Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 4/8 tsamba 15-17
  • Kuona Ng’ona Pafupi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuona Ng’ona Pafupi
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Nsagwada za Ng’ona
    Galamukani!—2015
  • Kuphunzira Baibulo M’malo Osonyezerako Nyama!
    Galamukani!—1996
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2005
  • Zochitika Padzikoli
    Galamukani!—2009
Galamukani!—1995
g95 4/8 tsamba 15-17

Kuona Ng’ona Pafupi

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU KENYA

MLENDO wina woona malo wa ku America anali kalikiliki kujambula zithunzithunzi za mvuwu m’mbali mwa Mara River pamene anaterereka pamiyala ina nagwera mumtsinjemo. Ng’ona, chilombo cha chikopa chokakala chimene chinali kuwothera dzuŵa panthaŵiyo chinaona zimenezo. Pamene kuli kwakuti chamoyo chokwaŵa chimenechi kaŵirikaŵiri chimadya nsomba, chinalephera kupirira pamene chinaona chakudya chokoma chimenechi. Nthaŵi yomweyo chinacholimira m’madzi kukafufuza. Mwamwaŵi, mlendoyo anaona ng’onayo ikubwera ndipo anatuluka mofulumira mumtsinjemo—kwakuti anangochita ngati anali kuyenda pamadzi!

Alendo oona mitsinje, nyanja ndi madambo a Afirika kaŵirikaŵiri amaona ng’ona, ngakhale kuti mlendo wotchulidwayu wogwidwa ndi mantha anakumana nayo powopsa. Kenya ndiye kwawo kwa ng’ona za Nile. M’chinenero cha m’dzikolo cha Chiswahili, iyo imadziŵika ndi dzina lakuti mamba. Ng’ona zili zamoyo zokwaŵa zaliŵiro pamtunda ndi m’madzi momwe, zautali wofika mamita asanu ndi aŵiri. Pamene zili m’madzi zimayenda mwaliŵiro lalikulu chifukwa cha mpangidwe wa michira yake yasadalala. Zingathe kusambira paliŵiro la makilomita 40 pa ola limodzi! Ndipo kukhala kwake pansi pa madzi kwa maola aŵiri kapena ngakhale atatu si kwachilendo. Pamene zili pamtunda zimathamanga pa liŵiro lalikulu komano lodukizadukiza.

Pamenepotu mposadabŵitsa kuti Baibulo mwachionekere limatchula za ng’ona monga chitsanzo cha cholengedwa chowopsa cha Mulungu chotchedwa Livyatanu. Yobu 41:8, 10 amati: “Isanjike [Livyatanu] dzanja lako; ukakumbukira nkhondoyi, sudzateronso. . . . Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa.” Machenjezo anzeru kwambiri amenewo! Malinga ndi kunena kwa buku lakuti The Fascination of Reptiles, lolembedwa ndi Maurice Richardson, ng’ona zimadziŵikanso kukhala zoukira mabwato oyenda ndi makina! Yobu 41:25 moyenerera amati: “Ikanyamuka, amphamvu achita mantha; chifukwa cha kuopsedwa azimidwa nzeru.”

Kodi nchifukwa ninji anthu amachita mantha nathaŵa akaona chilombo chamamba chimenechi? Vesi 14 likufotokoza chifukwa china: “Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pake? Mano ake awopsa pozungulira pawo.” Nsagwada za ng’ona yakumwamba ndi yapansi yomwe, ili ndi mano pafupifupi 24 osiyanasiyana kukula kwake, ndipo ena amamereranso mosalekeza m’moyo wake. Chochititsa chidwi nchakuti, dzino lachinayi la ng’ona la nsagwada ya pansi lili lotulukira kunja m’mbali mwa nsagwada ya kumwamba ndipo limaoneka mosavuta pamene nsagwadazo zili zotseka. Zimenezi zimathandiza kuisiyanitsa ndi nsuwani wakeyo, alligator. Vuto lake nlakuti, ngati muyandikira pafupi kwambiri kuti muone mano ameneŵa, mungawaone onsewo pamene mukudyedwa!

Nchifukwa chake kuli bwino kuona ng’ona muli pataliko, ndipo pali malo ambiri mu Kenya kumene mungachite motero. Mwachitsanzo, Mamba Village ndiwo malo a mu Mombasa kumene ng’ona zimasungidwa.

‘Koma kodi nchifukwa ninji munthu angafune kufuya ng’ona?’ inu mungafunse motero. Choyamba, kuti azitetezere pa kusolotsedwa. M’thengo, ng’ona zili pangozi yaikulu kwambiri ya kufa m’chaka chake choyamba. Mwachionekere ming’anzi, chumba, ndipo ngakhalenso anthu ena ali ndi nkhuli ya mazira a ng’ona ndi ana ake aang’ono ongoswa kumene. Komabe, ng’ona zikasamaliridwa bwino m’malo ake ofuyira, ngozi yake ya kufa imachepa kwambiri. M’chaka chimodzi, ana a ng’ona amatalika kufika pa mamita 1.5—aakuludi mokhoza kuthamangitsa adani ambiri. Kuthengo, kungatenge zaka zitatu kuti ana a ng’ona afikire pautali umodzimodziwo.

Zolengedwa zimenezi zimasungidwa kumalo osungira ng’ona kaamba ka malonda. Ku misika yake yakunja, mudzapezako nsapato, malamba, zikwama, ndi zinthu zina za m’fashoni zopangidwa ndi chikopa chofeŵa cha kumimba kwa ng’ona. Zikopa zofikira pafupifupi 2,000 zimatumizidwa kumaiko ena onga Italy ndi France kuchokera ku Mamba Village chaka ndi chaka, kuti zikanikidwe. Kodi nchiyani chimene chimachitidwa ndi nyama yake yonse? Ku Kenya, nyama ya ng’ona imagwiritsidwa ntchito m’malonda a alendo odzaona dziko monga chakudya cha mbambande.

Nyengo ya kuswana kwa ng’ona ndiyo October mpaka April. M’thengo, zazikazi zimaikira mazira oyambira pa 20 kufikira pa 80. M’nthaŵi imeneyo, zazikazi zosungidwazo zimaikira pafupifupi mazira 36 m’malo ake oswera kuzungulira m’maiŵe osiyanasiyana. Ndiyeno mazirawo amatoledwa ndi kusamutsidwira m’ma incubator kuti ana ake akaswe. Zimenezi zimatenga pafupifupi miyezi itatu.

Ku Mamba Village kumapereka mwaŵi wabwino kwambiri wa kuona zolengedwa zokondweretsa zimenezi motetezereka. Ali m’dera la malo a ngwenya a mahekita asanu ndi atatu amene anakonzedwa kukhala malo osungiramo ng’ona, munda wa maluŵa, maiŵe a za kunyanja, ndi kokasanguluka. Zokwaŵa zoposa 10,000 zimenezi zimakhala muno. Zoonadi, simungaone zonse. Koma m’madera ake aŵiri oswera, mungathe kuona zazikulu zoposa zana, ndipo m’madera ena, muli mazana ambiri a ng’ona zazing’ono zamisinkhu yosiyanasiyana.

Panthaŵi ya kuzidyetsa, ng’onazo zimachititsa chidwi kuzionerera. Zina zimadumphadi kuchokera m’madzi kuti zilume nyama yolenjeketsedwa pa dziŵe. Panopo mungathe kuona ng’ona ya mbiri yoipayo yotchedwa Big Daddy imene inavutitsa anthu ku dera la Tana River, ikumapha pafupifupi anthu asanu isanagwidwe ndi kutengeredwa ku malo kuno. Ngati kuona ng’ona moyang’anizana nazo kumakuchititsani mantha, mungathe kuziona bwino lomwe m’holo ya vidiyo.

Kuona kwanu ng’ona pafupi kungakukondweretseni kapena mwinamwake kukuwopsani. Komano mudzazindikira bwino kwambiri chifukwa chake Baibulo linanena za ng’ona pa Yobu 41:34 kuti: “Ndiyo mfumu ya zodzitama zonse.”

[Chithunzi patsamba 17]

Kulamanja: Kaonekedwe ka Mamba Village

[Chithunzi patsamba 17]

Kutaliko kulamanja: Ng’ona ikudumpha kuchokera m’madzi kuti ilume nyama panthaŵi ya kudyetsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena