Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 1/8 tsamba 12-17
  • Kusamalira Ovutika ndi Tsoka la ku Rwanda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusamalira Ovutika ndi Tsoka la ku Rwanda
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mapeto Adzidzidzi a Mkhalidwe Wabata
  • Anayesayesa Kuthandizana
  • Kusayambukiridwa ndi Udani wa Fuko
  • Kuvutika Kosaneneka
  • Kuchitapo Kanthu Mwamsanga pa Kuvutika
  • Kulimbana ndi Matenda
  • Anthu Oyamikira ndi Auzimu
  • Chisamaliro Chopitirizabe Chikufunika
  • Tsoka ku Rwanda—Ndani Amene Ali ndi Mlandu?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Ntchito Zachikristu Pakati pa Chipwirikiti
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Mmene Tinapulumukira Zoopsa Phiri Litaphulika N’kumatuluka Chiphalaphala!
    Galamukani!—2002
  • Kodi Zipembedzo Mungazikhulupirire pa Nkhani ya Nkhondo?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 1/8 tsamba 12-17

Kusamalira Ovutika ndi Tsoka la ku Rwanda

RWANDA, wopezeka chapakati pa Afirika, watchedwa “Switzerland wa mu Afirika.” Maonekedwe a msipu wobiriŵira kwa anthu ouluka m’ndege pamwamba pa dzikolo amawakumbutsa za munda wa Edene. Nzosadabwitsa kuti Rwanda ankatchedwa paradaiso.

Panthaŵi ina, pa mtengo uliwonse umene unalikhidwa, iŵiri inabzalidwa. Tsiku limodzi pachaka linapatuliridwa kukhala la kubwezeretsa nkhalango. Mitengo ya zipatso inabzalidwa m’mbali mwa misewu. Kuyenda m’dzikolo kunali kwaufulu ndi kosavuta. Misewu yaikulu imene inagwirizanitsa zigawo zina ndi likulu, Kigali, inali yaphula. Likululo linali kufutukuka mofulumira. Wantchito wamba analandira malipiro okwanira pakutha kwa mwezi opezera zofunika za moyo.

Ntchito Yachikristu ya Mboni za Yehova inali kupitanso patsogolo mu Rwanda. Kuchiyambi kwa chaka chathachi, Mboni zoposa 2,600 zinali pantchito ya kupereka mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu kwa anthu a dzikolo okwanira pafupifupi mamiliyoni asanu ndi atatu, amene unyinji wa iwo ndi Akatolika. (Mateyu 24:14) M’March Mboni zinali kuchititsa maphunziro a Baibulo oposa 10,000 m’nyumba za anthu. Ndipo panali mipingo 15 mkati ndi kuzungulira Kigali.

Woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova anati: “Mu November 1992, ndinali kutumikira mipingo 18. Koma pofika mu March 1994, inawonjezeka kufika 27. Chiŵerengero cha apainiya (atumiki anthaŵi yonse) chinali kuwonjezekanso chaka chilichonse.” Pa Loŵeruka, March 26, 1994, ofika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu anali 9,834.

Ndiyeno, mwadzidzidzi, mkhalidwe unasintha kowopsa mu Rwanda.a

Mapeto Adzidzidzi a Mkhalidwe Wabata

Pa April 6, 1994, cha m’ma 8:00 p.m., pulezidenti wa Rwanda ndi wa Burundi, onse Ahutu, anafa pamene ndege inagwa mu Kigali. Usiku umenewo mapintu a apolisi anamveka kulikonse m’likululo, ndipo misewu inatsekedwa. Ndiyeno m’maola a mbandakucha, asilikali ndi amuna onyamula zikwanje anayamba kupha anthu Achitutsi. Ntabana Eugène—woyang’anira mzinda wa Mboni za Yehova mu Kigali—mkazi wake, mwana wake wamwamuna, ndi mwana wake wamkazi anali pakati pa oyamba kuphedwa.

Banja lina Lachizungu la Mboni za Yehova linali litaphunzira Baibulo ndi anansi angapo Achitutsi. Asanu ndi anayi a anansi ameneŵa anabisala m’nyumba ya Azunguwo pamene akupha olusawo anapita kunyumba ndi nyumba. Patangopita mphindi zingapo, ofunkha okwanira 40 anali ataloŵa kale m’nyumbamo, akumaswa zinthu ndi kugubuduza mipando. Mwachisoni, anansi Achitutsiwo anaphedwa. Komabe, enawo, ngakhale kuti anayesayesa kupulumutsa anzawo, analoledwa kuthaŵitsa miyoyo yawo.

Kupululutsako kunapitiriza kwa milungu yambiri. Potsirizira pake, Arwanda okwanira 500,000 kapena kuposerapo anaphedwa. Zikwi zambiri anathaŵa, makamaka Atutsi. Ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ya ku Zaire inadziŵitsa abale ku France za chosoŵa chawo cha katundu wothandiza. “Tinapempha ngolo imodzi ya zovala zakale,” ikufotokoza motero nthambi ya Zaire. “Abale ku France atitumizira ngolo zisanu za zovala ndi nsapato zomwe zambiri zinali zatsopano.” Pa June 11, matani 65 a zovala anatumizidwa. Nthambi ya ku Kenya inatumiziranso othaŵawo zovala ndi mankhwala, limodzinso ndi magazini a Nsanja ya Olonda ya m’chinenero chawo.

Pofika mu July, gulu lankhondo la Atutsi, lotchedwa Rwandan Patriotic Front, linali litagonjetsa gulu lankhondo la boma la Ahutu. Pambuyo pa zimenezo, zikwi mazana za Ahutu anayamba kuthaŵa kuchoka m’dzikomo. Panakhala chipwirikiti pamene Arwanda mamiliyoni aŵiri kapena kuposerapo anathaŵira m’misasa yomangidwa mofulumira m’maiko apafupi.

Anayesayesa Kuthandizana

Aŵiri mwa asanu ndi mmodzi amene ankagwira ntchito mu Ofesi Yotembenuza Chinenero ya Mboni za Yehova mu Kigali anali Atutsi—Ananie Mbanda ndi Mukagisagara Denise. Zoyesayesa za abale Achihutu za kuwatetezera zinakhala zachipambano kwa milungu ingapo. Komabe, chakumapeto kwa May 1994, Mboni Zachitutsi ziŵiri zimenezi zinaphedwa.

Ataika miyoyo yawo pachiswe, ndipo ngakhale pangozi, Mboni za Yehova zinayesayesa kutetezera Akristu anzawo a fuko lina. (Yohane 13:34, 35; 15:13) Mwachitsanzo, Mukabalisa Chantal ndi Mtutsi. Pamene ziŵalo za Rwandan Patriotic Front zinali kufunafuna Ahutu m’sitediyamu mmene iye anali kukhala, anachinjiriza anzake Achihutu. Ngakhale kuti zigaŵengazo zinakwiya ndi zoyesayesa zakezo, chimodzi cha izo chinati: “Inu Mboni za Yehova muli ndi ubale wolimbadi. Chipembedzo chanu nchabwino kuposa zonse!”

Kusayambukiridwa ndi Udani wa Fuko

Zimenezo sizikutanthauza kuti Mboni za Yehova sizimakhudzidwa konse ndi maudani a fuko amene akhalapo kwa zaka mazana ambiri m’mbali imeneyi ya Afirika. Mboni yochokera ku France imene inali kugwira ntchito yopereka katundu wa chithandizo inati: “Ngakhale abale athu Achikristu ayenera kuyesayesa zolimba kuti apeŵe kuyambukiridwa ndi udani, umene wasonkhezera kuphana kosaneneka kumeneku.

“Tinakumana ndi abale omwe anaona mabanja awo akuphedwa pamaso pawo. Mwachitsanzo, mlongo wina Wachikristu anali atakwatiwa kwa masiku aŵiri okha pamene mwamuna wake anaphedwa. Mboni zina zinaona ana awo ndi makolo akuphedwa. Mlongo wina, amene tsopano ali ku Uganda, anaona banja lake lonse likuphedwa, kuphatikizapo mwamuna wake. Zimenezi zimangosonyeza nsautso, ponse paŵiri yamaganizo ndi yakuthupi, imene yakantha banja lililonse la Mboni za Yehova.”

Zonse pamodzi, pafupifupi Mboni 400 zinaphedwa m’chiwawa cha udani wa fuko chimenechi. Chikhalirechobe, palibe aliyense wa ameneŵa amene anaphedwa ndi Mboni zinzake. Komabe, ziŵalo za Roma Katolika ndi za matchalitchi Achiprotesitanti Zachitutsi ndi Zachihutu zinapha zikwi zambiri. Mogwirizana ndi mbiri yawo yolembedwa, Mboni za Yehova kuzungulira padziko lonse sizimatenga mbali ndi pang’ono pomwe m’nkhondo, zipanduko, kapena mikangano ina yotero ya dzikoli.—Yohane 17:14, 16; 18:36; Chivumbulutso 12:9.

Kuvutika Kosaneneka

Chilimwe chapitachi, anthu kuzungulira dziko anaona zithunzi za kuvutika kwa anthu kosakhulupiririka. Zikwi mazana za othaŵa a ku Rwanda anaonedwa akuthaŵira m’maiko apafupi ndi kukhala kumeneko m’mikhalidwe yauve kwambiri. Mmodzi wa Mboni za Yehova wokhala pantchito yopereka katundu wa chithandizo wa ku France analongosola mkhalidwe umene gulu la nthumwi limene analimo linaona pa July 30 motere.

“Tinaona zinthu zowopsa kwenikweni. Kwa makilomita ambiri, mitembo inali ngundangunda m’mbali mwa msewu. Manda aunyinji anadzazidwa ndi mitembo zikwi zambiri. Fungo linali losapiririka pamene tinali kudutsa pakati pa mitembo ya anthu yovunda, ana akumaseŵera pafupi ndi mitemboyo. Panali mitembo ya makolo omwe ana awo anali adakali ndi moyo kumsana kwawo. Kukumbukira zinthu zotero mobwerezabwezera kumavutitsa maganizo kwambiri. Munthu amathedwa mphamvu chifukwa cha kusoŵa chochita, ndipo sangapirire poona ukulu wake wa zowopsa ndi wa kusakazako.”

Pamene othaŵa okwanira zikwi makumi ambiri anali kuthaŵira mu Zaire pakati pa July, Mboni za m’Zaire zinapita ku malire adziko ndi kunyamula kumanja zofalitsidwa za Baibulo kotero kuti abale awo Achikristu ndi okondwerera aŵadziŵe. Ndiyeno Mboni zothaŵa za ku Rwanda zinasonkhanitsidwa pamodzi ndi kutengeredwa ku Nyumba Yaufumu yapafupi ku Goma, kumene anasamaliridwa. Mboni zokhala ndi chidziŵitso cha zamankhwala zinagwira ntchito zolimba kuchepetsako nsautso ya odwala, ngakhale kuti panalibe mankhwala okwanira ndi zipangizo zoyenera.

Kuchitapo Kanthu Mwamsanga pa Kuvutika

Pa Lachisanu, July 22, Mboni za Yehova m’France zinalandira uthenga wa SOS wotumizidwa pa fax wochokera ku Afirika. Unalongosola mkhalidwe wothetsa nzeru wa abale awo Achikristu othaŵa ku Rwanda. Mkati mwa mphindi zisanu kapena khumi atalandira chidziŵitsocho, abale anaganiza za kulongedza mitokoma ya katundu wa chithandizo m’ndege ya katundu. Zimenezi zinawafikitsa ku mapeto a mlungu a ntchito yaikulu ya kukonzekera, makamaka chifukwa chakuti anali osazoloŵera kulongedza katundu wa chithandizo wochuluka motero panthaŵi yochepa.

Panali mzimu wabwino kwambiri wa kuchita chopereka ku thumba la chithandizo. Mboni za ku Belgium, France, ndi Switzerland zokha zinapereka zoposa pa $1,600,000. Katundu wa chithandizo anagulidwa, kuphatikizapo chakudya, mankhwala, ndi ziŵiya zopulumutsira, ndipo zonse zinaikidwa m’mabokosi ndi kulembedwapo ku malo a Mboni za Yehova mu Louviers, France, ndi mu Brussels, Belgium. Mboni zinagwira ntchito usana ndi usiku kukonzekeretsa katunduyo kuti atumizidwe ku Ostend, Belgium. Kubwalo la ndege, pa Lachitatu, July 27, matani oposa 35 analongedzedwa m’ndege yakatundu. Tsiku lotsatira katundu wocheperapo, makamaka wa mankhwala, anatumizidwa. Pa Loŵeruka, pambuyo pa masiku aŵiri, ndege ina inanyamula katundu wowonjezereka wa mankhwala a ovutikawo.

Mboni za ku France, kuphatikizapo dokotala, anapita ku Goma katundu wochuluka asanapite. Pa Lolemba, July 25, pamene Dr. Henri Tallet anafika ku Goma, pafupifupi Mboni 20 zinali zitamwalira kale ndi cholera, ndipo zina zinali kufabe tsiku ndi tsiku. Chifukwa chakuti katunduyo anafunikira kutumizidwa kudzera ku Bujumbura, Burundi, makilomita pafupifupi 250, sanafike ku Goma kufikira pa Lachisanu mmaŵa, pa July 29.

Kulimbana ndi Matenda

Panthaŵiyi, Mboni pafupifupi 1,600 ndi mabwenzi awo zinasonkhanitsidwa pamodzi pamalo pamene panali Nyumba Yaufumu yaing’ono mu Goma. Pakati pa anthu onseŵa, panali chimbudzi chimodzi chokha, madzi panalibe, ndipo panali chakudya chochepa kwambiri. Ambiri odwala cholera anapanikizana mu Nyumba Yaufumu. Chiŵerengero cha akufa chinali kukwera kwambiri.

Cholera imathetsa madzi onse m’thupi la munthu. Maso amakhala ombuŵa ndipo amagadabukira kumwamba. Ngati chithandizo chobwezeretsa madzi chiyamba kuperekedwa mwamsanga, munthuyo angachire pamasiku aŵiri. Motero, zoyesayesa zinapangidwa za kupatsa abale mankhwala ochepa omwe analipo obwezeretsa madzi m’thupi.

Ndiponso, abale anayesa kupatula odwalawo kuti asayambukitse matenda kwa ena. Anayesayesa kusamutsira othaŵawo kutali ndi malo oipa m’Goma. Malo oyenera anapezeka pafupi ndi Lake Kivu, kutali ndi fumbi ndi fungo la mitembo lodzaza m’mpweya.

Zimbudzi zinakumbidwa, ndipo malamulo amphamvu aukhondo anaikidwa. Amenewa anaphatikizapo kusamba m’manja m’beseni la mankhwala ndi madzi pochoka kuchimbudzi. Kufunika kwa mikhalidwe imeneyi kunagogomezeredwa, ndipo anthu anatsatira zimene anauzidwa kuchita. Mwamsanga mliri wa nthenda yakuphayo unalekeka.

Pamene katundu wochuluka wa chithandizo anafika pa Lachisanu, July 29, kachipatala kakang’ono kanakhazikitsiwa pa Nyumba Yaufumu mu Goma. Mabedi opinda okwanira 60 anaikidwa, limodzinso ndi ziŵiya zoyeretsera madzi. Ndiponso, mahema anaperekedwa kwa Mboni zimene zinaikidwa kugombe la Lake Kivu. M’nthaŵi yochepa, anakhoma mahema 50 m’mizera yowongoka ndi yadongosolo.

Panthaŵi ina pafupifupi Mboni 150 ndi mabwenzi awo anadwala kowopsa. Pofika mlungu woyamba wa August, oposa 40 anali atamwalira mu Goma. Koma mankhwala ndi chithandizo zinafika panthaŵi yake kuti apulumutse miyoyo ndi kuthetsa kuvutika kwakukuluko.

Anthu Oyamikira ndi Auzimu

Mboni zothaŵa zinasonyeza kuyamikira kwakukulu pa zonse zimene zinachitidwa kwa iwo. Iwo anakhudzidwa ndi chikondi chosonyezedwa ndi abale awo Achikristu a ku maiko ena ndi umboni woonekera bwino wakuti alidi mbali ya ubale wa padziko lonse.

Mosasamala kanthu za kuvutika kwawo, othaŵawo asunga mkhalidwe wawo wauzimu. Kwenikweni, wopenyerera wina anati “iwo amaoneka kukhala odera nkhaŵa kwambiri za kulandira chakudya chauzimu kuposa chithandizo chakuthupi, ngakhale kuti ali m’kusoŵa kwakukulu kwa chilichonse.” Pempho litaperekedwa, makope 5,000 a buku lophunzirira Baibulo lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi m’chinenero cha ku Rwanda cha Kinyarwanda anatumizidwa ku misasa yosiyanasiyana.b

Othaŵawo anakambitsirana lemba la m’Baibulo tsiku ndi tsiku, ndipo analinganiza misonkhano yampingo. Makonzedwe anapangidwanso a kuchititsa makalasi a sukulu za ana. Aphunzitsi anagwiritsira ntchito mwaŵi wa makalasi amenewa kupereka malangizo pamalamulo aukhondo, akumagogomezera kuti kukhalabe ndi moyo kumadalira pa kuwasunga.

Chisamaliro Chopitirizabe Chikufunika

Mazana a Mboni zothaŵa anaikidwa m’malo enanso osakhala m’Goma, monga ku Rutshuru. Chithandizo chofananacho chinaperekedwa kwa abale ameneŵa. Pa July 31, nthumwi za Mboni zokwanira zisanu ndi ziŵiri zinauluka ndi ndege kumka kummwera ku Bukavu kuchokera ku Goma, kumene kunali Mboni zothaŵa zokwanira 450. Unyinji wa ameneŵa anachokeranso ku Burundi. Cholera inali itabuka kumeneko, ndipo chithandizo chinaperekedwa poyesayesa kuchinjiriza imfa pakati pa abalewo.

M’maŵa mwake nthumwizo zinayenda kwa makilomita 150 ndi msewu kupita ku Uvira, Zaire, kumene poyenda m’njira anapeza Mboni pafupifupi 1,600 m’malo asanu ndi aŵiri zochokera ku Rwanda ndi ku Burundi komwe. Malangizo anaperekedwa onena za mmene angadzitetezerere ku matenda. Lipoti lozikidwa pa zopezedwa ndi nthumwizo linati: “Zimene zachitidwa pakali pano ndizo chiyambi chabe, ndipo anthu okwanira 4,700 omwe akulandira chithandizo chathu tsopano adzafunikira chithandizo chowonjezereka kwa miyezi yambiri.”

Malipoti anena kuti Mboni mazana ambiri zinabwerera ku Rwanda pofika mu August. Komabe pafupifupi nyumba zonse ndi katundu zinafunkhidwa. Chotero ntchito yovuta imene ilipo ndiyo ya kumanganso nyumba ndi Nyumba Zaufumu.

Atumiki a Mulungu akupitirizabe kupempherera mosaleka awo amene avutika moipitsitsa mu Rwanda. Tikudziŵa kuti pamene mapeto a dongosolo ili la zinthu akuyandikira, chiwawa chingawonjezeke. Komabe, Mboni za Yehova padziko lonse zidzapitirizabe kusunga uchete wawo Wachikristu ndi kusonyeza chifundo chawo chenicheni.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 1994, yakuti “Tsoka ku Rwanda—Ndani Amene Ali ndi Mlandu?”

b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mapu patsamba 12]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

RWANDA

Kigali

UGANDA

ZAIRE

Rutshuru

Goma

Lake Kivu

Bukavu

Uvira

BURUNDI

Bujumbura

[Chithunzi patsamba 15]

Kumanzere: Ntabana Eugène ndi banja lake anaphedwa. Kulamanja: Mukagisagara Denise, Mtutsi, anaphedwa, mosasamala kanthu za zoyesayesa za abale Achihutu zakuti ampulumutse

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Pamwamba: Kusamalira odwala pa Nyumba Yaufumu mu Goma. Mmunsi kumanzere: Katundu wa chithandizo woposa matani 35 wokonzedwa ndi Mboni ndi kutumizidwa pa ndege ya katundu. Chapansipo: Pafupi ndi Lake Kivu, kumene Mboni zinasamutsidwira. Mmunsi kulamanja: Othaŵa a ku Rwanda pa Nyumba Yaufumu mu Zaire

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena