Kodi Zimene Zili mu Nyenyezi Kaamba ka Inu Nzotani?
NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRAZIL
“KODI mwamva kuti zili m’nyenyezi kuti, m’July wotsatira tidzagundana ndi Mars?” Mawu amenewo a nyimbo yosangalatsa ya Cole Porter amafotokoza bwino lomwe chikhulupiriro chofala ndi chakale chakuti mtsogolo mwa munthu muli mogwirizana mwanjira inayake ndi nyenyezi.a Koma kodi pali unansi weniweni uliwonse pakati pa zinthu zakumwamba ndi moyo wa anthu pa dziko lino lapansi? Ngati ndi tero, kodi mtundu wa anthu umayambukiridwa motani? Ngati sitero, kodi ndi chifuno chotani chimene nyenyezi zimakwaniritsa?
Mposadabwitsa kuti anthu ochuluka kwambiri amafuna kudziŵa za mtsogolo pamene tipenda zochitika zina zazikulu zaposachedwapa—kugwa kwa Berlin Wall ndi kunyonyotsoka kofulumira kwa dziko lomwe kale linali Soviet Union, kusoŵeka kwa chidaliro mwa atsogoleri andale, kudana kwa mafuko kumene kukubuka mu Afirika ndi Ulaya, udani wachipembedzo ku India ndi Ireland, kukwera mitengo komafulumira kumene kukukantha maiko ochuluka kwambiri, ndi chipanduko cha achichepere. Malinga ndi kunena kwa lipoti lina la University of Hamburg, chaka cha 1992 chinali chankhondo zambiri chiyambire mapeto a Nkhondo Yadziko II, chokhala ndi nkhondo 52 m’maiko osiyanasiyana. Anthu okonda mtendere amafunsa mwachibadwa kuti: ‘Kodi nkuti kumene tingayang’ane kaamba ka bata, mtendere, ndi chisungiko?’
Kusatsimikizirika kwa mtsogolo kwachititsa kuwonjezereka kwa kuombeza ula kwamipangidwe yosiyanasiyana. Mwinamwake kupenda nyenyezi ndiko kodziŵika koposa. Pokhala kosiyana ndi sayansi ya kupenda zakuthambo, kupenda nyenyezi ndiko “ula wa ziyambukiro zongoyerekezera za nyenyezi ndi mapulaneti pa zochita za anthu ndi zochitika zapadziko lapansi kupyolera mwa malo awo ndi mitunda pakati pake.” Lerolino, mamiliyoni a anthu sangaleke konse kuŵerenga horoscope yawo kuti apeze chidziŵitso chonena za mtsogolo mwawo.b
Mbali zina zimene openda nyenyezi amati amalosera mtsogolo mwake zimaphatikizapo zotulukapo za zovuta za muukwati ndi mavuto athanzi, kuyamba ndi kugwa kwa atsogoleri andale, tsiku labwino koposa lotsegulira bizinesi yatsopano, ndi manambala ogwiritsira ntchito kupambanira lotale.
Nkhani ya mu Reuters inasimba kuti wopenda nyenyezi Joan Quigley ankafunsidwa nthaŵi zonse ndi Nancy Reagan ponena za pamene mwamuna wake, amene panthaŵiyo anali prezidenti wa United States, akayenera kukamba nkhani zake ndi pamene ndege yake ikayenera kunyamuka ndi kutera. New Catholic Encyclopedia inavumbula kuti “kupenda nyenyezi kunagwiritsiridwa ntchito ndi Papa Julius II [1503-13] kukhazikitsira tsiku la kuikidwa kwake ndipo ndi Paul III [1534-49] kudziŵira nthaŵi yoyenera ya Msonkhano wake iliwonse ndi Akadinala.” Alfred Hug, mkulu wa kampani ina ya ku Switzerland imene imagwiritsira ntchito kupenda nyenyezi kulangiza ogula pa msika wa zikole zamalonda, akutsimikizira za zotsatirapo zabwino koposa. “Nzolembedwa m’nyenyezi,” iye akunenetsa motero.
Mwachionekere, ambiri amaganiza kuti nyenyezi sizimayambukira miyoyo ya anthu. Kodi kupenda nyenyezi kunayamba motani? Kodi Baibulo buku lakale lili ndi chonena chilichonse pa kupenda nyenyezi ndi openda nyenyezi?
[Mawu a M’munsi]
a “Ku China wakale, . . . zizindikiro zakuthambo limodzi ndi masoka achilengedwe zinalingaliridwa kukhala zikusonyeza zochita ndi zolakwa za Mfumu ndi boma lake.”—The International Encyclopedia of Astronomy.
b Horoscope ndiyo “chithunzithunzi cha malo ongoyerekezera a mapulaneti ndi zizindikiro za kumwamba panthaŵi yakutiyakuti (monga pakubadwa kwa munthu)” ndipo chimagwiritsiridwa ntchito ndi openda nyenyezi kuyesa kulosera zochitika za mtsogolo m’moyo wa munthu.