Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 4/8 tsamba 3-5
  • Zimene Akazi Ayenera Kudziŵa Ponena za Kansa ya Maŵere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Akazi Ayenera Kudziŵa Ponena za Kansa ya Maŵere
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbiri ya Banja
  • Zochititsa za Malo Okhala
  • Mbiri ya Munthu Mwini ndi Mahomoni
  • Chifukwa Chake Ali Paupandu
  • Kusintha Malo
  • Mfungulo za Kupulumuka
    Galamukani!—1994
  • Zimene Mungachite Ngati Mwapezeka ndi Khansa ya M’mawere
    Galamukani!—2011
  • Malangizo Ofunika a Kuyamwitsa Bere
    Galamukani!—1994
  • Tetezani Khungu Lanu
    Galamukani!—2005
Galamukani!—1994
g94 4/8 tsamba 3-5

Zimene Akazi Ayenera Kudziŵa Ponena za Kansa ya Maŵere

CHIŴERENGERO cha odwala kansa ya maŵere chikukwera pa kontinenti iliyonse. Malinga ndi zoyerekezera zina, podzafika chaka cha 2000, padzakhala pafupifupi odwala kansa ya maŵere atsopano miliyoni imodzi padziko lonse chaka chilichonse.

Kodi mkazi aliyense ali wotetezereka ku nthendayi? Kodi chinachake chingachitidwe kuiletsa? Ndipo kodi ndi chitonthozo ndi chichirikizo chotani chimene chimafunidwa ndi awo amene akulimbana ndi mdaniyu?

Makansa ambiri a khungu amachititsidwa ndi cheza cha dzuŵa cha ultraviolet. Makansa ambiri a mapapu amachititsidwa ndi kusuta. Koma palibe chochititsa chimodzi cha kansa ya maŵere chimene chatsimikiziridwa .

Komabe, malinga ndi kufufuza kwa posachedwapa, zinthu zokhudza majini, malo okhala, ndi mahomoni zingachititse kansa ya maŵere. Akazi amene amayang’anizana ndi zinthu zimenezi angakhale paupandu wowonjezereka.

Mbiri ya Banja

Mkazi amene ali ndi chiŵalo cha banja chokhala ndi kansa ya maŵere, monga ngati amayi, mchemwali, kapena ngakhale amayi aakulu kapena aang’ono kapena agogo akazi akuchikazi, ali ndi kuthekera kowonjezereka kwa kudwala nthendayo. Ngati angapo a iwo ali ndi nthendayi, upandu wake ngwaukulu kwambiri.

Dr. Patricia Kelly, katswiri wa majini mu United States, anauza Galamukani! kuti pamene kuli kwakuti zinthu za choloŵa zimaloŵetsedwamo, izo zingachititse kokha 5 mpaka 10 peresenti ya makansa onse a maŵere. Iye anafotokoza kuti: “Tikuganiza kuti unyinji wosadziŵika wa matendawa umachititsidwa ndi zinthu zosakhala kwenikweni zacholoŵa zikumagwirizana ndi malo okhala.” Ziŵalo zabanja zokhala ndi majini ofanana zimakondanso kukhala malo amodzi.

Zochititsa za Malo Okhala

“Mwachionekere pali zinthu zokhudza malo okhala, zimene zimalingaliridwa mofala, kuti zimaloŵetsedwamo” m’kuyambitsa nthendayi, anatero Devra Davis, katswiri amene anachitira ndemanga m’magazini a Science. Popeza kuti bere la mkazi lili chimodzi cha ziŵalo za thupi zimene zimayambukiridwa kopambana ndi mphamvu ya cheza, akazi amene amayang’anizana ndi cheza chimene chimaonjezera ma ion ali pa upandu wowonjezereka wa kudwala kansa ya maŵere. Zilinso choncho kwa akazi amene amayang’anizana ndi makemikolo a paizoni.

Chinthu china ndi zakudya. Ena amapereka lingaliro lakuti kansa ya maŵere ingakhale nthenda ya kupereŵera kwa mavitamini ndipo amatchula kusoŵa kwa vitamini D. Vitamini imeneyi imathandiza thupi kugwiritsira ntchito calcium, imene imathandiza kuletsa kansa.

Zopenda zina zimagwirizanitsa mafuta a m’zakudya, osati monga oyambitsa, koma monga ochirikiza kansa ya maŵere. Magazini a FDA Consumer ananena kuti mlingo wa imfa zochititsidwa ndi kansa ya maŵere unali wokwera m’maiko onga ngati United States, kumene amadya mafuta ndi nyama yochuluka. Magaziniwo ananena kuti: “Mwakupenda mbiri, akazi a ku Japan ali ndi upandu wotsika wakudwala kansa ya maŵere, koma upanduwo wakhala ukukwera mofulumira, pamodzi ndi kutsanzira kadyedwe ka anthu a ‘Kumadzulo’; ndiko kuti, kuleka zakudya zokhala ndi mafuta ochepa ndi kuyamba kudya zamafuta ambiri.”

Kupenda kwaposachedwa kunapereka lingaliro lakuti unyinji waukulu wa macalorie amene amadyedwa m’zakudya zamafuta ambiri ungatanthauze upandu weniweni. Science News inanena kuti: “Calorie yowonjezereka iliyonse imawonjezera upandu wa kansa ya maŵere, calorie iliyonse ya mafuta yowonjezereka imapereka pafupifupi upandu wa 67 peresenti kuposa macalorie ochokera ku zakudya zina.” Macalorie owonjezereka angawonjezere makilogalamu, ndipo akazi amene ali onenepa kwambiri amalingaliridwa kukhala pa upandu wa kansa ya maŵere woŵirikiza katatu, makamaka akazi amene analeka kukhala kumwezi. Mafuta a thupi amatulutsa estrogen, homoni ya akazi imene ingagwirire ntchito moipa pa minyewa ya bere, kuchititsa kansa.

Mbiri ya Munthu Mwini ndi Mahomoni

Mkati mwa bere la mkazi muli malo okhala mahomoni amene amachititsa masinthidwe m’berelo m’moyo wake wonse. Dr. Paul Crea, katswiri wochita opaleshoni ya zotupa, analemba mu Australian Dr Weekly kuti: “Komabe, mwa akazi ena, kuvumbulidwa kwa minyewa ya m’bere kwa nthaŵi yaitali ku kusonkhezera mahomoni . . . kudzachititsa kusintha kwa maselo kumene potsirizira pake kudzasanduka kwa malignant [kansa].” Chifukwa cha zimenezi kukulingaliridwa kuti akazi amene anayamba mwamsanga kukhala kumwezi, pofika pa msinkhu wa zaka 12, kapena amene anachedwa kuleka kukhala kumwezi, mkati mwa zaka za m’ma 50, ali ndi upandu wokwererapo.

Kuthekera kwa kugwirizanitsa maestrogen owonjezereka olandiridwa mwa ERT (estrogen replacement therapy) ndi kansa ya maŵere kwakhala kodzutsa mkangano. Pamene kuli kwakuti zopenda zina zimasonyeza kuti ERT simawonjezera upandu, zopenda zina zimasonyeza upandu waukulu kwa olandira mankhwalawo kwa nthaŵi yaitali. Polingalira za zopenda zomwe zapendedwanso, British Medical Bulletin ya 1992 inanena kuti pali kuthekera kwakuti “oestrogen yosapeŵetsa kutenga mimba ingawonjezere upandu wa kansa ya maŵere ndi 30-50%” pambuyo poigwiritsira ntchito kwa nthaŵi yaitali.

Malipoti onena za kugwirizana kwa pakati pa mankhwala akumwa opeŵetsa kutenga mimba ndi kansa ya maŵere amasonyeza upandu waung’ono m’kuwagwiritsira ntchito. Komabe, pali kagulu kakang’ono ka akazi amene ali paupandu waukulu. Akazi achichepere, akazi omwe sanabalepo ana, ndi akazi amene agwiritsira ntchito mibulu yoletsa kutenga mimba kwa nthaŵi yaitali angakhale ndi upandu waukulu wa 20 peresenti wa kukhala ndi kansa ya maŵere.

Komabe, akazi 3 mwa 4 alionse amene ali ndi kansa ya maŵere sangatchule chilichonse chachindunji chimene chinachititsa kuti adwale nthendayo. Chotero funso limafunsidwa lakuti, Kodi mkazi aliyense angadzilingalire kukhala wotetezereka ku kansa ya maŵere? FDA Consumer ikusimba kuti: “Malinga ndi lingaliro la dokotala, akazi onse ayenera kuonedwa kukhala paupandu wakudwala kansa ya maŵere.”

Chotero, akazi, makamaka okalamba, ali paupandu wakudwala nthendayi. Dr. Kelly akunena kuti pamene kuli kwakuti pali zochititsa zosiyanasiyana za kansa ya maŵere, ‘ndikulingalira kuti ina imangoyamba chifukwa cha kukalamba, ndipo kugaŵanikana kolakwika kwa maselo kumachitika.’

Chifukwa Chake Ali Paupandu

Kupenda kapangidwe ka bere la mkazi kumafotokoza chifukwa chake lili paupandu kwambiri. Mkati mwake muli mphako, ngalande zazing’ono zimene zimayendetsa mkaka kuchoka ku matumba otulutsa mkaka kupita ku nkhumbu. M’mphepete mwa mphakozo muli maselo amene amagaŵanikana ndi kusintha mosalekeza mogwirizana ndi nthaŵi ya kukhala kumwezi ya mkazi, kumkonzekeretsa kaamba ka kukhala ndi pakati, kutulutsa mkaka, ndi kuyamwitsa khanda lake. M’mphako mmenemu ndi mmene makansa ambiri a bere amachitika.

M’buku lakuti Alternatives: New Developments in the War on Breast Cancer, wofufuza Rose Kushner akulongosola kuti: “Dongosolo lokhazikika lililonse limene limasokonezedwa mosalekeza ndi zinthu zosiyanasiyana—ngakhale ngati lili lachilengedwe . . .—likhoza kukhala ndi zolakwika zazikulu.” Iye anawonjezera kunena kuti: “Selo la bere logwira ntchito mopambanitsa nthaŵi zonse limakhala m’mahomoni amene amalamula kuti, ‘Leka kuchita zimenezo. Yamba kuchita izi.’ Mposadabwitsa kuti maselo atsopano ambiri amasokonezeka.”

Kansa ya maŵere imayamba pamene selo losalingana ligaŵanikana, kulephera kulamulira kukula kwake, ndi kuyamba kuchuluka. Maselo oterowo samaleka kubalana, ndipo m’kupita kwa nthaŵi amagonjetsa minyewa yabwino yoyandikana nawo, kuchititsa chiŵalo chabwino kukhala chamatenda.

Kusintha Malo

Pamene kansa ikhala mkati mwa bere, chotupa chakansacho chingachotsedwe. Pamene kansa ya maŵere ifalikira kumbali zina za thupi, imatchedwa kansa ya maŵere yosintha malo. Chimenechi ndicho chochititsa chothekera cha imfa mwa odwala kansa ya maŵere. Pamene maselo a kansa akuwonjezeka m’bere ndipo chotupacho chikula, maselo a kansa angatuluke mwakachetechete ndi mwachinsinsi mmalo oyamba a chotupacho ndi kuloŵa m’zipupa za mitsempha ya mwazi ndi lymph nodes.

Panthaŵi imeneyi maselo a chotupacho angapite kumbali zakutali za thupi. Ngati aloŵa m’dongosolo lolimbana ndi matenda la thupi, limene limaphatikizapo maselo amene amawononga maselo oipa amene amayenda m’mwazi ndi madzi a lymph, maselo akansa ameneŵa angakute ziŵalo zofunika, monga ngati chiŵindi, mapapu, ndi ubongo. Kumeneko angachuluke ndi kufalikiranso, pambuyo pochititsa ziŵalozi kukhala ndi kansa. Pamene kusintha malo kuyamba, moyo wa mkaziyo uli pangozi.

Chotero, mfungulo ya kupulumuka ndiyo kupeza kansa ya maŵere ikungoyamba kumene, isanapeze mpata wa kufalikira. Kodi nchiyani chimene mkazi aliyense angachite kuti awongolere mwaŵi wakuipeza mwamsanga? Kodi pali chilichonse chimene chingachitidwe kuthandiza kuletsa kansa ya maŵere poyamba penipenipo?

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Akazi 3 mwa 4 alionse amene ali ndi kansa ya maŵere sangatchule chilichonse chachindunji chimene chinachititsa kuti adwale nthendayo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena