Kodi Ndiyo Njira Yosavuta Yothetsera Kunyong’onyeka?
KUPEREKA zosangulutsa zosatha kwa mamiliyoni a ogula onyong’onyeka tsopano ndiko malonda aakulu. Maholide a zinthu zosangalatsa kwambiri, ziŵiya zamagetsi zopita patsogolo kwambiri, zizoloŵezi zapamtima zabwino koposa, zonsezo zimalinganizidwira kuthandiza ogulawo kupeza potayira nthaŵi. Komabe, kunyong’onyeka kudakali vuto lalikulu. Ngakhale patchuthi, ochita holide onyong’onyeka amafuna zowasonkhezera kukhalabe osangalala. Ndipo ochita maseŵera a kuthamanga kolimbitsa thupi akhama amamva kukhala osoŵeka kanthu kena kofunika ngati alibe wailesi yoyenda nayo.
Mosakayikira, zosangulutsa zoterozo zonga wailesi yakanema, zimadzetsa chisangalalo ndi kuthetsa kunyong’onyeka, koma kwa utali wotani? Kwa ena kuli ngati mankhwala okulitsira chizoloŵezi. Nthaŵi yotsatira, pamafunikira chosonkhezera ndi chisangalalo chokulirapo—apo phuluzi malingaliro akuti anazionapo kale amafikanso. M’malo mwa kukhala njira yothetsera vuto, chosangulutsa choterocho chingakhaledi chimodzi cha zinthu zosonkhezera kunyong’onyeka.
TV, mwa iyo yokha, siimadzetsa kunyong’onyeka, komanso kupenyerera wailesi yakanema kopambanitsa sikungathetsenso kunyong’onyeka. Choipiraponso nchakuti, ‘pamene mudzisomeka’ kwambiri ku TV, mumakhala mutadzichotsa kwambiri ku zenizeni. Zimenezi zimachitikira ana kaŵirikaŵiri. Pa kufufuza kwina, pamene ana amisinkhu ya zaka zinayi ndi zisanu, anafunsidwa kaya ngati iwo akanakonda kuleka TV kapena atate awo, 1 mwa 3 ananena kuti moyo ungakhale wabwinopo popanda atate!
Kukhutiritsa chikhumbo chilichonse sindikonso njira yothetsera vuto. Achichepere ambiri tsopano “akukulira m’nyengo ya kulemera ndi zinthu zakuthupi, akumakhala ndi choseŵeretsa chilichonse, tchuthi chilichonse, fashoni iliyonse yatsopano,” anatero wachiŵiri m’chipani cha Social Democratic m’nyumba ya malamulo ya Germany. Kodi palinso chinthu chilichonse chimene chingawasangalatse? Zingachitike kuti makolo amene analeredwa bwino amene amapatsa ana awo zoseŵeretsa zonse zatsopano akutsogolera anawo panjira yodzakhala achikulire okanthidwa ndi kunyong’onyeka kosatha.
Zochititsa Kunyong’onyeka Zenizeni
Kuthaŵiratu kunyong’onyeka ndiko chonulirapo chosafikirika. Moyo m’dziko lino sungathe kukhala wa chisangalalo ndi chimwemwe chopitirizabe. Kuyembekezera zosatheka koteroko kungadzetse kusakhutira kosafunikira. Panthaŵi imodzimodziyo, pali zochititsa zina zimene zimaipitsiratu zinthu.
Mwa chitsanzo, lerolino mabanja owonjezerekawonjezereka akunyonyotsoka. Kodi zingakhale kuti mayi ndi tate ali otangwanidwa kwambiri ndi zowasangulutsa kwakuti samatheranso nthaŵi yokwanira ndi anawo? Mosadabwitsa, achinyamata amafunafuna njira zawo za kudzisangalatsa m’madisiko, nyumba za mavidiyo, kumasitolo, ndi zina zotero. Chotsatirapo nchakuti, kupita kokayenda monga banja ndi zinthu zina zochitira pamodzi kwakhala zinthu zachikale m’nyumba zambiri.
Komabe enanso ali osakhutira kwambiri ndi moyo wawo wotopetsa kwakuti mosadziŵa amadzipatula, akumachita zinthu za iwo okha ndi kuiŵaliratu za wina aliyense. Ndipo pamene kuli kwakuti amadzipatula mowonjezerekawonjezereka, amakhala ndi chiyembekezo chopanda pake cha kupeza chimene chingatchedwe kudzipezera wekha cholinga chako. Koma sizimachitika mwa njira imeneyo. Ndi iko komwe, munthu samakhala yekha. Timafunikira mayanjano ndi kulankhulana. Motero, kuli kosapeŵeka kuti anthu amene amadzipatula okha amawanditsa kunyong’onyeka, mosadziŵa akumachititsa moyo kukhala wosakondweretsa kwa iwo eni ndi kwa awo okhala nawo pafupi.
Komabe, vutolo lili lozamirapo, monga momwe Blaise Pascal, wafilosofi Wachifalansa wa m’zaka za zana la 17, ananenera molunjika kuti: “Kusukidwa [kumachokera] pansi pamtima mmene umakhala ndi mizu yachibadwa ndi [kudzaza] maganizo ndi paizoni wake.” Nzoona chotani nanga!
Malinga ngati mtima udzaza ndi malingaliro okayikira ponena za chifuno chenicheni cha moyo, kunyong’onyeka kudzakhalapo nthaŵi zonse. Chikhutiro cha pansi pamtima chakuti moyo wa munthu uli ndi tanthauzo nchofunikira. Komabe, kodi ndimotani mmene aliyense angakhalire ndi moyo ndi lingaliro labwino popanda kudziŵa chifukwa chake ali pano, popanda zonulirapo, popanda ziyembekezo za mtsogolo za maziko abwino?
Apa mpamene mafunso ofunika kopambana amabuka: Kodi tanthauzo la moyo nchiyani? Kodi nchifukwa ninji ndili pano? Kodi ndikupita kuti? “Kuyesayesa kupeza tanthauzo la moyo wa munthu ndiko chisonkhezero choyambirira mwa munthu,” anatero Dr. Viktor Frankl. Komabe, kodi tanthauzo la moyo lotero lingapezeke kuti? Kodi nkuti kumene mafunso ameneŵa angayankhidwe mokhutiritsa?
Kunyong’onyeka Kochepekera—Motani?
Buku lakale kwambiri kuposa onse limatsegula maso pa mafunso ofunika oterowo. Heinrich Heine, Mjeremani wolemba ndakatulo wa m’zaka za zana la 19 anati: “Ndatseguka maso chifukwa cha kuŵerenga buku chabe.” Buku liti? Baibulo. Charles Dickens ananena mofananamo kuti: “Ndilo buku labwino koposa limene lakhalapo kapena limene lidzakhalapo m’dziko, chifukwa chakuti limakuphunzitsa maphunziro abwino koposa amene munthu aliyense wolengedwa . . . angatsogozedwe nawo.”
Sizokayikitsa konse. Baibulo ndilo chitsogozo chotsimikizirika kulinga ku moyo wa tanthauzo. Kuyambira kuchiyambi mpaka kumapeto, limapereka mfundo yosonyeza kuti Mulungu anapatsa munthu ntchito yochita. Munthu anafunikira kusamalira dziko lapansi, kulikongoletsa, kuchita uyang’aniro wachikondi pa zinyama, ndipo, koposa zonse, kutamanda Mlengiyo, Yehova. Eya, ntchito yofuna zochuluka imene siikalola kunyong’onyeka! Mamiliyoni a Akristu okangalika apeza kuti kuchirikiza chifuniro cha Mulungu, kukhala wodzipatulira ndi wodzipereka kwa iye kotheratu, kumawonjezeradi tanthauzo pa moyo ndi kuchotsa kunyong’onyeka.
Kunyong’onyeka kofalikira kungakhale vuto lamakono—zinenero zambiri zakale zikuoneka kukhala zopanda liwu lake. Chikhalirechobe, Baibulo, pamene limatisonyeza tanthauzo la moyo, limatipatsanso malingaliro othandiza polimbana ndi kunyong’onyeka. Mwa chitsanzo, ilo limanena kuti ‘wopanduka akangana ndi nzeru yonse yeniyeni.’ (Miyambo 18:1) M’mawu ena, musadzipatule ndi kudzikhalira nokha!
Munthu ali ndi chibadwa cha kuyanjana ndi ena. Amafunikira kuchita ndi anthu ena, ndipo ali ndi chibadwa cha kufuna kutsagana ndi ena. Kupondereza chikhumbo chabwino chimenechi cha kuyanjana ndi anthu ena—kukhala wayekha, wopenyerera chabe—sikwanzeru. Mofananamo, kukhala ndi mayanjano kokha ndi zinthu zopanga ndiko kunyalanyaza nzeru yeniyeni.
Ndithudi, nkosavuta kumangopenyerera akanema kapena kumangolemba zinthu pa kompyuta. Kuyanjana ndi anthu ena nkovutirapo. Komabe, kukhala ndi kanthu kena kokanena kopindulitsa ndi kugaŵana ndi ena malingaliro ndi mikhalidwe ya mtima kuli kopindulitsa ndipo kumachotsapo kunyong’onyeka.—Machitidwe 20:35.
Solomo, amene anali ndi khama la kupenda mkhalidwe wa munthu, analangiza mwamphamvu zotsatirazi: “Kuli bwino kukhutira ndi zimene maso ako aona kuposa kungokhumba.” (Mlaliki 6:9, The New English Bible) M’mawu ena, yesani kupindula ndi mikhalidwe imene mulimo. Sumikani maganizo pa zimene mukuona tsopano. Zimenezo nzabwinopo kuposa kungokhumba kuthaŵa zenizeni kapena “kungokhumba,” monga momwe Solomo ananenera.
Masiku olinganizidwa bwino, zonulirapo zotsimikizirika, ndi chikhumbo choona mtima cha kupitirizabe kuphunzira zidzakuthandizaninso kulaka kunyong’onyeka. Inde, ngakhale pambuyo pakuti munthu wapumula pantchito, iye akhozabe kupambana m’zinthu zambiri. Mmodzi wa Mboni za Yehova ku Balearic Islands, mwamuna wopumula pantchito kuchiyambi kwa zaka zake za ma 70, akuphunzira Chijeremani mofunitsitsa. Ndi chonulirapo chotani? Iye akufuna kulankhula za Mawu a Mulungu kwa obwera kuholide ambiri onyong’onyeka ochokera ku Germany. Ndithudi, kunyong’onyeka sikuli vuto kwa iye!
Chomalizira, bwanji ponena za kuchita chinthu china ndi manja anu? Bwanji osaphunzira maluso a kupanga zinthu ndi manja, kujambula zithunzithunzi ndi manja, kapena kuliza chiŵiya choimbira? Kufunika kwaumwini kumakula ngati pali lingaliro la chipambano. Bwanji osalingalira za kukhala wakhama pa kuthandiza ntchito za panyumba? Pali zinthu zambiri zazing’ono zimene zikufunikira kukonzedwa m’nyumba iliyonse. M’malo mwa kungolingalira za moyo wanu wonyong’onyeka, dziperekeni, chitani ntchito zothandiza panyumba, khalani waluso m’ntchito zina zamanja. Simudzakhala wopanda mfupo.—Miyambo 22:29.
Ndiponso, Baibulo limatilangiza kugwira ntchito ndi mtima wonse pantchito iliyonse imene tingachite. (Akolose 3:23) Ndithudi, zimenezo zimatanthauza kukhala woloŵetsedwamo, kukhala ndi chikondwerero pa zimene tikuchita. Kukhala ndi chikondwerero kumatanthauza kumwerekera m’ntchito imene ikuchitidwa. Kutero kudzaipangitsa kukhala yokondweretsa.
Uphungu wabwino wonsewu wolembedwa zaka zambiri zapitazo, ngati ugwiritsiridwa ntchito, ungathandize kwambiri opsinjika maganizo ndi nthaŵi yomasuka. Motero, mwerekerani m’zimene mukuchita. Yanjanani ndi anthu ena. Chitirani anthu zinthu. Pitirizani kuphunzira. Lankhulanani ndi ena momasuka. Pezani chifuno chenicheni cha moyo. Mwa kuchita zonsezi, simudzakhoterera pa kudandaula kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji moyo uli wonyong’onya choncho?’
[Bokosi patsamba 24]
Mmene Mungagonjetsere Kunyong’onyeka
1. Musalole luntha la kuchita zinthu kufooketsedwa ndi zosangulutsa zopangidwa kale. Khalani wokhoza kusiyanitsa zododometsa ndi zosangulutsa.
2. Yanjanani ndi anthu.
3. Pitirizani kuphunzira. Khalani ndi zonulirapo zaumwini.
4. Khalani ndi luntha la kulenga. Chitani kanthu kena ndi manja anu.
5. Khalani ndi chifuno m’moyo. Lingalirani za Mulungu.