Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 5/8 tsamba 13-16
  • Njira Zodziŵira Chinsinsi cha Iceman

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Zodziŵira Chinsinsi cha Iceman
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Iye Anasungidwa Motani?
  • “Kazembe wa m’Nyengo za Middle Ages Wonyamula Mfuti”
  • Ötzi ndi Chitaganya Chake
  • Kudziŵa za Maganizo ndi chitaganya cha Iceman
    Galamukani!—1995
  • Mtembo Woumika Wopezedwa m’Madzi Oundana
    Galamukani!—1995
  • “M’mapiri Ake Mudzakumbamo Mkuwa”
    Nsanja ya Olonda—2013
Galamukani!—1995
g95 5/8 tsamba 13-16

Njira Zodziŵira Chinsinsi cha Iceman

KWA zaka mazana ambiri, Ötzi anali m’malo opumira abwino. Anali chigonere pamwambapo mamita 3,200 pamwamba pa nyanja m’phompho lopapatiza lodzaza madzi oundana limene linamtetezera ku mayendedwe a chiunda chapafupi cha madzi oundana. Thupi limeneli likanaumira mkati mwa chiunda cha madzi oundana, likanasweka kotheratu ndi kukokololedwa. Mwachionekere, malo ake otetezerekawo anamusunga bwino.

Mamita pang’ono chapafupipo panali ziŵiya zimene zinaoneka kukhala zogwiritsira ntchito m’moyo wake wa masiku onse: uta wa mtengo wopanda chingwe chake, thumba la chikopa cha mbaŵala lokhala ndi mivi 14 (iŵiri yomalizidwa kale kuti igwiritsiridwe ntchito, inayo yosamalizidwa), mpeni wamwala, nkhwangwa, chipangizo cholingaliridwa kukhala chosenzera katundu cha anthu akale, thumba la chikopa, chonyamulira cha khungwa la mtengo, ndi zidutswa za nsalu, limodzinso ndi ziŵiya ndi zinthu zina.

Pamene anapezedwa, Similaun Man (linanso la maina ake) anali chivalire zina za zovala zake ndipo anali ndi nsapato zachikopa zolongedwa udzu kuti asazizidwe. Pafupi ndi mutu wake panali “mphasa” yoluka ndi udzu. Zinali monga kuti, atatopa kwambiri ndi kuzizidwa madzulo ena, Iceman anagona tulo ndi “kudzaonanso” kuunika kwa usana pambuyo pa zaka zikwi zambirimbiri. Chopezedwacho chinali “chinthu chopereka chithunzi cha nyengoyo, chitaganya ndi anthu,” akutero katswiri wa zam’mabwinja Francesco Fedele, amene analongosola Similaun Man monga “thumba la mbiri yakale.”

Kodi Iye Anasungidwa Motani?

Si anthu onse amene amakhulupirira za njira imene Ötzi anasungidwira osawonongeka kwa nthaŵi yaitali kwambiri m’mikhalidwe yotero. “Kusungidwa kwake kuli kozizwitsa, ngakhale polingalira za chitetezo chake chonenedwacho cha phompho limene anapezedwamo,” ikutero Nature. Lingaliro limene tsopano likuoneka kukhala loyenera ndi lakuti kusungikako kunatheka ndi kusanganikana kwa “zochitika zitatu zosakayikika”: (1) kuumika kwachibadwa (kuphwa madzi m’thupi) chifukwa cha kuzizira, dzuŵa, ndi kuwomba kwa mphepo (yofunda ndi youma); (2) kuphimbidwa mofulumira ndi chipale chofeŵa kumene kunabisa thupilo ku zilombo; ndi (3) kutetezeredwa ku ziunda zoyenda za madzi oundana chifukwa cha kukhala m’phomphomo. Komabe ena samakhutira ngakhale ndi malongosoledwe ameneŵa, akumanena kuti mphepo siimafika pamwamba pautali umenewo kumbali imeneyi ya mapiri a Alps.

Komabe, zinthu zina zokhudza Iceman nzotsimikizirika. Kwakhala kotheka kutsimikizira kuti iye anali wazaka zakubadwa pakati pa 25 ndi 40, anali wotalika pafupifupi masentimita 160, ndipo anali wolemera makilogalamu pafupifupi 50. Anali wolimba ndi wamphamvu, ndipo tsitsi lake lobiriŵira linasamaliridwa bwino ndipo linali kumetedwa nthaŵi zonse. Kupenda DNA ya minofu yake kwaposachedwapa kwasonyeza kuti iye anali m’gulu limodzi la majini a anthu a chapakati ndi kumpoto kwa Ulaya. Mano ake okumbudzuka amasonyeza kuti ankadya mkate wolimba, kusonyeza kuti ayenera kuti anali mlimi, umboni ukumakhala mbewu ya tirigu yopezedwa m’zovala zake. Chokondweretsa nchakuti, kwakhala kotheka kutsimikizira kuti anafa chakumapeto kwa dzinja kapena kuchiyambi kwa chilimwe. Motani? M’thumba lake munapezeka zipatso za mthengo zosiyanasiyana zimene zimacha chakumapeto kwa dzinja; mwinamwake zinali zina za zakudya zake zotsirizira.

“Kazembe wa m’Nyengo za Middle Ages Wonyamula Mfuti”

Koma kodi Ötzi amavumbulanji? Magazini Achitaliyana otchedwa Archeo anafunsa mwachidule mafunso obutsidwa ndi kutumba kumeneko motere: “Kodi anali msilikali kapena wosaka nyama? Kodi anali munthu woyenda yekha, kodi anali kuyenda ndi gulu lake, kapenanso, kodi anali paulendo m’mapiri amenewo pamodzi ndi kagulu kapadera ka gulu lake? . . . Kodi anali yekha, pakati pa madzi oundana onsewo, kapena kodi tingayembekezere kupeza mitembo inanso?” Akatswiri ayesayesa kupeza mayankho makamaka mwa kupenda zinthu zopezedwa pa Mount Similaun ndi kuyesa kudziŵa ntchito zake. Pakhala kuperekedwa kwa malingaliro osiyanasiyana a chimene Ötzi anapezekera pamwambapo pa utali wa mamita oposa 3,200, koma lililonse la malingalirowo limatsutsidwa ndi mbali zina. Tiyeni tipende zitsanzo zingapo.

Uta, umene unalibe chingwe chake, ndi miviyo zikasonyeza mwamsanga kuti iye anali wosaka nyama. Kodi zimenezo zikuvumbula chinsinsicho? Mwinamwake, koma utawo, wotalika pafupifupi mamita 1.8, “unali waukulu kwambiri kwa munthu wamsinkhu umenewo,” akutero katswiri wina wa zam’mabwinja Christopher Bergman, ndipo “mosakayikira unali waukulu kwambiri kusakira nyama za mu Alps.” Kodi nchifukwa ninji iye angakhale ndi uta umene sakagwiritsira ntchito? Ndiponso, kuti munthu ayende m’mapiri, ayenera kusiya zolemera zonse, “zimene zikuchititsa kukhala kodabwitsa kwambiri kuti uta wa munthuyu ndi mivi yake 12 pa 14 inali yosamalizidwa, pamenenso zida zake (mpeni ndi nkhwangwa) zinali zokumbudzuka chifukwa cha kugwira ntchito kwa nthaŵi yaitali,” ikutero Nature.

Bwanji za nkhwangwa imene inapezedwa pa mamita oŵerengeka pafupipo? Poyamba, inalingaliridwa kukhala ya bronze, koma kupima kunasonyeza kuti, kwenikweni, inali ya mkuwa. Pachifukwa chimenechi ndi zina, akatswiri ambiri a zam’mabwinja amanena kuti Ötzi ndi wakale kwambiri kuchiyambi kwa nyengo yotchedwa Copper Age, ndiko kuti, zaka za chikwi chachinayi ndi chachitatu B.C.E. “Kupima kwa Carbon 14 . . . kunatsimikizira kuti iye anakhalako pakati pa zaka 4,800 ndi 5,500 zapitazo,” anatero magazini akuti Audubon.a Komabe, zinthu zina zingachititse akatswiri ena kuganiza kuti Iceman anali wakale kuposa pamenepo. Mwachionekere, sikotheka kuika Similaun Man m’nyengo imodzi ya kutsungula kwakale. Ponena za nkhwangwa ya mkuwa, katswiri wina wa zam’mabwinja akhulupirira kuti Ötzi “anali ndi chida chopangidwa mwaluso lalikulu limene silikanakhalako m’nyengo yake. Kunali ngati kupeza msilikali wa m’nyengo za middle age wonyamula mfuti. Kwenikweni, m’nyengo imeneyo, mkuwa unadziŵika Kummaŵa kokha.”

Ndiponso, monga momwe taonera kale, nkhwangwa ikanakhala chiŵiya chothandiza kwambiri kwa anthu a m’nthaŵi ya Iceman. Zotumbidwa zina, zonga ngati chimake cha mpeni wake, zinali zokonzedwa bwino kwambiri ndipo mwachionekere zinali “zinthu zaulemerero.” Koma ngati Ötzi anali munthu wapamwamba, mfumu, nchifukwa ninji anali yekha panthaŵi ya imfa yake?

Malinga ndi kunena kwa magazini a Popular Science, Konrad Spindler, wa pa University of Innsbruck, anapereka lingaliro lakuti: “Zimene poyamba zinalingaliridwa kukhala mphini zosazindikirika bwino zikufanana kwambiri ndi mfundo za m’mawondo kapena za akakolo zokumbudzuka ndi fupa la msana wake lowonongeka. Mwinamwake dokotala wa Iceman ankampatsa thandizo la mankhwala mwa kupsepsereza pamwamba pa khungu pamalo opweteka, ndiyeno kufikisa mankhwala pachilonda.”

Posachedwa, lingalirolo linaperekedwa pa msonkhano wa akatswiri a sayansi yotchedwa forensic medicine m’Chicago, kuti mwina Ötzi anali wothaŵa amene anamenyedwa ndipo wokhathamira ndi mwazi amene anafera m’malo obisalira pamene ena anali kumsaka. Kwatsimikiziridwa kuti anali ndi nthiti zingapo zothyoka ndi nsagwada yowonongeka. Komabe, sizikudziŵika kuti kuvulala kumeneku kunamchitikira liti—asanamwalire kapena pambuyo pake. Komabe, ngati kunalidi kumenyedwa, “nchifukwa ninji anapezeka akali ndi zipangizo zake zonse, ngakhale ‘zamtengo wapatali’?” zonga nkhwangwa ya mkuwa, ikufunsa motero Archeo.

Ofufuza akuganiza kuti maumboni amene alipo sali okwanira kupereka chithunzi chokhutiritsa, ndipo pakali mafunso ambiri osayankhidwa. Koma kuli kwachionekere kuti kutsungula kwa m’nthaŵi ya Ötzi kunali kolinganizika mwaluso kwambiri ndi kocholoŵana.

Ötzi ndi Chitaganya Chake

Polongosola chitaganya cha Similaun Man, akatswiri amazika malingaliro awo pa zotumbidwa m’malo a ku Alps amene amalingaliridwa kuti anakhalidwa ndi anthu a m’nthaŵi yake. Akatswiri a zam’mabwinja amatiuza kuti, ngakhale panthaŵi imeneyo, malo ena anali otukuka kuposa ena, ndipo ntchito zaluso zambiri zonga kupanga zinthu ndi mkuwa, zinachokera ku Middle East.

Malinga ndi lingaliro lina, mwinamwake Ötzi anakhala m’mudzi wina wa midzi ya alimi a m’dambo la mtsinje wotchedwa Adige River. Mtsinje umenewu unali njira yaikulu yochitirapo malonda yogwirizanitsa Italic Peninsula ndi Central Europe. Malo ambiri okhalamo anthu apezedwa m’malo osiyanasiyana m’dera limenelo la Alps, ngakhale m’malo okwezeka pafupifupi mamita 2,000. Midzi yaulimi ya m’nyengo imeneyo inali ya nyumba zitatu kapena zinayi, nthaŵi zina makumi angapo ngati zili zochuluka. Kodi zinali nyumba za mtundu wanji? Kufukula m’mabwinja kwavumbula pansi pokha pa nyumba, nthaŵi zambiri popamanthidwa ndi dothi. Nyumbazo zinali za chipinda chimodzi, kaŵirikaŵiri zokhala ndi malo a moto pakati pake ndipo nthaŵi zina ndi uvuni. Mwinamwake tsindwi linali losongoka, mofanana ndi nyumba zamakono zomangidwa pa mzati zimene zinapezedwa pafupi ndi nyanja zingapo za m’dera la mapiri a Alps. Mwinamwake m’nyumba iliyonse ya chipinda chimodzi munakhala banja limodzi.

Kodi panali kuchitirana zinthu kotani pakati pa zitaganya zoterozo za anthu osunga ziŵeto ndi alimi? Mosakayikira, panali malonda. Mwachitsanzo, nkhwangwa yopezedwa pa Mount Similaun inali yofanana ndi zija zosulidwa kutaliko cha kummwera, kugombe la Lake Garda, ndipo mwina chinali chinthu chogulitsana malonda. Ndiponso pakati pa ziŵiya za Ötzi panali miyala yantchito, zinthu zamalonda zamtengo wapatali panjira yodzera m’chigwa chotchedwa Adige Valley. Imodzi ya ntchito zimene zinachititsa anthu kuyendayenda kwambiri inali kusamutsa ziŵeto kwa panyengo yake. Monga momwe akuchitirabe ku Tirol lerolino, abusa anatsogolera nkhosa zawo m’zigwa za m’mapiri a Alps akumafunafuna malo amsipu atsopano. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zadziŵidwa ponena za kumene Iceman anachokera?

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze chidziŵitso chonena za kusadalirika kwa kupima kwa carbon-14, onani Awake! ya September 22, 1986, tsamba 21, ndi Life—How Did It Get Here?—By Evolution or by Creation?, tsamba 96, zofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mapu patsamba 14]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Iceman anapezedwa kumalire kwenikweni kwa Italy pa chiunda cha madzi oundana chotchedwa Similaun Glacier

GERMANY

AUSTRIA

Innsbruck

SWITZERLAND

SLOVENIA

ITALY

Bolzano

Similaun Glacier

Adriatic Sea

[Chithunzi patsamba 15]

X imasonyeza malo amene Ötzi anaferapo. Mphatika: 1. Nkhwangwa ya mkuwa, 2. Mpeni wamwala, 3. Mwinamwake njirisi, 4. Mbali yapafupi ndi mutu wa mpini wamtengo

[Mawu a Chithunzi]

Zithunzi 1-4: Archiv Österreichischer Alpenverein/Innsbruck, S.N.S. Pressebild GmbH

Chithunzi: Prof. Dr. Gernot Patzelt/Innsbruck

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena