Nyenyezi ndi Munthu—Kodi Pali Kugwirizana?
CHIZOLOŴEZI cha kuyang’ana nyenyezi sichili chatsopano. Malinga ndi kunena kwa The World Book Encyclopedia, alimi zaka zikwi zapitazo “anayang’ana nyenyezi kuti adziŵe pamene akabzala mbewu zawo. Aulendo anaphunzira kugwiritsira ntchito nyenyezi kudziŵira kopita.” Ngakhale lerolino m’maulendo a mumlengalenga, nyenyezi zimagwiritsiridwabe ntchito monga zotsogolera. Anthu akale nawonso anapeka nthanthi za anthu ndi zinyama zimene anaganiza kuti zinaimiridwa ndi magulu a nyenyezi, kapena makamu ake. M’kupita kwa nthaŵi anthu anayamba kuganiza kuti nyenyezi zingayambukire miyoyo yawo.
Nkhokwe Yaikulu ya Nyenyezi
Chiŵerengero chachikulu ndi ukulu wa nyenyezi zimawopsa. Kukuyerekezeredwa kuti muli makamu, kapena magulumagulu aakulu a nyenyezi, mamiliyoni zikwi zana m’chilengedwe! The International Encyclopedia of Astronomy imati: “Chimenecho ndicho chiŵerengero cha misenga ya mpunga imene ingadzale m’tchalitchi chachikulu.” Khamu la nyenyezi lotchedwa Mlalang’amba, limene dongosolo lathu la dzuŵa ndi mapulaneti lili mbali yake, limayerekezeredwa kukhala ndi nyenyezi zochuluka mofananamo kapena kuposerapo. Nyenyezi imene ili pafupi koposa ndi Dziko lathu Lapansi (kupatulapo Dzuŵa), la m’gulu la Alpha Centauri, ili pafupifupi pamtunda wa zaka 4.3 za kuunika. Chaka cha kuunika ndicho mtunda umene kuunika kumayenda m’chaka chimodzi. Zimenezo zimatanthauza kuti pamene muyang’ana nyenyezi imeneyo, kuunika kumene kumaloŵa m’diso lathu kunachoka ku nyenyeziyo zaka 4.3 zapitazo ndipo m’nthaŵi yonseyo kunali kuyenda kudutsa mlengalenga paliŵiro la makilomita 299,792 m’kamphindi. Sitikhoza konse kuyerekezera ndi nzeru zathu mtunda umene ulipo. Komabe, imeneyo yangokhala nyenyezi yapafupi koposa. Nyenyezi zina zili pamtunda wa zaka za kuunika mamiliyoni zikwizikwi kuchokera ku khamu lathu la nyenyezi. Nchifukwa chake mneneri wa Mulungu analengeza kuti: “Taonani, amitundu akunga dontho la m’mtsuko, naŵerengedwa ngati fumbi losalala la m’muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang’ono.” (Yesaya 40:15) Kodi ndani amene amadera nkhaŵa ndi tifumbi tochepetsetsa?
Chinthu chakumwamba chimene chili pafupi koposa ndi dziko lapansi ndicho mwezi, umene uli ndi chiyambukiro chotsimikizirika pa dziko lathu lapansi, mphamvu yake yokoka ikumachititsa ngakhale kusiyana koposa mamita 15 pakati pa kukwera kwa mafunde a madzi m’nyanja ndi kutsika kwake m’malo ena. Malinga ndi asayansi a ku France, mphamvu yokoka ya mwezi tsopano ikukhulupiriridwa kukhala imene imagwira mzera wapakati wa dziko lapansi kuti upitirize kukhala wopendeka ndi madigiri 23, motero ikumachititsa kusintha kokhazikika kwa nyengo. (Nature, February 18, 1993) Popeza kuti mwezi uli ndi chiyambukiro chakuthupi chotero pa pulaneti lathu, nkoyenera kufunsa kuti, Bwanji ponena za nyenyezi mamiliyoni zikwizikwi? Koma choyamba, kodi nchiyani chimene magwero akale, onga Baibulo, amatiuza ponena za nyenyezi?
Nyenyezi m’Malemba
Baibulo limatchula nyenyezi nthaŵi zambiri, ponse paŵiri m’lingaliro lenileni ndi lophiphiritsira. Mwachitsanzo, malinga ndi kunena kwa wamasalmo wina, Mlengi anapanga “mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku” kotero kuti nyenyezizo zingathandizire kuunikira dziko lapansi. (Salmo 136:9, Tanakh) Pambuyo pake, popanga pangano ndi Abrahamu wokhulupirika, Mulungu anati: “Tayang’anatu kumwamba, uŵerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziŵerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbewu zako.” (Genesis 15:5) Mtumwi Paulo akusonyeza kuti nyenyezi nzosiyanasiyana, akumanena kuti: “Kuli ulemerero wa dzuŵa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m’ulemerero.”a (1 Akorinto 15:41) Panthaŵi imodzimodziyo, chiŵerengero chachikulu chimenechi cha nyenyezi ndi ulemerero wawo sizili kunja kwa uyang’aniro kapena ulamuliro wa Mlengi wawo: “Aŵerenga nyenyezi momwe zili; azitcha maina zonsezi.”—Salmo 147:4.
Kumbali ina, m’Malemba timapeza kuti nyenyezi kaŵirikaŵiri zimagwiritsiridwa ntchito kutchulira anthu, olamulira, ndi angelo. Yosefe mwana wamwamuna wa Yakobo ali ndi loto limene likusonyeza makolo ake kukhala “dzuŵa ndi mwezi” ndipo abale ake kukhala “nyenyezi.” Angelo amatchulidwa kukhala “nyenyezi za m’maŵa.” Mfumu ya Babulo ikunenedwa kukhala ikukalimira kukhala pamwamba pa “nyenyezi za Mulungu,” olamulira a mzera wa Davide a mtundu wa Israyeli. Amuna osakhazikika mu mpingo Wachikristu amayerekezeredwa kukhala “nyenyezi zosokera,” pamene mabungwe okhulupirika a akulu ampingo amatchulidwa kukhala “nyenyezi” m’dzanja lamanja la Kristu.—Genesis 37:9, 10; Yobu 38:7; Yesaya 14:13; Yuda 13; Chivumbulutso 1:16.
Nkhani ina ya m’Baibulo imanena kuti ‘nyenyezi zinathirana nkhondo ndi Sisera m’mipita mwawo,’ kazembe wa gulu la nkhondo la Mfumu Yabini ya Kanani, amene anatsendereza mtundu wa Israyeli kwa zaka 20. Yehova anagaŵira Woweruza Baraki wa Israyeli kupulumutsa Israyeli ku ukapolo ndipo anampatsa chilakiko chachikulu pa Sisera, ngakhale kuti winayu anali ndi magareta mazana asanu ndi anayi azikwakwa m’magudumu awo. M’nyimbo yachilakiko, Aisrayeli anaimba kuti: “Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba, m’mipita mwawo zinathirana ndi Sisera.” Palibe mafotokozedwe amene amaperekedwa onena za mmene nyenyezi zinathirira nkhondoyo. Mmalo moganiza kuti nyenyezi zinali ndi chiyambukiro chachindunji pa nkhondoyo, nkoyenera kwambiri kukhulupirira kuti mawuwo akusonyeza kuloŵererapo kwinakwake kwa Mulungu m’malo mwa Israyeli.—Oweruza 5:20.
“Nyenyezi” ya ku Betelehemu
Mwinamwake imodzi ya nyenyezi zodziŵika koposa zotchulidwa m’Baibulo ndiyo “nyenyezi” ya ku Betelehemu imene inatsogolera openda nyenyezi a “kummaŵa” kunyumba imene Yesu anatengedwera ndi makolo ake pambuyo pa kubadwa kwake m’khola. Kodi nyenyezi imeneyo inali chiyani? Ndithudi sinali nyenyezi yamasiku onse, pakuti inali mmunsi kwambiri kuti openda nyenyeziwo aitsatire kwa makilomita pafupifupi chikwi chimodzi ndi mazana asanu ndi limodzi. “Nyenyezi” imeneyo choyamba inawatsogolera ku Yerusalemu. Itamva zimenezi, Mfumu Herode inawafunsa ndiyeno inasankha kupha Yesu khandalo. Ndiyeno “nyenyezi” imeneyo inatsogolera openda nyenyeziwo kunyumba yeniyeni imene Yesu anali kukhala. Ndithudi palibe nyenyezi yeniyeni imene ingachite zimenezo. Kodi chinthu chonga nyenyezi chimenechi chinachokera kwa Mulungu? Popeza kuti ulendo wa openda nyenyezi unatsogolera mwachindunji kukuphedwa kwa “tiana tonse ta m’Betelehemu ndi ta m’milaga yake yonse, takufikira zaka ziŵiri ndi tating’ono tonse,” kodi sikoyenera kunena kuti “nyenyezi” imeneyo inali chinthu china chogwiritsiridwa ntchito ndi Mdani wa Mulungu, Satana, poyesa kuwononga Mwana wa Mulungu?—Mateyu 2:1-11, 16.
Tiyeneranso kukumbukira kuti openda nyenyeziwo anachokera Kummaŵa, mwinamwake ku Babulo, amene anali likulu lakale la kupenduza, kubwebweta, ndi kupenda nyenyezi. Zinthu zakumwamba zingapo zatchedwa ndi maina a milungu ya Babulo. M’masiku a Mfumu Nebukadinezara, ula unagwiritsiridwa ntchito kumthandiza kusankha njira yotenga mumkupiti wake wankhondo.—Ezekieli 21:20-22.
Mneneri Yesaya anatokosa aphungu a Babulo, akumanena kuti: “Iwe [Babulo] watha mphamvu mosasamala kanthu za uphungu umene upatsidwa. Openda nyenyezi ako adze nadzakupulumutse—anthu aja amene amaphunzira za nyenyezi, amene amalemba zigawo za kumiyamba ndi kukuuza mwezi ndi mwezi zimene zidzakuchitikira. Adzakhala ngati ziputu za udzu, ndipo moto udzawatentha psiti! Iwo sadzakhoza ngakhale kudzipulumutsa . . . ndipo palibe amene adzatsala wokupulumutsa.” Mogwirizana ndi ulosi wa Yesaya, Babulo wamphamvuyo anagwa kwa Koresi Wamkulu mu 539 B.C.E. Chitsogozo chimene openda nyenyezi Achibabulo amenewo anati chinachokera ku nyenyezi chinakhala tsoka la onse okhudzidwa.—Yesaya 47:13-15, Today’s English Version.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitingaphunzire kalikonse ku nyenyezizo?
[Mawu a M’munsi]
a Kupenda zakuthambo kwamakono kumatsimikizira mawu a Paulo, pakuti nyenyezi zimasiyana m’kaonekedwe, ukulu, mlingo wa kuunika wotulutsidwa, kutentha, ndi kulemera kwake.
[Bokosi patsamba 5]
Zimene Ena Anena
KUPENDA NYENYEZI: “kuli kogwirizana ndipo ndi bwenzi la kupenda zakuthambo.”—Johannes Kepler (1571-1630), wopenda zakuthambo wa ku Germany.
“Kupenda nyenyezi ndi nthenda, si sayansi. . . . Ndi mtengo umene mumthunzi wake muli kukhulupirira malaulo kwa mitundu yonse.”—Moses Maimonides (1135-1204), katswiri Wachiyuda wa m’Zaka Zapakati.
“Sayansi yachiyambi imene imanena kuti ikhoza kupenda umunthu ndi kakhalidwe ka munthu yense ndi kulosera mikhalidwe ndi zochitika zamtsogolo mogwirizana ndi malo ndi mtunda pakati pa zakumwamba. . . . Mwinamwake pafupifupi m’zaka za zana la 6 BC—Akaldayo kummwera kwa Iraq amalingaliridwa kukhala atayambitsa horoscope yaumwini. Imeneyi inali yokhudza zisonkhezero zochitidwa ndi nyenyezi zosasunthika panthaŵi ya kubadwa, limodzinso ndi Dzuŵa, Mwezi ndi mapulaneti asanu. . . . Njira za kupenda nyenyezi ndi kamasuliridwe ka ma horoscope zimadalira pa malingaliro amene akatswiri azakuthambo ndi asayansi ena ochuluka amaona kukhala a munthu mwini ndi osalandirika.”—C. A. Ronan, wogwirizanitsa ntchitoyo, East Asian History of Science Trust, Cambridge, England, ndi amene analembako The International Encyclopedia of Astronomy kumene mawu ameneŵa agwidwako.
Kuti asonyeze kumasulira kwa munthu mwini kumeneku, Ronan akufotokoza kuti pamene kuli kwakuti kwa munthu Wakumadzulo, pulaneti lofiira, la Mars, limagwirizanitsidwa ndi nkhondo ndi ndewu, kwa anthu a ku China, maonekedwe ofiira n’ngokongola, ndipo Mars imaonedwa kukhala ndi chiyambukiro chabwino. Mosiyana ndi zimenezo, nthanthi Zakumadzulo zimagwirizanitsa Venus ndi kuyera ndi kukongola. Kwa anthu a ku China “kuyera . . . kumalingaliridwa kukhala maonekedwe a imfa, chivundi ndi chiwonongeko; chotero Venus inatchulidwa kuti ‘pulaneti lakuda bi la nkhondo.’”
Ronan akupitiriza kuti: “Mosasamala kanthu za mkhalidwe wake wasayansi yachiyambi, kupenda nyenyezi m’nthaŵi zakale kunachita mbali yothandiza kuchirikiza mapendedwe a kupenda zakuthambo ndi kupereka ndalama zowachitira.”
Opata mphotho ya Nobel 19, pamodzi ndi asayansi ena, anatulutsa chikalata mu 1975 chamutu wakuti “Zotsutsa Kupenda Nyenyezi—Ndemanga za Asayansi Otchuka 192.” Chinalengeza kuti: “Anthu m’nthaŵi zakale . . . analibe lingaliro la mitunda yaikulu pakati pa dziko lapansi ndi mapulaneti ena ndi nyenyezi. Tsopano popeza kuti mitunda imeneyi ingathe ndipo yaŵerengeredwa, timaona mmene mphamvu zokoka ndi ziyambukiro zina zotulutsidwa ndi mapulaneti apamtunda wautali ndi nyenyezi zakutali kwambiri zilili zazing’ono kwambiri. Ndi kungolakwa kulingalira kuti mphamvu zotulutsidwa ndi nyenyezi ndi mapulaneti panthaŵi ya kubadwa zingaumbe mwanjira iliyonse mtsogolo mwathu.”b
[Mawu a M’munsi]
b Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka ponena za kupenda nyenyezi, onani Awake! ya May 8, 1986, masamba 3-9.