Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 4/8 tsamba 29-31
  • Kodi Kudzipha Ndiko Yankho?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kudzipha Ndiko Yankho?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Ena Amalingalira Motero
  • Nsautso ya Pabanja
  • Zopsinja Maganizo Zina
  • Kupeza Chithandizo
  • Kulimbana Nazo
  • Kudzipha—Mliri Umene Ukuwononga Achinyamata
    Galamukani!—1998
  • Kodi ndingodzipha?
    Galamukani!—2008
  • Vuto Lapadziko Lonse
    Galamukani!—2001
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amatopa Nawo Moyo?
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 4/8 tsamba 29-31

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Kudzipha Ndiko Yankho?

“Ndatopa ndi kudzuka mmaŵa uliwonse. Ndasochera. Ndili wokwiya. Mtima wanga ukupweteka. . . . Chotero ndikulingalira za kuchoka. . . . Sindikufuna kuchoka, koma ndikulingalira kuti ndiyenera kutero. . . . Ndikayang’ana kutsogolo, ndingoonako mdima ndi zopweteka.”—Kakalata ka wodzipha wazaka 21 wotchedwa Peter.a

AKATSWIRI amanena kuti achichepere ambiri ofika ku mamiliyoni aŵiri mu United States ayesa kudzipha. Mwachisoni, pafupifupi 5,000 amadziphadi pachaka. Koma kudzipha pakati pa achichepere sikuli ku United States kokha. Mu India pafupifupi achichepere 30,000 anadzipha mu 1990. M’maiko onga ngati Canada, Finland, France, Israel, Netherlands, New Zealand, Spain, Switzerland, ndi Thailand, ziŵerengero za kudzipha pakati pa achichepere zakwera kowopsa.

Bwanji ngati munthu wina ali wosautsika mothedwa nzeru ndi chisoni—kapena ngati akudzimva wopanikizika m’kupsinjika maganizo ndipo sakuona njira iliyonse yotulukiramo? Kudzipha kungaoneke kolakalakika, koma kunena zowona iko kuli chabe tsoka lopanda pake. Pambuyo pake, kumangodzetsa nsautso ndi kupweteka kwa mabwenzi ndi a banja. Chinkana kuti mtsogolo mungaoneke mwamdima chotani ndipo mavuto angaoneke aakulu chotani, kudzipha sindiko yankho.

Chifukwa Chake Ena Amalingalira Motero

Munthu wolungama Yobu anadziŵa mmene kuthedwa nzeru kunaliri. Pokhala atatayikiridwa banja lake, chuma chake, ndi thanzi lake labwino, anati: “Moyo wanga usankha kupotedwa, ndi imfa, koposa mafupa anga awa.” (Yobu 7:15) Achichepere ena lerolino alingalira mwa njira yofananayo. Mlembi wina ananena motere: “Kupsinjika maganizo . . . kumachititsa kupweteka mtima (malingaliro amphamvu a kuŵaŵa mtima ndi mantha) [zimene] zimachititsa kufuna kudzitetezera (kuyesayesa kuthaŵa kupweteka mtimako).” Chotero kudzipha ndiko njira yonyenga ya kuthaŵa kupweteka kumeneko koonekera kukhala kosapiririka.

Kodi nchiyani chimachititsa kupweteka koteroko? Kungayambitsidwe ndi chochitika china, monga ngati mkangano wolalatirana ndi makolo, bwenzi lachimuna, kapena bwenzi lachikazi. Atathetsa chibwenzi ndi mtsikana wake, Brad, wazaka 16 anayamba kukhala wothedwa nzeru. Komabe, sanalankhule za malingaliro akewo. Iye anangodzipha mwa kudzimangirira.

Sunita wa zaka 19 anachita tondovi pamene makolo ake anadziŵa kuti iye ankachita chisembwere ndi bwenzi lake lachimuna. “Ndinadziŵa kuti sindinafune kupitiriza kukhala mmene ndinkachitira,” iye akukumbukira tero. “Motero ndinangofika panyumba usiku wina, ndi kuyamba kumeza mibulu ya asipilini. Mmaŵa mwake ndinali kusanza mwazi. Si moyo wanga umene ndinafuna kuthetsa koma njira ya moyo wanga.”

Sukulu ingakhalenso chochititsa kupanikizika kwakukulu. Pokakamizidwa ndi makolo ake kukhala dokotala (makolowo anali madokotala), Ashish wachichepere anakhala ndi vuto la kusapeza tulo nayamba kudzipatula kwa ena. Polephera kukwaniritsa ziyembekezo za makolo ake, Ashish anamwa mibulu yogoneka yopambana pamlingo wake. Izi zimakumbutsa za Miyambo 15:13 m’Baibulo pamene pamati: “Moyo umasweka ndi zoŵaŵa za m’mtima.”

Nsautso ya Pabanja

Vuto la pabanja—monga ngati chisudzulo cha makolo kapena kulekana, imfa ya chiŵalo cha banja, kapena kusamukira kumalo ena—zili zinthu zina zochititsa achichepere ena kudzipha. Mwachitsanzo, Brad wotchulidwa kaleyo, anatayikiridwa ndi mabwenzi apamtima aŵiri ndi wachibale wake m’ngozi yagalimoto. Ndiyeno banja lawo linayamba kukhala ndi mavuto a ndalama. Brad anathedwa nzeru kotheratu. Angakhale anamva monga momwe anachitira wamasalmo yemwe anadandaula kuti: “[Moyo, NW] wanga wadzala nawo mavuto . . . Zinandizinga pamodzi.”—Salmo 88:3, 17.

Ziŵerengero zowopsa za achichepere akupsinjika maganizo mwa mtundu winanso: nkhanza yakuthupi, yamalingaliro, ndi ya zakugonana. Mzinda wa Kerala, India, uli ndi ziŵerengero zokwera kwambiri za kudzipha kwa achichepere m’dzikolo. Atsikana ambiri kumeneko ayesa kudzipha chifukwa cha kuchitidwa nkhanza ndi atate awo. Nkhanza za pa ana za mitundu yosiyanasiyana zakula kukhala mliri wapadziko lonse, ndipo kwa mikhole yake yopanda liwongoyo, kupsinjika maganizo kungakhale koipitsitsa.

Zopsinja Maganizo Zina

Koma sikuti malingaliro onse akufuna kudzipha amachititsidwa ndi zinthu zakunja. Lipoti lina lofufuza anyamata ndi atsikana osakwatira linati: “Amuna ndi akazi omwe amadziloŵetsa m’kugonana ndi kumwa moŵa anali pangozi yokulirapo [ya kudzipha] kuposa osachita zinthuzo.” Uchiwerewere wa Sunita unamtengetsa mimba—imene anaitaya mwa kuichotsa. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 6:18.) Posautsidwa ndi chikumbumtima, iye anafuna kungofa. Mofananamo, Brad anali kumwa moŵa chiyambire msinkhu wa zaka 14, akumadziloŵetsa m’mapwando akuledzera kaŵirikaŵiri. Inde, utamwedwa mopambanitsa, moŵa ukhoza ‘kuluma ngati njoka.’—Miyambo 23:32.

Malingaliro akufuna kudzipha angachokere ngakhale ‘m’maganizo ovutitsa,’ a munthu mwini. (Salmo 94:19, NW) Madokotala amanena kuti kulingalira kopsinja maganizo nthaŵi zina kungachititsidwe ndi mikhalidwe yosiyanasiyana ya m’thupi. Mwachitsanzo, Peter, wotchulidwa poyambapo, anapimidwa ndi kupezedwa kuti anali ndi kusalinganizika kwa makemikolo muubongo wake asanadziphe. Malingaliro a kupsinjika maganizo amene samachepetsedwa akhoza kukula; kudzipha kungayambe kuoneka kukhala chosankha chabwino.

Kupeza Chithandizo

Komabe, kudzipha sikuyenera kulingaliridwa kukhala chosankha chabwino. Kaya tikudziŵa kapena ayi, tonsefe tili ndi zimene akatswiri a thanzi la maganizo Alan L. Berman ndi David A. Jobes amazitcha ‘zothandiza zamkati ndi zakunja pakulimbana mwachipambano ndi nsautso ndi mkangano.’ Chimodzi cha zothandizazo chingakhale banja ndi mabwenzi. Lemba la Miyambo 12:25 limati: “Nkhaŵa iŵeramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.” Inde, mawu abwino ochokera kwa munthu womvetsetsa angasinthe mkhalidwewo kwambiri!

Chotero ngati aliyense akudzimva wopsinjika maganizo kapena wodera nkhaŵa, nkwanzeru kuti asavutike payekha. (Miyambo 18:1) Wovutikayo angatulutse zakukhosi kwake kwa munthu amene amamdalira. Kulankhula kwa winawake kumathandiza kuchepetsa kupweteka kwa malingaliro amphamvu a munthu, ndipo kungapatse munthu lingaliro latsopano pamavutowo. Ngati munthu wina wasweka mtima potaikiridwa bwenzi kapena wokondedwa mu imfa, munthuyo ayenera kulankhula za zimenezo ndi woululira zakukhosi. Pamene kupweteka kwa kutayikiridwako kuzindikiridwa ndi chisonicho chimvedwa, munthuyo amatonthozedwa. (Mlaliki 7:1-3) Kungakhale kothandiza kuti munthuyo alonjeze kudziŵitsa woululira zakukhosi wake ngati malingaliro akufuna kudzipha abweranso.

Kunena zowona, kungakhale kovuta kukhulupirira munthu. Koma popeza kuti moyo weniweniwo uli pachiswe, kodi sikuli koyenerera kuyesako? Mwachionekere malingaliro akufuna kudziwononga angachoke ngati alankhulana zinthuzo. ‘Ndi yani?’ ena angafunse. Ngati makolo a munthu ali owopa Mulungu, bwanji osayesa ‘kupatsa mtima wanu’ kwa iwo? (Miyambo 23:26) Iwo akhoza kumvetsetsa bwinopo kuposa mmene ambiri amalingalirira ndipo angakhale okhoza kuthandiza. Ngati kukuoneka kuti pakufunikira chithandizo chowonjezereka—monga ngati kupimidwa ndi dokotala.

Ziŵalo za mpingo Wachikristu zili magwero ena a chithandizo. Amuna aakulu mwauzimu mumpingo angachirikize ndi kuthandiza opsinjika maganizo. (Yesaya 32:1, 2; Yakobo 5:14, 15) Pambuyo poyesa kudzipha, Sunita anapeza chithandizo kuchokera kwa mlaliki wanthaŵi yonse (mpainiya). Sunita akuti: “Iye anakhala nane m’zilizonse. Popanda iye, bwenzi panopo ndili wopenga.”

Kulimbana Nazo

Palinso zothandiza zamkati zimene zingagwiritsiridwe ntchito. Mwachitsanzo, kodi kuvutika kwa malingaliro a liwongo kwachititsidwa ndi mchitidwe wolakwa? (Yerekezerani ndi Salmo 31:10.) Mmalo molola malingaliro oterowo kukula, munthuyo ayenera kulimbikira pakuwongolera mkhalidwewo. (Yesaya 1:18; yerekezerani ndi 2 Akorinto 7:11.) Njira yabwino ndiyo kuululira makolo. Zowonadi, iwo angakhumudwe poyamba. Koma mwachionekere adzasumika maganizo pakupereka chithandizo. Ndiponso ndife otsimikiziridwa kuti Yehova ‘amakhululukira mokulira’ awo olapa zenizeni. (Yesaya 55:7) Nsembe yadipo ya Yesu imakwirira tchimo la anthu olapa.—Aroma 3:23, 24.

Akristu angapezenso chithandizo kuchokera m’chikhulupiriro chawo, chidziŵitso cha Malemba, ndi unansi wawo ndi Yehova Mulungu. Panthaŵi zosiyanasiyana wamasalmo Davide anakhala wopsinjika maganizo kwambiri kwakuti anati: “Mdani . . . apondereza pansi moyo wanga.” Iye sanagonje ku kutaya mtima. Analemba kuti: “Ndifuula nalo liwu langa kwa Yehova; ndi mawu anga ndipemba kwa Yehova.” “Zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.”—Salmo 142:1; 143:3-5.

Ngati chikhumbo cha kufuna kudzipha chikhala champhamvu, munthuyo ayenera kupemphera kwa Yehova. Iye amazindikira kupwetekako ndipo amafuna kuti wosautsikayo akhalebe ndi moyo! (Salmo 56:8) Iye akhoza kupereka “mphamvu yoposa yachibadwa” yothandiza kulimbana ndi kupwetekako. (2 Akorinto 4:7, NW) Munthu ayenera kulingaliranso, za kupweteka kumene imfa yodzichititsa ingadzetse pa banja, mabwenzi, ndi Yehova mwiniyo. Kulingalira pa zinthu zimenezi kungathandize kwambiri munthu kukhalabe ndi moyo.

Pakuti ngakhale kuti kwa ena zingaoneke monga kuti kupwetekako sikudzatha konse, iwo angatsimikiziridwe kuti alipo ena amene apyola m’zopweteka zofananazo. Iwo ali okhoza kunena mwa zokumana nazo zawo kuti zinthu zikhoza kusintha ndipo zimasinthadi. Ena akhoza kupereka chithandizo chopyolera m’nthaŵi yoŵaŵitsa yotero. Anthu opsinjika maganizo ayenera kufunafuna chithandizo chofunikiracho—ndi kukhalabe ndi moyo!

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 31]

Kumakhala bwinopo kulankhula za malingaliro opweteka ndi munthu wina

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena