Kodi Nyengo Yatsopano Yeniyeni Idzabwera Motani?
WOYAMBITSA wa gulu la Nyengo Yatsopano Shirley MacLaine analongosola lingaliro lofala kwambiri pamene analemba kuti: “Ndimadzipeza ndikulingalira mwamphamvu za chimene chinalikulakwika m’dziko. Sungathe kupeŵa zimenezo pamene uonadi umphaŵi, njala, ndi udani. Ndinayamba kuyendayenda pamene ndinali ndi zaka khumi ndi zisanu ndi zinayi, ndipo tsopano, pamsinkhu wa zaka za pakati pa makumi anayi, ndinganene motsimikiza kuti zinthu zakhala zikunyonyotsoka.”
Mofananamo, anthu kulikonse atopa ndi chinyengo cha chipembedzo ndi mabodza. Amakwiyitsidwa ndi kulekerera ndi kulephera kwa maboma. Amachita mantha ndi mikhalidwe yosasamala imene amaona ndi kulakwa kwa malo azamankhwala. Ndipo ambiri anavutitsidwa ndi osankhana mafuko kapena kusankhidwa chifukwa chokhala akazi kapena amuna ndi kudzikweza.
Yankho Lotsimikizirika?
Palibe kukayikira kulikonse, ife tilifunikiradi dziko latsopano. Koma kodi ziyembekezo za gulu la Nyengo Yatsopano nzotsimikizirika? Kapena kodi kuyerekezera kwake kwa mtsogolo kumafanana ndi akanema a science-fiction a ku Hollywood? Kodi zimaoneka kukhala zanzeru kuika chikhulupiriro m’maulosi ozikidwa pa miyambo yoiwalika, nthano zamakedzana, ndi malingaliro?
Zowona, malingaliro ambiri amene anatengedwa ndi gulu la Nyengo Yatsopano angachirikize ubwino wamaganizo ndi wakuthupi m’njira yochepa. Kadyedwe kabwino, maseŵera olimbitsa thupi, kupumula, ndi kudera nkhaŵa malo okhala zonsezo zili mbali zabwino za moyo. Mwinamwake akatswiri a zamankhwala akanakhala ndi chipambano chabwinopo ngati akanapereka chisamaliro chokulira ku zosoŵa za maganizo za odwala pochiritsa matenda awo akuthupi. Koma m’kupita kwa nthaŵi aliyense amadwala, ndipo ngakhale anthu athanzi labwino kopambana potsirizira pake amafa. Sitingathe kusangalala kotheratu ndi moyo ndi chiyembekezo cha kudwala ndi imfa zikumatiwopseza. Kodi aphunzitsi a Nyengo Yatsopano amapereka yankho lokhutiritsa la mavuto ameneŵa?
Anthu omawonjezereka ali achisoni ndi ochita tondovi, ndipo gulu la Nyengo Yatsopano lingachite zochepa kwambiri pa mkhalidwewo. International Herald Tribune ya ku London inati: “Ngati zaka za zana la 20 zinayambitsa Nyengo ya Kuda Nkhaŵa, kutha kwake kudzachititsa kuyambika kwa Nyengo ya Kuchita Tondovi.” Nyuzipepalayo inawonjezera kuti “kupenda koyamba kwa mitundu yonse kwa kuchita tondovi kwakukulu kukuvumbula kukwera kosalekeza kwa kupanda dongosolo kwa padziko lonse.”
Gulu la Nyengo Yatsopano, ndi malingaliro ake oonekera ngati achipembedzo, silimakhutiritsa kwenikweni chosoŵa chauzimu cha chitaganya chamakono. Ngakhale m’mikhalidwe yabwino kwambiri, mpumulo wauzimu wolingaliridwawo umene gululo limapereka umakhala wakanthaŵi. Zowona, chipembedzo chokhazikika, makamaka Dziko Lachikristu, sichinapereke mpumulo ku njala yauzimu yofala. Nyuzipepala ina inatsutsa mwapoyera “kulephera kwa Tchalitchi kuyesa kuthandiza awo odziona kukhala opatulidwa, osakhudzidwa, osakondedwa.” Nyuzipepalayo inafotokoza chipembedzo chamakono kukhala chosatonthoza, “cholanda munthuyo lingaliro lililonse la kudziŵa Mulungu mwachindunji.”
Baibulo—Buku la Mayankho
Dziko Lachikristu laipitsa ndi kusukulutsa mphamvu ya chowonadi cha Baibulo. Mofananamo, ziphunzitso zambiri za Nyengo Yatsopano nzosemphananso ndi ziphunzitso za Baibulo. Mwachitsanzo, talingalirani za lingaliro la Nyengo Yatsopano lakuti anthu akhoza kuthetsa mavuto a dziko lapansi. Baibulo limanena momvekera bwino pa Yeremiya 10:23 kuti: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Lemba lina limati: “Chipulumutso ncha Yehova.”—Salmo 3:8.
Baibulo silimaphunzitsa kuti anthu ali ndi moyo wosafa umene umakhalabe ndi moyo paokha, wopatuka ku thupi. Malinga ndi kunena kwa Malemba, moyo umafa, ndipo imfa ndiyo mapeto a kulingalira ndi ntchito zonse. (Numeri 23:10; 35:11; Mlaliki 9:5, 10) Zimenezi zimatsutsa momvekera bwino lingaliro la Nyengo Yatsopano la kuvala thupi lanyama.
Ndiponso, nkosatheka kulankhula ndi akufa. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, konenedwa kukhala kulankhula ndi akufa kulikonse kwenikweni kuli kulankhula ndi ziŵanda—adani auzimu a Mulungu ndi anthu. Chotero, Lamulo la Mulungu linachititsa kulankhula ndi mizimu, kuphatikizapo mtundu uliwonse wa kubwebweta, kupenda nyenyezi, ndi kulankhula ndi obwebweta, kukhala tchimo loyenerera chilango cha imfa.—Levitiko 19:31; 20:6, 27; Deuteronomo 18:10-12.
Baibulo ndilo magwero a kuchiritsa kowona kwauzimu. Lili ndi mpambo wa ziphunzitso zimene zimathandiza Akristu kumvetsetsa khalidwe lawo ndi kusintha umunthu wawo. (Aroma 12:2; 2 Akorinto 13:5; Aefeso 4:21-24) Limaphunzitsa kudzilanga, kulama maganizo, kudzilemekeza ndi kulemekeza ena.
Baibulo limatigwirizanitsa ndi munthu wapamwamba koposa m’chilengedwe chonse, Mlengi wathu. (Machitidwe 17:24-28) Limasonyeza kuti mwa kusonyeza chikhulupiriro m’nsembe yadipo ya Mwana wake, anthu angapeze moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Aroma 6:23) Limapereka mayankho okhutiritsa a mafunso onga akuti: Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola kuvutika kwakukulu motere? Kodi ndani amene ali anthu amphamvu mmalo osaoneka? Kodi ndiwo amene amachititsa zochuluka za zimene zimatchedwa zochitika zosakhala zachilengedwe?
Ponena za mtsogolo, Baibulo limalonjeza thanzi langwiro ndi moyo wosatha ndi dziko latsopano la mtendere ndi kugwirizana, lokhala ndi malo okhala audongo, pompano padziko lapansi. (Yesaya 33:24; 2 Petro 3:13) M’dziko latsopano limenelo, mosakayikira anthu adzawonjezera chidziŵitso chawo ndipo, motsogozedwa ndi Mulungu, adzavumbula zinsinsi zambiri zonena za thupi la munthu, pulaneti lathu, ndi chilengedwe chonse. Zonsezi zidzakwaniritsidwa ndi mphamvu ya Yehova, Mulungu amene amakonda anthu.
Kodi Mudzakhalamo?
Komabe, Baibulo limaphunzitsanso kuti madalitso ameneŵa adzaperekedwa kokha kwa awo amene amakhala mogwirizana ndi malamulo a Mulungu. Malamulo ameneŵa sali otsendereza. Koma ayenera kumveredwa. (Miyambo 4:18, 19; 1 Yohane 5:3) Nkosatheka kuvomereza lingaliro losakhala lamalemba la Nyengo Yatsopano ndipo panthaŵi imodzimodziyo kukhulupirira Baibulo.—1 Akorinto 3:18-20; 10:18-22; Yakobo 4:4.
Chotero, Akristu enieni amapeŵa kugwidwa ndi kulingalira kosakhala kwamalemba kwa gulu la Nyengo Yatsopano. Kuganiza bwino ndi kulingalira nzofunika. Tiyenera kudziŵa kuti, chizindikiro cha “Nyengo Yatsopano” chafikira pakugwiritsiridwa ntchito mofala pa zinthu zimene sizinayambitsidwe ndi gulu la Nyengo Yatsopano ndi zimene kwenikweni sizili zosakhala za malemba. Zimenezi nzowona makamaka m’mbali za thanzi, kadyedwe, luso, ndi nyimbo. Chotero Akristu ayenera kusonyeza kuzindikira ndi kupenda mwaluntha pamene akutsimikizira kutalikirana ndi chilichonse chotsutsidwa ndi Baibulo. Moyenerera, lemba la Miyambo 14:15 mwanzeru limalangiza kuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”
Inde, Baibulo ndilo mfungulo ya kuunikiridwa kowona. Kunyalanyaza Malemba kwa okhulupirira Nyengo Yatsopano kungangobweretsa mdima wowonjezereka m’dziko. Koma Baibulo limapereka kuunika kwauzimu ndi chiyembekezo cha dziko latsopano monga momwe lalonjezeredwa ndi Mulungu kuti: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pampando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi owona.”—Chivumbulutso 21:3-5.