Chimene Matchalitchi Anakhalira Chete
PA DECEMBER 8, 1993, Dr. Franklin Littel wa pa Baylor University analankhula za “choonadi chotsimikizika” chovutitsa mtima pamene anali ku Holocaust Memorial Museum ya United States. Kodi choonadi chimenecho chinali chiyani?
Choonadicho, anatero Littell, chinali chakuti “Ayuda mamiliyoni asanu ndi imodzi anasakidwa ndi kumaphedwa mkati mwenimweni mwa Dziko Lachikristu, ndi Aroma Katolika, Aprotesitanti, ndi a Eastern Orthodox obatizidwa amene sanachotsedwe m’tchalitchi, osati ngakhale kudzudzulidwa komwe.” Komabe, pali liwu limodzi limene linalankhula mosalekeza ponena za kuloŵerera kwa atsogoleri achipembedzo m’boma la Hitler. Ndipo liwulo, monga momwe taonera, linali la Mboni za Yehova.
Hitler anali Mroma Katolika wobatizidwa, mofanana ndi atsogoleri ambiri m’boma lake. Kodi nchifukwa ninji sanachotsedwe mumpingo? Nchifukwa ninji Tchalitchi cha Katolika sichinatsutse masoka omwe anthuŵa anali kuchita? Kodi nchifukwa ninji matchalitchi Achiprotesitanti nawonso anakhala chete?
Kodi nzoona kuti matchalitchi anakhaladi chete? Kodi pali umboni uliwonse wakuti anachirikiza nkhondo ya Hitler?
Mbali ya Tchalitchi cha Katolika
Wolemba mbiri Wachikatolika E. I. Watkin analemba kuti: “Ngakhale kuti nkopweteka kuvomereza, sitingakane kapena kunyalanyaza choonadi cha m’mbiri yakale, kaamba kofuna kupereka chithunzi chonyenga kapena kusonyeza kukhulupirika kwachiphamaso, chakuti Abishopu nthaŵi zonse achirikiza nkhondo zomenyedwa ndi boma la dziko lawo. . . . Ponena za mzimu wautundu wandewu, iwo alankhula monga cholankhuliramo cha Kaisara.”
Pamene Watkin ananena kuti mabishopu a Tchalitchi cha Katolika “anachirikiza nkhondo zonse zomenyedwa m’boma la dziko lawo,” anaphatikizapo nkhondo zoputa ena zomenyedwa ndi Hitler. Monga profesa wa Roma Katolika pa Vienna University, Friedrich Heer, anavomereza kuti: “M’mbiri ya Germany ya zochitika zenizeni, Mtanda ndi swastika zinayandikana kwambiri nthaŵi zonse, kufikira pamene swastika inalengeza uthenga wa chilakiko kuchokera m’nsanja za matchalitchi a Germany, mbendera za swastika zinali pa maguwa ansembe ndipo ophunzitsa zaumulungu Achikatolika ndi Achiprotesitanti, apasitala, nduna za tchalitchi ndi nduna za boma anavomereza chigwirizano ndi Hitler.”
Atsogoleri a Tchalitchi cha Katolika anapereka chichirikizo chonse pa nkhondo za Hitler kwakuti profesa wa Roma Katolika Gordon Zahn analemba kuti: “Mkatolika Wachijeremani yemwe anayembekezera atsogoleri ake achipembedzo kupereka chitsogozo chauzimu ndi malangizo a mmene adzatumikirira m’nkhondo za Hitler analandira mayankho amodzimodzi omwe akanalandira kwa wolamulira wa Nazi mwiniyo.”
Kulondola chitsogozo cha atsogoleri awo a tchalitchi kwa Akatolika kunalembedwa ndi Profesa Heer. Iye analemba kuti: “Pa Akatolika Achijeremani pafupifupi mamiliyoni makumi atatu ndi aŵiri—mwa amene mamiliyoni khumi ndi asanu ndi theka anali amuna—[anthu] asanu ndi aŵiri okha ndiwo anakana poyera ntchito ya nkhondo. Asanu ndi mmodzi a ameneŵa anali Aostriya.” Umboni waposachedwa umasonyeza kuti Akatolika ena angapo, ndiponso Aprotesitanti ena, anatsutsa Boma la Nazi molimba mtima chifukwa cha zikhulupiriro zawo. Ena anaphedwa ndithu, pamene panthaŵi imodzimodzi atsogoleri awo auzimu anali kuwapereka ku Ulamuliro wa Nazi.
Kodi Ena Amene Anakhala Chete Ndani, Ndipo Ndani Sanatero
Monga momwe taonera kale, Profesa Heer anaphatikiza atsogoleri Achiprotesitant pakati pa aja amene “anavomereza chigwirizano ndi Hitler.” Kodi nchoona chimenecho?
Aprotesitanti ambiri anadzipalamulira mlandu pokhala chete pa nkhondo za Hitler. Mwachitsanzo, atsogoleri achipembedzo otchuka okwanira 11 anakumana mu October 1945 kuti alembe kalata yotchedwa kuvomereza liwongo kwa ku Stuttgart. Iwo anati: “Tikudziimba mlandu ife eni posakhala olimba mtima kwenikweni kuvomereza zikhulupiriro zathu, pokhala osakhulupirika kwenikweni popereka mapemphero athu, pokhala osakondwa kwenikweni kusonyeza chikhulupiriro chathu, ndipo posakhala akhama kwenikweni posonyeza chikondi chathu.”
History of Christianity ya Paul Johnson inati: “Pa apasitala a Evangeliko 17,000, sanapose konse pa makumi asanu omwe analoŵa m’ndende kwa nthaŵi yaitali [kaamba kosachirikiza boma la Nazi] panthaŵi iliyonse.” Poyerekezera apasitala oterowo ndi Mboni za Yehova, Johnson analemba kuti: “Olimba mtima koposa anali Mboni za Yehova, amene analengeza poyera chitsutso chawo cha chiphunzitso kuyambira pachiyambi ndipo anavutika chifukwa cha zimenezo. Anakana kugwirizana kulikonse ndi boma la Nazi.”
Kalelo mu 1939, chaka chimene Nkhondo Yadziko II inayamba, Consolation inagwira mawu T. Bruppacher, mbusa Wachiprotesitanti, kukhala akunena kuti: “Pamene kuli kwakuti amuna amene amadzitcha Akristu alephera pa mayeso otsimikizira zonena zawo, mboni za Yehova zosadziŵika zimenezi, monga Akristu ofera chikhulupiriro, zikukana mosasunthika kupondereza chikumbumtima ndi kulambira mafano kwachikunja. Wolemba mbiri wamtsogolo ayenera tsiku lina kudzavomereza kuti amene anayamba kuima ndi kuyang’anizana molimba mtima ndi ukali wa chiŵanda cha Nazi anali anthu onenezedwa ndi onyodoledwa ameneŵa, osati matchalitchi aakulu . . . Iwo akana kulambira Hitler ndi Swastika.”
Mofananamo, Martin Niemoeller, mtsogoleri wa tchalitchi cha Chiprotesitanti amene anali mu msasa wachibalo wa Nazi, pambuyo pake anavomereza kuti: ‘Tiyenera kukumbukira moona mtima kuti, m’nyengo zonse, matchalitchi Achikristu nthaŵi zonse anavomereza kudalitsa nkhondo, asilikali, ndi zida ndipo anapemphera mwa njira yosakhala yachikristu konse kuti adani awo aphedwe.’ Anavomerezanso kuti: “Zonsezi ndi mlandu wathu ndi mlandu wa abambo athu, ndipo moonekeratu suli konse mlandu wa Mulungu.”
Ndiyeno Niemoeller anawonjezera kuti: “Ndipotu ife Akristu amakono tiyenera kuchita manyazi ndi otchedwa ampatukowo amene ali ophunzira Baibulo akhama [Mboni za Yehova], amene mazanamazana ndi zikwizikwi za iwo aloŵa m’misasa yachibalo ndi kuferamo chifukwa chakuti anakana kutumikira m’nkhondo ndipo anakana kuwombera mfuti anthu anzawo.”
Susannah Heschel, profesa wa maphunziro Achiyuda, anapeza zikalata za tchalitchi zotsimikizira kuti atsogoleri achipembedzo cha Lutheran anali ofunitsitsa, inde, olakalaka kuchirikiza Hitler. Anati anachita kupempha mwaŵi wa kusonyeza swastika m’matchalitchi awo. Kufufuza kwake kunasonyeza kuti atsogoleri achipembedzo ochuluka sanakakamizidwe kuchirikiza malingaliro a Hitler ndi malingaliro ake Achiariyani, koma anali okondwa kumchirikiza.
Popereka nkhani, Heschel amafunsidwa kaŵirikaŵiri ndi ziŵalo za tchalitchi kuti, “Kodi tikanachitanji?”
Iye amayankha kuti, “Mukanakhala monga Mboni za Yehova.”
Chimene Anakhalira Chete
Chifukwa chimene matchalitchi anakhalira chete chikuonekera. Ndi kaamba kakuti atsogoleri a Dziko Lachikristu ndi nkhosa zawo anali atasiya ziphunzitso zawo za Baibulo ndi kukonda kuchirikiza boma landale. Mu 1933 Tchalitchi cha Roma Katolika chinapanga pangano ndi Anazi. Kadinala wa Roma Katolika Faulhaber analembera Hitler kuti: “Kugwirana chanza kumeneku ndi Apapa . . . ndiko dalitso losayerekezeka. . . . Mulungu asungetu Nduna Yaikulu ya Boma [Hitler].”
Ndithudi, Tchalitchi cha Katolika ndi matchalitchi enanso anakhala atumiki a boma loipa la Hitler. Ngakhale kuti Yesu Kristu ananena kuti otsatira ake oona “siali a dziko lapansi,” matchalitchi ndi anthu awo anakhala mbali yothandiza kwambiri ya ulamuliro wa Hitler. (Yohane 17:16) Chotsatirapo nchakuti analephera kulankhula molimba mtima za zinthu zowopsa zimene Anazi anachita pa anthu omwe anawaponya m’misasa yawo yachibalo yopherako anthu.
Ndithudi, anthu angapo olimba mtima a tchalitichi cha Katolika, Protesitanti, ndi ena a zipembedzo zosiyanasiyana anaima ndi kutsutsa Boma la Nazi. Koma pamene ena analipirira ndi miyoyo yawo, atsogoleri awo auzimu omwe anati anatumikira Mulungu, anatumikira monga akapirikoni a Ulamuliro wa Nazi.
Komabe, panali liwu limodzi limene linalankhula molimba mtima kosalekeza. Ngakhale kuti kwakukulukulu ofalitsa nyuzi ananyalanyaza matchalitchi monga ochirikiza kwambiri zochitika za Anazi, Mboni za Yehova zinakakamizika kuvumbula ukathyali ndi chinyengo cha atsogoleri achipembedzo, zochita zawo zamtseri. M’magazini oyamba, ano asanakhaleko limodzinso ndi m’zofalitsa zonse za m’nyengo ya ma 1930 ndi ma 1940, analembamo milandu ya zipembedzo zimene zinakhala atumiki a Nazi.
Kudziŵikitsa Otsatira Oona a Kristu
Mboni za Yehova nzosiyana kotheratu ndi zipembedzo za dziko. Posakhala mbali ya dziko, sizimatenga mbali m’nkhondo za mitundu. Pomvera malangizo a Mulungu, ‘zasula malupanga awo kukhala zolimira.’ (Yesaya 2:4) Inde, potsatira malangizo a Kristu, zimakondana wina ndi mnzake. (Yohane 13:35) Izi zimatanthauza kuti izo sizimapita kunkhondo ndi kuvulazana dala wina ndi mnzake.
Ponena za kudziŵikitsa alambiri oona a Mulungu, Baibulo limanena momvekera bwino kuti: “Mmenemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: Yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake.”—1 Yohane 3:10-12.
Inde, zochitika za m’mbiri zasonyeza kuti Mboni za Yehova nthaŵi zonse zasonyeza chikondi kwa anthu anzawo, ngakhale mkati mwa mavuto aakulu. Pamene Hitler anamenya nkhondo mu Ulaya yense, Mboni zinaima nji poyang’anizana ndi nkhanza za Anazi zoyesa kuzikakamiza kuloŵa mumzimu wakuphana. Profesa Christine King anapereka chidule chabwino cha nkhaniyo kuti: “Mboni za Yehova zinalankhula mopanda mantha. Zinalankhula kuyambira pachiyambi. Zinalankhula ndi liwu limodzi. Ndipo zinalankhula molimba mtima, ndipo zimenezo zimaphunzitsa tonsefe kanthu kena.”
Kufikira pamene dzikoli lidzakhala m’chisungiko cha boma la Yehova, ndipo lopanda nkhondo ndi kuipa, Mboni za Yehova zidzapitirizabe kulankhula molimba mtima. Malinga ngati chili chifuniro cha Ambuye Mfumu Yehova, magazini ano adzavumbulabe zoipa za dziko lausatanali ndi kulengeza chiyembekezo choona chokha cha anthu, Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 6:9, 10.
[Zithunzi patsamba 27]
Nkhani za nyuzi za ku United States zinatsimikizira za kuchirikiza Nazi kwa tchalitchi
New York Post, August 27, 1940, Blue Final Edition, tsamba 15
The New York Times, December 7, 1941, Late City Edition, tsamba 33
The New York Times, September 25, 1939, Late City Edition, tsamba 6
[Chithunzi patsamba 29]
Mosiyana ndi matchalitchi, Mboni za Yehova zinalankhula molimba mtima kwa Anazi