“Chipululutso cha Zachuma”
YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! MU NIGERIA
MALINGA ndi kunena kwa lipoti la UNICEF (United Nations Children’s Fund), Afirika wa kummwera kwa Sahara akuvutika ndi “chipululutso cha zachuma.” Pafupifupi theka la anthuwo—pafupifupi 220 miliyoni—ali paumphaŵi wadzaoneni, osakhoza kupeza zofunika za moyo. Nzika ya pakati ili paumphaŵi wa 20 peresenti kuposa zaka khumi zapitazo.
“Mu zamaphunziro,” likutero lipotilo, “ma 1980 angangofotokozedwa kukhala zaka khumi zotayika.” Kuwonongera ndalama pa mwana wa sukulu aliyense kunatsika ndi gawo limodzi mwa zitatu, ndipo kulembetsa ana kusukulu kunatsika kuchokera pa 79 peresenti kufika pa 67 peresenti. Chithandizo cha chipatala nachonso chikucheperachepera m’maiko ambiri a mu Afirika, makiliniki ambiri akumatsekedwa chifukwa chosoŵa antchito ndi mankhwala.
Lipoti likundandalika zifukwa zambiri zochititsa vuto la zachuma m’kontinenti imeneyi, kuphatikizapo kuwonongera ndalama pa zankhondo, kutsika kwa malonda, ndi ngongole zochulukitsitsa, zimene akatswiri amati nkosatheka kuzilipira. Lipotilo la UNICEF likuti: “Afirika sangakhalenso bwino popanda thandizo lalikulu la maiko onse limene silinayambe lalingaliridwapo.”
Kodi zimenezi zingachitike? Baibulo limanena motsimikiza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Salmo 146:3) Njira yothetsera mavuto aakulu a Afirika siili m’manja mwa maboma a anthu. Uli Ufumu wa Mulungu umene udzabweretsa mpumulo wokhalitsa—osati mu Afirika mokha koma padziko lonse.—Mateyu 6:10.
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
WHO/OXFAM