Kodi Ndinu Womvetsera Wachifundo?
TAYEREKEZERANI kuti munali wachuma wokhoza kupatsa munthu aliyense mphatso ya mtengo wapatali m’moyo wanu. Ha, iwo angakhale achimwemwe ndi oyamikira chotani nanga! Kunena zoona, inu mungathe kupatsa ena mphatso yapadera, kanthu kena kamene amafunikiradi. Sikangafune ndalama iliyonse kwa inu. Kodi iko nchiyani? Kutchera khutu kwanu. Anthu ochuluka amafuna kutcheredwa khutu ndipo amachita moyamikira pamene asonyezedwa mkhalidwewo. Komabe, kuti musonyeze kutchera khutu kwabwino, muyenera kukhala womvetsera wachifundo.
Ngati muli kholo kapena wolemba ntchito kapena pamalo alionse amene anthu ena amafika kwa inu kudzapempha chilangizo ndi chitsogozo, mufunikira kumvetsera mwachifundo. Ngati simutero, anthu adzaona kupanda chifundo kwanu, ndipo mbiri yanu idzaipa.
Ngakhale ngati simupemphedwa kaŵirikaŵiri kupereka chilangizo, mufunikirabe kumvetsera mwachifundo, monga ngati pamene bwenzi lidza kwa inu kudzafuna chitonthozo. Monga momwe mwambi wa Baibulo umanenera, kulephera kumvetsera musanalankhule kungachititse manyazi. (Miyambo 18:13) Nangano, kodi nziti zimene zili njira zina zimene mungadzisonyeze inu mwini kukhala womvetsera wachifundo?
Khalani Wodziloŵetsamo
Kodi womvetsera wachifundo ngwotani? Webster’s New Collegiate Dictionary imamasulira “chifundo” kuti: “Kukhoza kudziloŵetsa m’malingaliro kapena maganizo a munthu wina.” Dikishonale imodzimodziyo imamasulira “kumvetsera” kuti: “Kumva ndi kulingalira kosamalitsa.” Chotero womvetsera wachifundo amachita zambiri koposa kungomva chabe zimene wina akunena. Iye amatchera khutu ndi kudziloŵetsa m’malingaliro a munthuyo.
Zimenezi zimafuna kuti mukhale wodziloŵetsa m’zimene mukumva, osalola maganizo anu kuyendayenda. Ngakhalenso kuganiza za mmene mudzayankhira kumadodometsa kumvetsera. Dziphunzitseni kusumika maganizo pa zimene munthu winayo akunena.
Yang’anani kumaso kwa munthu amene akulankhula ndi inuyo. Ngati mucheukacheuka, mudzaonedwa kukhala wosakondweretsedwa. Yang’anitsitsani majesichala ake ndi mmene thupi lake likuchitira. Kodi iye akumwetulira kapena akuchita tsinya? Kodi maso ake akusonyeza kusangalala, chisoni, kapena mantha? Kodi zimene akusiya zosanenedwa nzofunika? Musavutike mtima ndi yankho lanu; lidzabwera lokha pamene mumvetsera mosamalitsa.
Pamene mukumvetsera, mwinamwake mudzakhala mukuvomereza ndi mutu ndi kunena mawu ovomereza, onga akuti ‘Oo!’ ndi ‘Kodi!’ Zimenezi zingasonyeze kuti mukutsatira nkhaniyo. Komabe, musaganize kuti kuvomereza ndi mutu kapena ndi mawu kudzapangitsa anthu kuganiza kuti mukumvetsera ngati simukuterodi. Kunena zoona, kumangovomereza kaŵirikaŵiri ndi mutu kungasonyeze kusaleza mtima. Kuli monga ngati kuti mukunena kuti, ‘Fulumira. Nena msanga. Maliza.’
Muli monse mmene zilili, simufunikira kukhala ndi nkhaŵa yopambanitsa ponena za mchitidwe wake. Ingomvetserani moona mtima, ndipo kulabadira kwanu kudzasonyeza kuona mtima kwanuko.
Mafunso abwino amasonyezanso kuti mwadziloŵetsa m’nkhaniyo ndipo mukuitsatira. Amasonyeza kuti muli ndi chifuno. Funsani kuti mumvetsetse mfundo zimene sizinanenedwe kapena zosamveka bwino. Funsani mafunso amene amachititsa munthu kufotokoza mwatsatanetsatane ndi kusimba za kukhosi kwake mowonjezereka. Musadere nkhaŵa kuti mwina mungakhale mukudodometsa, koma musachite mopambanitsa. Kumvetsetsa bwino zinthu kuli mbali ya mchitidwe wa kumvetsera. Ngati kudodometsa kuchitidwa mosapambanitsa, munthu winayo adzayamikira kufuna kwanu kumvetsera bwino lomwe zinthu zonse zimene akunena.
Sonyezani Kumvetsetsa
Imeneyi ingakhale mbali yovuta kwambiri, ngakhale ngati inu moonadi muchitira chifundo munthu amene akulankhula kwa inuyo. Pamene munthu wopsinjika mtima adza kwa inu, kodi mumangofikira kupereka malingaliro ndi mayankho osonyeza kuti zinthu zidzakhala bwino? Kodi mumafulumira kuuza munthuyo kuti mkhalidwewo suli woipa kwambiri pouyerekezera ndi kuvutika kwa munthu wina? Zimenezitu zingaonekere ngati kuti nzothandiza, koma zingakhale ndi chiyambukiro choipa.
Pali zifukwa zingapo zimene zingakuchititseni kuleka kumvetsera ndi kuyamba kuthetsa vuto. Mungaganize kuti malingaliro anu abwinowo ndiwo amene akungofunika kuchititsa wovutikayo kumva bwino. Kapena mungalingalire kuti ndi thayo lanu “kukonza” “cholakwa” chilichonse, ndi kuti ngati simutero, simukukhala wothandiza kapena “simukuchita thayo lanu.”
Komabe, kaŵirikaŵiri kupereka mwamsanga mayankho kumaonedwa monga mukunena kuti, ‘Ndikuona kuti vuto lanu silalikulu kwambiri monga mmene mukunenera.’ Kapena, ‘Ndimakonda kwambiri kudziŵika kwanga monga wothetsa mavuto koposa ndi ubwino wanu.’ Kapena, kuti, ‘Sindikumvetsetsa nkomwe—ndipo sindikufuna kutero.’ Kuyerekezera vuto la wovutikayo ndi la ena kaŵirikaŵiri kumaonedwa monga kunena kuti, ‘Mulibe ndi manyazi omwe kuti mukuvutika ndi zimenezo pamene anthu ena akuvutika ndi mavuto enieni.’
Ngati mupereka mauthenga olefulitsa otero mosadziŵa, bwenzi lanulo lidzalingalira kuti simunalimvedi, kuti silikumvedwa. Iye angaganize kuti mukulingalira kuti muli womposa. Panthaŵi ina, iye adzakafuna chitonthozo kwa munthu winawake.—Afilipi 2:3, 4.
Bwanji ngati bwenzi lanulo likuvutika mosafunikira? Mwachitsanzo, iye angamve kukhala waliwongo popanda chifukwa chenicheni. Kodi muyenera kufulumira kumuuza zimenezo kuti apeze bwino? Ayi, chifukwa ngati simunamvetsere kwa iye choyamba, mawu anu sadzakhala otonthoza kwenikweni. M’malo mwa kukhala wotonthozedwa, adzaona kuti sanapepukiridwe, kuti adakali waliwongo. Monga momwe wafilosofi wina wa m’zaka za zana la 19 Henry David Thoreau ananenera, “kunena choonadi kumafuna anthu aŵiri: wina wochinena ndipo wina wochimva.”
Nchoyenera chotani nanga chitsogozo cha Baibulo chakuti: ‘Khalani wotchera khutu, wodekha polankhula.’ (Yakobo 1:19) Ndiponso kumvetsera ndi chifundo nkofunika kwambiri! Dziloŵetseni m’malingaliro a munthu amene akukudandaulirani. Vomerezani vuto lake, ukulu wa nsautso yake. Musachepetse vuto lake ndi mawu onga akuti, ‘Ndiyesa mwangokhala ndi tsiku lovuta’ kapena, ‘Sizovuta kwenikweni.’ Ndiponso, kuchepetsa vuto kotero kungakulitsedi malingaliro ake ovutikawo. Ndipo adzakhala wogwiritsidwa mwala chifukwa chakuti simukuona lingaliro lake mwamphamvu. Chotero lolani kuti mayankho anu asonyeze kuti mukumva zimene zikunenedwa ndi kuti mukuvomereza kuti umu ndimo mmene akumvera zinthu kwatsopano lino.
Kumvetsera kwachifundo sikumafuna kuti mungovomereza zonena za wokudandauliraniyo. Mungaone kuti sizoona pamene iye akunena kuti, “Ndimada ntchito yanga!” Koma ngati munena mawu otsutsa (‘Simuyenera kulingalira choncho’) kapena kulandula (‘Ayi ndithu simukunenetsa’), iye adzalingalira kuti simukumvetsetsa. Mawu anu ayenera kusonyeza kumvetsetsa kwanu. Kwa munthu amene amada ntchito yake, munganene kuti, ‘Iyenera kukhaladi yovutitsa maganizo.’ Ndiyeno pemphani kuti afotokoze mwatsatanetsatane. Motero inu kwenikweni simukuvomereza kuti iye ayenera kuda ntchito yake koma mukungovomereza chabe kuti ndimo mmene akumvera pakali pano. Mwa kutero, mukumpatsa chikhutiro cha kukhala womvedwa, cha kukhala atafotokoza mokwanira malingaliro ake. Kaŵirikaŵiri, kukambitsirana vuto ndi wina kungalichepetse.
Mofananamo, munthu amene anena kuti, “Mkazi wanga wakapimidwa kuchipatala lero,” angatanthauze kuti, “Ndikudera nkhaŵa.” Yankho lanu liyenera kusonyeza kuti mwadziŵa zimene akunena. Zimasonyeza kuti mwamvetsera tanthauzo la mawu ake, kumene kuli kotonthoza kwambiri kuposa ngati mukanangonyalanyaza tanthauzo lake, kulilandula, kapena kuyesa kumsintha mwa kumuuza kuti sayenera kudera nkhaŵa.—Aroma 12:15.
Omvetsera Abwino Amalankhulanso!
The Art of Conversation limafotokoza za awo amene amamvetsera komano amangolankhula pang’ono, “akumaganiza kuti kutero kumawapatsa kaonekedwe kolemekezeka.” Zimenezi zimachititsa munthu winayo kusenza mtolo wonse wa kukamba, ndipo chimenecho nchipongwe. Komanso, ngati munthu amene mukumumvetsera apitiriza kulankhula popanda kuima kuti akuloleni kukamba zakukhosi, chimenechonso nchipongwe, ndipo chimalefula munthu. Chotero, pamene kuli kwakuti mufunikira kukhala womvetsera wabwino, mungafunenso kulola munthu winayo kudziŵa kuti muli ndi kanthu kena kothandiza koti munene.
Kodi munganene chiyani? Pokhala mutamvetsera mwaulemu mawu a bwenzi lanulo, kodi tsopano muyenera kupereka chilangizo? Mwinamwake, ngati inu muli woyenerera kuchipereka. Ngati muli ndi njira yothetsera vuto la bwenzi lanu, ndithudi muyenera kukambitsirana naye. Mawu anu adzamlimbikitsa, popeza kuti choyamba mwapatula nthaŵi ya kumvetsera. Ngati simuli oyenerera kupatsa bwenzi lanu chilangizo chokoma mtima kapena thandizo limene akufunikira, yesani kumthandiza kuti aonane ndi wina wake amene ali woyenerera kuchita zimenezo.
Komabe, m’zochitika zina, chilangizo sichimafunika kapena kupemphedwa. Chotero, samalani kuti musafooketse chiyambukiro chabwino cha kumvetsera kwanu mwa kuwonjezerapo mawu ambirimbiri. Bwenzi lanu lingangofunikira kuti lipirire mkhalidwe wina wosalamulirika kapena kupeza nthaŵi ya kugonjetsa malingaliro ake osakondweretsawo. Iye wadza kwa inu kudzakambitsirana nanu za vuto lake. Inu mwamvetsera. Munakambitsirana naye malingaliro ake, munamtsimikizira kuti mukudera nkhaŵa ndipo mudzakhala mukumkumbukira m’malingaliro ndi m’mapemphero. Muuzeni kuti akhale waufulu kudzakufikiraninso ndi kuti mudzasunga chinsinsi cha mavuto ake. Mwinamwake angafunikire chitonthozo chotero m’malo mwakuti muthetse mavuto ake.—Miyambo 10:19; 17:17; 1 Atesalonika 5:14.
Kaya kumvetsera kukuloŵetsamo chilangizo kapena ayi, kumapindulitsa onse aŵiriwo. Amene akulankhulayo amakhala ndi chikhutiro cha kukhala atamvedwa ndi kumvetsetsedwa. Amatonthozedwa podziŵa kuti winawake amasamala kumumvetsera. Nayenso womvetserayo amapindula. Ena amazindikira nkhaŵa yake. Ngati apereka chilangizo, chimakhaladi choyamikirika kwambiri chifukwa chakuti iye samalankhula kufikira atazindikira mokwanira mkhalidwe wofotokozedwa kwa iye. Nzoona kuti kumvetsera mwachifundo kumafunikira nthaŵi. Koma ndi kopindulitsa chotani nanga kumeneku! Ndithudi, mwa kutchera khutu kwa anthu, mumawapatsa mphatso yapadera.