Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 4/8 tsamba 18-20
  • Kuzengereza—Mbala ya Nthaŵi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuzengereza—Mbala ya Nthaŵi
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi ndi Kuzengereza?
  • Kugwira Mbalayo
  • Lingalirani za Zotulukapo Zake
  • Kodi Tingachitenji?
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamachite Zinthu Mozengereza?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Zimene Zingatithandize Kuti Tisamazengereze Pochita Zinthu
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Ndingatani Kuti Ndizigawa Bwino Nthawi Yanga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Ikapita Siibweranso Choncho Igwiritseni Ntchito Bwino
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 4/8 tsamba 18-20

Kuzengereza—Mbala ya Nthaŵi

“Kuzengereza ndiko mbala ya nthaŵi.”—Edward Young, cha m’ma 1742.

IYAYI! Musalekeze kuŵerenga nkhaniyi! Mukudziŵa zimene zingachitike. Mungalekeze kuŵerenga ndi kunena kuti: “Imeneyi ndi nkhani yabwino, koma tsopano ndilibe nthaŵi kuti ndiiŵerenge. Ndidzaiŵerenga pambuyo pake.” Koma mwina pambuyo pakepo sipadzafika konse.

Musazengereze kuŵerenga nkhaniyi yonena za kuzengereza! Dzipimireni nthaŵi. Mwachionekere mudzakhoza kuŵerenga nkhaniyi pafupifupi m’mphindi zisanu. Panthaŵiyo mudzakhala mutamaliza pafupifupi 10 peresenti ya magazini onseŵa! Onani pa watchi yanu ndi kuyamba kuŵerengera nthaŵi tsopano. (Mwaŵerenga kale pafupifupi 5 peresenti!)

Kodi ndi Kuzengereza?

Ngati mulekeza—kukankhira kutsogolo chimene mungathe kuchita, kapena chimene muyenera kuchita tsopano, pamenepo mukuzengereza. M’mawu ena, mukusiyira maŵa chimene mungachite tsopano, lero lomwe. Munthu wozengereza amachedwetsa chinthu pamene chili chofunika kuchitidwa.

Mkulu wantchito amafunsira lipoti kwa wantchito; makolo amauza mwana kusesa m’chipinda mwake; mkazi amapempha mwamuna wake kukonza mpope. “Ndinatanganidwa kwambiri” kapena, “Ndinaiŵala” kapena, “ndinalibe nthaŵi” ndizo zodzikhululukira zimene zimaperekedwa pamene sanachite zinthuzo. Choonadi nchakuti, ndi oŵerengeka chabe a ife amene amakonda kukonza malipoti kapena kusesa m’zipinda kapena kukonza mipope ngati pali zinthu zina zosangalatsa kuchita. Motero timalekeza, timachedwetsa kuchita ntchitoyo.

Komabe, kodi mukudziŵa kuti nthaŵi zina sikumakhala kuzengereza pamene tileka kuchita kanthu kena? Mkazi wina wamalonda amene amalandira pempho limene samadziŵa chochita nalo amaliyika m’faelo m’bokosi lolembedwapo kuti “zoyembekeza” padesiki lake. Patapita milungu ingapo, amapendanso zinthuzo ndi kuona kuti theka la izo sizinafunikira chilichonse. Sizofunikiranso. Ngati muli wosatsimikiza kuti kaya muyenera kuyembekeza kapena kuchita kanthu, yesani kuona chimene chingachitike ngati simuchita konse chimene mukuzengerezacho. Kodi zotulukapo zake zingakhale zabwinopo ngati muchita chinthucho kapena kodi zingakhale zoipa?

Ngati tiyenera ndipo tikhoza kuchita tsopano ndipo ngati kuchedwetsa chinthu chofunikira kuchitidwacho kungachititse mavuto aakulu pambuyo pake, pamenepo kuchedwa ndiko kuzengereza. Mwachitsanzo, kutsuka mbale zitakhala kwa nthaŵi yaitali kumavuta kutchotsa zoumirira zake. Kuchedwetsa kukonzetsa galimoto kungafune kukonzetsa kwa ndalama zambiri pambuyo pake. Kuchedwa kulipira ngongole kungadzafune malipiro aakulu kapena kulandidwa chithandizo chake. Mkazi wina anaŵerengera kuti kuchedwa kwake kulipirira milandu ya kuswa malamulo apamsewu, malipiro a kuchedwetsa matepu a vidiyo obwerekedwa, ndi mabuku a ku laibulale zinafika madola 46! Zimenezo zinali za mwezi umodzi wokha!

Kugwira Mbalayo

Dziŵani chifukwa chake mumazengereza. Pendani zifukwa zotsatirazi, ndi kuona ngati mungadziŵe chimene chikugwirizana ndi ntchito imene simunayambebe kapena imene simunamalizebe:

Chizoloŵezi:

Ngati ndiyembekezera kutatsala nthaŵi yaing’ono, ndidzakhala ndi chisonkhezero chachikulu cha kuimaliza.

Ndimakonda chisangalalo chimene ndimakhala nacho mwa kuichita kutatsala nthaŵi yaing’ono.

Ndidzayembekezera kufikira mkulu wantchito atandikumbutsa kangapo konse, pamenepo ndidzadziŵa kuti akufunadi kuti chinthucho chichitidwe.

Ndimakhala ndi zambiri zochita kwakuti zinthu zodetsa nkhaŵa zokha ndi zimene ndimasamalira.

Mkhalidwe wa Maganizo:

Ndilibe chifuno kapena chisonkhezero cha kuchita ntchitoyo.

Ndimachita zinthu pamene ndafuna.

Ndimafuna kuchita chinthu china.

Ndilephera kudzilamulira.

Mantha:

Sindili wotsimikiza kwenikweni kaya ngati ndingakwanitse kuchita ntchitoyo.

Ndilibe nthaŵi yokwanira kuti ndiichite.

Ndi ntchito yaikulu kwambiri. Ndifunikira thandizo.

Bwanji ngati ndilephera kapena sindimaliza?

Ndiyenera kupeza zogwirira ntchitoyo kuti ndiimalize.

Ndikuwopa kuti ndidzasulizidwa kapena kuchita manyazi.

Anthu osiyanasiyana amazengereza zinthu panthaŵi zosiyanasiyana. Ena amazengereza asanayambe pakuti amaona ntchitoyo kukhala yaikulu kwambiri. Ena amayamba, koma pamene afika chapakati, chifuno chimatha, ndipo amailekeza. Enanso amatsala pang’ono kumaliza koma nkuyambanso ntchito ina, nasiya yoyambayo isanathe. (Mukuchita bwino ndithu. Mwafika kale pakati pa nkhani ino.)

Zifukwa zanu zimene simumayambira kapena zimene simumalizira ntchito zingagwere m’magulu onse atatuwo. M’buku lakuti The Now Habit, Neil Fiore analemba kuti: “Zifukwa zazikulu zitatu zimene zimachititsa mavuto ambiri a kuzengereza ndizo: kumva kukhala ndi vutolo, kudera nkhaŵa, ndi kuwopa kulephera.” Pa zifukwa zilizonse, ngati mungadziŵe zochititsa zake, mudzakhala pafupi ndi mankhwala ake.

Ngati simukudziŵa bwino chifukwa chake mumazengereza, lembani zochita zanu za mlungu umodzi ndi kuzilekanitsa ndi theka la ola. Pezani mmene mumathera nthaŵi. Ingakhale njira yeniyeni yotsegula maso kuti tione kuchuluka kwa nthaŵi imene timawonongera pa zinthu zazing’ono pochita ntchito zofunika kwambiri. Ndiyenonso nkutani?

Lingalirani za Zotulukapo Zake

Kuyembekezera kuti chinthu chidzachitika popanda kuchitapo kanthu kungachititse kuvutika m’maganizo. Pamene muyandikira tsiku limene ntchitoyo iyenera kumalizidwa, mumayamba kupanikizika ndi kudera nkhaŵa. Pamene malingaliro otereŵa akula, luso lanu lochita zinthu lingafooketsedwe. Simumakhala wofunitsitsa kupenda kapena kupima njira zosiyanasiyana zokwaniritsira chonulirapo koma mumangofuna kuchichita kuti zikuchokeni.

Mwachitsanzo: Mwapatsidwa nkhani yoti mukambe. Usiku wakuti m’maŵa mwake mudzaikamba, mukhala pansi kuti mulembe mawu angapo papepala. Simunakhale ndi nthaŵi yokwanira ya kufufuza nkhaniyo, motero mungoikonza mwa patalipatali. Mwinamwake mwa kuyesayesa pang’ono, mukanaphatikizapo zokumana nazo, mfundo zochirikiza, kapena matchati othandizira omvetsera anu kulingalira bwino nkhaniyo.

China chimene chimatsatirapo pamene tichedwetsa ntchito ndicho kulephera kumasuka maganizo pamene tikupuma. Chifukwa chake nchakuti timakhala ndi lingaliro lotivutitsa (kapena munthu amene amangotikumbutsa) kuti sitinatsirize ntchito.

Kodi Tingachitenji?

Pangani ndandanda. Chitani zimenezi usiku tsikulo lisanafike. Lembani papepala zinthu zimene mufuna kuchita tsiku lotsatira. Mwa njira imeneyi simudzaiŵala kanthu, ndipo mudzaona kupita patsogolo kwanu pamene muchonga zinthu zimene mwachita. Kulamanja la chinthu chilichonse, lembani nthaŵi imene muganiza kuti ntchitoyo idzatenga. Ngati mukupanga ndandanda ya ‘Zofunika Kuchita’ ya tsikulo, gwiritsirani ntchito mphindi. Ngati mukupanga ndandanda ya ntchito, gwiritsirani ntchito maola. Pangani ndandanda imeneyi usiku tsikulo lisanafike. Patulani mphindi zingapo zakuti mukonze ndandanda yanu ya tsiku lotsatira. Khalani ndi kalenda ya mwezi ndi mwezi pafupi. Pamene mulandira ntchito ndi mapangano, zilembeni mmenemo.

Pamene mupenda ntchito za tsiku lotsatira, zindandalikeni motsatira kufunika kwake mwa kuona pa kalenda, mukumaika A, B, C, basi motero pafupi ndi chinthu chofunikira kuchitidwa. Anthu ena amagwira bwino ntchito mmaŵa, ena masana kapena madzulo. Ikani ntchito zanu zazikulu kwambiri panthaŵi zimene mumagwira ntchito kwambiri. Ikani ntchito zosasangalatsa kwambiri patsogolo pa zosangalatsa.

Dziŵani nthaŵi. Ngati nthaŵi zonse mumachedwa, mukumachita zinthu mothamanga chifukwa chakuti mwachedwa, dziŵani nthaŵi. Ndiko kuti, ŵerengerani bwino lomwe nthaŵi imene mudzafunikira kuchita ntchitoyo. Wonjezerani mphindi zingapo pa ntchitoyo kaamba ka “ngozi” imene ingachitike. Musaiŵale kusiya mpata wa nthaŵi pakati pa mapangano. Muyenera kuwonjezerapo nthaŵi yoyenda. Simungamalize msonkhano wina pa 10:00 a.m. ndi kukhalanso pa wina pa 10:00 a.m. ngakale ngati ikuchitikira m’chipinda chimodzimodzi, koposa chotani nanga ngati ndi mbali ina ya mzinda. Lolani mpata wa nthaŵi yokwanira pakati pake.

Gaŵirani ntchito. Kaŵirikaŵiri timayesa kuchita chinthu chilichonse ife eni ngakhale kuti si nthaŵi zonse pamene tifunikira kutero. Munthu wina akhoza kukatipositira kalata ngati tadziŵa kuti akupita ku positi ofesi.

Muigaŵegaŵe. Nthaŵi zina sitimayamba ntchito poona ukulu wake. Bwanji osaigaŵagaŵa ntchito yaikuluyo m’zigawo zazing’onozing’ono? Pamene timaliza ntchito zazing’onozo, tidzaona kupita kwathu patsogolo ndi kulimbikitsidwa kumalizanso mbali yotsatira.

Konzekerani za zododometsa. Nthaŵi zonse pamakhala zododometsa pa tsiku lathu la ntchito—mafoni, alendo, mavuto, makalata. Timafuna kugwira ntchito mokhutiritsa, kumene kumaphatikizapo kugwira ntchito ndi anthu ena amene alinso ndi nthaŵi zoyikidwa zomalizira ntchito zawo. Ngati tingosamala za kagwiridwe ka ntchito kabwino chabe, tidzakhumudwa pamene ena adodometsa zochita zathu. Chifukwa chake, konzekerani za kudodometsedwa. Lolani nthaŵi tsiku ndi tsiku ya zochitika zosayembekezera. Pamene zimenezi zichitika, mungazisamalire, mukumadziŵa kuti mwazikonzekerera nthaŵi.

Mfupo. Pamene mupanga ndandanda yanu, muyenera kulinganiza kugwira ntchito mwamphamvu kapena mosumika maganizo kwa pafupifupi mphindi 90. Musaiŵale kundandalika nthaŵi yokonzekera ntchito. Mutayamba ntchitoyo ndipo mwaigwira kwa pafupifupi ola limodzi ndi theka, mungapume pang’ono. Ngati mumagwira ntchito mu ofesi, yambani mwalekeza, dziwongoleni, pendani zimene mwachita. Ngati mumagwirira ntchito pabwalo, pumulani pang’ono. Dzifupeni kaamba ka ntchito yanu.—Mlaliki 3:13.

Tangolingalirani, mwamaliza nkhani ino m’mphindi pafupifupi zisanu kuchokera pamene mwaŵerenga mutu wake. Mungakhale mutayamba kuwongokera!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena