Chiyembekezo Chenicheni kwa Ana
“Sipadzakhalanso . . . mwana wokhala masiku oŵerengeka chabe . . . Sadzagwira ntchito pachabe kapena kubala ana oyang’anizana ndi tsoka; pakuti adzakhala anthu odalitsidwa ndi AMBUYE.”—Yesaya 65:20, 23, New International Version.
MOSASAMALA kanthu za zoyesayesa za munthu zoyamikirika za kuwongolera zinthu, mamiliyoni a makanda obadwa chatsopano akukhalabe “oyang’anizana ndi tsoka.” Sizidzakhala motero kwa nthaŵi zonse. Ulosi wa Yesaya sumangotitsimikizira kuti mwana aliyense tsiku lina adzakhala ndi mtsogolo mosungika koma umalongosolanso mmene chonulirapo chimenecho chingakwaniritsidwire.
Pa Yesaya 65:17, Mulungu amati: “Ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.” Kuti ana onse padziko asamaliridwe bwino, “kumwamba kwatsopano” ndi “dziko lapansi latsopano” lomwe, zimafunikira.
“Dziko lapansi latsopano” limeneli ndilo chitaganya chatsopano cha anthu osunga malamulo a mkhalidwe amene Yesu Kristu anaphunzitsa. Limodzi la malamulo a mkhalidwe amenewo, omwe Yesu anafotokoza, nlakuti “munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira ine.” (Marko 9:37) Chitaganya chimene chikachitira mwana wamng’ono aliyense monga ngati kuti anali Kristu mwiniyo ndithudi chikakhala “dziko lapansi latsopano”! Ndipotu, mamiliyoni a anthu akukalimira kale kuchita zimenezo, ndipo apambana m’kupereka chiyembekezo kwa ena a ana a padziko.
Ana Omwe Tsopano Ali Ndi Chiyembekezo
Tshepo, limodzi ndi achimwene ndi achemwali ake aakulu anayi, ankakhala m’komboni mu South Africa. Pamene iye anali ndi chaka chimodzi chakubadwa, anali atakhala kale ndi kamimba kofufuma ka manyutilishoni. Makolo ake ankawawanyira pamoŵa mbali yaikulu ya tindalama tomwe ankapeza ndi cholinga chosaphula kanthu chakuti aiŵale mavuto awowo. Tshepo sankadya chakudya chotentha kaŵirikaŵiri, ndipo analekereredwa kumaseŵera pazinyalala ndi zitini zothamo moŵa zotayidwa paliponse panyumbapo.
Mtsogolo mwa Tshepo munaonekera kukhala mowopsa kufikira pamene kanthu kena kanachitika kusintha kalingaliridwe ka makolo ake. Mnansi wotchedwa George anawapatsa kosi yaulere yophunzira Baibulo. Zotulukapo zinali zokondweretsa—vuto la kumwa linatha, nyumba inayeretsedwa, banja linayamba kudya chakudya chotentha tsiku lililonse, ndipo Tshepo ndi achimwene ndi achemwali akewo anayamba kuoneka audongo, ovala bwino, ndi achimwemwe.
George anathandiza banja la Tshepo chifukwa chakuti, monga mmodzi wa Mboni za Yehova, amadziona kukhala ndi thayo kulinga kwa onse, kuphatikizapo amphaŵi ndi osaphunzira. Ndithudi, zinatenga nthaŵi yaikulu ndi kuleza mtima kuthandiza banjalo kusintha njira yawo ya moyo, kuwaphunzitsa mikhalidwe yatsopano yozikidwa pa Mawu a Mulungu. Koma George akuona kuti kuyesayesako kunali koyenerera, makamaka pamene akuona kusintha kwakukulu kumene kwachitika kwa anawo.
Mu tauni ya San Salvador Atenco ku Mexico mumakhala mlimi wina wotchedwa José, tate wa ana asanu ndi anayi. Anali chidakwa chadzaoneni, ndipo ana ake ankamuopa chifukwa chakuti akaledzera ankawakalipira mwachiwawa ndi kuwakwapula. Panyumba pawo panali pauve nthaŵi zonse, ndipo pabwalo pawo panali pokhala pa abulu awo ndi nkhumba, zimene zinkaloŵa ndi kuyendayenda m’nyumbamo modzifunira. Chifukwa cha zimenezo anawo anadwala matenda a m’mimba, ndipo nthaŵi zina matupi awo anali zilonda zokhazokha.
Zinthu zinasintha pamene José anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye analeka kumwa moŵa kwambiri nakhala tate wabwino kwa ana ake. “Tsopano timaseŵera ndi atate!” amatero monyadira mmodzi wa ana aang’ono. Nyumba yawo tsopano ndi imodzi ya nyumba zaukhondo koposa—mmalo mwa kukhala imodzi ya zauve koposa—m’taunimo. Nkhumbazo ndi abulu zimasungidwa kumunda, ndipo banjalo limaphitsa madzi akumwa nthaŵi zonse. Ukhondo wowongoleredwa wachititsa anawo kukhala athanzi labwinopo ndi achimwemwe kwambiri.
Monga momwe zitsanzo ziŵirizi zikusonyezera, kaŵirikaŵiri chinsinsi chothandizira ana ndicho kuthandiza makolo. Pangano la Msonkhano wa Atsogoleri Wadziko Lonse wa Ana linavomereza kuti “banja ndilo lili ndi thayo lalikulu la kusunga ndi kutetezera ana.” Ndipo kaya mabanja amasamalira ndi kutetezera ana awo kapena ayi zimadalira kwambiri pa maphunziro monga momwe zimadalirira pa ndalama.
Kusintha Mwana wa m’Mkhwalala
Mu Brazil, Domingos anali ndi zaka zisanu ndi zinayi zokha pamene atate wake anamwalira. Pamene amayi ake anakwatiwanso, iye anakaikidwa kunyumba ya ana amasiye. Nkhanza imene anachitiridwa m’nyumba ya ana amasiye inampangitsa kuganiza za kugwirizana ndi kagulu kamene kanali kupangana za kuthaŵa. Ngakhale kuti amayi ake anamtenganso pamene anamva zimene anafuna kuchita, kukwapulidwa kaŵirikaŵiri ndi atate ake opeza kunamkhutiritsa maganizo kuti anayenera kuchoka panyumba. Iye anakhala mmodzi wa zikwi za ana a m’khwalala mu São Paulo omwe amapukuta nsapato, kugulitsa maswiti, kapena ngakhale kuperekera mankhwala oledzeretsa kotero kuti achirikize moyo wawo.
Pamene Domingos anafika pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova kwanthaŵi yoyamba, anali wokayikira aliyense ndipo analibe ulemu—nzosadabwitsa polingalira za makulidwe ake. Komabe, Mboni zachikulire zinampangitsa kuzidalira, ndipo kupyolera mwa phunziro la Baibulo laumwini, zinamthandiza kuphunzira makhalidwe atsopano. Potsirizira pake anaphunzira kuti anali wokhoza kudalira Mulungu ndi anthu ena. Mbonizo zinamthandiza kupeza ntchito, choyamba monga wothandiza omanga ndiyeno monga ofesiboyi. Tsopano, pambuyo pa zaka zingapo, akutumikira monga mtumiki wanthaŵi yonse Wachikristu.
Zitsanzo zimenezi zimasonyeza kuti chitaganya chosamalira anthu chikhoza kuchepetsa ena a mavuto a ana padziko. Ndithudi, Mboni za Yehova zimazindikira kuti zochitika ndi mikhalidwe yovutitsa sizingathe kuchotsedwa kotheratu ndi zoyesayesa za anthu. Chithandizo chotsimikizirika chothetsera mavuto a ana padziko chikafunikira mphamvu yoposa yaumunthu, chithandizo chosalephera, ndi ulamuliro wa dziko lonse.
“Miyamba Yatsopano” Kaamba ka Dziko Labwinopo
Mulungu yekha ndiye angapereke chithandizo chothetseratu vuto. Chifukwa chake, ulosi wa Yesaya umafotokoza kuti “dziko lapansi latsopano” lidzatsagana ndi “kumwamba kwatsopano.” Kangapo konse Baibulo limalonjeza kuti “m’mwamba mwatsopano” kapena “miyamba yatsopano” idzakhazikitsidwa. (Yesaya 65:17; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1) Paliponse pamene kukhazikitsidwa kwa “miyamba yatsopano” imeneyi kutchulidwa, kumasonyezedwa kukhala njira yofunika kwambiri yochotsera mavuto ndi kudzetsa chilungamo padziko lapansi. Kodi “miyamba yatsopano” imeneyi ndiyo chiyani kwenikweni?
Kaŵirikaŵiri Baibulo limagwiritsira ntchito liwulo “miyamba” monga liwu lofanana ndi lakuti ulamuliro, kaya wa Mulungu kapena wa anthu. (Yerekezerani ndi Danieli 4:25, 26.) Boma latsopano limeneli ndilo Ufumu wakumwamba, Ufumu wa Mulungu—umene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuupempherera. (Mateyu 6:10) Ufumu wa Mulungu udzakhala ndi mphamvu yochotsera tsoka lililonse limene lingawopseze ana a padziko, ndipo udzachitadi zimenezo.
Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kwambiri za zimenezo? Chifukwa chakuti boma limasonyeza umunthu wa olamulira ake. Chotero, Ufumu wa Mulungu udzalamulira mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu ndi ya Mwana wake, Yesu Kristu, Mfumu yoikidwa ya Mulungu. Onse aŵiriwo asonyeza chikondwerero chachikulu mu ubwino wa ana.—Salmo 10:14; 68:5; Marko 10:14.
Pamene tikuyembekezera mwachidwi Ufumu wolonjezedwa umenewu, kapena “miyamba yatsopano,” tikhoza kugwirira ntchito pa kuwongolera mkhalidwe wa ana a m’chitaganya chathu. Monga momwe Msonkhano wa Atsogoleri Wadziko Lonse wa Ana unagamulira moyenerera: “Sipangakhale ntchito yolemekezeka kwambiri kuposa yokonzera mwana aliyense mtsogolo mwabwinopo.”
[Bokosi patsamba 11]
Makonzedwe Ogwira Ntchito Othandiza Ana
Ntchito yophunzitsa ya Mboni za Yehova imapereka chithandizo chogwira ntchito ndi chokhalitsa kwa ana. Mbali zina za makonzedwe ameneŵa ndi izi:
Maphunziro a Achikulire. Ameneŵa amaphatikizapo kosi ya kuŵerenga ndi kulemba ya achikulire amene satha kutero, limodzinso ndi malangizo ochuluka a Baibulo ophunzitsa mikhalidwe yabwino yosamalirira bwino ana.
Chitsogozo cha Banja. Baibulo limalangiza makolo—ngakhale awo amene ali osauka kwambiri—kusamalira ana awo onse mmalo mwa kutumiza ena kukakhala ndi achibale. Buku lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe lakhaladi lothandiza pakuthandiza mabanja omwe ali ndi mavuto apadera.a
Kuloŵetsedwamo kwa Ana ndi Kuzoloŵetsedwa. Pamene ana aloŵetsedwamo m’maphunziro, zaumoyo, ndi ukhondo, zotulukapo zimakhala zabwino kwambiri. Kaŵirikaŵiri Mboni zimaphunzira Baibulo ndi ana, zikumagwiritsira ntchito mabuku oyenerera onga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndi Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza kuwathandiza kusamalira mavuto panyumba ndi kuwongolera ukhondo wawo.b
Malangizo pa Ukhondo ndi Zaumoyo. Mboni za Yehova zimafalitsa magazini a Galamukani! m’zinenero 74, ndipo magazini ameneŵa kaŵirikaŵiri amakhala ndi nkhani zonena za umoyo.
Ntchito Yothandiza Patsoka. Pamene kugwa tsoka, Mboni za Yehova zimalinganiza mofulumira ntchito zopereka chithandizo mwachindunji ku malo a tsokawo.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Zithunzi patsamba 10]
Chithandizo chotsimikizirika chothetsera mavuto a ana a padziko chikafunikira mphamvu yoposa yaumunthu. Chithandizo choterocho chikhoza kuperekedwa ndi Mulungu yekha