Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 9/8 tsamba 20-26
  • Kuvumbula Zoipa za Nazi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuvumbula Zoipa za Nazi
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Pempho Lakuti Azindikiridwe
  • Kuukira Kuyambika
  • Kaimidwe ka Mboni Kosasunthika
  • Mboni Zivumbula Nkhanza za Anazi
  • Kuvumbula Zowopsa za m’Misasa Yachibalo
  • Anazi Athedwa Nzeru ndi Mboni
  • Kulaka Nkhalwe
  • Mboni za Yehova—Zinalimba Mtima Poyang’anizana ndi Chiopsezo cha Anazi
    Galamukani!—1998
  • Okhulupirika Olimba Mtima Anapambana Chizunzo cha Nazi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Umboni wa Chikhulupiriro Chawo
    Galamukani!—1996
  • Chimene Matchalitchi Anakhalira Chete
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 9/8 tsamba 20-26

Kuvumbula Zoipa za Nazi

M’MA 1920, pamene Germany anali kuyesetsa kulimbanso pambuyo pogonjetsedwa m’Nkhondo Yadziko I, Mboni za Yehova zinali zotanganitsidwa ndi kufalitsa mabuku ochuluka ofotokoza Baibulo. Zimenezi sizinangopereka chitonthozo ndi chiyembekezo kwa Ajeremani komanso zinawachititsa kuzindikira za kukula kwa ulamuliro pa zankhondo. Pakati pa 1919 ndi 1933, Mboni zinagaŵira mabuku, timabuku, kapena magazini pa avareji ya asanu ndi atatu kwa lililonse la mabanja pafupifupi 15 miliyoni mu Germany.

Magazini a Golden Age ndi a Consolation kaŵirikaŵiri anadziŵitsa anthu za zochitika zotsogolera ku nkhondo mu Germany. Mu 1929, kutatsala zaka zoposa zitatu Hitler asanayambe kulamulira, magazini Achijeremani a The Golden Age ananena molimba mtima kuti: “National Socialism ndi . . . chipani chimene chimachita zinthu . . . motumikira mdani wa munthu, Mdyerekezi.”

Kutatsala tsiku limodzi kuti Hitler atenge ulamuliro, The Golden Age ya January 4, 1933 inati: “Chipani cha National Socialism chikukula mochititsa mantha monga therezi lofuna kugumuka. Zikuoneka kukhala zosakhulupiririka kuti chipani cha ndale chimene chinali chaching’ono motero poyamba, cha malamulo achilendo motero, chingakule m’zaka zoŵerengeka chabe ndi kufika pamlingo wakuphimba kaimidwe ka boma la dzikolo. Komabe, Adolf Hitler ndi chipani chake cha National Socialism (Anazi) wakhoza kukhala ndi chipambano chimenechi.”

Pempho Lakuti Azindikiridwe

Hitler anakhala nduna yaikulu ya Germany pa January 30, 1933, ndipo patapita miyezi ingapo, pa April 4, 1933, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Magdeburg inalandidwa. Komabe, lamulolo linabwezedwa pa April 28, 1933, ndipo ofesiyo inabwezeretsedwa. Kodi chotsatirapo chinali chiyani?

Mosasamala kanthu za nkhanza yoonekeratu ya boma la Hitler, Mboni za Yehova zinakonza msonkhano m’Berlin, Germany, pa June 1933. Pamsonkhanowo panapezeka anthu 7,000. Pa June 25 Mbonizo zinamveketsa bwino lomwe zolinga zawo kuti: “Gulu lathu silili landale m’njira iliyonse. Chimene tingofuna ndicho kuphunzitsa Mawu a Yehova Mulungu kwa anthu, ndipo tikufuna kuchita zimenezo popanda wotiletsa.”

Motero Mboni za Yehova zinayesa mokhulupirika kunena zoona za ntchito yawo. Kodi chotulukapo chinali chiyani?

Kuukira Kuyambika

Kaimidwe kosasunthika kosaloŵa m’ndale ka Mboni, limodzi ndi kukhulupirika kwawo ku Ufumu wa Mulungu, zinali zosaloleka ndi boma la Hitler. Anazi sanafune kulekerera aliyense wokana kuchirikiza chiphunzitso chawo.

Pamene msonkhano wa ku Berlin unangomalizidwa, Anazi analandanso ofesi ya nthambi ku Magdeburg, pa June 28, 1933. Iwo anayamba kusokoneza misonkhano ya Mboni ndi kumazigwira. Posapita nthaŵi Mboni zinayamba kupitikitsidwa pantchito. Anaziloŵera m’nyumba zawo, kuzimenya, ndi kuzigwira. Pofika kumayambiriro kwa 1934 Anazi analanda Mboni matani 65 a mabuku ofotokoza Baibulo ndipo anakawatentha kunja kwa Magdeburg.

Kaimidwe ka Mboni Kosasunthika

Mosasamala kanthu za ziukiro zoyambirira zimenezi, Mboni za Yehova zinaima nji ndipo zinatsutsa poyera chitsenderezo chimenecho ndi chisalungamo. Kope la The Watchtower ya November 1, 1933 linali ndi nkhani yakuti “Musawawope.” Linakonzedwera makamaka Mboni Zachijeremani, likumazilimbikitsa kulimba mtima poyang’anizana ndi chitsenderezo chomakulacho.

Pa February 9, 1934. J. F. Rutherford, pulezidenti wa Watch Tower Society, anatumiza kalata yotsutsa zochita za Hitler akumati: “Ungapambane kutsutsa anthu onse, koma sungapambane kutsutsa Yehova Mulungu. . . . M’dzina la Yehova Mulungu ndi Mfumu Yake yodzozedwa, Kristu Yesu, ndikukuuza kuti upereke lamulo kwa nduna zonse ndi atumiki a boma lako kuti mboni za Yehova m’Germany ziloledwe kusonkhana mwamtendere ndi kulambira Mulungu popanda choletsa.”

Rutherford anapereka March 24 1934 kukhala tsiku lomaliza. Iye anati ngati chimasuko sichifika kwa Mboni Zachijeremani pofika tsikulo, maumboni a chizunzo adzafalitsidwa m’Germany monse ndi padziko lonse. Anazi anayankha pempho la Rutherford mwa kuwonjezera nkhanza, akumatumiza Mboni za Yehova zambiri ku misasa yachibalo yomangidwa chatsopano. Motero, zinali pakati pa akaidi oyambirira m’misasa imeneyi.

Mboni Zivumbula Nkhanza za Anazi

Monga momwe Mboni za Yehova zinali zitalonjezera, zinayamba kuvumbula nkhanza zochitika m’Germany. Mboni kuzungulira dziko lapansi zinalembera boma la Hitler zikumatsutsa zochita zake.

Pa October 7, 1934, mipingo yonse ya Mboni za Yehova m’Germany inasokhana kuti imve kuŵerengedwa kwa kalata imene inali kutumizidwa kwa akuluakulu a boma la Hitler. Iyo inati: “Pali kuwombana koonekeratu pakati pa lamulo lanu ndi lamulo la Mulungu . . . Choncho pano tikukudziŵitsani kuti zivute zitani tidzamvera malamulo a Mulungu, tidzasonkhana pamodzi kuphunzira Mawu Ake, ndipo tidzalambira ndi kutumikira Iye monga momwe Iye walamulilira.”

Patsiku limodzimodzi, Mboni za Yehova za m’maiko ena 49 zinakhala ndi misokhano yapadera ndipo zinatumiza telegramu yotsatirayi kwa Hitler: “Nkhanza yanu pa mboni za Yehova yasokoneza maganizo anthu abwino onse pa dziko lapansi ndipo ikunyoza dzina la Mulungu. Musazunzenso mboni za Yehova; apo phuluzi Mulungu adzakuwonongani pamodzi ndi chipani cha dziko lanu.”

Anazi anayankha posapita nthaŵi mwa kuwonjezera chizunzo chawo. Hitler iye mwini anafuula kuti: “Ndidzautha mtunduwu m’Germany!” Koma pamene chitsutso chinakula, mpamene kulimbika mtima kwa Mbonizo kunazamanso kwambiri.

Mu 1935, The Golden Age inavumbula njira zozunzira anthu zonga za Bwalo la Inquisition za boma la Nazi ndi azondi ake. Inavumbulanso kuti chinali cholinga cha chipani cha Hitler Youth kutayitsa achichepere Achijeremani chikhulupiriro chawo mwa Mulungu. Chaka chotsatira kampeni ya dziko lonselo ya Agestapo inachititsa zikwizikwi za Mboni kumangidwa. Posapita nthaŵi, pa December 12, 1936, Mboni zinachitapo kanthu mwa kuyamba kampeni yawo, zikumadzaza Germany yense ndi makope zikwizikwi a chigamulo chotsutsa chizunzo pa Mboni za Yehova.

Pa June 20, 1937, Mboni zimene zinali zomasukabe zinafalitsa uthenga wina umene sunabise kanthu ponena za chizunzo. Uthengawo unatchula maina a akuluakulu a boma ndi kusonyeza masiku ndi malo. Agestapo anazunguzika maganizo poona kuvumbula koteroko ndi kulimba mtima kwa Mboni pokuchita.

Chikondi chawo cha pa mnansi nchimene chinasonkhezera Mboni kuchenjeza anthu m’Germany kuti asapusitsidwe ndi maloto a ulamuliro wa zaka chikwi waulemerero wolonjezedwa ndi Ulamuliro wa Nazi. “Tiyenera kunena zoona ndi kupereka chenjezo,” kanatero kabuku kakuti Face the Facts kofalitsidwa mu 1938. “Timaona boma lotsenderezali . . . kukhala lopangidwa ndi Satana loikidwa m’malo mwa ufumu wa Mulungu.” Mboni za Yehova zinali pakati pa anthu oyamba kuzunzidwa ndi Anazi, koma izonso zinadandaula ndi kuzunzidwa kwa Ayuda, Apolishi, anthu opunduka, ndi ena.

Chigamulo chakuti “Chenjezo!,” chomwe chinalandiridwa pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova mu 1938 mu Seattle, Washington, U.S.A., chinati: “Afasisti ndi Anazi, zipani zazikulu zandale, zalanda ulamuliro wa maiko ambiri mu Ulaya mwa njira yolakwa . . . Anthu onse adzaponderezedwa, adzalandidwa ufulu wawo wonse, ndipo onse adzakakamizidwa kugonjera ku ulamuliro wa mfumu yotsendereza ndiyeno Bwalo la Inquisition lakalelo lidzaukanso.”

Rutherford nthaŵi zonse analankhula pawailesi, akumapereka nkhani zamphamvu pa mkhalidwe wausatana wa Nazi. Nkhanizo zinaulutsidwa pa dziko lonse lapansi mobwerezabwereza ndipo zinasindikizidwa kuti zifalitsidwe m’makope mamiliyoni ambiri. Pa October 2, 1938, anapereka nkhani yakuti “Chifasizimu kapena Ufulu,” mwa imene anadzudzula Hitler mosabisa.

Rutherford analengeza kuti: “Mu Germany anthu wamba amakonda mtendere. Mdyerekezi waika mtumiki wake Hitler paulamuliro, munthu wopenga, wankhanza, wanjiru ndi wankhalwe . . . Amazunza Ayuda mwankhanza chifukwa chakuti anali anthu a pangano la Yehova ndipo anali ndi dzina la Yehova, ndipo chifukwa chakuti Kristu Yesu anali Myuda.”

Pamene ukali wa Anazi pa Mboni za Yehova unakula kwambiri, mpamenenso mawu otsutsa a Mboni anakhala amphamvu kwambiri. Kope la Consolation ya May 15, 1940 linati: “Hitler ali mwana weniweni wa Mdyerekezi kwakuti zokamba zake ndi zigamulo zotuluka m’kamwa mwake zili ngati madzi otuluka m’chimbudzi.”

Kuvumbula Zowopsa za m’Misasa Yachibalo

Ngakhale kuti anthu ambiri sanadziŵe za kukhalapo kwa Misasa yachibalo mpaka mu 1945, kaŵirikaŵiri zinalongosoledwa mwatsatanetsatane m’zofalitsa za Watch Tower m’ma 1930. Mwachitsanzo, mu 1937 Consolation inasimba za kuyesa mpweya wa poizoni ku Dachau. Pofika mu 1940, zofalitsa za Mboni zinatchula misasa yosiyanasiyana yokwanira 20 ndipo zinalongosola za mikhalidwe yowopsa mmenemo.

Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zinali zodziŵa bwino lomwe zochitika za m’misasa yachibalo? Pamene Nkhondo Yadziko II inayamba mu 1939, munali kale Mboni zokwanira 6,000 m’misasa ndi m’ndende. Wolemba mbiri Wachijeremani Detlef Garbe akuyerekezera kuti Mboni panthaŵiyo zinali pakati pa 5 ndi 10 peresenti ya anthu onse m’misasa!

Pamsonkhano wina wonena za Mboni ndi Chipululutso cha Anazi, Garbe anati: “Mwa anthu 25,000 amene anavomera kukhala Mboni za Yehova kuchiyambi kwa Ulamuliro wa Nazi, pafupifupi 10,000 anamangidwa kwa utali wa nthaŵi wosiyanasiyana. Mwa ameneŵa, oposa 2,000 anaperekedwa ku misasa yachibalo. Izi zikutanthauza kuti Mboni za Yehova, kusiyapo Ayuda, ndizo zinazunzidwa koipitsitsa ndi a SS pa magulu onse a zipembedzo.”

Mu June 1940, Consolation inati: “Mu Poland munali Ayuda 3,500,000 pamene Germany anayamba nkhondo yake . . . , ndipo ngati malipoti amene amafika m’maiko a Kumadzulo ali olondola, kusakaza kwawo kukuoneka kuti kwafika patali.” Mu 1943, Consolation inati: “Mitundu yathunthu monga Agiriki, Apolishi ndi Asebu akuphedwa mosalekeza.” Pofika mu 1946, The Golden Age ndi Consolation anali atadziŵikitsa ndende zokwanira 60 pamodzi ndi misasa yachibalo.

Anazi Athedwa Nzeru ndi Mboni

Ngakhale kuti Anazi anayesa kuletsa kufalikira kwa mabuku a Watch Tower, mkulu wa boma ku Berlin anavomereza kuti: “Nkovuta kupeza malo obisika m’Germany kumene mabuku a Ophunzira Baibulo amasindikizidwa; palibe amene amanyamula maina kapena makeyala ndipo palibe amene angaulule mnzake.”

Ngakhale kuti Agestapo anayesayesa zolimba, sanakhoze kugwira oposa pa theka la Mboni zonse m’Germany panthaŵi iliyonse. Tangolingalirani kuthedwa nzeru kwa azondi a Nazi ochenjerawo—sanathe kugwira ndi kutontholetsa kagulu kakang’ono kameneka kapena kuletsa kufalikira kwa mabuku awo. Mabukuwo anafika m’makwalala ndipo ngakhale kupyola m’mawaya a minga ochinga misasa yachibalo!

Kulaka Nkhalwe

Anazi, amene anaonedwa kukhala akatswiri pa kuswa chikhulupiriro cha munthu, anayesa mothedwa nzeru kuti achititse Mboni za Yehova kuswa uchete wawo Wachikristu, koma analephera momvetsa chisoni. Buku lakuti The Theory and Practice of Hell linati: “Munthu sangakane kuti, m’maganizo, a SS anali ochepa pachitokoso choperekedwa kwa iwo ndi Mboni za Yehova.”

Ndithudi, Mbonizo, pochirikizidwa ndi mzimu wa Mulungu, zinapambana nkhondoyo. Wolemba mbiri Christine King, chansela wa Staffordshire University mu England, analongosola olimbana m’nkhondoyo kuti: “Winayo [Anazi] ali wamkulu, wamphamvu, wooneka kukhala wosagonjetseka. Winayo [Mboni] wamng’ono kwambiri, . . . wopanda chida chilichonse, koma chikhulupiriro chokha . . . Mboni za Yehova zinagonjetsa Gestapo wamphamvuyo pa chikhulupiriro.”

Mboni za Yehova zinali kagulu kakang’ono kamtendere kotsekeredwa mu ulamuliro wa Anazi. Komabe, izo zinamenya nkhondo ndi kupambana m’njira yawoyawo—nkhondo yomenyera ufulu wa kulambira Mulungu wawo, nkhondo ya kukonda mnansi wawo, ndi nkhondo ya kunena choonadi.

[Bokosi patsamba 22]

Mboni Zinali Pakati pa Oyamba kuperekedwa ku Misasa Yachibalo

MADAME Geneviève de Gaulle, mdzukulu wa Charles de Gaulle pulezidenti wa France, anali chiŵalo cha French Resistance. Atagwidwa ndi kuikidwa m’ndende pambuyo pake mu msasa wachibalo wa Ravensbrück mu 1944, anakumana ndi Mboni za Yehova. Pambuyo pa Nkhondo Yadziko II, Madame de Gaulle anakamba nkhani kuzungulira mu Switzerland monse ndipo analankhula kaŵirikaŵiri za umphumphu ndi kulimba mtima kwa Mboni. Pofunsidwa pa May 20, 1994, iye anati za izo:

“Zinali pakati pa oyamba kuperekedwa ku msasa wachibalo. Ambiri anali atafa kale . . . Timawadziŵira pa baji lawo lowadziŵikitsa. . . . Sizinaloledwe ngakhale mpang’ono pomwe kulankhula za zikhulupiriro zawo kapena kukhala ndi mabuku alionse achipembedzo, makamaka Baibulo, limene linaonedwa kukhala buku lalikulu la chipanduko. . . . Ndikudziŵa [wina mmodzi wa Mboni za Yehova], ndipo panali ena amene ndinauzidwa za iwo, amene ananyongedwa chifukwa chopezeka ndi masamba oŵerengeka a malemba a Baibulo. . . .

“Chimene ndinakhumbira kwambiri mwa iwo nchakuti akanatuluka kalekale mwa kungosaina kukana chikhulupiriro chawo. Kwenikweni, akazi ameneŵa, amene anaoneka kukhala ofooka kwambiri ndi othedwa mphamvu, anali olimba kuposa a SS, amene anali ndi mphamvu ndi zonse zimene akanagwiritsira ntchito. [Mboni za Yehova] zinali ndi nyonga yawo, ndipo inali kulimba mtima kwawo kumene palibe amene akanakugonjetsa.”

[Bokosi patsamba 23]

Mboni Zinavumbula za Kukhalako kwa Misasa Yachibalo

NGAKHALE kuti Auschwitz, Buchenwald, Dachau, ndi Sachsenhausen anali maina osadziŵika kwa anthu ambiri kufikira pambuyo pa Nkhondo Yadziko II, iwo anali odziŵika bwino lomwe kwa aŵerengi a The Golden Age ndi Consolation. Malipoti a Mboni za Yehova, amene anabedwa m’misasa yachibalo mwa njira yangozi kwenikweni ndi kufalitsidwa m’mabuku a Watch Tower, anavumbula cholinga cha mbanda cha Ulamuliro wa Nazi.

Mu 1933, The Golden Age inali ndi malipoti ambiri onena za kukhalapo kwa misasa yachibalo mu Germany. Mu 1938, Mboni za Yehova zinafalitsa buku lakuti Crusade Against Christianity, m’Chifrenchi, Chijeremani, ndi Chipolishi. Linalongosola mwatsatanetsatane ziukiro zankhanza zosiyanasiyana za Anazi pa Mboni ndipo inaphatikizapo zithunzi za misasa yachibalo ya Sachsenhausen ndi Esterwegen.

Wopata mphotho ya Nobel Dr. Thomas Mann analemba kuti: “Ndaŵerenga buku lanu ndi malipoti ake movutika mtima kwenikweni. Sinditha kufotokoza kunyansidwa ndi kuipidwa kumene ndikumva mumtima mwanga pamene ndakhala ndikutsatira zolembedwa zimenezi za kuipitsitsa kwa munthu ndi nkhanza yosaneneka. . . . Kukhala chete kudzangosonyeza kusasamala kwa dziko za makhalidwe abwino . . . Mwachita thayo lanu pofalitsa bukuli ndi kuulula zoona.”—Kanyenye ngwathu.

[Bokosi patsamba 25]

Khalidwe la Mboni m’Misasa Yachibalo

CHIFUKWA cha chikondi cha pa mnansi—anzawo a m’chipinda cha ndende, a mu msasa wa asilikali, a mu msasa wachibalo—Mbonizo sizinangoŵana ndi ena chakudya chauzimu chokha komanso chakudya chakuthupi chilichonse chimene zinali nacho.

Myuda wina amene anapulumuka mu msasa wachibalo wa Buchenwald anafotokoza kuti: “Kumeneko ndinakumana ndi a Bibelforscher. Anapereka umboni wa zikhulupiriro zawo nthaŵi zonse. Ndipotu palibe chimene chikanawaletsa kulankhula za Mulungu wawo. Anali othandiza kwambiri kwa akaidi anzawo. Pamene akuphawo anatumiza Ayuda ambirimbiri ku msasa wachibalo pa November 10, 1938, ‘Jehovah’s schwein,’ monga momwe alondawo anawatchera, anazungulira kugaŵira buledi kwa Ayuda okalamba ndi anjala, ngakhale kuti iwo anakhala masiku mpaka anayi osadya chakudya.”

Mofananamo, mkazi wina Wachiyuda woikidwa m’ndende mu msasa wachibalo wa ku Lichtenburg anati ponena za Mboni: “Anali anthu opanda mantha, amene anapirira moleza mtima mavuto omwe anakumana nawo. Ngakhale kuti akaidi osakhala Ayuda analetsedwa kulankhula ndi ife, akazi ameneŵa sanamvere lamulo limeneli. Anatipempherera monga ngati tinali a banja lawo, ndipo anatipempha kusagonja.”

[Bokosi patsamba 26]

Kuyesa Kukana za Chipululutso cha Nazi Kunaloseredwa

M’KOPE lake la September 26, 1945, Consolation inanena kuti mtsogolo pangakhale za kuyesa kutembenuza mbiri yakale ndi kukana zimene zinachitika. Nkhani yakuti “Kodi Chinazi Chawonongedwa?” inati:

“Amanenanena akulingalira kuti anthu adzaiŵala mwamsanga. Cholinga chawo ndicho kufafaniza mbiri yakumbuyo, kudzionetsa ngati ndi othandiza amakono, akumaphimba mbiri ya maupandu awo.”

Magaziniwo anapereka chenjezo ili: “Kufikira pamene Yehova amenya nkhondo pa Armagedo, Chinazi chidzapitiriza kukhala chikumbukiro chovutitsa mtima.”

[Chithunzi patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Zithunzi za misasa ya chibalozi zinali m’zofalitsa za Mboni mu 1937

[Chithunzi patsamba 21]

Antchito 150 pa ofesi ya nthambi ya Magdeburg ya Mboni za Yehova mu 1931

[Zithunzi patsamba 24]

Zofalitsa za Mboni za Yehova zivumbula mayanjano a tchalitchi ndi Nazi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena