Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 4/8 tsamba 21-23
  • Kodi Ndingaletse Motani Zilakolako Zimenezi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingaletse Motani Zilakolako Zimenezi?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuzindikira Kaganizidwe Kolakwa
  • “Maphunziro” Oipa Akale
  • Kusanduliza Maganizo a Munthuwe
  • Kodi Ndingapewe Bwanji Mtima Wofuna Kugonana ndi Amuna Kapena Akazi Anzanga?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Achichepere Akufunsa Kuti
    Galamukani!—1995
  • Umathanyula—Kodi Ngwoipa Kwambiridi?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Ndingapewe Bwanji Khalidwe Lofuna Kugonana ndi Amuna Kapena Akazi Anzanga?
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 4/8 tsamba 21-23

Achichepere Akufunsa Kuti

Kodi Ndingaletse Motani Zilakolako Zimenezi?

“Umathanyula ndimauona kukhala wonyansa kotheratu, koma nthaŵi zina ndimakopeka nawo. Zilakolako zimenezi zimandivutitsa, nthaŵi zina usana ndi usiku. Ndapemphera kwa Yehova mosalekeza kuti, ‘Ndichotsereni zilakolako zoipa zimenezi!’ Kodi zidzathadi?”—Dennis.a

AKRISTU achichepere ambiri—amuna ndi akazi—achonderera thandizo lofananalo. Amakhoterera ku umathanyula komano samafuna kukhala anthu achiwerewere, otenga nthenda, ndi amakhalidwe oipa zimene umenewo uli nazo. Makamakanso, iwo amafuna kukondweretsa Mulungu, ndipo m’Mawu ake iye mwachindunji amatsutsa umathanyula.—Aroma 1:26, 27; Akolose 1:10.

Kaŵirikaŵiri kumanenedwa kuti amathanyula sangasinthe. Komabe, zimenezi si zoona. Akristu ena oyambirira poyamba anali amathanyula, koma anasintha. (1 Akorinto 6:9-11) Inde, mosiyana ndi nkhani zotchukazo, anthu ambiri angathe kusintha ndipo amasintha. Komabe, pamene kuli kwakuti wachichepere angapeŵe bwino lomwe machitidwe amathanyula, iyeyo angaone kukhala kovuta kuchotseratu chikhumbo chamathanyula. Mnyamata wina anavomereza: “Ndayesa kuletsa zilakolako zanga. Ndapemphera kwa Yehova kaamba ka thandizo. Ndimaŵerenga Baibulo. Ndamva nkhani zake. Koma sindikudziŵa kumene ndingatembenukire.”

Palibe mankhwala ochiritsiratu nthaŵi yomweyo. Dennis akukumbukira: “Ndinadziloŵetsa mu ntchito yauchiwerewere ndi akazi poyesayesa kukhala ‘mwamuna.’ Zonsezi zinali zopanda pake ndipo zinangodzetsa kupweteka kwa mtima.” Chikhalirechobe, mwa kugwiritsira ntchito malamulo a Baibulo, munthu angathe kuletsa zilakolako zotero.

Kuzindikira Kaganizidwe Kolakwa

Choyamba, zindikirani kuti machitidwe amayambiriridwa ndi maganizo. (Yesaya 55:6, 7; Yakobo 1:14, 15) Ndithudi, Dr. Wayne W. Dyer akunena kuti: “Simungakhale ndi chilakolako (chikhumbo) popanda kuganiza choyamba.” Chotero muzu wa zikhumbo zamathanyula ungakhale kaganizidwe kokhota ponena za munthu mwini, anthu osiyana nawo ziŵalo, chikondi, ndi zina zotero. Munthu ‘asanasandulize maganizo ake’ ndi kusintha zilakolako zotero, choyamba munthuyo ayenera kuwadziŵa. (Aroma 12:2, NW ) Kuchita motero kungapatse munthu chidziŵitso chofunika ponena za chifukwa chake iye amakopeka ndi aziŵalo zofanana ndi zake.

Kodi munthu angachite bwanji motero? Njira imodzi ndiyo kupemphera, monga momwe wamasalmo anachitira: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa.” (Salmo 139:23, 24) Kukambitsirana malingaliro a munthuwe ndi Mkristu wanzeru ndi wokhwima maganizo kungathandizenso. Monga momwe Miyambo 27:17 imanenera, “chitsulo chinola chitsulo.” Motero mnyamata wina anaululira za kukhosi mkulu wina Wachikristu amene anali wodziŵika kukhala womvetsetsa ndi wachifundo. Kunali kovuta kwa iye kudalira munthu wina kuti amuuze chinsinsi chake, koma panabuka unansi waukulu kwambiri. “Ndikhoza kulankhula naye chilichonse,” iye akutero. Mkuluyo samangomvetsera komanso, mwa kufunsa mafunso mwaluso, amathandiza mnyamatayo kuulula za kukhosi.—Yerekezerani ndi Miyambo 20:5.

Ngati mnyamata anali ndi atate wosamkonda kapena wankhanza, angapeze kuti akukopeka ndi aziŵalo zofanana naye kwenikweni chifukwa cha kuyesayesa kosaphula kanthu kwa kupeza chikondi chosoŵacho cha atate. Pokhala analibe chitsanzo cha munthu wamphongo, angamve kukhala “wofooka ndi wosakhoza pa mikhalidwe yachimuna, ndiko kuti, mphamvu, chidaliro, ndi nyonga,” malinga ndi kunena kwa Dr. Joseph Nicolosi. Ngati munthu apenda mikhalidwe ina yapadera imene amalingalira kuti ali wopereŵera, iye angadabwe kupeza kuti imeneyo ndiyo mikhalidwe yeniyeniyo imene amakopedwa nayo mwa amuna ena.

“Maphunziro” Oipa Akale

Achichepere ena amazindikira kuti ali ndi vutolo chifukwa cha zinthu zosautsa maganizo zimene zinawachitikira kalelo. Msungwana wina akukumbukira kuti: “Ndinali kuona zithunzithunzi zaumaliseche zonena za mathanyula. Ndinayamba kukhala ndi zikhumbo zimene sizinali zachibadwa.” Mnyamata wina akunena kuti: “Ndinagonedwa ndi atate. Chotero, kugonana ndi mwamuna kunaonekera kukhala kwachibadwa kwa ine.” Zochitika zokwiyitsa zimenezo zingaphunzitse anthuwo kuipidwa kapena kuwopa aziŵalo zosiyana ndi zawo kapena kuona ngati kuti kugonana ndiko chikondi. Motero mkazi wina amene anagonedwapo anafotokoza chikhumbo chake cha kugonana kukhala “kufuna chikondi, osati chilakolako cha thupi—kufunafuna kukondedwa ndi kumvetsetsedwa.”

Koma kunena zoona, zochititsa umathanyula nzocholoŵana, ndipo zambiri nzovuta kuzifotokoza bwinobwino.b Komabe, mosasamala kanthu za zimene zimachititsa kuganiza kolakwako, pali zinthu zambiri zimene munthu angachite kukuwongolera.

Kusanduliza Maganizo a Munthuwe

Njira yabwino koposa ndiyo kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, lingalirani za mnyamata amene amakopeka ndi amuna amene ali ndi mikhalidwe yachimuna imene amaganiza kuti alibe. Kapena msungwana amene amawopa amuna. Njira imodzi imene onsewo angakulitsire lingaliro labwino la pa amuna ndiyo kuphunzira chitsanzo cha Yesu. (1 Petro 2:21) Iye anali chitsanzo changwiro cha mwamuna wamphamvu amenenso anali wofatsa. (Mateyu 19:14; Yohane 19:5) Motero mnyamata wina amapeza kuti kuphunzira buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalakoc nkothandiza. “Kudziŵa Yesu kumawongolera chithunzi chimene ndili nacho ponena za mmene mwamuna ayenera kukhalira,” iye akutero.

Kusinkhasinkha pa mavesi a m’Baibulo onena za lingaliro la Mulungu pa kugonana, chikondi, ndi kupalana chibwenzi kwa aziŵalo zofanana nkothandizanso powongolera kuganiza kwa munthu.—Genesis 1:27, 28; Rute 1:16, 17; 1 Samueli 18:1; Miyambo 5:18, 19; 1 Akorinto 13:4-8.

Nkofunikanso kupeŵa kumangoganiza zoipa. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimakhala zamphamvu kwambiri pamene munthu ali wosukidwa, wopsinjika maganizo, ndi wogwiritsidwa mwala. (Miyambo 24:10) “Njira yokha yosinthira zimene tili ndiyo kuchotsa malingaliro athu oipa ndi kuloŵetsa abwino,” akutero mkazi wina Wachikristu. Pamene maganizo oipa amfikira, amakumbukira ponena za lingaliro la Mulungu pa umathanyula. Mnyamata wina akuti: “Nthaŵi iliyonse pamene chilakolako cha mathanyula chibuka, ndimasinkhasinkha pa mavesi anga a m’Baibulo apamtima.” (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 10:4; Afilipi 4:8.) Ena apeza kukhala kothandiza kugona akumvetsera makaseti osiyanasiyana ofotokoza Baibulo a Watch Tower Society.

Monga momwe maganizo athu amayambukirira ntchito zathu, nasonzo ntchito zathu zingayambukire maganizo athu. Chotero munthu ayeneranso kuleka khalidwe ndi mayanjano amene amayambitsa kapena kuchirikiza chikhumbo choipa. (1 Akorinto 15:33) Munthu angafunikirenso ‘kusamala’ pamene ali m’zimbudzi, kumagombe, m’malo osinthira zovala, ndi m’malo ena amene angampatse chiyeso.—Salmo 119:9.

Psotopsoto ali chizoloŵezi china choipa choyenera kupeŵedwa. Kwa amuna ndi akazi ambiri amathanyula, chimenechi chimakhala chisonkhezero chosalamulirika. “Ndinavutika ndi kuchita psotopsoto kuyambira pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi chimodzi,” akuulula motero mnyamata wina. “Kulingalira za kugonana kunachirikiza zilakolako zanga za mathanyula.” Thetsani chizoloŵezi chimenechi!d—Akolose 3:5.

Ndiyeno, nkofunikanso kwambiri kuti munthu akhale ndi njira yabwino ya khalidwe. Ena apereka lingaliro lakuti ngati mnyamata akhala ndi mikhalidwe yamphongo, adzakhala wosakopedwa kwambiri ndi amuna ena. Zoonadi, mnyamata sangadziŵe mmene angachitire zimenezi ngati analibe munthu wamphongo amene anali chitsanzo chake pamene anali kamwana. Iye sangakhale pamtendere ndi thupi la iye mwini ndipo angakhale wozunguzika kapena wosanga mwamuna. Kuchita ntchito yakuthupi, kulimbitsa thupi koyenerera, kapena maseŵero ena osangulutsa kaŵirikaŵiri amathandiza pankhaniyi. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:8.) Koma monga momwe mnyamatayo Timoteo anakhalira ngati mwana kwa mtumwi Paulo, munthu angaone kukhala kothandiza kwenikweni kukulitsa kumvana kwabwino ndi mwamuna wolingalira bwino wokulirapo Wachikristu. (Afilipi 2:19-22; 2 Timoteo 3:10) Mwa kukhazikitsa malire enieni a khalidwe ndi kukulitsa kukambitsirana komasuka, unansi wotero ungakhale wachikondi ndi wodalirika, komanso wopanda malingaliro achabe akugonana.

Kuposa zonsezo, munthu ayenera kumenya nkhondo yauzimu zolimba. Phunziro la Baibulo lanthaŵi zonse, pemphero, ndi kuuza ena chikhulupiriro cha munthuwe zimathandiza kuika maganizo a munthuwe m’njira yauzimu. (Salmo 55:22; 119:11; Aroma 10:10) Nthaŵi zina malingaliro a kukhala wopanda pake angachititse kukhala kovuta kuti tikhale pakati pa Akristu anzathu, koma Baibulo limachenjeza ponena za kudzipatula. (Miyambo 18:1) Kuyanjana kwabwino ndi Akristu achimuna ndi achikazi kungathandize munthu kukhala wolingalira bwino.—Ahebri 10:24, 25.

Ngati mukuvutika ndi chikhumbo chamathanyula, malingaliro ameneŵa angakuthandizeni. Komabe, musakhale wogwiritsidwa mwala mopambanitsa ngati zilakolako zoipazo zipitirizabe. Mulungu amadziŵa bwino mmene mumamveramo ndipo amachitira chifundo awo amene amamenyera nkhondo kumtumikira. (1 Yohane 3:19, 20) M’dziko latsopano, anthufe tidzachiritsidwa pa matenda onse amene amatisautsa. (Chivumbulutso 21:3, 4) Pakali pano, dalirani Mulungu ndi kumenyana ndi zikhumbo zoipa. (Agalatiya 6:9) Limodzi ndi kupyola kwanthaŵi ndi kuyesayesa kwakhama, mwinamwake ngakhale zikhumbo zoipa zenizenizo zingazimiririke.

(Kuyambira kope lino, nkhani zakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” zidzatulutsidwa kamodzi m’kope lililonse.)

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena asinthidwa.

b Onani “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” m’kope lathu la February 8, 1995.

c Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

d Mitu 25 ndi 26 ya buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza (lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.) ili ndi malingaliro othandiza wachichepere kuthetsa chizoloŵezi chovuta chimenechi.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Kulitsani lingaliro labwino la mwamuna mwa kuphunzira chitsanzo cha Yesu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena