Mtembo Woumika Wopezedwa m’Madzi Oundana
YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU ITALY
Mwinamwake poyamba panaoneka ngati malo amene paphedwa munthu. Panali mtembo woumika wa munthu, mbali yake ina ili m’madzi oundana, nkhope yake itapenya pansi. Kodi inali imfa ya ngozi? Kuphedwa kobwezera? Kapena inali chabe imfa ina ya okwera mapiri amene amafa? Muli monse mmene zingakhalire, kodi iye anali kuchitanji kumalo otontholawo a Tirolean Alps okwezeka mamita 3,200 pamwamba pa nyanja? Kodi iye anali yani? Ndipo kodi anafa motani?
“ICEMAN,” dzina limene anapatsidwa atangopezedwa, kapena Homo tyrolensis, monga momwe asayansi amamutchera, anapezedwa mwangozi mu September 1991 ndi Ajeremani aŵiri okwatirana amene anali kukwera m’phiri lotchedwa Mount Similaun (mu Ötztaler Alps), pakati pa malire a Austria ndi Italy. Chilimwe chotentha kwambiri cha chakacho chinasungunula chipale chofeŵa chochuluka, chikumavumbula zinthu zokwiririka zimene zikanakhalabe zobisika—kaya ndi kwautali wotani? Ofufuza atatsimikizira za zokayikitsa zina zapoyamba za chotumbidwacho, thupilo linakanganulidwa m’madzi oundanawo, likumawonongeka polizula. Komabe, posapita nthaŵi kunadziŵika kuti sunali mtembo wamba. Pafupi ndi thupilo panali ziŵiya zosiyana kwambiri ndi zimene okwera mapiri amakono amagwiritsira ntchito pokwera kumalo okwezeka oterowo.
Ena anazindikira kuti mtembowo unali wakale kwambiri. Pambuyo pa kupima koyamba, Konrad Spindler, wa pa Innsbruck University, ku Austria, anapereka ndemanga yodabwitsa—yakuti thupi loumikalo lopezedwa pa Mount Similaun linali litakhala kwa zaka zikwi zambiri! Kupenda ndi kufufuza kowonjezereka pamalopo kunachititsa akatswiri kugamula kuti mtembo umene anali kupendawo unali “thupi la munthu lakale kwambiri lopezedwapo lili lamphumphu.” (Time, October 26, 1992) Akatswiri a zam’mabwinja amakhulupirira kuti Iceman, wopatsidwa dzina lopeka lakuti Ötzi (lotengedwa ku Ötztal, dzina la Chijeremani la chigwa chapafupipo), anafa m’ma 3000 B.C.E.
Pamene phindu la chotumbidwacho linazindikiridwa, akatswiri a zam’mabwinja anabwerera nthaŵi zambiri ku Mount Similaun kukafunafuna zinthu zakale zina zothandiza kuzindikira chimene chinachitika kwa munthuyo zaka mazana ambiri kalelo. Kodi iwo apezanji? Kodi nchifukwa ninji pakhala chifuno chachikulu chakudziŵa za mtembo woumika umenewo wokwiririka m’madzi oundana? Kodi kwakhala kotheka kuvumbula chilichonse cha zinsinsi za munthuyo?
[Chithunzi patsamba 12]
Ötzi, Iceman
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi: Archiv Österreichischer Alpenverein/Innsbruck, S.N.S. Pressebild GmbH