Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 11/8 tsamba 24-25
  • Akristu Oona ndi Nkhondo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akristu Oona ndi Nkhondo
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Akristu Oona Lerolino Alipo?
  • Kodi Zidzatheka Kuti Anthu Onse Adzakondanedi?
    Galamukani!—1998
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sapita Kunkhondo?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chakuti Nkhondo Idzatha?
    Galamukani!—1993
  • N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizimenya Nawo Nkhondo?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 11/8 tsamba 24-25

Akristu Oona ndi Nkhondo

YESU anauza ophunzira ake kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34) Kodi Akristu oona angasonyeze chikondi chotero kwa wina ndi mnzake ndipo panthaŵi imodzimodziyo akumapita kunkhondo kukaphana wina ndi mnzake?

Lingaliraninso funso limene linafunsidwa ndi mtumwi Paulo lakuti: “Kodi Kristu wagaŵika?” (1 Akorinto 1:13) Dzifunseni kuti: ‘Kodi pangakhalenso kugaŵanika koipitsitsa koposa kumene kumachitika pakati pa ziŵalo za chipembedzo chimodzimodzi zomaphana?’

Ndithudi, sitiyenera kudabwa kudziŵa kuti Akristu oyambirira sanapite kukamenya nkhondo. Encyclopædia of Religion and Ethics ya Hastings yotchuka inati: “Lingaliro lakuti nkhondo ndiyo tchimo lolinganizidwa limene Tchalitchi ndi otsatira a Kristu ayenera kupeŵa kotheratu linali lofala kwambiri m’Tchalitchi choyambirira.”

Akristu oyambirira anakhala ndi moyo mogwirizana ndi lamulo la Yesu la kukondana. Katswiri wophunzitsa zaumulungu wa ku Germany Peter Meinhold anafotokoza kuti: “Pamene kuli kwakuti Chipangano Chatsopano sichimanena kanthu za nkhani yakuti kaya Akristu ayenera kapena sayenera kukhala asilikali ndi kuti kaya ayenera kuleka usilikali pamene akhala Akristu, tchalitchi chakalecho chinachirimika pankhaniyi. Kukhala Mkristu ndi msilikali kunaonedwa kukhala kosagwirizana.” Kodi lerolino pali aliyense amene amachirimika monga aja a “tchalitchi chakale” ?

Kodi Akristu Oona Lerolino Alipo?

Encyclopedia Canadiana imati: “Ntchito ya Mboni za Yehova ndiyo kuyambitsidwanso ndi kukhazikitsidwanso kwa Chikristu chakale chochitidwa ndi Yesu ndi ophunzira ake mkati mwa zana loyamba ndi lachiŵiri la nyengo yathu. . . . Onsewo ali abale.”

Kodi zimenezo zimachitidwa motani? “Mboni za Yehova zimasunga uchete mwamphamvu mu nthaŵi ya nkhondo,” ikutero Australian Encyclopædia. Pamene kuli kwakuti, iwo angasankhe kaimidwe kameneka, monga munthu aliyense payekha samaloŵerera m’nkhani za boma limene amakhalamo. Chifukwa chake iwo sanachirikize nkhondo ya Hitler, motero palibe aliyense wa iwo amene analangidwa mkati mwa kuzenga milandu kwa ku Nuremberg monga apandu ankhondo.

Mjeremani wina amene anapezedwa ndi mlandu ndi kuphedwa anali Alfred Rosenberg, mkulu wa Dipatimenti Yoona Nkhani Zakunja ya Chipani cha Nazi. Pochinjiriza lamulo la Nazi la kuika Mboni za Yehova m’misasa yachibalo, Rosenberg anasonyeza m’kuimbidwa kwake mlanduko kuti: “Mbusa wina Wachimereka mokoma mtima wandipatsa nyuzipepala ya tchalitchi ya ku Columbus [Ohio] m’chipinda changa cha ndende. Kuchokera mmenemo ndaona kuti United States nayenso, anamanga Mboni za Yehova mkati mwa nkhondo ndi kuti kufikira December 1945, zokwanira 11,000 zinali zikali m’ndende.” Nzoona kuti Mboni za Yehova zakhala zauchete mwamphamvu, zosachirikiza mbali ina m’mikangano ya ndale. Sizinakhetse mwazi uliwonse, mu Nkhondo Yadziko II kapena m’nkhondo ina iliyonse.

Ku Hungary, wolemba nkhani m’magazini a Ring a November 4, 1992, anati ponena za Mboni za Yehova: “Angasankhe kufa koposa kupha munthu wina. Chotero, ndikhulupirira kuti ngati Mboni za Yehova zokha ndizo zinakhala pa dziko lapansi pamenepo nkhondo sizikanabuka kulikonse.” Reo M. Christenson, profesa wa sayansi ya ndale, anafotokoza mu The Christian Century ngati Mkristu weniweni angayenere kukhala ndi phande mu nkhondo, ndipo iye anati:

“Kodi pali aliyense amene angaganizire Yesu kukhala akuponya mabomba a m’manja kwa adani ake, akumagwiritsira ntchito mfuti yachiwaya, akumagwiritsira ntchito chida choponya malaŵi, akumaponya pansi mabomba a nyukliya ndi ndege kapena akumaponya chida cha ICBM chimene chingaphe kapena kupundula anakubala ndi ana zikwi zambiri? Funsolo nlachibwana kwambiri kwakuti nlosafunikira yankho. Ngati Yesu sakanachita zimenezi nakhala monga momwe analili, nangano ndimotani mmene ife tingachitire zimenezi ndi kukhala monga momwe iye alili?” Funso lotokosa maganizodi.

Komabe, zipembedzo za dziko zikupitirizabe kuchirikiza mbali ina mu nkhondo. Akatolika akupitirizabe kupha Akatolika, ndipo a zipembedzo zina amapha anthu a chipembedzo chawo kapena ziŵalo za matchalitchi ena. Kutsatira ziphunzitso za Yesu Kristu kumafuna kutsimikiza mtima kwamphamvu ndi kulimba mtima, monga momwe nkhani yochitikadi yotsatirayo idzasonyezera.

[Chithunzi patsamba 25]

Kodi pali aliyense amene angaganizire Yesu kukhala akugwiritsira ntchito mfuti yachiwaya ku nkhondo?

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi cha National Archives ya United States

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena