Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 4/8 tsamba 3-5
  • Kusiyana m’Zathanzi kwa Padziko Lonse—Vuto Lomakula

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusiyana m’Zathanzi kwa Padziko Lonse—Vuto Lomakula
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maumboni Owopsa
  • Thanzi ndi Umphaŵi—Kugwirizana Kwake
  • Miliri m’Zaka za Zana la 20
    Galamukani!—1997
  • Dziko Lopanda Matenda
    Galamukani!—2004
  • Njira Yatsopano Yolimbana ndi Chifuwa cha TB
    Galamukani!—1999
  • Tizilombo Ta matenda Tibwezera Chilango
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 4/8 tsamba 3-5

Kusiyana m’Zathanzi kwa Padziko Lonse—Vuto Lomakula

NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU BRAZIL

PAMENE Ali Maow Maalin anadwala nthomba ku Somalia mu 1977, inamloŵetsa m’chipatala ndipo dzina lake linaonekera m’mitu ya nkhani. Atapatsidwa mankhwala ndi kuchira, WHO (World Health Organization) inalengeza mu 1980 kuti nthomba—pambuyo posakaza anthu ambirimbiri kwa zaka mazana ambiri—inali itafafanizidwa pa dziko lapansi. Ali ananenedwa kukhala wodwala nthendayo womaliza padziko lonse.

Mu 1992, WHO inatchulanso kupita patsogolo kwina m’zathanzi: M’ma 1980, anthu ambiri m’maiko osatukuka anapeza madzi abwino akumwa ndi njira zosungira ukhondo. Ndiponso, chiŵerengero chokulirapo cha anthu m’maiko osatukuka anakhala ndi zipatala kwawoko. Chotero, m’zaka khumi zapitazo, chiŵerengero cha imfa za ana chinatsika m’madera ena.

Maumboni Owopsa

Komabe, anthu amene akufa limodzi ndi ziwopsezo zimene zikutukusira zikubwevutsa kupita patsogolo kumeneku ndi kukuphimba. Talingalirani za maumboni angapo owopsa.

HIV/AIDS—Anthu oposa 17,000,000 padziko lonse ali ndi HIV, kachilombo kamene kamayambitsa AIDS. Anthu pafupifupi 3,000,000 anakatenga m’chaka chimodzi cha posachedwapa, pafupifupi 8,000 pa tsiku. Ana oposa miliyoni imodzi atenga HIV. Mwina posachedwapa imfa za AIDS pakati pa ana zidzafafaniziratu kupita patsogolo kulikonse kumene kwakhalapo kwa kupulumutsa ana m’zaka makumi angapo zapitazo. Ndipo mliriwo tsopano ukuyamba kumene kuwonjezereka mofulumira m’madera ambiri, monga ku Asia. Anthu oposa 80 peresenti mwa amene ali ndi HIV, ikutero Aids and Development, ali m’maiko osatukuka.

Tuberculosis (TB)—Ngakhale kuti inanyalanyazidwa kwambiri m’zaka makumi aŵiri zapitazo, TB ikusakazanso dziko lonse, ikumapha anthu ngati mamiliyoni atatu chaka ndi chaka, ikumakhala wakupha woposa padziko lonse pakati pa nthenda zoyambukira. Zoposa 98 peresenti za imfa zimenezo zinachitika m’maiko osatukuka. Kuwonjezera kuipa kwa mkhalidwewo, kachilombo ka TB kanagwirizana ndi HIV, kupanga mgwirizano wowopsa kwambiri wokhala ndi zotsatirapo zosakaza. Anthu okwanira miliyoni imodzi amene ali ndi HIV ayenera kuti adzafa ndi TB chaka ndi chaka pofika chaka cha 2000.

Kansa—Anthu odwala kansa m’maiko osatukuka tsopano ali ambiri kuposa aja a m’maiko otukuka.

Nthenda ya Mtima—“Tili pafupi ndi tsoka lokantha dziko lonse la kutsekeka kwa mitsempha yakumtima,” akuchenjeza motero Dr. Ivan Gyarfas wa WHO. Nthenda ya mtima siilinso mliri wa maiko otukuka okha. Mwachitsanzo, ku Latin America anthu kuŵirikiza kaŵiri kapena katatu adzafa ndi nthenda ya mtima kuposa ndi nthenda zoyambukira. M’zaka zingapo kutsogoloku, kutsekeka kwa mitsempha yakumtima ndi masitroko zidzakhala zochititsa imfa zazikulu m’maiko onse osatukuka.

Nthenda za Kumalo Otentha—WHO ikuchenjeza: “Nthenda za kumalo otentha zikuchita ngati kuti zapenga, cholera ikumafalikira ku America . . . , mliri wa yellow fever ndi dengue ukuyambukira anthu ambiri, ndi nthenda ya malungo ikuipiraipira.” Magazini a Time akuti: “M’maiko osauka kwambiri, nkhondo yolimbana ndi nthenda zoyambukira yalephera kale.” Malungo okha tsopano akupha anthu ngati mamiliyoni aŵiri pa chaka—ngakhale kuti analingaliridwa kukhala atathetsedwa zaka ngati 40 zapitazo.

Nthenda za Kutseguka m’Mimba—Chiŵerengero cha ana amene akufa m’maiko osatukuka nchowopsa. Ana ngati 40,000 amafa tsiku ndi tsiku ndi nthendazo kapena matenda a njala; mwana mmodzi amafa ndi nthenda za kutseguka m’mimba pa masekondi asanu ndi atatu alionse.

Thanzi ndi Umphaŵi—Kugwirizana Kwake

Kodi chithunzi cha thanzi chimenechi chikutisonyezanji? “Maiko osatukuka akuyang’anizana ndi vuto la mbali ziŵiri,” katswiri wa zathanzi akutero. “Akukanthidwa ndi nthenda zonse zalizunzo zamakono zomwe zikubuka pamene nthenda za kumalo otentha zilipo kale.” Zotulukapo zake? “Kusiyana kwa malo” kodetsa nkhaŵa kwaonekera, likutero buku lakuti Achieving Health for All by the Year 2000. Motero, zipatala m’maiko ngati 40 a m’Afirika ndi Asia “sizikuyendera pamodzi ndi za m’maiko ena otsala.” Kusiyanako nkwakukulu kwambiri—ndipo kukukulirakulira.

Ngakhale kuti pali zifukwa zambiri zochititsa kusiyana komakula kumeneku, chochititsa chimodzi chachikulu cha thanzi loipa, akutero magazini a World Health, “ndicho umphaŵi.” (Yerekezerani ndi Miyambo 10:15.) Kaŵirikaŵiri umphaŵi umachititsa anthu kukhala m’malo aang’ono opanda njira zosungira ukhondo, opanda madzi akumwa abwino okwanira, amene anthu amakhalamo mopanikizana kwambiri. Zinthu zitatu zimenezi sizimangolepheretsa thanzi labwino komanso zimachirikizadi matenda. Palinso matenda a njala, amene amafooketsa mphamvu ya thupi yoletsa matenda, ndipo simwaona nanga chifukwa chake umphaŵi umawononga thanzi monga momwe chiswe chimawonongera mtengo.

Pamene nthenda zakupha ziipitsa malo okhala, kulemaza anthu, ndi kupha ana, osauka ndiwo amavutika koposa. Taonani zitsanzo zina. Kudera la osauka ku South Africa, odwala TB ngambiri kuŵirikiza zana limodzi kuposa akumadera apamwamba a m’dziko limenelo. Kumadera a osauka ku Brazil, anthu kuŵirikiza kasanu ndi kamodzi amafa ndi chibayo ndi fuluwenza kuposa kumadera apafupi a olemera. Ndipo unyinji wa ana amene amafa m’mabanja osauka ku India umaŵirikiza nthaŵi khumi kuposa m’mabanja olemera koposa mu India momwemo. Choonadi chovutitsa maganizo chikuonekera bwino lomwe: ‘Umphaŵi umawononga thanzi lanu!’

Nchifukwa chake anthu oposa mamiliyoni chikwi chimodzi okhala m’zithando amakhalabe osoŵa chochita. Sakhoza kuletsa zochititsa umphaŵi zazikulu, ndipo zotulukapo zake zoipa zodzetsa matenda zimalamulira miyoyo yawo. Ngati mukuvutika ndi ziyambukiro zoipa za umphaŵi, mwina inunso mungaganize kuti palibe chimene mungachite kuti muchoke kumbali yoipa ya kusiyana kwa thanzi. Komabe, kaya ndinu wosauka kapena wolemera, pali njira zina zimene mungatsatire kuti mutetezere thanzi lanu ndi la ana anu. Kodi njirazo ndi ziti? Nkhani yotsatira imasonyeza njira zimenezo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena