Kodi Chuma Chingagule Chimwemwe?
MWACHIONEKERE kukhala ndi ndalama zambiri sikumapanga anthu kukhala achimwemwe mokulira. Magazini a Psychology Today akuti: “Umphaŵi utapyoledwa, modabwitsa kuwonjezeka kwa malipiro kumakhala ndi kugwirizana kochepa ndi chimwemwe cha munthu mwini.”
Zimenezi zinatsimikiziridwa ndi mawu olongosola za munthu wakufa a mu New York Times ya pa October 29, 1993, amene anali ndi mutu wakuti: “Doris Duke, Wazaka 80, Woloŵa Nyumba Amene Chuma Chake Chochuluka Sichinagule Chimwemwe, Wamwalira.” Nkhaniyo inati: “Usiku wina mu Roma mu 1945, Miss Duke, amene panthaŵiyo anali ndi zaka 33 zakubadwa, anauza bwenzi kuti chuma chake chochuluka chinali mwa njira ina chopinga ku chimwemwe.”
“Nthaŵi zina ndalama zochuluka motero zimabweretsa mavuto,” Duke anaululira bwenzi lina. “Pambuyo poyenda ndi mwamuna kwa nthaŵi zingapo, amayamba kundiuza mmene amandikondera. Koma kodi ndingadziŵe bwanji kuti akunenadi zoona? Kodi ndingatsimikizire motani?” Times inati: “Mawu ake usiku umenewo anasonyeza kuti moyo wake unayambukiridwa kwambiri, ngakhale kuwopsezedwa, ndi chuma chake.”
Mofananamo, Jean Paul Getty, yemwe panthaŵi ina ananenedwa kukhala munthu wolemera kopambana m’dziko, anati: “Ndalama sizigwirizana konse ndi chimwemwe. Mwinamwake ndi kupanda chimwemwe.” Ndipo Jane Fonda, wochita seŵero wotchuka wa ku Hollywood, amene mkati mwa ma 1970 analandira madola theka la miliyoni pa kanema mmodzi aliyense, anati: “Ndalaŵa kale kukhala wolemera ndi zinthu zina zonse zakuthupi. Izo sizitanthauza kanthu. Pali kusokonezeka maganizo kumene kumapita ndi dziŵe losambiramo lililonse pano, kuwonjezera pa kutha kwa maukwati ndi ana amene amada makolo awo.”
Pamene kuli kwakuti chuma chokha sichingadzetse chimwemwe, kusauka nakonso sikungatero. Motero, mwamuna wanzeru kalelo anati: “Musandipatse umphawi, ngakhale chuma.” (Miyambo 30:8, 9) Wolemba Baibulo wina ananena kuti zimene munthu amafunikira kuti akhale wachimwemwe ndizo “chipembedzo pamodzi ndi kudekha . . . pakuti sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”—1 Timoteo 6:6-10.