Kudzipangira Ntchito m’Maiko Osatukuka
YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! MU SENEGAL
ATATE a mtsikana wina anafa pamene iye anali mwana, nasiya amayi a mtsikanayo ndi banja lalikulu la ana asanu ndi atatu. Tsopano popeza kuti amayi akewo akukalamba, mtsikanayo ayenera kuthandiza kusamalira banja mwa kupeza ntchito. Chiyembekezo chake cha kupitiriza sukulu chathera pamenepo. Afunikira kugwira ntchito, ngakhale kuti alibe maluso antchito kapena maphunziro.
Mikhalidwe yonga umenewu njofala m’maiko osatukuka. Ntchito nzovuta kupeza, ngakhale kwa amene ali ndi madigiri a ku yunivesite. Komabe, ambiri amene ali ofunitsitsa ndi okonda kugwira ntchito akhala okhoza kudzipangira ntchito. Mwinamwake ntchito zoterozo sizingalemeretse munthu, koma Baibulo limati pa 1 Timoteo 6:8: “Pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”
Tikumakumbukira mawu achilangizo oyenera amenewo, tiyeni tipende njira zina zaluso zimene Akristu okhala m’maiko osatukuka achirikizira moyo wawo ndi kupita patsogolo.
Bizinesi ya Chakudya—ya Mtundu wa mu Afirika
Chakudya chimafunidwa nthaŵi zonse. Kuno ku West Africa, akazi ochita malonda apeza njira zosiyanasiyana zochititsa chidwi zochititsa ntchito imeneyi kukhala yopezetsa phindu. Mwachitsanzo, ena amamanga kamsasa pafupi ndi malo antchito yomanga namaphikira antchitowo chakudya chamasana. Ena amakonzera chakudya anthu odutsa ndi njira omapita kuntchito mmaŵa. Iwo amaika thebulo yaing’ono ndi mabenchi, akumaŵiritsa madzi pa mbaula, ndi kugulitsa mfisulo wosavuta kukonza—khofi wotentha ndi buledi wa batala. Madzulo amatsegulanso kashopo kawoko ndi kugulitsa zakudya zazing’ono kwa antchito ataŵeruka. Kuyendetsa lesitilanti ya mtundu umenewu kumafuna kukhala ndi ndandanda yopanikiza, koma imakhozetsa anthu akhama kupeza ndalama zokhalira moyo.
Palinso mwaŵi wa kugulitsa zakudya zopepuka. Akazi ena amafuna malo ochulukapo anthu pafupi ndi msika ndipo amakazinga mtedza. Mafayata—mapayi ang’onoang’ono anyama a msunzi wa tsabola—amayendanso kwambiri. Choteronso masangweji a msuzi wanyama woikidwa zonunkhira. Zimenezi ndi zinthu zogulidwa mwamsanga m’maiko a mu Afirika onga Gambia ndi Mali.
Mu Guinea-Bissau ndi Senegal, achichepere ambiri omwe ali Mboni za Yehova amadzichirikiza mu utumiki wa nthaŵi yonse mwa kuphika ndi kugulitsa chakudya china chokondedwa: makeke ang’onoang’ono. Moses, wokhala mu Dakar, likulu la Senegal, akufotokoza kuti: “Ine ndi mkazi wanga tinali kutumikira monga apainiya apadera [alaliki anthaŵi yonse] pamene tinayamba kukhala ndi ana. Tsopano ndinafunikira kupeza njira yowasungira, motero ndinaganiza za kumapanga makeke ang’onoang’ono ndi kumagulitsa.
“Ndinali ndi ndalama zochepa kwambiri zoyambira, choncho ndinafunikira kusamala kusiyanitsa ndalama zomwe ndikafunikira kusunga monga phindu ndi zimene ndinafunikira kuikanso m’bizinesi kugulira zofunika, zonga ufa wa tirigu ndi mazira. Tsopano ndimakhoza kugulitsa makeke okwanira kupezera zofunika za banja langa laling’ono.
“Kuti athandizire, mkazi wanga, Esther, amasoka madiresi panyumba. Zimenezi zimamulola kukhala panyumba ndi anyamata athu aŵiri aang’ono. Motero aŵirife mothandizana, tili okhoza kusamalira bwino banja lathu, mosasamala kanthu kuti tikukhala m’nthaŵi zovuta.”
Nali lingaliro lina la bizinesi yaing’ono: Popeza kuti anthu ogwira ntchito amakhala otanganitsidwa ndipo kaŵirikaŵiri samakhala ndi nthaŵi yoyenda mtunda wautali kupita ku msika, iwo angakonde kumagula pamalo apafupipo zipatso kapena ndiwo zamasamba. Eni malo ogulitsira ena amachita mautumiki operekera zinthu, akumapereka ndiwo zamasamba zaziŵisi pamakomo penipeni pa makasitoma awo. Mbiri imafalikira mofulumira yakuti ndinu woona mtima ndi kuti mumagulitsa zinthu zabwino. Komabe, samalani kuti musamadulitse kwambiri, chifukwa anthu angaleke ndi kubwerera kumsika wa nthaŵi zonse.
Ntchito Zotumikira
Ngati kugulitsa zinthu zolimidwa sikukukomerani, lingalirani za kuchita mautumiki osiyanasiyana. Ntchito yapanyumba, yonga kuyeretsa, kuphika, ndi kuchapa ndi kusita zovala, zimapezeka nthaŵi zonse. Ndipo palinso mipata ina yambiri.
Mwachitsanzo, kodi mumakhala pafupi ndi nyanja yamchere kapena pafupi ndi msika wa nsomba? Bwanji osapempha ntchito ya kukonza nsomba—mwamsanga ndipo pamalipiro otsikirapo? Zimene mungofunikira ndizo thabwa lalikulu labwino ndi mpeni wabwino. Kutsuka galimoto kulinso ntchito ina yopezetsa phindu. Kodi pamafunikira zipangizo zanji? Bekete, madzi, sopo pang’ono, ndi nsalu yabwino. Mu Dakar, achichepere okonda bizinesi angaonedwe pafupifupi pamalo alionse oikapo galimoto ndi pamakwalala ochingidwa ambiri akumachita ntchito imeneyi.
Kodi madzi a pampope ali ovuta m’mbali yanu ya dziko? Nthaŵi zina akazi amaima pamizera kwa maola ambiri pampope umodzi wa anthu onse kuti adzaze zotengera zawo. Ndiyeno amanyamula mitsuko yolemera pamutu pawo mtunda wonsewo kupita kunyumba. Motero ambiri ali ofunitsitsa kulipira munthu amene angawanyamulire madzi. Chinsinsi chake ndicho kufika potunga madzipo mmamaŵa kotero kuti mudzaze zotengera zanu ndi kuziika pa wilibala kapena ngolo yokokedwa ndi abulu. Ndiyeno mukhoza kupereka madziwo ku nyumba za anthu kapena malo antchito.
Kodi muli ndi maphunziro a kusukulu? Mwinamwake mungadzipereke kuphunzitsa ana aang’ono kumapeto a mlungu. Kaŵirikaŵiri makalasi amadzala kwambiri m’maiko osatukuka, ndipo makolo angakonde kumalipira kuti ana awo apatsidwe chithandizo chaumwini.
Luso lina lothandiza limene mungakhale nalo kale ndilo la kuluka tsitsi. Popeza kuti njira zolukira tsitsi nzokondedwa kwambiri pakati pa akazi mu Afirika, malonda alipo kwa anthu okhala ndi luso la ntchito imeneyi.
Kugwiritsira Ntchito Nzeru
M’nthaŵi za Baibulo, mkazi waluso anali wokhoza kupeza njira zanzeru zopezera ndalama. Miyambo 31:24 imati: “Asoka malaya abafuta, nawagulitsa; napereka mipango kwa wogulitsa malonda.” Mofananamo, ambiri m’maiko osatukuka apeza chipambano cha kuyendetsa timaindasitale toteroto, kapena timabizinesi tating’ono. Mwachitsanzo, wopala matabwa angamange kashopo kantchito ndi kumapanga mipando yosavuta, mabenchi, ndi zinthu zina za m’nyumba. Zipangizo zoyambira zokha nzimene zimafunikira. Ngati munaphunzira za ulimi, mwinamwake mungayambe malonda osunga nkhuku ndi kumagulitsa mazira ndi nkhuku.
Nzeru njofunikira kwambiri poyamba timaindasitale tating’ono. Anthu ena atenga zitini zotaidwa ndi kupanga masutukesi okongola ndi mabokosi onyamulira. Ena apanga nsapato ndi matayala a galimoto. Enanso atenga mapaipi achitsulo ndi kupanga mabekete. Zothekera nzambiri, koma zimangodalira pa nzeru yanu yoganizira zinthu.
M’maiko osatukuka muyenera kukhala ndi luso lantchito ndi nzeru yoganizira zinthu kuti mukhale ndi moyo, koma mufunikiranso kuleza mtima ndi mkhalidwe wabwino wa maganizo. Musabwevuke msanga. Khalani wokhoza kusintha, wokonzekera kusintha ntchito ngati kuli kofunika. Ngati mukuyamba bizinesi kapena ntchito yotumikira, tsimikizirani kufunsira za malamulo a kumaloko ndi malamulo aboma. Akristu afunikira kulemekeza lamulo la dziko.—Aroma 13:1-7.
Musanayambe kugulitsa chinthu kapena kuchita ntchito yotumikira, dzifunseni kuti: ‘Kodi zosoŵa ndi miyambo ya kumaloko nzotani? Kodi mkhalidwe wa chuma kumaloko uli wotani? Kodi makasitoma angakhoze kugula zogulitsa zanga? Kodi pali angati amene akugulitsa chinthu chimodzimodzi kapena kuchita utumiki umodzimodzi? Kodi ndilidi ndi maluso antchito, nyonga, chidziŵitso, kudziletsa, ndi dongosolo lofunikira kuchita malonda ameneŵa? Kodi padzafunikira ndalama zingati zoyambira? Kodi ndidzafunikira kukongola? Kodi ndidzakhala wokhoza kubweza ngongoleyo?’
Funso la Yesu pa Luka 14:28 lili loyenera: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?”
Zoona, sionse omwe ali ndi maluso kapena mtima wakudzilemba okha ntchito. Komabe Yehova Mulungu akhoza kudalitsa nzeru yanu ndi zoyesayesa zanu zakhama pamene zichitidwa ndi cholinga chabwino. (Yerekezerani ndi 2 Petro 1:5.) Motero chitani zonse zomwe mungathe kuti mupeze ntchito—ngakhale yodzipangira inu mwini!
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Kusoka madiresi, kutsuka galimoto, kuperekera madzi abwino, ndi kukonza nsomba zili njira zina zimene anthu amakhalira moyo