Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 8/8 tsamba 8-10
  • Makolo—Khalani Ochirikiza a Mwana Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo—Khalani Ochirikiza a Mwana Wanu
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mathayo a Makolo ndi Aphunzitsi
  • Khalani Wochirikiza wa Mwana Wanu
  • Kachitidwe Koyenera
  • Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino
    Galamukani!—1996
  • Thandizani Mwana Wanu Kulimbana ndi Mavuto Kusukulu
    Galamukani!—1994
  • Mavuto a Uphunzitsi
    Galamukani!—2002
  • Mmene Makolo Angathandizire
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 8/8 tsamba 8-10

Makolo—Khalani Ochirikiza a Mwana Wanu

MAKOLO amafuna zabwino koposa kwa ana awo aamuna ndi aakazi. Ndithudi, mtumwi Wachikristu Paulo analangiza atate kulera ana awo m’chilangizo cha Mulungu. (Aefeso 6:4) Mfumu Solomo wakale analangiza ana kuti: “Mvetsera zimene atate wako ndi amako akuuza. Kuphunzitsa kwawo kudzawongolera khalidwe lako.”—Miyambo 1:8, 9, Today’s English Version.

Pamenepo, kodi sukulu zimachita mbali yotani m’kakonzedwe ka kuphunzitsa kwa makolo? Ndipo kodi payenera kukhala unansi wotani pakati pa makolo ndi aphunzitsi akusukulu?

Mathayo a Makolo ndi Aphunzitsi

“Makolo ndiwo . . . aphunzitsi ofunika koposa a ana awo,” akutsimikizira motero Doreen Grant, woyambitsa wa kufufuza chiyambukiro cha sukulu pa mkhalidwe wa kunyumba. Koma monga kholo, mungaone lingaliro limenelo kukhala lovuta kulivomereza.

Mwinamwake mwaona kuti njira zophunzitsira zasintha kwambiri kuyambira panthaŵi imene inuyo munali kusukulu. Masiku ano, sukulu zimaphunzitsa maphunziro amene anali osadziŵika poyambapo, monga ngati maphunziro a kufalitsidwa kwa nkhani, maphunziro a zaumoyo, ndi microelectronics. Zimenezi zachititsa makolo ena kuchepetsa mayanjano awo ndi sukulu. “Kulankhula ndi aphunzitsi a mwana wake kungachititse kholo lodzidalira koposa kudziona ngati lili ndi zaka zisanu ndi kutalika mapazi anayi,” akulemba motero Dr. David Lewis mu Help Your Child Through School. “Mmalo mokambitsirana mavuto kapena nkhaŵa ndi aphunzitsi monga achikulire, ena amasonyeza khalidwe lachibwana.”

Ndithudi, makolo ena amafikira aphunzitsi a ana awo kokha pamene kwachitika mavuto aakulu. Ndiyeno, kaŵirikaŵiri amapita kukadandaula. Komabe, makolo akhoza, ndipo ambiri amatero, kuthandizira kwambiri maphunziro a ana awo mwa kugwirizana ndi aphunzitsi.

Thayo la makolo limafuna kuti mupende ndi kukhala ndi chikondwerero m’zimene mwana wanu akuphunzira kusukulu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti aphunzitsi, mwa ukatswiri wawo, amatumikira monga opereka chitsanzo anu. Makhalidwe amene amachirikiza amayambukira ophunzira awo, popeza kuti ana amayang’ana kwa aphunzitsi monga zitsanzo zozitengera. Ku mbali yawo, aphunzitsi ochuluka amayamikira chigwirizano cha makolo a ophunzira awo.

Hedimasitala wina kummwera kwa Germany analembera makolo kuti: “Kwakhala koonekeratu kwa ife aphunzitsi, kuposa ndi chaka china chilichonse chapita, kuti gulu lonse la ophunzira athu, makamaka amene akuyamba sukulu [mu Germany, pa msinkhu wazaka zisanu ndi chimodzi], ngakhale tsopano ali opanda chifundo ndi ankhanza, amakhalidwe oipa kwenikweni. Ambiri ali osadziletsa mpang’ono pomwe, osadziŵa malire; alibe lingaliro la liwongo; ali odzikonda mopambanitsa, osayanjana ndi ena; ndipo amakhala ankhanza popanda chifukwa chenicheni, kukama pakhosi ndi kuponda chidyali [ena].”

Mphunzitsi ameneyu anapitiriza kuti: “Ngakhale kuti aphunzitsife tili ndi mavuto okulira kwambiri monga chotulukapo chake, sitikufuna kudandaula. Koma tiyenera kuzindikira kuti, mosasamala kanthu za zoyesayesa zonse, sukulu singaphunzitse ndi kulera ana payokha. Tingakonde kulimbikitsa makolo okondedwanu kuchitapo kanthu motsimikiza mwa kuchita zochuluka inu eni m’kulera ana anu ndipo osati kuwapereka ku wailesi yakanema kapena ku makwalala zimene kwenikweni zili gawo lanu la [thayo la] kuumbika kwa umunthu wawo, kuwaphunzitsa miyezo ya makhalidwe.”—Kanyenye ngwathu.

Ngakhale pamene aphunzitsi achonderera motero kaamba ka kugwirizana, makolo ambiri adakali kuzengereza kuthandiza. “Osati chifukwa chakuti sali osamala, otanganitsidwa kwambiri kapena opanda chidaliro,” akutero David Lewis, “koma chifukwa cha chikhulupiriro chawo champhamvu chakuti kaya mwana amachita bwino motani, kapena moipa m’kalasi, zimenezo sizimadalira konse pa kuleredwa ndi maluso awo achibadwa.” Koma lingaliro limeneli siloona konse.

Monga momwe kaŵirikaŵiri mavuto panyumba amayambukirira ntchito ya m’kalasi ya mwana, momwemonso moyo wabwino wapanyumba ungathandize mwana kupindula kwambiri kusukulu. “Banja lili ndi thayo lalikulu kuposa sukulu pa kupambana kapena kulephera maphunziro,” kunatsimikizira motero kufufuza kwina kwa zamaphunziro. Buku la How to Help Your Child Through School likuvomereza kuti: “Ngakhale kholo lotanganitsidwa koposa liyenera kuzindikira kuti mkhalidwe wawo wamaganizo—chikondwerero ndi chilimbikitso chimene amasonyeza, ndi chichirikizo chimene amapereka, ngakhale pamene ali kutali—chingakhale chofunika koposa pa kupita patsogolo kwa ana.”

Pamenepo, kodi kugwirizana kwabwino kumeneku mungakupeze motani ndi aphunzitsi a mwana wanu?

Khalani Wochirikiza wa Mwana Wanu

(1) Khalani ndi chikondwerero chachikulu m’zimene mwana wanu akuphunzira kusukulu. Nthaŵi yabwino koposa kuyamba ndiyo pamene mwana wanu akuyamba kupita kusukulu. Ana ocheperapo mwachisawawa amalandira bwino chithandizo cha makolo kuposa okulirapo.

Ŵerengani ndi mwana wanu. “Pafupifupi 75 peresenti ya kuphunzira kwa nthaŵi zonse,” malinga ndi kunena kwa David Lewis, “kumachitika mwa kuŵerenga.” Motero mungachite mbali yotsogolera m’kukulitsa kusadodoma kwa mwana wanu poŵerenga. Kufufuza kukupereka lingaliro lakuti kupita patsogolo kwa ana amene amathandizidwa kuŵerenga kunyumba kaŵirikaŵiri kumaposa kwa ana amene amalandira chithandizo kuchokera kwa aphunzitsi aukatswiri kusukulu.

Mofananamo, mungathandize mwana wanu kulemba, inde, ngakhale masamu. “Simutofunikira kukhala katswiri wa masamu kuti muthandize ndi masamu oyambirira,” akuthirira ndemanga motero mphunzitsiyo Ted Wragg. Ndithudi, ngati inuyo mufunikira chithandizo m’mbali zimenezi, musalole kusoŵa luso kulikonse kukuletsani kukhala ndi chikondwerero chenicheni m’zimene mwana wanu akuphunzira.

(2) Funsani mphunzitsi wa mwana wanu ponena za makosi. Mwa kuŵerenga chikalata cha zodzaphunziridwa, dziŵani zimene mwana wanu adzaphunzitsidwa. Kuchita zimenezo temu ya sukulu isanayambe kudzakuchenjezani za mbali zovuta. Ndiyeno, kupita kukakambitsirana ndi mphunzitsiyo mmene zofuna zanu monga kholo zingalemekezedwere kudzatsegula njira ya kugwirizana kwabwino. Gwiritsirani bwino ntchito misonkhano imene sukuluyo imalinganiza yakuti aphunzitsi adziŵane ndi makolo. Pa masiku amene makolo amaloledwa kufika m’kalasi, pitani kusukuluko, ndipo lankhulani ndi aphunzitsi a mwana wanu. Kulankhulana koteroko kumatsimikizira kukhala kopindulitsa koposa, makamaka pamene mavuto abuka.

(3) Thandizani mwana wanu kusankha maphunziro ake. Dziŵani zimene mwana wanu amakonda ndi zimene amada. Lankhulani za zonulirapo zopindulitsa. Funsani aphunzitsi kuti mudziŵe zosankha zonse zothekera. Iwo adzadziŵa ponena za mavuto alionse a zondandalikidwazo amene adzalepheretsa kusankha maphunziro ena.

Malingaliro oipa angapeŵedwe mwa kulankhula momvekera bwino. Sukulu zambiri zimaika chitsenderezo pa ophunzira anzeru kuti apitirize ndi maphunziro apamwamba. Koma ophunzira amene amasankha utumiki Wachikristu monga ntchito yawo kaŵirikaŵiri amapeŵa kutenga makosi a ku yunivesite otenga nthaŵi yaitali. Mmalo mwake, ngati asankha maphunziro owonjezera, iwo amakonda kuphunzira maphunziro amene amawakonzekeretsa kudzichirikiza okha. Aphunzitsi osamala nthaŵi zina amaona molakwa lingaliro limeneli monga kukana zonse zimene ayesa kuphunzitsa. Kulongosolera aphunzitsiwo moleza mtima za kuthekera kwa maphunziro owonjezereka amene ali otsegukira mwana wanu m’gawo losankhidwa ndi mwana wanu kudzatsimikizira aphunzitsi kuti makolo Achikristu amafunadi kuti ana awo apitirizebe kuphunzira.a

Kachitidwe Koyenera

Mungapeŵe nkhaŵa zochuluka ndi kuwawa mtima pa maphunziro a mwana wanu mwa kukumbukira kuti ubwenzi wachipambano umamangidwa pa kulankhulana kwabwino.—Chonde onani bokosi lakuti “Njira za Kulankhulana Kwabwino kwa Kholo ndi Mphunzitsi.”

Mmalo modandaula ndi kusuliza, khalani wochirikiza wa mwana wanu mwa kukambitsirana ndi kugwirizana ndi aphunzitsi. Mwakuchita motero, mudzathandiza mwana wanu kupindula koposa kusukulu.

[Mawu a M’munsi]

a Mboni za Yehova zimene zasankha utumiki Wachikristu monga ntchito yawo ndi kutumikira monga atumiki anthaŵi yonse zili ndi mwaŵi wa kuchita kosi ya milungu iŵiri ya Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Ena pambuyo pake amayeneretsedwa kulembetsa kosi ya miyezi isanu ya maphunziro aumishonale ochititsidwa ndi Sukulu ya Baibulo ya Watchtower ya Gileadi kuwakonzekeretsa monga amishonale.

[Bokosi patsamba 10]

Njira za Kulankhulana Kwabwino kwa Kholo ndi Mphunzitsi

1. Dziŵani aphunzitsi a mwana wanu.

2. Pendani bwino mfundo zanu musanapereke madandaulo.

3. Ngati mwavutika maganizo kapena kukwiya, yambani mwakhazika mtima pansi musanalankhule ndi mphunzitsi.

4. Musanafikire mphunzitsi, lembani mafunso amene mukufuna kufunsa, ndipo ndandalitsani zonulirapo zimene mukuyembekezera kukwaniritsa.

5. Nenani kaimidwe kanu mwamphamvu ndi momvekera bwino, ndiyeno gwirizanani ndi mphunzitsi kuona njira zogwira ntchito zimene zingatsatiridwe kufuna kuthetsa mavuto alionse.

6. Dziikeni m’malo mwa mphunzitsi. Dzifunseni zimene inuyo mukanachita mu mkhalidwe wake. Zimenezi zidzakuthandizani kugwirizana pa mfundo yokhutiritsa.

7. Mvetserani ndiponso lankhulani. Musawope kufunsa mafunso ngati simukumvetsetsa chinachake. Ngati simukugwirizana ndi zimene zikunenedwa, nenani choncho, ndipo longosolani mwaulemu chifukwa chake.

—Zozikidwa pa Help Your Child Through School, lolembedwa ndi Dr. David Lewis.

[Chithunzi patsamba 9]

Ŵerengani ndi mwana wanu

[Chithunzi patsamba 9]

Onanani ndi aphunzitsi kuti mukambitsirane makosi a sukulu

[Chithunzi patsamba 9]

Thandizani mwana wanu kusankha maphunziro

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena