Lingaliro la Baibulo
Chithandizo cha Chisoni Chanu
“CHISONI CHIMACHITITSA TONSEFE KUKHALANSO ANA—CHIMATHETSA KUSIYANA KONSE KWA LUNTHA. ANZERU KOPOSA SAMADZIŴA KALIKONSE.”—RALPH WALDO EMERSON, WANDAKATULO NDI WOLEMBA NKHANI WA KU AMERICA WA M’ZAKA ZA ZANA LA 19.
MBOLA ya imfa simangopweteka chabe koma imathetsanso nzeru otsala—mwamuna, mkazi, atate, amayi, mwana wamwamuna, mwana wamkazi, kapena bwenzi. Anzeru angafunse mafunso koma osapeza mayankho otonthoza, ndipo olimba angalire chifukwa cha chisoni chachikulu koma osapeza chitonthozo. Oŵerenga Baibulo angakumbukire za kulira kwakukulu kwa Davide pamene Abisalomu wopanduka anaphedwa: “Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!” (2 Samueli 18:33) Kulira kwa mfumuku sikunali kaamba ka mdyera kuŵiri; kunali kulira kwa atate kaamba ka mwana wake wakufa. Mwina nanunso munadzimva mofananamo pamene munaferedwa.
Panthaŵi ya chisoni chachikulu, mafunso osautsa angabwere m’maganizo. ‘Kodi nchifukwa ninji zinachitika? Kodi Mulungu anadziŵa kuti zimenezi zidzachitika? Ngati anadziŵa, nchifukwa ninji sanaziletse?’ Ngakhale ngati munthu angakhale wodziŵa bwino Baibulo ndi kudziŵa kuti akufa adzaukitsidwa, mafunso ovutitsa angafune kusinkhasinkha kwakuya kuti munthu apeze chitonthozo ndi mpumulo.
Mayankho olakwika samadzetsa chikhutiro chenicheni, amangodzetsa chitonthozo chonyenga. Kaŵirikaŵiri kuuzidwa kuti ‘Mulungu anafuna wokondedwa wanu’ kumachititsa kufufunuka kwa Mulungu moipidwa. Chowonadi, chimene chili m’Baibulo, chimayankha mafunso onena za chisoni ndipo chimayandikitsa munthu kwa Yehova Mulungu, mmalo mwa kumchotsako. Timalimbitsidwa mtima pa 2 Akorinto 1:3, 4 kuti iye ndi Atate a zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.
Nzeru ndi Mphamvu za Mulungu Zili Zolinganizika
Yehova, Wamphamvuyonse, amadziŵa zonse zimene zimachitika m’chilengedwe chake chachikulukulucho. Salmo 11:4 limatitsimikiziritsa kuti: “Yehova, mpando wachifumu wake uli m’mwamba. Apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.” Pa Ahebri 4:13 mtumwi Paulo analemba kuti: “Palibe cholengedwa chosaonekera pamaso pake.” Mulungu samangodziŵa chabe komanso amasamala! Yesu anati: “Kodi mpheta ziŵiri sizigulidwa kakobiri? ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu [kudziŵa, NW]. . . . Inu mupambana mpheta zambiri.”—Mateyu 10:29, 31.
Kodi Mulungu akanaletsa imfa yosayembekezera ya wokondedwa ndi chisoni chimene chinatsatirapo? Inde, akanatero. “Zinthu zonse zitheka ndi Mulungu,” Yesu anatero. (Marko 10:27) Kalekale, Yehova anamvera pemphero la Hezekiya amene anali kufa ndi kumchiritsa nawonjezera zaka za moyo wake. (Yesaya 38:2-5) Palibe chikayikiro chilichonse ponena za kukhoza kwa Yehova kuchita chimene afuna, koma tiyenera kumvetsetsa zowonjezereka ponena za chifuniro chake. Tonsefe taŵerenga nkhani zonena za anthu amene anavulala kapena kudwala kwambiri, komabe anakhala ndi moyo. Kodi Yehova analoŵererapo kuwathandiza?
Anthu ena ali ndi mphamvu zochuluka za kuchira ndi chikhumbo champhamvu cha kukhala ndi moyo. Zimenezi zingafotokoze kuchira kwakwo kooneka ngati kozizwitsa. Kapena mankhwala atsopano angakhale atapambana. Chotero, sitiyenera kunena kamodzi nkamodzi kuti Yehova analoŵererapo.—Afilipi 4:13.
Mawu a Mulungu Amafotokoza Chifukwa Chimene Anthu Amafera
Pa Aroma 5:12, mtumwi Paulo amafotokoza mosavuta konse kuti kholo lathu Adamu linapandukira Mlengi wake ndipo moyenerera linaweruzidwa kufa. Popeza tili mbadwa zake, ndife ochimwa ndipo tikhoza kufa nthaŵi iliyonse. Tilibe chitsimikizo cha kupitirizabe kukhala ndi moyo. Mfumu yanzeruyo Solomo wakale amakumveketsa bwino kuti nthaŵi ndi zochitika zosaonedweratu zingafikire aliyense panthaŵi iliyonse, kaya zikhale ngozi yakupha kapena nthenda yosachiritsika yamwadzidzidzi. Kapena wina angabadwe ndi chirema chimene chimafupikitsa moyo wake. Ndiponso Solomo akufotokoza kuti Mulungu ali ndi nthaŵi ndi nyengo ya zonse. Mulungu wakhazikitsa nthaŵi yakuchiritsa, osati munthu mmodzi kapena angapo, koma anthu onse okhulupirira mkati mwa ulamuliro wa Kristu Yesu.—Mlaliki 3:1; 9:11; 1 Akorinto 15:25, 26.
Kumbukirani lingaliro losonkhezera maganizo ili: Akristu sali opatulidwa pa masoka okantha fuko la anthu ndipo chotero amakumana ndi zinthu zimene zimagwera anthu onse. “Mayeso amene mufunikira kupirira saposa amene anthu akhala nawo nthaŵi zonse.”—1 Akorinto 10:13, The Jerusalem Bible.
Mmene Mungachirire
Nthaŵi ya imfa ndinthaŵi yogwetsa misozi limodzi ndi kuchonderera Yehova, Wakumva pemphero, mowona mtima. Tsopano koposa ndi kalelonse, yandikirani kwambiri kwa Mulungu. Tsopano koposa ndi kalelonse, tsegulani mtima wanu m’pembedzero kupempha chidziŵitso, ndi nyonga yakuti musinthe. Baibulo limatilimbikitsa kuchita zimenezo kumene. Petro akuti: ‘Tayani pa iye nkhaŵa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.’ (1 Petro 5:7) Mmene mawu a Mulungu pa Yesaya 57:15 alili otonthoza nanga: “Atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m’malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa.” Wamzimu wosweka amamamatira kwa Atate; pamakhala unansi wolimbirapo kuposa ndi kalelonse. “Pamene muyandikira kwambiri kwa Mulungu, mpamenenso iye adzayandikira kwambiri kwa inu,” akulemba motero Yakobo. (Yakobo 4:8, JB) Yakobo akutitsimikiziritsa kuti Mulungu ali wofunitsitsa kutipatsa nzeru ndi nyonga zofunikira kuti tichire.
Ndiponso, mudzaona kuti mudzakhala munthu wachifundo kwambiri, wokoma mtima kwambiri, ponena za ziyeso ndi masoka a ena. Mudzadziŵa zambiri ponena za mmene anthu ena amamvera ndi mmene mungawauzire mawu otonthoza ndi opatsa chiyembekezo. Mungakhoze kuthandiza munthu wachisoni kupirira chisoni chake. Inde, mudzakhala ndi chifundo chokulirapo kwa ena amene ali m’nsautso.—Afilipi 2:1.
Kutayikiridwa ndi wokondedwa kumadzetsa chisoni ndipo kumapweteka kwakanthaŵi, mwinamwake kwanthaŵi yaitali. Komabe, pomalizira, kungadzetse lingaliro labwino la chiyembekezo chimene chili mtsogolo, chiyembekezo cha kutumikira Mulungu popanda zochitika zopweteka. Ndiponso umunthu wathu Wachikristu ungakhale wolimba kwambiri.—1 Petro 1:6, 7.
Chotero ngakhale kuti mukupwetekedwa ndi chisoni, musagonje konse! Kukhaletu kutsimikiza mtima kwanu kupitiriza kutumikira Mulungu mokhulupirika, ku ulemerero ndi ulemu wake ndi ku chipulumutso chanu chosatha.
[Mawu a Chithunzi patsamba 29]
The Day Before Parting ndi Jozef Israels: Mphatso ya Alice N. Lincoln, Courtesy, Museum of Fine Arts, Boston