Mvuu pa Ntchito Yopulumutsa!
YOLEMERA kufikira kumatani anayi, mvuu ili nyama yoyamwitsa yachiŵiri mu ukulu pa za pamtunda. Mano ake amphamvuwo angathe kuphwanya bwato mwa kuluma kamodzi kokha. Motero, kagulu kena ka amuna ku Hwange National Park, Zimbabwe, kanadabwa kwambiri pamene kanaona mvuu ikuchita zinthu mumkhalidwe umene unawachititsa chidwi ndi wachilendo—kunena mosawonjezera mawu.
Amunawo, pamene anali pafupi ndi dziŵe, anaona nswala ziŵiri zikuthamangitsidwa kowopsa ndi mimbulu isanu ndi inayi. Pokhala zosoŵa kothaŵira, nswalazo zinalumphira m’madzi. Mimbuluyo inathamanga m’mbali mwa madzimo, ikumayembekezera pamene nswalazo ziti zitulukire.
Ndiyeno, nswala ina yotopa inayamba kusambira kumka kutsidya lakutali, yosazindikira kuti mimbuluyo inali kuyembekezera kumeneko. Komabe, pamene nswalayo inayandikira kumtunda, amunawo anaona mvuu pafupipo ikumasambira kumka kwa nswalayo. Itaipeza, magazini a African Wildlife akusimba kuti, mvuuyo “inaitembenuza ndi kuikankha bwinobwino kuti isambire kumka kwina.” Nswalayo inamvera. Mvuuyo inatsatira, ikumaikankha panthaŵi ndi nthaŵi pamene nswalayo inafuna kumka kwina.
Pamene nswalayo inafika kolekezera madzi, amunawo anapenyerera mvuuyo ikukankhira nswalayo kutsidya bwinobwino komabe mwamphamvu. Nswalayo inayenda mapazi angapo modzandira, ndiyeno inaima ikumanjenjemera. Posapita nthaŵi, nswalayo inayamba kupita. Mvuuyo inatsatira kufikira nyama ziŵirizo zinazimiririka.
Kodi nchiyani chimene chinachitikira nswala ina ija? Amunawo akusimba kuti mimbuluyo “inamwerekera kwambiri ndi kuonerera kupulumutsako kwakuti nswala inayo inathaŵa mosaonedwa.”