Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 3/8 tsamba 10
  • Kodi Adzalalikira Khomo ndi Khomo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Adzalalikira Khomo ndi Khomo?
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchezera kwa Papa ku Australia—Kokha Ulendo Wachipembedzo?
    Galamukani!—1988
  • Tchalitchi cha Katolika mu Afirika
    Galamukani!—1995
Galamukani!—1995
g95 3/8 tsamba 10

Kodi Adzalalikira Khomo ndi Khomo?

“PAPA Atumiza Alaliki m’Misewu ya Roma.” Umenewo unali mutu wankhani ya m’nyuzipepala yolembedwa ndi Greg Burke. Iye analemba kuti: “Papa John Paul walimbikitsa Akatolika mu Italy kutsatira chitsanzo cha timagulu tampatuko tonga Mboni za Yehova, zimene zakhala zikutembenuza anthu m’dzikolo, ndi kuwayambitsa kulalikira khomo ndi khomo.

“‘Si nthaŵi ya kuchita manyazi ndi Uthenga Wabwino, ndi nthaŵi ya kuulalikira pamachindwi a nyumba,’ anatero Papayo pa Lolemba kwa alaliki oyendayenda ndi aphunzitsi achipembedzo okwanira 350. . . .

“‘Ndikhulupirira kuti ntchito yanu ya kulengeza Uthenga Wabwino m’misewu . . . idzadzetsa zipatso zambiri,’ iye anawauza motero. ‘Inu mwatulukiranso njira ya kulalikira imene imafikira ngakhale awo amene asokera pa chikhulupiriro.’”

Mtolankhaniyo Burke anati: “Chiŵerengero cha Akatolika opita ku Tchalitchi chatsika kwambiri mu Italy m’zaka makumi aŵiri zapitazi, ndipo chikhumbo cha Papa cha kukhala ndi alaliki a kukhomo ndi khomo mwapang’ono chikuonekera kukhala chochititsidwa ndi kuzirala kwa chisonkhezero chake.”

Chilimbikitso chimenecho cha “kuyamba kulalikira khomo ndi khomo” sichatsopano konse. Papa wapapitapo, Paul VI, ananena kuti Tchalitchi cha Katolika “chilipo kuti chilalikire.” Ndipo papa amene alipo, John Paul II, anatulutsa chikalata chake chomka kwa mabishopu cha Redemptoris Missio mu 1991 kuti azindikiritse tchalitchi chake za kufunika kwa kumvera lamulo la Yesu la kulalikira poyera.

Mlembi wa Roma Katolika Peter Hernon anadzutsa funso mu Catholic Herald ya ku London lakuti: “Kodi nchiyani chimene chinachitikira kulalikira?” Iye anali ndi nkhaŵa ponena za “zaka khumi za kulalikira” zolengezedwa kwambiri zimene tsopano zili zaka zingapo. Pamene anafunsa bishopu ponena za kusapita patsogolo kwake, bishopuyo anayankha kuti: “Sufunikira kutengera phuma. Tchalitchi changokhalako kwa zaka 2000 zokha.”

Mposadabwitsa kuti Hernon anafunsa kuti: “Kodi changu chimene Yesu anasonyeza pamene Iye anatumiza ophunzira Ake kukalalikira midzi yapafupi nawo chili kuti? Kapena cha St Paul: ‘Tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino! (1 Akor 9:16)’?” Indedi, kodi Akatolika adzatsanzira Akristu oyambirira amene analalikira poyera “ndi kunyumba ndi nyumba”—Machitidwe 5:42; 20:20, Douay Version.

Hernon anavomereza kuti ngati tinena za ulaliki wa khomo ndi khomo, iye “angamve okayikira akunena kuti ‘ndi malingaliro chabe, nzosatheka.’ Ayi sizili choncho,” akuyankha motero Hernon. “Kuti ndiwongolere mfundo imeneyo ndifunikira kugwiritsira ntchito liwu lina lomveka kukhala lachipongwe. Ndikudziŵa kuti nlachipongwe chifukwa chakuti nthaŵi ina pamene ndinaligwiritsira ntchito m’nkhani Yachikatolika chigawo chonse chinafafanizidwa (ngakhale kuti palibe chilichonse chinasinthidwa). Liwulo ndilo Mboni za Yehova. . . . Mboni iliyonse imaphunzitsidwanso kuti, mwa kuitanidwa kwake kwenikweniko, iye moyenerera ali mmishonale.”

Ngakhale kuti Hernon samagwirizana ndi zikhulupiriro za Mboni za Yehova, iye akuvomereza kuti pamene munthu alingalira za njira zawo za kulalikira, “amakumbutsidwa msanga za Tchalitchi choyambirira monga momwe kwasonyezedwera m’machitidwe a Atumwi.”

Mboni za Yehova zimapitirizabe utumiki wawo wa khomo ndi khomo, motero zikumakwaniritsa lamulo la Yesu m’masiku ano amakono lakuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.”—Machitidwe 1:8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena