza kuŵerenga chikwangwani cha msewu, nyuzipepala, kapena ndime ya m’Baibulo. Amamanidwa chidziŵitso chochuluka chopezeka m’magazini ndi mabuku. Sakhoza kulemba kalata kapena kulemba fomu wamba. Ochuluka satha kulemba ngakhale dzina lawo lomwe. Pokhala osakhoza kuloŵa ntchito zimene zimafuna kuŵerenga ndi kulemba wamba, ambiri amakhalabe paulova, maluso awo samagwiritsiridwa ntchito, kukhoza kwawo sikumafutukulidwa.

Ziŵerengero zimenezi sizimaphatikizapo achikulire ochuluka amene ali osaphunzira kwambiri—okhoza kuŵerenga ndi kulemba zinthu zofeŵa koma osakhoza kusamalira bwino lomwe ntchito zovuta kwambiri za kuŵerenga ndi kulemba za masiku onse. Mu United States mokha, achikulire osaphunzira kwambiri ali okwanira mamiliyoni 27.

Ndipo bwanji za ana? Ngakhale kuti ziŵerengero zawo zili zosakwanira, popeza kuti kufufuza sikunachitidwe m’maiko onse, United Nations Children’s Fund ikuyerekezera kuti ana ausinkhu wa kusukulu mamiliyoni 100 padziko lonse sadzaloŵa konse m’kalasi. Enanso mamiliyoni 100 sadzamaliza ngakhale maphunziro wamba. Kwenikweni, Department of Public Information ya UN ikunena kuti m’madera akumidzi a maiko osatukuka, theka la ana ndilo lokha limene limachita zaka zoposa zinayi za maphunziro a pulaimale. Ndipo m’maiko ena otukuka, ana ambiri amathera nthaŵi yochuluka akuonerera wailesi yakanema kuposa imene amathera kusukulu.

Kaŵirikaŵiri ana osaphunzira amadzakhala achikulire osaphunzira. Kodi nchiyani chimene chimachititsa vuto la dziko lonse limeneli? Kodi nchiyani chimene chingachitidwe kuthandiza wachikulire amene sangathe kuŵerenga kapena kulemba? Mafunso ameneŵa adzapendedwa m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Malinga ndi kumasulira kwa UNESCO, munthu wosaphunzira ndiamene ali ndi zaka 15 kapena kuposapo amene sakhoza kuŵerenga kapena kulemba mozindikira mawu wamba, aafupi onena za moyo wake.

[Chithunzi patsamba 3]

Anthu oposa chigawo chimodzi mwa zinayi cha anthu achikulire padziko satha kuŵerenga kapena kulemba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena