Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 3/8 tsamba 11
  • Nyengo Yoleka Kusamba—Kuvumbula Zinsinsi Zake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyengo Yoleka Kusamba—Kuvumbula Zinsinsi Zake
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kupirira Mavuto Amene Azimayi Amakumana Nawo Akamasiya Kusamba
    Galamukani!—2013
  • Kulimbana ndi Nyengo Yoleka Kusamba
    Galamukani!—1995
  • Nyengo Yoleka Kusamba—Kuidziŵa Bwino
    Galamukani!—1995
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 3/8 tsamba 11

Nyengo Yoleka Kusamba—Kuvumbula Zinsinsi Zake

PAMENE akazi akukalamba, nyengo yoleka kusamba imakhala chochitika choyembekezereka m’moyo wawo. Chikhalirechobe, iyo yalingaliridwa molakwa kwambiri. Malinga ndi kunena kwa buku lakuti The Silent Passage—Menopause, akatswiri a zakubala a m’zaka za zana la 19 anakhulupirira kuti nyengo yoleka kusamba “imakhwethemula dongosolo la minyewa ya akazi ndipo imathetsa kukongola kwawo.”

Malingaliro olakwa oterowo adakalipo. Chotulukapo nchakuti, akazi ambiri amawopa ndi kuda nkhaŵa za kufika kwa nyengo yoleka kusamba. Kulaka mavuto a m’maganizo ochititsidwa ndi zimenezo kunanenedwa kukhala “chimodzi cha zinthu zovuta kwenikweni kuchita nazo m’moyo wa mkazi,” m’buku lakuti Natural Menopause—The Complete Guide to a Woman’s Most Misunderstood Passage.

Kumalo kumene chigogomezero chimaikidwa pa kukhala wachitsikana ndi wamaonekedwe achitsikana, kufika kwa zizindikiro za nyengo yoleka kusamba kungapereke lingaliro lolakwika lakuti: mapeto amwadzidzidzi a utsikana ndi kuyamba kwa ukalamba. Chifukwa chake, akazi ena akhala akuwopa nyengo yoleka kusamba chifukwa imaoneka kukhala yosonyeza kuyambika kwa nyengo ya moyo watsopano wosakondweretsa kwambiri. Ena amakuona kukhala “imfa yaing’ono.”

Akazi amakono safunikira kuvutika mosodziŵa pamene akupyola m’nyengo ya moyo imeneyi. Zinsinsi za nyengo yoleka kusamba zikuvumbulidwa. Kufufuza kowonjezereka kukuchitidwa, ndipo njira zothandiza zikupezedwa zopeputsira kusintha kumeneko. Magazini, manyuzipepala, ndi mabuku akufotokoza kwambiri za nkhaniyo, akumapereka mayankho a mafunso amene ena anali kuchita nawo manyazi kufunsa. Nawonso madokotala adziŵa zochulukirapo ponena za mavuto amene akazi angakumane nawo.

Kodi nchifukwa ninji pakhala kupereka chisamaliro chonsecho pa nkhani imeneyi? Chifukwa chakuti kudziŵa bwino za nyengo yoleka kusamba kungachotse malingaliro amantha, zikayikiro, ndi kulefulidwa kumene akazi ambiri ali nako. Akazi m’maiko ambiri akukhala ndi moyo kwa nthaŵi yotalikirapo, ndipo akufuna kuthetsa chimene chaonedwa kukhala chiwembu cha kusawaululira zinsinsi za nkhaniyo kuti akhale odziŵa. Amafuna mayankho osavuta ndi olunjika. Iwo ali oyeneradi kutero, popeza kuti ambiri a iwo adzakhala ndi moyo kwa utali wa gawo limodzi mwa atatu la moyo wawo atapyola nyengo yoleka kusamba.

Kupenda ziŵerengero za anthu mu United States kumasonyeza chiwonjezeko cha 50 peresenti cha akazi ofika msinkhu woleka kusamba m’zaka khumi zilinkudza. Akazi oterowo amafuna kudziŵa za maupandu ake pa thanzi, kutentha thupi kwadzidzidzi, kusinthasintha mtima, kusapeza bwino m’thupi, ndi kusinthasintha kwa thupi ndi malingaliro. Kodi nchifukwa ninji zinthuzi zimachitika? Kodi moyo wopindulitsa wa mkazi umathera pa nyengo yoleka kusamba? Kodi nyengo yoleka kusamba imasintha umunthu wa mkazi? Nkhani zotsatira zidzapenda mafunso ameneŵa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena