Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 2/8 tsamba 20-21
  • Kodi Moyo Wanu ngwonyong’onyeka? Mukhoza Kuusintha!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Moyo Wanu ngwonyong’onyeka? Mukhoza Kuusintha!
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukungotaya Nthaŵi Chabe?
  • Zotulukapo Zosakondweretsa za Kunyong’onyeka
  • Kodi Ndiyo Njira Yosavuta Yothetsera Kunyong’onyeka?
    Galamukani!—1995
  • Ndingatani Ngati Mwana Wanga Akumaboweka?
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Ndingatani Ngati Ndaboweka?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Moyo Wosatha M’Paradaiso Udzafika Potopetsa?
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 2/8 tsamba 20-21

Kodi Moyo Wanu ngwonyong’onyeka? Mukhoza Kuusintha!

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SPAIN

MARGARET ndi Brian anali m’zaka zawo za pakati pa ma 50 pamene analandira mwaŵi waukulu: kupuma pantchito kwa mwamsanga ndi penshoni yabwino ndithu. Pamenepo anaganiza zosamukira kummwera kaamba ka kuŵala kwa dzuŵa kumeneko ndi madoko a Mediterranean. Opanda nkhaŵa, opanda zodandaulitsa—ndiwo moyo umene anayembekezera m’nyumba yawo ya m’mphepete mwa nyanja.

Pambuyo pa zaka ziŵiri, zinthu zinasintha. Brian anafotokoza kuti: “Kunaoneka kukhala kopanda pake—masiku kumangopita popanda chochita. Zoona, ndinkasambira, kuseŵera pang’ono gofu kapena tenesi, ndi kulankhula mosalekeza kwa aliyense amene akanamvetsera. Ponena za chiyani? Zopanda pake zokhazokha.”

Gisela, mayi wa m’zaka zoyambirira za ma 20, ali ndi kamtsikana kokongola. Masana, mayiyo ndi mwana wake wamkaziyo, mwa nthaŵi zonse amapita ku paki, kumene mwana wake wamkaziyo amaseŵera ndi mchenga, amatengeka maganizo kwambiri, akumasangalala kupanga ma pie ndi nsanja za mchenga. Pamene akutero, mayiyo wakhala pabenchi ya m’pakimo yapafupi akumapenyerera kamwana kakeko. Kodi akulipenyereradi? Iye wakhala pamenepo, akutchera khutu ku wailesi yake yoyenda nayo. Chifukwa cha utsi wa ndudu yake, iye satha konse kuonanso kamwana kakeko. Ali wonyong’onyeka kotheratu.

Peter, wa zaka 17 wophunzira sukulu ya sekondale, wakhala m’chipinda chake, atazingidwa ndi ziŵiya zamagetsi za mtundu watsopano. Akutsegula limodzi la maseŵero ake a pavidiyo, naona kuti silikumsangalatsanso. Iye waliseŵerapo kale kwa nthaŵi zambiri, ndipo tsopano amadziŵiratu zochita kuti apambane pa vidiyopo. Kodi amvetsere nyimbo zina? Komabe, palibe nyimbo zojambulidwa zimene alinazo zimene sanazimvetserepo kale kwa nthaŵi zambiri. Atanyong’onyeka mothedwa nzeru, akudandaula kuti: “Sindidziŵa chimene ndingachite.”

Kodi Mukungotaya Nthaŵi Chabe?

Kunena zoona, si tsiku la munthu aliyense limene lili losasangalatsa ndi logwetsa ulesi. Ambiri akukhalabe ndi miyoyo yachimwemwe ndi yatanthauzo, akumapeza chikhutiro mwa kuphunzira zinthu zatsopano, mwa kukhutiritsa luntha lawo la kulenga, ndipo, mwa kukulitsa maunansi abwino ndi anthu ena—ndipo choposa kwambiri, ndicho unansi ndi Mulungu.

Komabe, kunyong’onyeka kumayambukira anthu a mikhalidwe yonse ya moyo—1 mwa Ajeremani 3 alionse, malinga ndi kuŵerengera kwaposachedwapa. Wotchedwa Muyupe wachikhumbo chachikulu amene amafika nthaŵi zonse m’malo onse osangulukira mu mzindamo, lova lachinyamata limene limapeza potayira nthaŵi m’nyimbo zopokosa kwambiri ndi moŵa wotsika mtengo, wachikulirepo wogwira ntchito za ovololo amene amathera nthaŵi ya kumapeto a mlungu akupenyerera wailesi yakanema, wantchito yapamwamba amene amasoŵa chochita atachoka mu ofesi yake—onse amakhala ndi dandaulo limodzi: kunyong’onyeka.

Afilosofi akale anakutcha taedium vitae (liwu Lachilatini lotanthauza kutopa ndi moyo). M’Chijeremani liwu lake ndilo Langeweile (mphindi yaitali). Nthaŵi imene imachedwa, ntchito imene imaoneka kukhala yopanda tanthauzo, chikhumbo cha “kungosiya zonse,” zonsezo ndi zizindikiro zofala za kunyong’onyeka.

Ngakhale olemera sali ochinjirizika. Atalongosola moyo wokhala ndi zambiri wa anthu olemera, Roger Rosenblatt wa m’magazini a Time anati: “Atakhala ndi nyumba yaikulu ndi yadi yaikulu yokhala ndi maluŵa ndi nyama zazikulu, mapwando ndi anthu otchuka, kodi anthu olemera ochuluka a dzikoli amalengezanji? Kuti ali onyong’onyeka. Kunyong’onyeka.”

Panthaŵi ina kunalingaliridwa kuti kusanguluka kowonjezereka kukakhala mankhwala a kunyong’onyeka. Lingaliro linali lakuti mikhalidwe yabwino ya pantchito, kuthetsa njira yogwirira ntchito imodzimodzi yotopetsa, ndi nthaŵi yochuluka yosanguluka zikachititsa moyo kukhala wopindulitsa kwa munthu wamba. Komabe mwatsoka, sikuli kosavuta motero. Kusankha chochita ndi nthaŵi yomasuka yonseyi kwakhala kovuta kwambiri kuposa mmene kungaganizidwire. Ambiri amayembekezera kwa mlungu wonse kukhala ndi mapeto a mlungu okondweretsa, koma akafika samakhala molingana ndi zimene anayembekezera.

Zotulukapo Zosakondweretsa za Kunyong’onyeka

Ena amayesa kuthaŵa kunyong’onyeka mwa kudzimwerekeretsa ndi zochita. Omwerekera ndi ntchito ena anakhala otero chifukwa chakuti sanadziŵe chochita ndi nthaŵi yawo pamene sanali ku ofesi. Ena amayesa kuthetsa kunyong’onyeka kwawo mwa kudziloŵetsa mu uchidakwa kapena m’kusanguluka mwa kugwiritsira ntchito anamgoneka. Otchuka m’zokondweretsa ambiri a moyo wotangwanidwa amatembenukira ku anamgoneka, onga cocaine, poyesa kuthaŵa kunyong’onyeka atatsiriza kuseŵera kwawoko. Kunyong’onyeka kwadziŵika kukhala chimodzi cha zifukwa zochititsa chiŵerengero chomakula nthaŵi zonse cha anakubala achitsikana osakwatiwa, ambiri amene mwina analingalira kuti kukhala ndi khanda kukathetsa kunyong’onyeka kwa miyoyo yawo.

Kunyong’onyeka kumalingaliridwa kuti kumachititsa upandu kuwonjezereka kwambiri. Magazini a Time ananena kuti achichepere ochulukirapo amatsiriza sukulu pausinkhu wa zaka 16 ndipo amakhala osoŵa chochita ndikuti malova a ku Western Europe, powayerekezera ndi anzawo ogwira ntchito, ali “othekera kwambiri kudzipha, othekera kwambiri kuyamba kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka, okhoterera kwambiri pa kukhala ndi mimba za pathengo ndi oyedzamira kwambiri pa kuswa malamulo.” Zimenezi zikuoneka kutsimikiziranso mwambi wakuti “ulesi ndiwo mtsamilo wa Satana.”—Yerekezerani ndi Aefeso 4:28.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena