Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 6/8 tsamba 24-27
  • Umboni wa Chikhulupiriro Chawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Umboni wa Chikhulupiriro Chawo
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chionetsero cha ku France
  • Zokumana Nazo za Munthu Mwini
  • Kutsegulira
  • Mmene Chinakhudzira Ena
  • Kuvumbula Zoipa za Nazi
    Galamukani!—1995
  • Okhulupirika Olimba Mtima Anapambana Chizunzo cha Nazi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Achimwemwe M’dziko Lopanda Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kodi a Mboni za Yehova Zinawathera Bwanji pa Nthawi Imene Anthu Ambirimbiri Anaphedwa mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi ku Germany?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 6/8 tsamba 24-27

Umboni wa Chikhulupiriro Chawo

CHAKA cha 1995 chinali chaka cha 50 chokumbukira chimasuko m’misasa yachibalo ya Anazi. Mu Ulaya monse, ozunzidwa ndi Anazi anakumbukira nthaŵi imeneyi mwa kuchita misonkhano yaikulu imene atsogoleri a Boma anafikapo ku Auschwitz, Bergen-Belsen, Buchenwald, Dachau, Ravensbrück, Sachsenhausen, ndi misasa ina. Lingaliro limodzi limene linali kubwerezedwa linali lakuti, “Tisaiŵale zimene zinachitika!”

Kaamba ka chifukwa chimenechi Mboni za Yehova zinasonyeza chionetsero ku Ulaya mkati mwa chaka chokumbukiracho. Zambiri za Mbonizo zinamangidwa ndi boma la Hitler chifukwa cha kukana kwawo kuchitira suluti Hitler ndi kuchirikiza nkhondo. Kuyambira mu 1933 ndi mtsogolo mwake, zikwi zambiri za izo zinamangidwa, ndipo zambiri zinafa chifukwa cha zimene anazichitira.

Komabe, zokumana nazo zawo sizimadziŵika kwambiri ndi anthu. Zimenezi zayambitsa mawu akuti “anthu ochitiridwa nkhanza oiŵalidwa m’mbiri.” Gulu la Mboni zomwe zili ndi moyo linasonyeza chikhumbo cha kukumbukira mabanja awo ndi mabwenzi amene anazunzidwa, kumangidwa, kusautsidwa, kapena kuphedwa mwambanda ndi kudziŵikitsa umboni wa chikhulupiriro ndi kulimba mtima kumene a Bibelforscher ameneŵa anasonyeza, dzina limene Mboni za Yehova zinali kudziŵidwa nalo m’misasa yachibalo.

Pa September 29, 1994, United States Holocaust Memorial Museum, ya ku Washington, D.C., inachita msonkhano wonena za Mboni za Yehova m’misasa yachibalo. Misonkhano iŵiri yaikulu ya kukumananso kokumbukira inachitidwa mu France ndi opulumuka m’misasa, pa March 28, 1995, ku Strasbourg ndipo pa March 30, ku Paris. Kunali kochititsa nthumanzi kumva amuna ndi akazi ameneŵa amene tsopano ali okalamba, amene akali okhulupirikabe kwa Mulungu pambuyo pa zaka 50, akumasimba zokumana nazo zawo. Pa April 27, msonkhano wofanana ndi umenewo unachitidwa pafupi ndi Berlin, ku Brandenburg, Germany, kumene Mboni zambiri zinaphedwa mwa kudulidwa mutu. Patsiku lotsatira, ambiri a opulumukawo anafika pa zochitika zolinganizidwa ndi boma la Brandenburg napita ku misasa yosiyanasiyana.

Chionetsero cha ku France

Pakuonananso kumeneku, chionetsero cha mutu wakuti “Mémoire de Témoins” (Umboni wa Mboni) chinasonyezedwa. Kuyambira May 1995 mpaka April 1996, chinasonyezedwa m’mizinda 42 mu France ndi m’mizinda ina yosiyanasiyana mu Belgium ndi m’madera achifalansa a Switzerland. Makamaka, amuna ndi akazi a m’chionetsero chimenechi ndiwo Mboni za Yehova Mulungu. Komanso ali mboni za kuvutika kumene iwowo ndi ena anapirira m’misasa yachibalo. Ndiwo umboni wamoyo wa lingaliro la kusalekerera kumene kunabala mavuto ndi imfa kwa anthu mamiliyoni ambiri chifukwa cha fuko lawo kapena chipembedzo. Ndiponso, umboni wa Mbonizo ukusonyeza mmene otchedwa kuti Akristu anakondera mesiya wachinyengo, Hitler, m’malo mwa Yesu Kristu; kuda m’malo mwa kukonda mnansi; ndi chiwawa.

Chionetserocho chinali ndi magulu 70, kuyambira pa nthaŵi ya zochitika—kutsegulidwa kwa misasa ya Dachau ndi Oranienburg, mu March 1933; mpambo wa Nuremberg Laws “wotetezera mwazi wa German,” mu September 1935; Anschluss, kapena kugwirizanitsidwa kwa Austria ndi Germany, mu March 1938; Kristallnacht (Usiku wa Krustalo), mu November wa chaka chimodzimodzicho, mmene masitolo zikwi zambiri a Ayuda anafunkhidwa ndipo anthu oposa 30,000 anagwidwa ndi kutumizidwa kwina; chiletso chomadza mwapang’onopang’ono pa Mboni za Yehova; kuloŵereredwa kwa Soviet Union, mu June 1941; ndi kuphera chifundo odwala misala, kuyambira 1939 mpaka 1941.

Magulu angapo anasonyeza kuphunzitsidwa mwambo kwa achichepere m’gulu la Hitler Youth [Anyamata a Hitler] ndi chikondwerero chimene misonkhano yaikulu ya Nazi ku Nuremberg inachititsa pa anthu. Zithunzithunzi zinakumbutsa kukana kwa Mboni za Yehova kulumbira kukhulupirika kwa führer ndi kuchitira suluti Hitler. Magulu ena anasonyeza mmene Mboni za Yehova zinalili anthu onenezedwa monama ndi mmene, kuyambira 1935, zinagaŵirira magazini ndi matrakiti ovumbula nkhanza yoipitsitsa ya Nazi.

Zokumana Nazo za Munthu Mwini

Pafupifupi magulu 40 anasimba za zokumana nazo za amuna ndi akazi wamba a mu Ulaya yense amene anazunzidwa ndipo ngakhale kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Opulumuka m’misasa anachirikiza chionetserocho mwa kukhalapo kwawo, ndipo ofikapo anawamvetsera mwatcheru. Ana anachita kakasi pamene Louis Arzt anasimba nkhani yake. Poyamba anali kukhala ku France, anachotsedwa kwa makolo ake ndi kutumizidwa ku Germany chifukwa chokana kunena kuti “Tamandani Hitler!” kusukulu. “Msilikali wa SS anandimenya chifukwa cha kukana kuchitira suluti Hitler. Anandikwapula zikoti 30. Patapita masiku aŵiri anandigwira papheŵa nayesa kusokoneza malingaliro anga. ‘Talingalira za amako. Angakondwere kwambiri kukuona. Chinthu chokha chimene ufunikira kuchita ndicho kunena kuti “Tamandani Hitler!” ndipo udzakwera sitima.’ Zinali zovuta kwa mwana wazaka 12,” anawonjezera motero. Ambiri anakhudzidwa mtima ndi zokumana nazo za Joseph Hisiger amene anasinthanitsa phoso lake la buledi ndi Baibulo la mkaidi mnzake wachiprotesitanti.

Kufunsa otumizidwa kwina kojambulidwa pa vidiyo kunali mbali ina ya chionetserocho. Kufunsa kwina kunachitidwa kumalo a misasayo—mwachitsanzo, ku Ebensee ku Austria ndi ku Buchenwald ndi ku Sachsenhausen ku Germany. Ofunsidwa ena anasimba za mbali zosiyanasiyana za moyo wa m’misasa kapena za Mboni zimene zinatumizidwa kwina zikali ana.

Kutsegulira

Mwambo waufupi unatsegulira chionetsero chilichonse, pamene woimira otumizidwa kwina akalewo anafotokoza za kukana Chinazi kwauzimu kwa Mboni za Yehova. Otumizidwa kwina osakhala Mboni ndiponso olemba mbiri angapo ndi akuluakulu ena a boma, kuphatikizapo yemwe kale anali nduna ya boma la France, anavomeranso atapemphedwa kudzalankhula.

Yemwe kale anatumizidwa kwina amene anadziŵa Mboni za Yehova ku Buchenwald ananena kuti ponena za izo: “Sindikudziŵanso gulu lina lililonse la otumizidwa kwina, kusiyapo Ayuda, limene analichitira monyazitsa ngati iwo: kumenyedwa, kunyazitsidwa, kutukwanidwa, kupatsidwa ntchito zonyansitsitsa. Popanda chikhulupiriro chawo, sakanatha kuchirimika. Ndimawachitira ulemu waukulu ndi kuwakhumbira.”

Mmene Chinakhudzira Ena

Anthu oposa 100,000 anafika pa chionetserocho. M’malo ena anthu mazana ambiri, kuphatikizapo achichepere ambiri, anaima pamzere kuti aloŵe m’holo ya chionetsero. Odzaonerera ambiri anasonyeza malingaliro awo ndi mawu angapo m’buku la alendo. Mwachitsanzo, wachichepere wina analemba kuti: “Dzina langa ndine Sabrina. Ndili ndi zaka khumi zakubadwa ndipo ndikufuna kukhala wolimba mtima monga Ruth kuti ndikondweretse Yehova.”a

Nawonso ofalitsa nkhani anasimba za chionetserocho. Kulikonse, m’tauni iliyonse nkhani imodzi kapena ziŵiri zinatuluka m’manyuzipepala akumaloko. Ndiponso, nyumba za wailesi zakumaloko kaŵirikaŵiri zinafalitsa za chionetserocho ndi kuulutsa maprogramu onena za kufunsidwa kwa omwe kale anatumizidwa kwina. Wailesi yakanema yakumaloko inapereka malipoti achidule. Lipoti lina la pawailesi yakanema linanena kuti chionetserocho chinali “nkhani yomveka komanso yowopsa imene ikusonyeza zenizeni ponena za nkhanza yosasimbika. ‘Umboni wa Mboni’ wochirikiza ulemu umene sungachotsedwe.”

Kwa opulumukawo, kukumbukira zaka 50 za chimasukocho kudzapitirizabe kukhala kokhomerezeka m’maganizo mwawo. Ngakhale kuti kukumbukira zinthu zopwetekazo sikunali kokhweka nthaŵi zonse, mwa kuuza ena ndi kukumbutsa zochitikazo, Mbonizo zinakhoza kulimbitsa chikhulupiriro cha ena. Anauyesa mwaŵi kukhala ndi phande m’chionetsero chimenechi ndi kuthetsa malingaliro ena olakwika ndi umbuli umene ukalipo patapita zaka 50. Pa zonsezo, anapeza chikhutiro pa kudziŵa kuti umboni wawo umapereka ulemu kwa Yehova, Mulungu wawo, ndi kutsimikizira kuti ena sadzaiŵala konse zimene anapirira monga Mboni zake.

[Mawu a M’munsi]

a Ruth Danner anatumizidwa kwina pa usinkhu wa zaka zisanu ndi zinayi limodzi ndi makolo ake ndipo anamangidwa m’misasa isanu ndi umodzi yosiyanasiyana. Onani 1980 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., tsamba 105.

[Chithunzi patsamba 24]

Nkhani za mu “The Golden Age” zinatsutsa nkhanza ya Chinazi

[Chithunzi patsamba 24]

Magulu 70 anasimba nkhani zawo za kuzunza kwa Nazi amuna, akazi, ndi ana amene anakana kuleka chikhulupiriro chawo

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Zina za Mboni za Yehova zimene zinatumizidwa kwina ndi kumangidwa ndi boma la Hitler zinasimba nkhani zawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena